Baibulo Lomveka Bwino Kwambiri
“Mawu a Mulungu ndi amoyo.”—AHEB. 4:12.
NYIMBO: 37, 116
1. a) Kodi Yehova anapatsa Adamu ntchito yotani? (b) Kodi kuchokera nthawi imeneyo, anthu a Mulungu amagwiritsa ntchito bwanji chilankhulo?
YEHOVA MULUNGU analenga anthu m’njira yoti azitha kulankhula komanso kuphunzira chilankhulo. M’munda wa Edeni, iye anapatsa Adamu ntchito yopereka mayina kwa nyama ndipo Adamuyo anapatsa nyama iliyonse dzina loyenerera. (Gen. 2:19, 20) Kuchokera nthawi imeneyo, anthu a Mulungu amagwiritsa ntchito chilankhulo pomutamanda komanso pouza ena zimene iye amafuna. M’zaka zaposachedwa, anthu a Mulungu akhala akumasulira Baibulo m’zilankhulo zosiyanasiyana n’cholinga choti anthu ambiri adziwe Mulungu.
2. a) Kodi Komiti Yomasulira Baibulo la Dziko Latsopano inatsatira mfundo ziti? (b) Kodi tikambirana chiyani m’nkhaniyi?
2 Pali Mabaibulo ambiri koma si onse omwe anamasuliridwa bwino. Choncho, m’zaka za m’ma 1940, Komiti Yomasulira Baibulo la Dziko Latsopano inakhazikitsa mfundo zitatu zomwe omasulira Baibulo ayenera kutsatira. Mfundozi zakhala zikutsatiridwa pomasulira Baibulo m’zilankhulo Mateyu 6:9.) (2) Tizimasulira potsatira mawu alionse omwe anali m’Baibulo loyambirira ngati zingatheke. Koma ngati kuchita zimenezi kungasokoneze tanthauzo lake, tizingomasulira zimene mawuwo akutanthauza. (3) Tizimasulira pogwiritsa ntchito mawu osavuta kumva. * (Werengani Nehemiya 8:8, 12.) Tiyeni tikambirane mmene anagwiritsira ntchito mfundo zimenezi pokonzanso Baibulo la Dziko Latsopano lachingelezi komanso polimasulira m’zilankhulo zina.
zoposa 130. Mfundo zake ndi: (1) Tizilemekeza dzina la Mulungu polibwezeretsa m’malo ake onse m’Mawu a Mulungu. (WerenganiLIMALEMEKEZA DZINA LA MULUNGU
3, 4. a) Kodi ndi zolemba zakale ziti zomwe zinkapezeka ndi zilembo zoimira dzina la Mulungu? (b) Kodi omasulira Mabaibulo ena anachita zotani ndi dzina la Mulungu?
3 M’mipukutu imene inapezeka pafupi ndi Nyanja Yakufa komanso m’zolemba zina zakale zachiheberi, mumapezeka kambirimbiri zilembo 4 zoimira dzina la Mulungu. Dzina la Mulungu limapezekanso m’Mabaibulo ena achigiriki (a Septuagint) omwe anapezeka pakati pa zaka pafupifupi 200 Yesu asanabadwe ndi zaka pafupipafupi 100 iye atabadwa.
4 Ngakhale kuti pali umboni wokwanira woti dzina la Mulungu liyenera kupezeka m’Baibulo, pali Mabaibulo ambiri amene dzinali linachotsedwamo. Baibulo la Dziko Latsopano Lomasulira Malemba Achigiriki lachingelezi linatuluka mu 1950. Patangodutsa zaka ziwiri, panatulukanso Baibulo lina lodziwika bwino lachingelezi. (Revised Standard Version) M’Baibuloli anachotsamo dzina la Mulungu ngakhale kuti pamene linkatuluka koyamba mu 1901 dzinali linkapezekamo. Mawu ake oyamba amafotokoza chifukwa chimene anachotsera dzinali. Amati: “Kugwiritsa ntchito dzina lenileni la Mulungu . . . n’kosayenera pa chikhulupiriro cha Akhristu.” Izi zitachitika, omasulira ena anachotsanso dzina la Mulungu m’Mabaibulo awo.
5. N’chifukwa chiyani dzina la Mulungu liyenera kupezeka m’Baibulo?
5 Kodi dzina la Mulungu limayeneradi kupezeka m’Baibulo? Kuti munthu amasulire bwino nkhani, ayenera kuganizira kaye uthenga umene wolemba nkhaniyo akufuna kuti anthu amve. Yehova amene analemba Baibulo amafuna kuti anthu adziwe dzina lake. Tikutero chifukwa chakuti malemba ambiri amasonyeza kuti dzina la Mulungu ndi lofunika kwambiri ndipo liyenera kulemekezedwa. (Eks. 3:15; Sal. 83:18; 148:13; Yes. 42:8; 43:10; Yoh. 17:6, 26; Mac. 15:14) Yehova anachititsa kuti anthu amene anawagwiritsa ntchito polemba Baibulo alembe dzina lake kambirimbiri. (Werengani Ezekieli 38:23.) Choncho anthu akachotsa dzinali m’Baibulo, amasonyeza kuti salemekeza Yehova.
6. N’chifukwa chiyani mu Baibulo la Dziko Latsopano la 2013, anawonjezeramo dzina la Mulungu m’mavesi enanso 6?
6 Masiku ano kwapezeka umboni winanso wosonyeza kuti dzina la Mulungu liyenera kupezeka m’Baibulo. Mu Baibulo la Dziko Latsopano lomwe linatuluka mu 1984, dzina la Mulungu linkapezekamo ka 7,210. Koma mu Baibulo lachingelezi lokonzedwanso lomwe linatuluka mu 2013, anawonjezera dzinali m’mavesi enanso 6, choncho limapezekamo ka 7,216. Mavesi ake ndi 1 Samueli 2:25; 6:3; 10:26; 23:14, 16 ndiponso Oweruza 19:18. Anawonjezera dzina la Mulungu pa Oweruza 19:18 chifukwa cha zimene akatswiri anapeza atafufuza m’zolemba zina zakale za Baibulo. Pamavesi enawo, anawonjezera dzinali chifukwa cha zimene anapeza m’mipukutu ya ku Nyanja Yakufa ija. *
7, 8. Kodi dzina lakuti Yehova limatanthauza chiyani?
* Mabuku athu akale ankafotokoza kuti dzinali limangotanthauza zimene lemba la Ekisodo 3:14 limanena. Lembali limati: “Ndidzakhala Amene Ndidzafune Kukhala.” Choncho Baibulo lomwe linatuluka mu 1984, linanena kuti dzinali limatanthauza kuti “Yehova amadzichititsa kukhala Wokwaniritsa malonjezo ake.” * Koma mawu a mu Zakumapeto A4 mu Baibulo lokonzedwanso limene linatuluka mu 2013, amati: “Ngakhale kuti imeneyi ndi mbali ina ya tanthauzo la dzina la Mulungu lakuti Yehova, sikuti dzinali limangotanthauza kuti Mulungu angathe kukhala chilichonse chimene akufuna. Limatanthauzanso kuti angathe kugwiritsa ntchito zimene analenga pokwaniritsa cholinga chake.”—Onaninso Kabuku Kothandiza Kuphunzira Mawu a Mulungu, patsamba 5.
7 Tanthauzo la dzina la Mulungu ndi lofunika kwambiri kwa Akhristufe. Ndipo Zakumapeto za mu Baibulo la Dziko Latsopano lokonzedwansoli zimafotokozanso mfundo zatsopano zokhudza tanthauzo la dzinali. Dzina lakuti Yehova limatanthauza kuti, “Amachititsa Zinthu Kuchitika.”8 Dzina la Mulungu limatanthauzanso kuti iye angagwiritse ntchito anthu kapena chilichonse chimene analenga kuti akwaniritse zimene akufuna. Mwachitsanzo, Mulungu anachititsa kuti Nowa akhale mmisiri wokhoma chingalawa komanso kuti Bezaleli akhale katswiri wokonza zinthu. Anachititsanso kuti Gidiyoni akhale msilikali wodziwa nkhondo ndiponso kuti Paulo akhale mmishonale. Choncho dzina la Mulungu ndi lofunika kwambiri kwa anthu a Mulungu. N’chifukwa chake Komiti Yomasulira Baibulo la Dziko Latsopano inaonetsetsa kuti dzinali lipezeke m’Baibuloli.
9. Fotokozani chifukwa chimodzi chimene chinachititsa kuti Baibulo la Dziko Latsopano limasuliridwe m’zilankhulo zina.
9 Masiku ano omasulira ambiri akuchotsa dzina la Mulungu m’Mabaibulo awo. M’malomwake, amaikamo dzina lakuti “Ambuye” kapena mayina ena amene amatchulira Mulungu kwawoko. Ichi ndi chifukwa chachikulu chimene chinachititsa kuti Bungwe Lolamulira liyesetse kuti anthu ambiri akhale ndi Baibulo limene dzina la Mulungu limapezekamo. (Werengani Malaki 3:16.) Panopa Baibulo la Dziko Latsopano likupezeka m’zilankhulo zoposa 130.
LOMVEKA BWINO KOMANSO LOMASULIRIDWA MOLONDOLA
10, 11. Kodi omasulira Baibulo la Dziko Latsopano m’zilankhulo zina ankakumana ndi mavuto otani?
10 Takhala tikukumana ndi mavuto ambiri pomasulira Baibulo la Dziko Latsopano m’zilankhulo zina kuchokera ku Chingelezi. Mwachitsanzo, mu Baibulo la Dziko Latsopano lachingelezi, anagwiritsa ntchito mawu achiheberi akuti “Sheol” pa Mlaliki 9:10 komanso pamavesi ena, potsatira zimene Mabaibulo enanso achingelezi anachita. Vesi limeneli linkati: “Kulibe kugwira ntchito, kuganiza zochita, kudziwa zinthu, kapena nzeru, ku Sheoli kumene ukupitako.” Koma omasulira Mabaibulo m’zilankhulo zina anaona kuti sangagwiritse ntchito mawuwa chifukwa anthu ambiri sakuwadziwa ndipo angaone ngati ndi dzina la malo enieni. Choncho anauzidwa kuti akhoza kungomasulira tanthauzo la mawu achiheberi akuti “Sheol,” komanso mawu ofanana nawo achigiriki akuti “Hades.” Choncho mawu awiriwa anayamba kuwamasulira kuti “Manda,” omwe ndi mawu olondola komanso osavuta kumva.
11 Omasulira m’zilankhulo zina, ankavutikanso pomasulira mawu achiheberi ndiponso achigiriki omwe amatanthauza “moyo.” Mawu omwe ankagwiritsa ntchito pomasulira mawuwa, m’mavesi ena ankachititsa anthu kuganiza kuti munthu ali ndi mzimu womwe umachoka m’thupi,
munthuyo akamwalira. Choncho omasulira anauzidwa kuti azimasulira mawuwa mosiyanasiyana mogwirizana ndi nkhani yake. Anauzidwanso kuti azimasulira mawuwo potengera matanthauzo omwe ali mu Zakumapeto mu Baibulo la Dziko Latsopano lachingelezi lokhala ndi malifalensi. Nthawi zina akaona kuti n’zofunika, ankalemba mawu achiheberi ndi achigirikiwo m’mawu am’munsi, n’kufotokoza tanthauzo lake. Zonsezi zathandiza kuti anthu asamavutike kumvetsa tanthauzo la mavesiwo.12. Kodi anachita zotani pokonzanso Baibulo la Dziko Latsopano lachingelezi? (Onaninso nkhani yakuti, “Baibulo la Dziko Latsopano Lokonzedwanso Lomwe Linatuluka mu 2013” patsamba 14.)
12 Mafunso amene omasulira ankafunsa kulikulu lathu, anasonyeza kuti Baibulo la Dziko Latsopano linkayenera kukonzedwanso. Choncho mu September 2007, Bungwe Lolamulira linavomereza kuti Baibulo lachingelezi likonzedwenso. Pokonza Baibuloli, anaonanso mafunso ambirimbiri amene omasulira ankafunsa. Ndiyeno anachotsa mawu achikale ndipo anayesetsa kuti likhale lomveka bwino komanso losavuta kuwerenga. Koma anaonetsetsanso kuti likhale lolondola. Anatsatiranso zimene omasulira m’zilankhulo zina anachita pomasulira Baibulo ndipo izi zinathandiza kwambiri.—Miy. 27:17.
ANTHU AMAYAMIKIRA KWAMBIRI BAIBULOLI
13. Kodi anthu ambiri ananena zotani zokhudza Baibulo la Dziko Latsopano lokonzedwanso?
13 Kodi anthu ambiri ananena zotani zokhudza Baibulo la Dziko Latsopano lokonzedwanso limeneli? Abale ndi alongo anatumiza kulikulu lathu ku Brooklyn makalata ambiri oyamikira Baibuloli. Mlongo wina anati: “Baibulo limeneli ndi lomveka bwino kwambiri ndipo lili ngati chuma chamtengo wapatali. Ukamawerenga mfundo zake, zimakhala ngati ukuyang’ana miyala yamtengo wapatali n’kuona kukongola kwake. Baibuloli landithandiza kudziwa bwino Yehova yemwe ali ngati bambo wachikondi. Ndikamaliwerenga, ndimamva ngati wandikumbatira ndipo akundiwerengera mawu olimbikitsa.” Umu ndi mmenenso anthu ambiri amamvera.
14, 15. Kodi anthu ambiri anamva bwanji Baibulo la Dziko Latsopano litatuluka m’chilankhulo chawo?
14 Koma si Baibulo la Dziko Latsopano lachingelezi lokha limene anthu amaliyamikira. Mwachitsanzo, munthu wina wachikulire wa ku Bulgaria anayamikira Baibulo la Dziko Latsopano
lachibugariya. Iye anati: “Ndakhala ndikuwerenga Baibulo kwa zaka zambiri, koma ndinali ndisanawerengepo Baibulo lomveka bwino komanso logwira mtima ngati limeneli.” Mlongo wina wa ku Albania atalandira Baibulo la Dziko Latsopano m’chilankhulo chake, anati: “Mawu a Mulungu akumveka bwino kwambiri m’Chiabaniya. Tili ndi mwayi waukulu kuti Yehova akutilankhula m’chilankhulo chathu.”15 M’mayiko ambiri, Mabaibulo ndi odula ndiponso osowa. Choncho anthu a m’mayikowo akalandira Baibulo amaona kuti ndi mwayi wamtengo wapatali. Mwachitsanzo, abale ena a ku Rwanda ananena kuti: “Anthu ambiri amene ankaphunzira Baibulo ndi abale ndi alongo, ankachedwa kusintha zinthu pa moyo wawo. Anthuwa analibe Baibulo chifukwa sakanakwanitsa kugula Mabaibulo a tchalitchi chawo. Komanso ankavutika kumvetsa mavesi ena. Zimenezi zinkachititsa kuti azichedwa kuyamba kutumikira Yehova.” Koma zinthu zinasintha pamene Baibulo la Dziko Latsopano linatuluka m’zilankhulo zawo. Banja lina la ku Rwanda komweko, lomwe lili ndi ana 4 achinyamata linati: “Tikuthokoza kwambiri Yehova ndiponso kapolo wokhulupirika chifukwa chotipatsa Baibuloli. Ndife osauka ndipo sitikanakwanitsa kugulira aliyense Baibulo. Koma panopa aliyense walandira Baibulo lake. Tsiku lililonse timawerenga Baibulo pamodzi posonyeza kuyamikira zimene Yehova watichitira.”
16, 17. a) Kodi Yehova amafunitsitsa kuti anthu ake onse akhale ndi chiyani? (b) Kodi tiyenera kuyesetsa kuchita chiyani?
16 M’tsogolomu, Baibulo la Dziko Latsopano lokonzedwanso lidzatuluka m’zilankhulo zina. N’zoona kuti Satana amafuna kulepheretsa zimenezi. Koma Yehova sangalole chifukwa akufunitsitsa kuti anthu ake onse akhale ndi Baibulo lomveka bwino kuti azimva pamene iye akuwalankhula. (Werengani Yesaya 30:21.) Posachedwapa, “dziko lapansi lidzadzaza ndi anthu odziwa Yehova ngati mmene madzi amadzazira nyanja.”—Yes. 11:9.
17 Tiyeni tiziyesetsa kugwiritsa ntchito bwino zinthu zonse zimene Mulungu amatipatsa monga Baibulo la Dziko Latsopano limene limalemekeza dzina lake. Tiziwerenga Mawu a Mulungu tsiku lililonse chifukwa ndi njira imene Yehova amatilankhulira. Tisaiwalenso kuti iye amamvetsera tikamapemphera. Tikamawerenga Baibulo ndiponso kupemphera timadziwa bwino Yehova komanso timayamba kumukonda kwambiri.—Yoh. 17:3.
^ ndime 2 Onani mutu wakuti, “Kodi Mungadziwe Bwanji Baibulo Lomasuliridwa Bwino?” mu Nsanja ya Olonda ya May 1, 2008 ndiponso Zakumapeto A1 mu Baibulo la Dziko Latsopano lachingelezi lokonzedwanso.
^ ndime 6 Mipukutu yomwe inapezeka ku Nyanja Yakufa inalembedwa zaka zoposa 1,000, Amasorete asanayambe kukopera Malemba. Zimene Amasorete anakopera ndi zomwe zinagwiritsidwa ntchito pomasulira Baibulo la Dziko Latsopano.
^ ndime 7 Mabuku enanso amafotokoza tanthauzo lomweli la dzina la Mulungu ngakhale kuti akatswiri ena a Baibulo sagwirizana ndi tanthauzoli.
^ ndime 7 Onani Zakumapeto 1 mu Baibulo la Dziko Latsopano pamutu wakuti, “Dzina la Mulungu M’Malemba Achiheberi Komanso M’Malemba Achigiriki,” patsamba 1933.