Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Tiziyamikira Zimene Yehova Amatipatsa

Tiziyamikira Zimene Yehova Amatipatsa

YEHOVA amatipatsa zinthu zambiri. (Yak. 1:17) Timaona umboni wa zimenezi tikayang’ana nyenyezi kumwamba komanso zinthu zokongola padzikoli.—Sal. 65:12, 13; 147:7, 8; 148:3, 4.

Wolemba masalimo wina ankayamikira kwambiri zinthu zimene Mulungu analenga moti anaimba nyimbo yomutamanda. Nanunso muyenera kuti mungagwirizane kwambiri ndi zimene ananena m’nyimboyi, yomwe ili mu Salimo 104. Mawu ena amene ananena ndi akuti: “Ndidzaimbira Yehova moyo wanga wonse. Ndidzaimba nyimbo zotamanda Mulungu wanga nthawi yonse ya moyo wanga.” (Sal. 104:33) Kodi inunso mumafunitsitsa kutamanda Yehova?

CHITSANZO CHABWINO KWAMBIRI PA NKHANI YA KUPATSA

Yehova amafuna kuti ifenso tizikhala ndi mtima wopatsa. Iye anatiuzanso zifukwa zomveka zotichititsa kukhala ndi mtima umenewu. Mwachitsanzo, anagwiritsa ntchito mtumwi Paulo kuti alembe malangizo akuti: “Lamula achuma a m’nthawi ino kuti asakhale odzikweza, ndiponso kuti asamadalire chuma chosadalirika, koma adalire Mulungu, amene amatipatsa mowolowa manja zinthu zonse kuti tisangalale. Uwalamule kuti azichita zabwino, akhale olemera pa ntchito zabwino, owolowa manja, okonzeka kugawira ena, ndiponso asunge maziko abwino a tsogolo lawo monga chuma, kuti agwire mwamphamvu moyo weniweniwo.”—1 Tim. 6:17-19.

M’kalata yachiwiri imene Paulo analembera mpingo wa ku Korinto, anafotokoza za maganizo oyenera amene tiyenera kukhala nawo pa nkhani ya kupatsa. M’kalatayo analemba kuti: “Aliyense achite mogwirizana ndi mmene watsimikizira mumtima mwake, osati monyinyirika kapena mokakamizika, chifukwa Mulungu amakonda munthu wopereka mokondwera.” (2 Akor. 9:7) Kenako, anafotokoza kuti anthu amene amapatsidwa zinthu amathandizidwa ndipo nawonso amene amapereka zinthuzo amadalitsidwa kwambiri.—2 Akor. 9:11-14.

Pomaliza kalata yakeyi, Paulo ananena za umboni wamphamvu wosonyeza kuti Mulungu ali ndi mtima wopatsa. Iye anati: “Tikuyamika Mulungu chifukwa cha mphatso yake yaulere, imene sitingathe n’komwe kuifotokoza.” (2 Akor. 9:15) Mphatso imene Paulo ankanenayi ikuphatikiza zinthu zonse zabwino zimene Mulungu watipatsa pogwiritsa ntchito Yesu Khristu. Kunena zoona, timasowa chonena tikaganizira mphatso yamtengo wapatali kwambiri imeneyi.

Kodi tingasonyeze bwanji kuti timayamikira zimene Yehova ndi Mwana wake amatichitira? Njira imodzi imene tingachitire zimenezi ndi kukhala ndi mtima wopatsa pogwiritsa ntchito nthawi, mphamvu ndiponso chuma chathu potumikira Yehova.—1 Mbiri 22:14; 29:3-5; Luka 21:1-4.