Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mfundo Yoti Zamoyo Zinachita Kusanduka ndi Yogwirizana ndi Baibulo?

Kodi Mfundo Yoti Zamoyo Zinachita Kusanduka ndi Yogwirizana ndi Baibulo?

Kodi Mfundo Yoti Zamoyo Zinachita Kusanduka ndi Yogwirizana ndi Baibulo?

ANTHU ena amati Mulungu anachita kusandutsa anthu kuchokera ku anyani omwenso anachokera ku nyama zina. Iwo amati nyamazi zinachokera ku zokwawa zam’madzi zomwenso zinachokera ku tizilombo ting’onoting’ono? Kodi zimenezi ndi zoona? Asayansi ndiponso atsogoleri ena a zipembedzo amanena kuti amakhulupirira zimenezi komanso amakhulupirira Baibulo. Iwo amati buku la Genesis ndi buku lofotokoza zinthu mophiphiritsa. Mwina munadzifunsapo kuti, ‘Kodi zoti anthu anachita kusanduka kuchokera ku zinyama n’zogwirizana ndi Baibulo?’

Kudziwa mmene moyo wathu unayambira n’kofunika kuti timvetse kuti ndife ndani kwenikweni, kuti tikulowera kuti, ndiponso kuti tizikhala motani. Sitingamvetse chifukwa chimene Mulungu walolera anthu kumavutika ndiponso zimene akufuna kudzawachitira m’tsogolo ngati sitikudziwa mmene moyo wathu unayambira. Sitingakhale paubwenzi wabwino ndi Mulungu ngati timakayikira zoti iyeyo ndiye anatilenga. Motero tiyeni tione zimene Baibulo limanena pa nkhani ya mmene moyo wa anthu unayambira, mmene zinthu zilili panopo, ndiponso mmene tsogolo lawo lidzakhalire. Kenaka tiona ngati mfundo yoti anthu anachita kusanduka ili yogwirizana ndi Baibulo.

Munthu Woyamba

Asayansi ena amakhulupirira kuti nyama zinazake zinayamba kusintha pang’onopang’ono n’kukhala anthu, ndipo amatsutsa zoti panthawi inayake kunali munthu mmodzi yekha basi. Komatu izi si zimene Baibulo limanena. Baibulo limati anthu tonsefe tinachokera kwa munthu mmodzi yekha, dzina lake Adamu.Ndipolimati Adamu anali munthu weniweni, amene anakhalakodi. Limatiuza dzina la mkazi wake ndiponso mayina a ena mwa ana ake. Limatiuzanso mwatsatanetsatane zinthu zosiyanasiyana zimene anachita, zimene ananena, ndiponso nthawi imene anakhalako ndi kumwalira. Yesu sanaone nkhani ya m’Baibuloyi ngati nthano youza anthu osaphunzira. Polankhula ndi atsogoleri a chipembedzo ophunzira kwambiri, Yesu anati: “Kodi simunawerenge kuti iye amene analenga iwo pachiyambi pomwe anapanga iwo mwamuna ndi mkazi.” (Mateyo 19:3-5) Kenaka Yesu anatchula mawu onena za Adamu ndi Hava, opezeka pa Genesis 2:24.

Luka, yemwe analemba nawo Baibulo ndiponso yemwe analemba mbiri ya anthu m’njira yolondola kwambiri anasonyeza kuti Adamu anali munthu weniweni monga analili Yesu. Luka analondoloza mzera wa makolo a Yesu mpaka kufika pa munthu woyambayo. (Luka 3:23-38) Komanso panthawi inayake mtumwi Paulo analankhula pagulu limene linali ndi anthu ena omwe anachita maphunziro apamwamba m’masukulu otchuka a Agiriki. Iye anawauza anthuwa kuti: “Mulungu amene anapanga dzikoli ndi zinthu zonse zili mmenemu . . . kuchokera mwa munthu mmodzi anapanga mtundu wonse wa anthu, kuti akhale pa nkhope yonse ya dziko lapansi.” (Machitidwe 17:24-26) N’zoonekeratu kuti Baibulo limaphunzitsa kuti tinachokera kwa “munthu mmodzi.” Kodi zimene Baibulo limanenazi n’zogwirizana ndi zoti anthu anachita kusanduka kuchokera ku zinyama?

Mmene Munthu Anakhalira Wopanda Ungwiro

Baibulo limati Yehova anapanga munthu wangwiro, chifukwatu n’zosatheka kuti Mulungu apange munthu wopanda ungwiro. Nkhani yofotokoza za mmene Mulungu analengera zinthu imati: “Mulungu ndipo adalenga munthu m’chifanizo chake . . . Ndipo anaziona Mulungu zonse zimene adazipanga, ndipo, taonani, zinali zabwino ndithu.” (Genesis 1:27, 31) Kodi munthu wangwiro ndi wotani?

Munthu wangwiro amakhala ndi ufulu wosankha yekha zochita ndipo amatha kutsanzira ndendende makhalidwe a Mulungu. Baibulo limati: “Mulungu analenga anthu oongoka mtima; koma iwowo afunafuna malongosoledwe a mitundu mitundu.” (Mlaliki 7:29) Adamu anasankha yekha kupandukira Mulungu, motero iye komanso mbadwa zake sanakhalenso angwiro. N’chifukwa chake ngakhale tikafuna kuchita zabwino, timachitabe zinthu zimene timakhumudwa nazo. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Zimene ndimafuna kuchita, sindichita; koma zimene ndimadana nazo ndi zimene ndimachita.”​—Aroma 7:15.

Baibulo limati anthu akanakhala angwiro bwenzi akukhala ndi moyo wathanzi kosatha. Tikaganizira mawu amene Mulungu anauza Adamu, timaona kuti munthu woyamba akanamvera Mulungu, sakanafa. (Genesis 2:16, 17; 3:22, 23) Atamaliza kulenga munthu, Yehova sakananena kuti zinali “zabwino ndithu” ngati munthuyo akanalengedwa ndi thupi lomadwala ndiponso mtima wopanduka. Kupanda ungwiro kunachititsa kuti anthu azidwala ndiponso azilumala, ngakhale kuti thupi lathuli linapangidwa modabwitsa. Motero mfundo yoti anthu anachita kusanduka ndi yosagwirizana ndi Baibulo. Imasonyeza kuti anthu kwenikweni ndi nyama zimene moyo wawo ukusintha kuti ukhale wangwiro. Koma Baibulo limasonyeza kuti anthu anachokera kwa munthu yemwe anadzakhala wopanda ungwiro, motero moyo wa mbadwa zake zonse ukuipiraipira.

Mfundoyi ndi yosagwirizananso ndi zimene Baibulo limanena zokhudza khalidwe la Mulungu, chifukwa ngati Mulungu ndiye anachititsa zoterezi, ndiye kuti iyeyo ndiye anachititsanso kuti anthu ayambe kudwala ndi kuvutika. Komatu Baibulo limati: “Thanthwe, ntchito yake ndi yangwiro; pakuti njira zake zonse ndi chiweruzo; Mulungu wokhulupirika ndi wopanda chisalungamo; iye ndiye wolungama ndi wolunjika. Anam’chitira zovunda sindiwo ana ake, chirema n’chawo; iwo ndiwo mbadwo wopulukira ndi wokhotakhota.” (Deuteronomo 32:4, 5) Motero, mavuto amene anthu akukumana nawo masiku ano anabwera chifukwa choti munthu woyamba anasankha yekha kukhala wopanda ungwiro ndipo zimenezi zinakhudzanso mbadwa zake. Iye anatero popandukira Mulungu. Tsopano tiyeni tikambirane za Yesu. Kodi zoti Mulungu anachita kusandutsa anthu kuchokera ku zinyama n’zogwirizana ndi zimene Baibulo limanena zokhudza Yesu?

Kodi N’zotheka Kukhulupirira Mfundo Imeneyi Ndiponso Chikhristu?

Monga mukudziwira, mfundo imodzi yodziwika kwambiri yachikhristu ndi yakuti, “Khristu anafera machimo athu.” (1 Akorinto 15:3; 1 Petulo 3:18) Mfundoyi ndi yosemphana ndi zoti Mulungu anachita kusandutsa anthu kuchokera ku zinyama. Kuti timvetse m’pofunika kuti tiyambe tamvetsa chifukwa chimene Baibulo limanenera kuti ndife ochimwa ndiponso mmene tchimo limakhudzira munthu.

Tonsefe ndife ochimwa m’njira yakuti sitingathe kutsanzira Mulungu ndendende pa makhalidwe ake apamwamba monga chikondi ndiponso chilungamo. N’chifukwa chake Baibulo limati: “Pakuti onse ndi ochimwa ndipo ndi operewera pa ulemerero wa Mulungu.” (Aroma 3:23) Baibulo limaphunzitsa kuti uchimo ndiwo umabweretsa imfa. Lemba la 1 Akorinto 15:56 limati: “Mbola imene imabala imfa ndiyo uchimo.” Uchimo umene tinatengera kwa makolo athu aja ndi umenenso umachititsa kuti tizidwala. Yesu anasonyeza kuti pali mgwirizano winawake pakati pa matenda ndi uchimo wathuwu. Iye anauza munthu wakufa ziwalo kuti: “Machimo ako akhululukidwa.”​—Mateyo 9:2-7.

Kodi imfa ya Yesu imatithandiza motani? Ponena za Adamu ndi Yesu, Baibulo limati: “Pakuti monga mwa Adamu onse akufa, momwemonso mwa Khristu onse adzapatsidwa moyo.” (1 Akorinto 15:22) Popereka moyo wake kukhala nsembe, Yesu anatilipirira uchimo umene tinatenga kwa Adamu. Motero, anthu amene amakhulupirira Yesu n’kumamumvera adzalandira madalitso amene Adamu anataya. Madalitso ake ndiwo mwayi wokhala ndi moyo wosatha.​—Yohane 3:16; Aroma 6:23.

Motero, kodi mukutha kuona kuti zoti Mulungu anachita kusandutsa anthu kuchokera ku zinyama n’zosemphana ndi Chikhristu? Kodi ngati timakayikira zoti “mwa Adamu onse akufa,” tingakhale bwanji ndi chiyembekezo chakuti “mwa Khristu onse adzapatsidwa moyo”?

N’chifukwa Chiyani Anthu Ambiri Amakopeka ndi Mfundo Yabodzayi?

Baibulo limatchula chifukwa chimene chimachititsa anthu ambiri kukhulupirira mfundo zabodza monga yakuti anthu anachita kusanduka. Limati: “Idzafika nthawi imene anthu sadzafunanso chiphunzitso chopindulitsa, koma mogwirizana ndi zilakolako za iwo eni, adzadzipezera okha aphunzitsi kuti amve zowakomera m’khutu. Adzachotsa makutu awo ku choonadi, nadzatembenukira ku nkhani zonama.” (2 Timoteyo 4:3, 4) Ngakhale kuti mfundo yoti anthu anachita kusanduka imatchulidwa ngati yasayansi, kwenikweni mfundoyi ndi yachipembedzo, chifukwa imaphunzitsa anthu mmene ayenera kuonera moyo ndiponso Mulungu. Anthu amakopeka nayo chifukwa imawalimbikitsa kuchita zinthu zowakomera ndiponso zakumtima kwawo. Anthu ambiri amene amakhulupirira mfundoyi amanenanso kuti amakhulupirira Mulungu. Koma samaona vuto kukhulupirira zoti Mulungu sanalenge zinthu, salowerera pa zochita za anthu, ndiponso sadzaweruza anthu. Anthu ambiri amasangalala ndi mfundo imeneyi chifukwa choti ndi imene imawakomera.

Anthu ambiri amaphunzitsa mfundoyi osati chifukwa choti ndi yomveka, koma chifukwa cha “zilakolako za iwo eni,” zomwe mwina ndi zinthu monga kufuna kulemekezedwa ndi asayansi anzawo. Pulofesa wina wa sayansi, dzina lake Michael Behe, yemwe wakhala zaka zambiri akuphunzira zinthu zosiyanasiyana zovuta kumvetsa zomwe zimachitika m’maselo a zinthu zamoyo, anafotokoza kuti anthu amene amaphunzitsa zoti maselo a zinthu zamoyo amasintha pang’onopang’ono mpaka zamoyozo kusintha, alibe umboni womveka wotsimikizira zimenezi. Kodi n’zotheka kuti maselo oterewa asinthe n’kukhala zinthu zamoyo? Iye analemba kuti: “Mfundo yoti maselo ankasintha pang’onopang’ono n’kukhala zinthu zamoyo si yogwirizana ndi sayansi. Palibe magazini kapena buku lililonse la sayansi limene limafotokoza mmene maselo a zamoyo zinazake anasinthira n’kukhala zamoyo zopangidwa m’njira yovuta kumvetsa kwambiri. . . . Motero mfundo yoti zamoyo zinachita kusanduka kuchokera ku timaselo ting’onoting’ono ndi nkhambakamwa zopanda umboni uliwonse.”

Ngati anthu amene amanena kuti anthu anachita kusanduka kuchokera ku zinyama alibe umboni wotsimikizira mfundo yawoyi, n’chifukwa chiyani amaikakamira kwambiri? A Behe anati: “Anthu ambiri, kuphatikizapo asayansi ambiri otchuka ndiponso opatsidwa ulemu, safuna kuvomereza kuti kungakhalenso winawake amene analenga zinthu.”

Atsogoleri a zipembedzo zosiyanasiyana amakhulupirira chiphunzitso choti anthu anachita kusanduka kuchokera ku zinyama pofuna kuoneka ngati ophunzira. Anthu amenewa ali ngati anthu omwe mtumwi Paulo anawafotokoza m’kalata imene analembera Akhristu a ku Roma. Iye analemba kuti: “Zimene anthu angathe kudziwa ponena za Mulungu zikuonekera pakati pawo . . . makhalidwe a Mulungu osaoneka ndi maso akuonekera bwino lomwe. Makhalidwe a Mulungu amenewa, ngakhalenso mphamvu zake zosatha ndiponso Umulungu wake, zikuonekera m’zinthu zimene anapanga moti anthuwo alibenso chifukwa chomveka chodzilungamitsira. Chifukwa chakuti, ngakhale atam’dziwa Mulungu, iwo sanam’patse ulemerero monga Mulungu kapena kumuyamikira. M’malo mwake anayamba kulingalira zinthu zopanda pake ndipo mtima wawo wopusawo unachita mdima. Ngakhale anali kunenetsa kuti ndi anzeru, iwo anakhala opusa.” (Aroma 1:19-22) Kodi mungatani kuti mupewe kupusitsidwa ndi aphunzitsi onyengawa?

Chikhulupiro Choti Kuli Mlengi Chili ndi Umboni Wotsimikizirika

Ponena za tanthauzo la chikhulupiriro, Baibulo limasonyeza kuti umboni ndi wofunika kwambiri kuti munthu akhale ndi chikhulupiriro. Limati: “Chikhulupiriro ndicho chiyembekezo chotsimikizika cha zinthu zoyembekezeredwa, umboni wooneka wa zinthu zenizeni, ngakhale kuti n’zosaoneka.” (Aheberi 11:1) Chikhulupiriro chenicheni mwa Mulungu chiyenera kukhala chogwirizana ndi umboni umene ulipo wosonyeza kuti Mlengi alikodi. Baibulo limasonyeza kumene mungapeze umboni umenewu.

Mouziridwa ndi Mulungu, Davide analemba kuti: “Ndikuyamikani chifukwa kuti chipangidwe changa n’choopsa ndi chodabwiza; ntchito zanu n’zodabwiza; moyo wanga uchidziwa ichi bwino ndithu.” (Salmo 139:14) Kupeza nthawi yoganizira za kudabwitsa kwa thupi lathu lenilenili komanso za kudabwitsa kwa zamoyo zina kumatichititsa kugoma kwambiri chifukwa cha nzeru zakuya za Mlengi. Zinthu zosawerengeka zimene zimachitika m’thupi mwathu, monga kayendedwe ka magazi, zomwe zimathandiza kuti tikhale ndi moyo, n’zodabwitsa kwambiri. Kasanjidwe ndiponso kayendedwe ka zinthu zosiyanasiyana zakuthambo kamaperekanso umboni wakuti panagona masamu ndiponso dongosolo logometsa kuti zinthu zimenezi zikhalepo. Davide analemba kuti: “Zakumwamba zimalalikira ulemerero wa Mulungu; ndipo thambo lionetsa ntchito ya manja ake.”​—Salmo 19:1.

Baibulonso palokha limapereka umboni wosaneneka wakuti kuli Mlengi. Pezani nthawi yowerenga Baibulo kuti muone nokha kugwirizana kwa mabuku ake 66, komanso kuti muone mfundo zake zapamwamba ndiponso maulosi ake omwe salephera kukwaniritsidwa. Mukatero mudzapeza umboni wakuti mlembi wa buku limeneli ndiye Mlengi. Kumvetsa zimene Baibulo limaphunzitsa kungakuthandizeninso kuona kuti n’zoonadi, Baibulo ndi Mawu a Mlengi. Mwachitsanzo, mukayamba kumvetsa zimene Baibulo limaphunzitsa zokhudza zinthu monga chifukwa chimene anthu amavutikira, Ufumu wa Mulungu, tsogolo la anthu, ndiponso njira yokhalira wosangalala, mudzaona nokha umboni wosonyeza nzeru za Mulungu. Mukatero mungathe kumva ngati mmene Paulo anamvera polemba kuti: “Ha, kuchuluka kwa chuma cha Mulungu! Nzeru zake n’zozama, ndipo kudziwa kwake zinthu n’kozamanso zedi! Ziweruzo zake ndi zosasanthulika, ndipo ndani angatulukire njira zake?”​—Aroma 11:33.

Mukamaona umboni umenewu ndiponso chikhulupiriro chanu chikayamba kukula, mudzakhutira kuti mukamawerenga Baibulo, kwenikweni mumakhala mukumvetsera mawu a Mlengi. Iye amati: “Ine ndalenga dziko lapansi, ndalengamo munthu; ine, ngakhale manja anga, ndafunyulula kumwamba, ndi zonse za mmenemo, ndinazilamulira ndine.” (Yesaya 45:12) Ndithu, mukatero simunganong’oneze bondo chifukwa cha khama lanu lofuna kutsimikizira kuti Yehova ndi Mlengi wa zinthu zonse.

[Mawu Otsindika patsamba 14]

Mtumwi Paulo anauza Agiriki ophunzira kuti: “Mulungu . . . kuchokera mwa munthu mmodzi anapanga mtundu wonse wa anthu”

[Mawu Otsindika patsamba 15]

Mfundoyi imasonyeza kuti anthu kwenikweni ndi nyama zimene moyo wawo ukusintha kuti ukhale wangwiro. Koma Baibulo limasonyeza kuti anthu anachokera kwa munthu yemwe anadzakhala wopanda ungwiro, motero moyo wa mbadwa zake zonse ukuipiraipira.

[Mawu Otsindika patsamba 16]

“Mfundo yoti maselo ankasintha pang’onopang’ono n’kusanduka zinthu zamoyo si yogwirizana ndi sayansi”

[Mawu Otsindika patsamba 17]

Kudabwitsa kwa zinthu zamoyo kumatichititsa kugoma kwambiri chifukwa cha nzeru zakuya za Mlengi