Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Zimene Zachitika M’zaka 100 Zimene Ufumu Wakhala Ukulamulira

Zimene Zachitika M’zaka 100 Zimene Ufumu Wakhala Ukulamulira

“Mulungu wamtendere . . . akukonzekeretseni ndi chilichonse chabwino kuti muchite chifuniro chake.”—AHEB. 13:20, 21.

NYIMBO: 13614

1. Kodi Yesu anasonyeza bwanji kuti ankakonda kulalikira za Ufumu?

YESU ali padziko lapansi, ankakonda kulalikira za Ufumu wa Mulungu. Baibulo limasonyeza kuti iye anatchula za Ufumu wa Mulungu maulendo oposa 100. Zimenezi zikusonyeza kuti iye ankaona kuti Ufumuwo ndi wofunika kwambiri.—Werengani Mateyu 12:34.

2. (a) Kodi n’kutheka kuti panali anthu angati pamene Yesu anapereka lamulo la pa Mateyu 28:19, 20? (b) Kodi tikudziwa bwanji kuti ambiri mwa anthuwa anadzakhala Akhristu?

2 Tsiku lina Yesu ataukitsidwa, anakumana ndi anthu oposa 500. (1 Akor. 15:6) N’kutheka kuti pa nthawiyi m’pamene anapereka lamulo lakuti otsatira ake azikalalikira “anthu a mitundu yonse.” * Koma ntchito imene anawauza kuti agwireyi sinali yophweka. Iye ananeneratu kuti ntchito yolalikirayi idzachitika mpaka “m’nyengo ya mapeto a nthawi ino.” Choncho tikamagwira nawo ntchito imeneyi timathandiza kuti ulosiwu ukwaniritsidwe.—Mat. 28:19, 20.

3. Kodi m’nkhaniyi tikambirana chiyani?

3 Yesu atauza ophunzira ake kuti azilalikira, ananenanso kuti: “Ine ndili pamodzi ndi inu.” (Mat. 28:20) Choncho iye analonjeza kuti adzapitiriza kuwatsogolera pa ntchitoyi n’kuwathandiza kuti azilalikira padziko lonse. Nayenso Yehova amatipatsa “chilichonse chabwino” kuti tizigwira bwino ntchito imeneyi. (Aheb. 13:20, 21) M’nkhaniyi, tikambirana (1) zinthu zimene takhala tikugwiritsa ntchito, (2) njira zosiyanasiyana zolalikirira ndiponso (3) maphunziro amene amatithandiza pa ntchito yolalikira. Choyamba, tiyeni tikambirane zinthu zina zimene takhala tikugwiritsa ntchito m’zaka 100 zapitazi.

ZINTHU ZIMENE ZATITHANDIZA PA NTCHITO YOLALIKIRA

4. Kodi zida zosiyanasiyana zatithandiza bwanji pa ntchito yolalikira?

4 Yesu anayerekezera “mawu a ufumu” ndi mbewu yofesedwa panthaka zosiyanasiyana. (Mat. 13:18, 19) Mlimi amagwiritsa ntchito zida zosiyanasiyana. M’zaka zapitazi, Mfumu yathu Yesu watipatsanso zida zosiyanasiyana zoti tizigwiritsa ntchito. Zida zina tinazigwiritsa ntchito kwa zaka zochepa zokha pomwe zina zikutithandizabe mpaka pano. Komabe zida zonsezi zatithandiza kuti tizilalikira mwaluso komanso kuti anthu amve uthenga wathu mosavuta.

5. Kodi kuyambira mu 1933, abale ndi alongo ankagwiritsa ntchito chiyani, ndipo ankazigwiritsa ntchito bwanji?

5 Kuyambira mu 1933, abale ndi alongo ankagwiritsa ntchito timakadi tolalikirira. Timakaditi tinkakhala ndi uthenga wachidule wa m’Baibulo ndipo nthawi zina pankatuluka timakadi tina tokhala ndi uthenga watsopano. Pogwiritsa ntchito timakadi timeneti, abale ndi alongo sankalankhula mawu ambiri. M’bale wina amene anayamba kugwiritsa ntchito timakadi tolalikirira ali ndi zaka 10, anati: “Tinkangonena kuti, ‘Kodi mungawerenge kakhadika?’ Munthuyo akawerenga, tinkamugawira mabuku n’kumapita.”

6. Kodi timakadi tolalikirira tinkathandiza bwanji abale ndi alongo?

6 Timakaditi tinkathandiza abale ndi alongo m’njira zosiyanasiyana. Akhristu ena ankafunitsitsa kulalikira koma anali amanyazi ndipo ankadzikayikira. Koma ena anali olimba mtima moti akangokumana ndi munthu, ankamuuza zonse zimene ankadziwa ndipo nthawi zina sankalankhula mwaulemu. Koma timakadi timeneti tinkathandiza kwambiri abale ndi alongo onsewa chifukwa tinkafotokoza uthenga wa m’Baibulo mwachidule ndiponso momveka bwino.

7. Kodi abale ndi alongo ankakumana ndi mavuto ati akamagwiritsa ntchito timakadi polalikira?

7 Nthawi zina ankakumana ndi mavuto ena pogwiritsa ntchito timakaditi. Mlongo wina amene wakhala wa Mboni kwa nthawi yaitali, dzina lake Grace, ananena kuti: “Nthawi zina anthu ankanena kuti, ‘Bwanji osangondiuza zimene zili pakhadipo?’” Anthu ena sankatha kuwerenga pomwe ena ankaganiza kuti tangowapatsa khadilo ndipo ankalowa nalo m’nyumba n’kutseka chitseko. Nthawi zina, anthu ena odana nafe ankang’amba khadilo. Ngakhale zinali choncho, timakadi tinathandiza abale ndi alongo kuphunzira kulalikira anthu osiyanasiyana n’kuwauza za Ufumu wa Mulungu.

8. Kodi anthu ankagwiritsa ntchito bwanji galamafoni? (Onani chithunzi patsamba 26.)

8 M’ma 1930 ndi m’ma 1940, Akhristu ankagwiritsa ntchito galamafoni ndipo abale ena ankangoitchula kuti Aroni chifukwa chakuti inkawalankhulira. (Werengani Ekisodo 4:14-16.) Abale ndi alongo akakhala mu utumiki ankapempha anthu kuti amvetsere nkhani ya m’Baibulo ya maminitsi pafupifupi 5, kenako ankawapatsa mabuku. Panyumba zina, banja lonse linkasonkhana kuti limvetsere nkhaniyo. Mu 1934, gulu linayamba kupanga lokha magalamafoniwa kuti anthu aziwagwiritsa ntchito mu utumiki. Patapita nthawi, panali nkhani zokwana 92 zimene anthu ankatha kuzigwiritsa ntchito.

9. Kodi galamafoni inathandiza bwanji pa ntchito yolalikira?

9 Munthu wina atamvetsera nkhani ina, anapempha kuti abwereke galamafoni n’cholinga choti anthu okhala nawo pafupi amvenso uthenga wa Ufumu. M’bale amene anamubwereka galamafoniyo atapitanso kwa munthuyo, anapeza kuti kuli anthu ambiri ofuna kuphunzira. Ambiri mwa anthuwo anadzabatizidwa. Komanso ana awiri a munthu amene anabwereka galamafoniyo anapita ku Sukulu ya Giliyadi n’kukakhala amishonale kudziko lina. Galamafoni inathandizanso anthu ambiri kuti ayambe kulalikira. Kenako Sukulu ya Utumiki wa Mulungu inakhazikitsidwa ndipo anthu a Yehova anayamba kuphunzitsidwa kuti azilalikira mwaluso.

NJIRA ZOSIYANASIYANA ZOLALIKIRIRA

10, 11. Kodi manyuzipepala ndi wailesi zinathandiza bwanji kuti anthu amve uthenga wathu?

10 Yesu wakhala akutsogolera atumiki a Yehova kuti azigwiritsa ntchito njira zosiyanasiyana polalikira uthenga wabwino. Njirazi zinali zothandiza kwambiri pa nthawi imene Akhristu anali ochepa. (Werengani Mateyu 9:37.) Mwachitsanzo, kale tinkagwiritsa ntchito manyuzipepala polalikira. Mlungu uliwonse M’bale Russell ankalemba nkhani n’kuzitumiza kuti zikasindikizidwe m’manyuzipepala a ku United States, ku Canada komanso ku Europe. Pofika chaka cha 1913, nkhani za M’bale Russell zinkasindikizidwa m’manyuzipepala okwana 2,000 ndipo anthu pafupifupi 15 miliyoni ankaziwerenga.

11 M’bale Russell atamwalira, gulu lathu linayamba kulalikira pogwiritsa ntchito wailesi. Ndipo pa 16 April, 1922, M’bale Joseph F. Rutherford anakamba nkhani yake yoyamba pa wailesi ndipo anthu pafupifupi 50,000 anamvetsera nkhaniyi. Kenako pa 24 February, 1924, tinayamba kugwiritsa ntchito wailesi yathu yotchedwa WBBR. Nsanja ya Olonda ya December 1, 1924 inati: “Tikayerekezera ndi njira zina, tikuona kuti wailesi ikuthandiza kuti anthu ambiri amve uthenga wathu ndipo njirayi siwononga ndalama zambiri.” Nyuzipepala komanso wailesi zinathandiza kuti anthu ambiri a m’madera amene munali abale ochepa amve uthenga wabwino.

Abale ndi alongo ambiri amakonda kulalikira m’malo opezeka anthu ambiri ndipo amasonyeza anthu webusaiti yathu ya jw.org (Onani ndime 12 ndi 13)

12. (a) Kodi inuyo mumakonda kulalikira m’malo ati opezeka anthu ambiri? (b) N’chiyani chingatithandize kuti tisamaope kulalikira m’malo opezeka anthu ambiri?

12 Masiku ano, gulu la Yehova limatilimbikitsa kuti tizilalikira m’malo opezeka anthu ambiri monga m’madepoti, m’malo oimika magalimoto komanso m’misika. Kodi mumachita mantha kulalikira m’malo oterewa? Ngati ndi choncho, mungachite bwino kupemphera komanso kuganizira zimene woyang’anira woyendayenda wina ananena. Iye anati: “Timaona kuti utumiki uliwonse watsopano umatipatsa mwayi wosonyeza kuti ndife okhulupirika ndiponso kuti timafunitsitsa kutumikira Yehova m’njira iliyonse imene watipempha.” Kuchita utumiki uliwonse ngakhale umene sutisangalatsa kwenikweni kumatithandiza kuti tizidalira kwambiri Yehova ndiponso kukhala naye pa ubwenzi wolimba.—Werengani 2 Akorinto 12:9, 10.

13. (a) Kodi webusaiti yathu ikuthandiza bwanji anthu? (b) Fotokozani zimene mwachita posonyeza anthu webusaitiyi.

13 Abale ndi alongo ambiri amakonda kusonyeza anthu webusaiti yathu ya jw.org. Pa webusaitiyi anthu amatha kuwerenga kapena kupanga dawunilodi mabuku athu m’zilankhulo zoposa 700. Tsiku lililonse anthu oposa 1.6 miliyoni amatsegula webusaiti yathuyi. Choncho webusaitiyi ikuthandiza anthu ambiri, ngakhale a kumadera akutali, kuti amve uthenga wabwino.

MAPHUNZIRO OTITHANDIZA KUTI TIZILALIKIRA MWALUSO

14. Kodi atumiki a Mulungu anayenera kuphunzitsidwa chiyani, ndipo ndi sukulu iti imene inawathandiza?

14 M’nkhaniyi takambirana zinthu komanso njira zimene takhala tikugwiritsa ntchito polalikira. Tsopano tiyeni tikambirane maphunziro amene akhala akutithandiza kuti tizilalikira mwaluso. Maphunzirowa anali ofunika kwambiri kuti abale azidziwa zochita akapeza anthu otsutsa kapena ofuna kudziwa zambiri. Ndiyeno M’bale Nathan H. Knorr anazindikira ubwino wophunzitsa anthu kuti azilalikira mwaluso ndipo n’zosakayikitsa kuti mzimu wa Yehova ndi umene unamuthandiza. Choncho mu 1943, Sukulu ya Utumiki wa Mulungu inakhazikitsidwa m’mipingo ndipo yakhala ikuthandiza anthu kuti aziphunzitsa mwaluso.

15. (a) Fotokozani zimene zinachitikira anthu ena akukamba nkhani m’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu. (b) Kodi inuyo mukuona kuti Yehova wakuthandizani bwanji mogwirizana ndi lemba la Salimo 32:8?

15 Pamene sukuluyi inkayamba, panali anthu ambiri amene ankavutika kulankhula pa gulu. Mwachitsanzo, m’bale wina amakumbukira zimene zinachitika atapatsidwa nkhani yake yoyamba mu 1944. Iye anauzidwa kuti akambe nkhani yofotokoza za Doegi, yemwe amangotchulidwa m’mavesi 5 okha m’Baibulo. M’baleyu anati: “Ndinkachita mantha kwambiri moti manja, mano komanso mawondo anga ankanjenjemera.” Iye ananenanso kuti: “Nkhaniyi ndinangoikamba maminitsi atatu okha. Kunena zoona, ulendo woyambawu ndinavutika kwambiri koma sindinasiye kukamba nkhani kupulatifomu.” Ana nawonso ankalembetsa m’sukuluyi. Woyang’anira woyendayenda amene tamutchula kale uja amakumbukira zimene mwana wina wamng’ono anachita. Iye anati: “Kamwanako katangoyamba nkhani yake kanachita mantha kwambiri mpaka kuyamba kulira. Koma sikanasiye kukamba mpaka kanamaliza nkhaniyo kakulirabe.” Mwina inunso mumaopa kuyankha pa misonkhano kapena kukamba nkhani. Ngati ndi choncho, muyenera kupempha Yehova kuti akuthandizeni. Iye anathandiza anthu amene tatchulawa, choncho akhoza kukuthandizaninso inuyo.—Werengani Salimo 32:8.

16. (a) Kodi poyamba, cholinga cha Sukulu ya Giliyadi chinali chiyani? (b) Kodi sukuluyi inasintha bwanji kuyambira mu 2011?

16 Palinso maphunziro ena amene amathandiza atumiki a Yehova. Mwachitsanzo, Sukulu ya Giliyadi yathandiza amishonale komanso abale ndi alongo ena. Mlangizi wina ananena kuti cholinga cha sukuluyi “ndi kuthandiza ophunzira kuti azikonda kwambiri ntchito yolalikira.” Sukulu ya Giliyadi inatseguliridwa mu 1943 ndipo panopa anthu oposa 8,500 aphunzitsidwa ndipo atumizidwa m’mayiko pafupifupi 170. Kuyambira mu 2011, anthu amene amaitanidwa kusukuluyi ndi amene ali kale mu utumiki wapadera monga apainiya apadera, oyang’anira madera, atumiki a pa Beteli komanso amishonale amene sanalowe sukuluyi.

17. Kodi maphunziro a ku Sukulu ya Giliyadi athandiza bwanji?

17 Kodi maphunziro a ku Sukulu ya Giliyadi athandiza bwanji? Tingayankhe funsoli tikaganizira zimene zinachitika ku Japan. Mu August 1949, kunali ofalitsa osakwana 10 koma m’chakachi kunabwera amishonale 13 kudzathandiza pa ntchito yolalikira. Panopa, m’dzikoli muli ofalitsa pafupifupi 216,000 ndipo pafupifupi hafu ya ofalitsawo ndi apainiya.

18. Tchulani masukulu ena amene akuthandiza anthu a Mulungu.

18 Ndiye palinso masukulu ena monga Sukulu ya Utumiki wa Ufumu, Sukulu ya Utumiki Waupainiya, Sukulu ya Akhristu Olalikira za Ufumu, Sukulu ya Oyang’anira Madera ndi Akazi Awo ndiponso Sukulu ya Abale a M’komiti ya Nthambi ndi Akazi Awo. Masukulu onsewa akuphunzitsa bwino abale ndi alongo ndiponso kuwathandiza kuti akhale ndi chikhulupiriro cholimba. Zonsezi zikusonyeza kuti Khristu akuphunzitsa anthu ake.

19. Kodi M’bale Russell ananena zotani pa nkhani yolalikira ndipo zakwaniritsidwa bwanji?

19 Tsopano padutsa zaka zoposa 100 kuchokera pamene Ufumu wa Mulungu unakhazikitsidwa. Mfumu yathu Yesu Khristu akupitiriza kutiphunzitsa. Mu 1916, M’bale Russell atatsala pang’ono kumwalira, anasonyeza kuti ankakhulupirira zoti ntchito yolalikira idzakula mpaka kufika padziko lonse. Iye anauza mnzake wina kuti: “Ntchitoyi ikuwonjezereka ndipo zimenezi zipitirira chifukwa chakuti ‘uthenga wabwino wa ufumu’ uyenera kulalikidwa padziko lonse.” (Buku lakuti, Faith on the March lolembedwa ndi A. H. Macmillan, tsamba 69) Zimene ananenazi zikuchitikadi. Timasangalala kwambiri kuti Mulungu wathu wamtendere akutipatsabe zinthu zonse zofunika kuti tizigwira bwino ntchito yolalikira.

^ ndime 2 Zikuoneka kuti ambiri mwa anthuwa anadzakhala Akhristu. Tikutero chifukwa chakuti m’kalata imene Paulo analembera Akhristu a ku Korinto, ananena kuti anthu oposa 500 aja tsopano anali “abale.” Iye ananenanso kuti: “Ambiri a iwo akali ndi moyo mpaka lero, koma ena anagona mu imfa.” Choncho zikuoneka kuti Paulo ankadziwana ndi ena mwa Akhristu amene analipo pamene Yesu ankapereka lamulo loti ophunzira ake azilalikira.