Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Atate Yemwe Alibe Wofanana Naye

Atate Yemwe Alibe Wofanana Naye

Yandikirani Mulungu

Atate Yemwe Alibe Wofanana Naye

Mateyo 3:​16, 17

“ATATE.” Mawu ochepa amenewa amapangitsa anthu kuganiza zambiri. Tate yemwe amakondadi ana ake amawathandiza kuti akule bwino. Baibulo limatchula Yehova kuti “Atate,” ndipo pali chifukwa chomveka. (Mateyo 6:9) Kodi Yehova ndi Atate wotani? Kuti tiyankhe funso limeneli, tione kaye mawu amene Yehova ananena kwa Yesu pa ubatizo wake. Ndipotu mmene tate amalankhulira kwa ana ake, zimasonyeza bwino kuti iye ndi kholo labwino kapena ayi.

Cha mu October 29 C.E., Yesu anapita ku mtsinje wa Yorodano kukabatizidwa. Baibulo limafotokoza motere zimene zinachitika: “Atabatizidwa, nthawi yomweyo Yesu anavuuka m’madzimo; pamenepo kumwamba kunatseguka, ndipo Yohane anaona mzimu wa Mulungu ukutsika ngati nkhunda kudzatera pa iye. Ndipo panamvekanso mawu ochokera kumwamba onena kuti: “Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, amene ndimakondwera naye.” * (Mateyo 3:​16, 17) Mawu achikondi amenewa ananenedwa ndi Yehova ndipo akutithandiza kumvetsa bwino kuti iye ndi Atate wotani. Taonani zinthu zitatu zimene Yehova ananena kwa Mwana wake.

Choyamba, ponena kuti “uyu ndiye Mwana wanga,” Yehova anali kutanthauza kuti ‘Ndimanyadira kuti ndine Atate wako.’ Tate wozindikira amayesetsa kusonyeza ana ake kuti amawalabadira ndiponso kuti iwo ndi ofunika. Ana amafunika kuwatsimikizira kuti iwo ndi ofunika pabanjapo. Taganizirani mmene Yesu anamvera mu mtima mwake atamva zimene Atate wake ananena, ngakhale kuti panthawiyi iye anali wamkulu kale.

Chachiwiri, potchula Mwana wake kuti “wokondedwa,” Yehova anasonyeza poyera chikondi chake pa Yesu. M’mawu ena iye anali kunena kuti ‘ndimakukonda.’ Tate wabwino amauza ana ake kuti amawakonda kwambiri. Mawu ngati amenewa ndiponso zinthu zina zosonyeza chikondi, zimathandiza ana kukula bwino. Yesu ayenera kuti anakhudzidwa mtima kwambiri kumva Atate wake akunena kuti amamukonda.

Chachitatu, ponena kuti ‘ndimakondwera nawe,’ Yehova anasonyeza kuti amasangalala ndi Mwana wake. Zimene Yehova ananenazi n’zofanana ndi kunena kuti, ‘Mwana wanga, ndasangalala ndi zimene wachita.’ Tate wachikondi amayesetsa kupeza mpata wosonyeza ana ake kuti iye wasangalala ndi zimene anawo anena kapena kuchita. Ana amalimbikitsidwa makolo awo akamawayamikira. Mosakayikira, Yesu analimbikitsidwa kwambiri kumva mawu oyamikira ochokera kwa Atate wake.

Ndithudi, Yehova ndi Atate yemwe alibe wofanana naye. Kodi inu mumafuna mutakhala ndi tate wotere? Ngati ndi choncho, khazikani mtima pansi, chifukwa kukhala paubwenzi ndi Yehova n’kotheka. Ngati muli ndi chikhulupiriro ndiponso ngati mumaphunzira za iye ndi kuyesetsa kuchita zimene amafuna, angathe kukhala bwenzi lanu. Baibulo limati: “Yandikirani Mulungu, ndipo iyenso adzakuyandikirani.” (Yakobe 4:8) Kodi pali chinthu chinanso chimene chingakupangitseni kumva kuti ndinu wotetezeka kuposa kukhala paubwenzi ndi Yehova Mulungu amene ndi Atate wosayerekezereka?

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 2 Nkhani ngati yomweyi imapezeka mu Uthenga Wabwino wa Luka, ndipo imasonyeza kuti Yehova anagwiritsa ntchito m’lowam’malo wakuti “iwe” motere: “Iwe ndiwe Mwana wanga wokondedwa; ndimakondwera nawe.”​Luka 3:22.