Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Muzigwiritsa Ntchito Bwino Lilime Lanu

Muzigwiritsa Ntchito Bwino Lilime Lanu

‘Mawu a pakamwa panga akukondweretseni, inu Yehova.’—SAL. 19:14.

NYIMBO: 82, 77

1, 2. N’chifukwa chiyani Baibulo limayerekezera lilime ndi moto?

MU OCTOBER 1871, m’nkhalango ina ya ku United States munabuka moto umene unafalikira mwamsanga. Motowu unapha anthu oposa 1,200 n’kuwononga mitengo pafupifupi 2 biliyoni. N’kutheka kuti motowu unayamba chifukwa cha sitima zapamtunda zimene zinkadutsa m’mbali mwa nkhalangoyi. Moto unkathetheka pamene mawilo a sitimazi ankakwechesana ndi njanji. Zimene zinachitikazi zikutikumbutsa mawu a pa Yakobo 3:5 akuti: ‘Kamoto kakang’onong’ono kamayatsa nkhalango yaikulu.’ Kodi n’chifukwa chiyani Yakobo ananena zimenezi?

2 Vesi 6 limatithandiza kudziwa chifukwa chake ananena zimenezi. Limati: “Lilimenso ndi moto.” Apa lilime likuimira zimene timalankhula. Mofanana ndi moto, zimene timalankhula zikhoza kuyambitsa mavuto aakulu. Paja Baibulo limanenanso kuti: “Imfa ndiponso moyo zili mu mphamvu ya lilime.” (Miy. 18:21) Koma sitisiya kugwiritsa ntchito moto chifukwa choopa kuwotcha zinthu. Choncho sitiyeneranso kusiyiratu kulankhula poopa kuti tingalankhule zinthu zolakwika. Chofunika ndi kukhala osamala. Moto tikamaugwiritsa ntchito mosamala, tikhoza kuphikira, kuwotha ndiponso kuunikira. N’chimodzimodzinso lilime lathu. Tikhoza kuligwiritsa ntchito potamanda Mulungu komanso polimbikitsa anthu ena.—Sal. 19:14.

3. Kodi m’nkhaniyi tikambirana zinthu zitatu ziti?

3 Kaya timalankhula ndi pakamwa kapena ndi manja, tiyenera kukumbukira kuti kulankhula ndi mphatso yamtengo wapatali yochokera kwa Mulungu. Kodi tingagwiritse ntchito bwanji mphatsoyi polimbikitsa ena osati kuwakhumudwitsa? (Werengani Yakobo 3:9, 10.) M’nkhaniyi tikambirana zimene zingatithandize kusankha bwino nthawi yolankhula, zimene tingalankhule komanso mmene tingalankhulire.

NTHAWI YOLANKHULA

4. Kodi ndi nthawi iti pamene tiyenera kukhala chete?

4 Anthufe timakonda kulankhula, komabe Baibulo limanena kuti pali nthawi ina imene tiyenera ‘kukhala chete.’ (Mlal. 3:7) Mwachitsanzo ena akamalankhula, tiyenera kukhala chete posonyeza kuti tikuwalemekeza. (Yobu 6:24) Tiyeneranso kupewa kulankhula nkhani zachinsinsi. (Miy. 20:19) Komanso ena akatikhumudwitsa, ndi bwino kukhala chete ndipo izi zimasonyeza kuti ndife anzeru.—Sal. 4:4.

5. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timayamikira mphatso yolankhula imene Mulungu anatipatsa?

5 Komabe Baibulo limanenanso kuti pali “nthawi yolankhula.” (Mlal. 3:7) Tiyerekeze kuti mnzanu wakupatsani mphatso yamtengo wapatali, kodi mungangoisunga osaigwiritsa ntchito? N’zodziwikiratu kuti mungaigwiritse ntchito bwino posonyeza kuti mukuyamikira. N’chimodzimodzinso ndi mphatso yolankhula imene Yehova anatipatsa. Tingasonyeze kuti timaiyamikira tikamaigwiritsa ntchito bwino. Tingachite zimenezi potamanda Mulungu, polimbikitsa anzathu komanso pouza ena mmene tikumvera kapena zimene tikufuna. (Sal. 51:15) Koma kodi tingadziwe bwanji nthawi yoyenera kulankhula?

6. Kodi Baibulo limasonyeza bwanji kufunika kosankha bwino nthawi yolankhula?

6 Lemba la Miyambo 25:11 limasonyeza kufunika kosankha bwino nthawi yolankhula. Limati: “Mawu olankhulidwa pa nthawi yoyenera ali ngati zipatso za maapozi agolide m’mbale zasiliva.” Zinthu zagolide zimakhala zokongola ndipo mukaziika m’mbale zasiliva zimaoneka bwino kwambiri. Choncho lembali likusonyeza kuti tikasankha mawu abwino n’kuwalankhulanso pa nthawi yoyenera, tingalimbikitse amene tikulankhula naye. Koma kodi tingachite bwanji zimenezi?

7, 8. Kodi abale a ku Japan anatsanzira bwanji Yesu posankha nthawi yabwino youza anthu zoti akufa adzauka?

7 Zimene tikufuna kunena zikhoza kukhala zolimbikitsa, komabe ngati sitinazilankhule pa nthawi yoyenera sizingathandize. (Werengani Miyambo 15:23.) Mwachitsanzo mu March 2011, ku Japan kunachitika chivomerezi komanso kunasefukira madzi ndipo mizinda yambiri inawonongeka. Anthu oposa 15,000 anafa. Ngakhale kuti abale ndi alongo akuderali nawonso anakhudzidwa ndi vutoli, anayesetsa kulimbikitsa anzawo pogwiritsa ntchito Baibulo. Komabe anthu ambiri akumeneko ndi achipembedzo chachibuda moti sadziwa mfundo za m’Baibulo ndipo amakhulupirira zosiyana kwambiri ndi zimene limaphunzitsa. Choncho abale anadziwa kuti nthawiyi sinali yabwino kuti auze anthu amene anaferedwa zoti Mulungu adzaukitsa akufa. M’malomwake anangowalimbikitsa n’kuwauza kuchokera m’Baibulo chifukwa chake anthu abwino nawonso amakumana ndi mavuto.

8 Abale ndi alongowa anatsatira chitsanzo cha Yesu. Iye ankadziwa nthawi yoyenera kulankhula komanso yokhala chete. (Yoh. 18:33-37; 19:8-11) Pa nthawi ina, anauza ophunzira ake kuti: “Ndili ndi zambiri zakuti ndikuuzeni, koma padakali pano simungathe kuzimvetsa zonsezo.” (Yoh. 16:12) Patatha zaka ziwiri ndi hafu kuchokera pamene chivomerezi chija chinachitika, abale a ku Japan anazindikira kuti iyi inali nthawi yabwino youza anthuwo kuti amene anamwalira adzakhalanso ndi moyo. Choncho anagawira kapepala ka Uthenga wa Ufumu Na. 38 kamutu wakuti, “Kodi N’zoonadi Kuti Akufa Adzauka?” Anthu ambiri anasangalala ndi uthenga umenewu ndipo analandira timapepalati. N’zoona kuti zikhalidwe komanso zikhulupiriro za anthu zimasiyanasiyana. Komabe chofunika ndi kudziwa nthawi yoyenera kulankhula.

9. Ndi nthawi ina iti, pamene kudziwa nthawi yoyenera kulankhula kumathandiza kwambiri?

9 Kodi ndi nthawi inanso iti yomwe tiyenera kudikira tisanalankhule? Nthawi zina munthu akhoza kunena zinthu zotikhumudwitsa ngakhale kuti sichinali cholinga chake. Zikatere ndi bwino kuganiza kaye ngati tiyenera kumuyankha kapena ayi. Ngati taona kuti tifunika kumuyankha, tiyenera kudikira kuti mtima wathu ukhale kaye pansi. (Werengani Miyambo 15:28.) Tiyeneranso kudziwa nthawi yoyenera kuuza achibale athu omwe si Mboni uthenga wa m’Baibulo. Ngakhale kuti timafuna kuti achibale athuwa adziwe Yehova, tiyenera kukhala oleza mtima komanso osamala. Tikamayesetsa kulankhula mawu abwino pa nthawi yoyenera, achibale athu angayambe kumvetsera uthenga wathu.

ZIMENE TINGALANKHULE

10. a) N’chifukwa chiyani tiyenera kusankha bwino mawu polankhula? (b) Kodi ndi mawu ati amene tiyenera kupewa?

10 Zimene timalankhula zikhoza kukhumudwitsa kapena kulimbikitsa munthu. (Werengani Miyambo 12:18.) Anthu ambiri m’dzikoli amakonda kulankhula mawu opweteka. Mafilimu ndi mapulogalamu ena a pa TV amapangitsa kuti anthu ambiri azigwiritsa ntchito lilime lawo ngati “lupanga” kapena “mivi” polankhulira anzawo ‘mawu owawa.’ (Sal. 64:3) Ena mwa mawu amenewa amakhala onyoza kapena ofuna kuchititsa manyazi anthu ena. Akhristufe tiyenera kupewa kulankhula mawu ngati amenewa. Anthu ena amalankhula mawu oterewa ngati nthabwala, koma angachititse winayo kuona kuti sakumulemekeza. Mawu onyoza ali m’gulu la mawu achipongwe amene Akhristu ayenera kupewa. Nthabwala zimachititsa kuti anthu asangalale ndi zimene tikulankhula. Komabe tiyenera kupewa kulankhula nthabwala zonyoza ena pongofuna kuseketsa anthu. Baibulo limatichenjeza kuti: “Mawu alionse owola asatuluke pakamwa panu, koma alionse olimbikitsa monga mmene kungafunikire, kuti asangalatse owamva.”—Aef. 4:29, 31.

11. Kodi n’chiyani chingatithandize kusankha mawu oyenera tikamalankhula?

11 Yesu ananena kuti: “Pakamwa pamalankhula zosefukira mumtima.” (Mat. 12:34) Choncho kusankha mawu oyenera, kumayambira mumtima. Zimene timalankhula zimasonyeza ngati timalemekeza ena kapena ayi. Ngati timakonda ena kuchokera mumtima, zolankhula zathu zingakhale zabwino komanso zolimbikitsa.

12. Kodi n’chiyani chingatithandize kusankha bwino mawu?

12 Pamafunika khama kuti tidziwe mawu oyenera kuwagwiritsa ntchito polankhula. Solomo, ngakhale kuti anali wanzeru kwambiri, ‘ankasinkhasinkha ndi kufufuza zinthu mosamala’ n’cholinga choti alembe ‘mawu okoma komanso olondola a choonadi.’ (Mlal. 12:9, 10) Kodi inuyo zimakuvutani kupeza “mawu okoma”? Ngati ndi choncho, muziwerenga Baibulo komanso mabuku athu kuti mudziwe mawu ena abwino omwe mungalankhule. Yesetsani kudziwa matanthauzo a mawu omwe ndi achilendo kwa inu. Chitsanzo cha Yesu chingakuthandizeninso kudziwa zimene mungachite kuti muzilankhula mawu olimbikitsa. Chifukwa cha zimene Yehova anamuphunzitsa, Yesu ankadziwa ‘mmene angayankhire munthu wotopa.’ (Yes. 50:4) Kuganizira kaye tisanalankhule kungatithandize kupeza mawu oyenera. (Yak. 1:19) Tizidzifunsa kuti: ‘Ndikalankhula mawu amenewa, kodi zimene munthuyu angamve ndi zimenedi ndikutanthauza? Kodi mawu amene ndikufuna kulankhulawa sangamukhumudwitse?’

13. N’chifukwa chiyani tiyenera kulankhula zomveka bwino?

13 Kale ku Isiraeli, ankaimba malipenga akafuna kusonkhanitsa anthu, kuwauza kuti azipita kwawo ndiponso akamakonzekeretsa asilikali kuti apite ku nkhondo. Baibulo limanena kuti zimene timalankhula zili ngati kulira kwa lipenga. Ngati lipenga silikulira momveka bwino, linkasokoneza kwambiri asilikali. Ifenso tiyenera kulankhula zomveka bwino kuti tisasokoneze anthu. Komanso tiziyesetsa kulankhula mwaulemu ndiponso mowaganizira.—Werengani 1 Akorinto 14:8, 9.

14. Perekani chitsanzo chosonyeza kuti Yesu ankagwiritsa ntchito mawu osavuta kumva.

14 Yesu ndi chitsanzo chabwino kwambiri pa nkhani yosankha mawu oyenera. Taganizirani mawu amene anagwiritsa ntchito pa ulaliki wake umene umapezeka m’chaputala 5 mpaka 7 cha buku la Mateyu. Yesu sanalankhule mawu ambirimbiri, ovuta kapena ongofuna kugometsa anthu. Sanalankhulenso mawu omwe akanakhumudwitsa anthuwo. M’malomwake analankhula mawu osavuta kumva komanso ogwira mtima. Mwachitsanzo, anagwiritsa ntchito chitsanzo cha mmene Yehova amadyetsera mbalame. Anachita zimenezi pofuna kuthandiza anthu kuti asamadere nkhawa za mmene angapezere chakudya. Kenako anawafunsa kuti: “Nanga inu sindinu amtengo wapatali kuposa mbalame kodi?” (Mat. 6:26) Mawu osavutawa anathandiza anthuwo kumvetsa mfundo yofunika kwambiri komanso anawalimbikitsa.

MMENE TINGALANKHULIRE

15. N’chifukwa chiyani tiyenera kulankhula mwaulemu?

15 Tikafuna kulankhula zinazake, tiyeneranso kuganizira mmene tingalankhulire. Pamene Yesu ankalankhula m’sunagoge wa kwawo ku Nazareti, anthu ambiri ‘anadabwa ndi mawu ake ogwira mtima.’ (Luka 4:22) Tikamalankhula mwaulemu, mawu athu amakhala ogwira mtima ndipo anthu savutika kutsatira zimene tanena. (Miy. 25:15) Tingatsanzire Yesu polankhula mokoma mtima ndiponso kuchita zinthu moganizira ena. Pa nthawi ina, anthu anayesetsa kupita kumene kunali Yesu, n’cholinga choti akamve mawu ake. Iye atawaona, anawamvera chifundo ndipo “anayamba kuwaphunzitsa zinthu zambiri.” (Maliko 6:34) Ngakhale pamene anthu ankamunyoza, sanabwezere ndi mawu achipongwe.—1 Pet. 2:23.

16, 17. a) Kodi tingasonyeze bwanji kuti timatsanzira Yesu tikamalankhula ndi achibale kapena anzathu a mu mpingo? (Onani chithunzi patsamba 18.) (b) Perekani chitsanzo chosonyeza kuti kulankhula mwaulemu kumathandiza.

16 Nthawi zina zimakhala zovuta kulankhula mwaulemu kwa achibale kapena anzathu mu mpingo chifukwa choti tinawazolowera. Tingaganize kuti tikhoza kuwalankhula mawu alionse ndipo sangakhumudwe. Koma kodi Yesu ankaona kuti akhoza kulankhula mawu alionse kwa ophunzira ake chifukwa choti anali anzake? Ayi. Mwachitsanzo, atumwi ake atakangana pa nkhani yakuti wamkulu ndani, Yesu anawathandiza mokoma mtima pogwiritsa ntchito chitsanzo cha mwana wamng’ono. (Maliko 9:33-37) Nawonso akulu angachite bwino kutsanzira Yesu popereka malangizo “ndi mzimu wofatsa.”—Agal. 6:1.

17 Ngakhale munthu wina atatilankhula zokhumudwitsa, ndi bwino kumuyankha mwaulemu. (Miy. 15:1) Chitsanzo pa nkhaniyi ndi mlongo wina amene anali ndi mwana wachinyamata yemwe ankaoneka kuti akutumikira Yehova koma kumbali ankachita zinthu zoipa. Ndiyeno mlongo wina amene ankamvera chisoni mayi wa mnyamatayo anamuuza kuti: “Pepani kwambiri kuti mwalephera kuphunzitsa bwino mwana wanu.” Mayiyu ataganizira, anayankha kuti: “N’zoona kuti panopa zinthu sizikuyendadi bwino, koma ndikuyesetsabe kumuthandiza. Zonse zidzaoneka Aramagedo ikadzadutsa.” Mayiyu anayankhadi mwaulemu ndipo izi zinathandiza kuti alongowa apitirize kugwirizana. Komanso mwanayo anamva zimene mayi ake anayankha ndipo zinamulimbikitsa. Anazindikira kuti mayi ake sankamuona kuti ndi wokanika. Zimenezi zinamulimbikitsa kuti asiye kucheza ndi anthu oipa. Patapita nthawi, anabatizidwa ndipo kenako anayamba kutumikira pa Beteli. Kaya tikulankhula ndi abale a mu mpingo, achibale kapena anthu amene sitikuwadziwa, mawu athu azikhala ‘achisomo, okoma ngati tawathira mchere.’—Akol. 4:6.

18. Kodi tingatsanzire bwanji Yesu tikamalankhula?

18 Timayamikira kwambiri Yehova chifukwa chotipatsa mphatso imene imatithandiza kuti tiziuza anzathu za mumtima mwathu. Choncho tiyeni tiziyesetsa kutsanzira Yesu posankha mawu abwino, nthawi yoyenera kulankhula ndiponso polankhula mwaulemu. Tikamachita zimenezi tidzalimbikitsa kwambiri anthu ena ndiponso tidzasangalatsa Yehova amene anatipatsa mphatso yolankhula.