Kodi Ufumu wa Mulungu Uli mu Mtima Mwanu?
Zimene Owerenga Amafunsa
Kodi Ufumu wa Mulungu Uli mu Mtima Mwanu?
Anthu ambiri masiku ano amakhulupirira kuti yankho la funsoli n’lakuti inde. Mwachitsanzo, buku lina lachikatolika (The Catholic Encyclopedia) limati: “Ufumu wa Mulungu umatanthauza kuti . . . Mulungu akulamulira m’mitima yathu.” Atsogoleri a zipembedzo nthawi zambiri amaphunzitsa zimenezi. Koma kodi Baibulo limaphunzitsadi kuti Ufumu wa Mulungu uli m’mitima ya anthu?
Anthu ena amaganiza kuti Yesu ndi amene anaphunzitsa mfundo yakuti Ufumu wa Mulungu uli m’mitima ya anthu. N’zoona kuti Yesu anati: “Ufumu wa Mulungu uli pakati panu.” (Luka 17:21) Pa vesi limeneli, Mabaibulo ena amati: “Ufumu wa Mulungu uli mwa inu” kapenanso “uli m’kati mwanu.” Kodi Mabaibulo amenewa anamasulira molondola zimene Yesu ananenazi? Kodi Yesu ankatanthauzadi kuti Ufumu wa Mulungu uli m’mitima ya anthu?
Poyamba, tiyeni tione kaye kuti mtima wa munthu n’chiyani. Baibulo likamatchula za mtima wophiphiritsa limatanthauza umunthu wa m’kati, makhalidwe a munthu ndiponso maganizo ake. Mwachitsanzo, mfundo yoti Ufumu wa Mulungu womwe ndi chinthu chapamwamba kwambiri uli m’mitima mwa anthu ingamveke yosangalatsa chifukwa chakuti Ufumuwo ungasinthe munthuyo kukhala wabwino. Koma kodi Ufumu wa Mulungu ulidi mu mtima mwa munthu?
Baibulo limatiuza kuti: “Mtima ndiwo wonyenga koposa, ndi wosachiritsika.” (Yeremiya 17:9) Ndipotu Yesu anati: “M’katimo, mu mtima mwa munthu, mumatuluka maganizo oipa: za dama, za kuba, za umbanda, za chigololo, kusirira kwa nsanje, kuchita zoipa.” (Maliko 7:20-22) Taganizirani izi: Kodi simukuvomereza kuti mavuto ambiri amene alipo m’dzikoli anayamba chifukwa cha mitima yochimwa ya anthu? Nangano kodi Ufumu wolungama wa Mulungu ungachokere bwanji m’mitima yotereyi? Ndithudi, Ufumu wa Mulungu sungachokere mu mtima mwa munthu mofanana ndi mmene nthula sizingaberekere nkhuyu.—Mateyo 7:16.
Chachiwiri, taganizirani anthu amene Yesu ankawauza mawu amene ali pa Luka 17:21. Vesi la m’mbuyo mwa limeneli limati: “Afarisi atam’funsa za kuti Ufumu wa Mulungu udzabwera liti, iye anawayankha.” (Luka 17:20) Afarisi anali adani a Yesu. Ndipotu Yesu ananena kuti anthu achinyengo amenewo sadzalowa mu Ufumu wa Mulungu. (Mateyo 23:13) Choncho chifukwa choti Afarisi sanali oyenera kulowa mu Ufumu wa Mulungu, kodi Ufumuwo unali m’mitima yawo? Sizingatheke. Ndiyeno kodi Yesu ankatanthauza chiyani?
Pofotokoza mawu a Yesu amenewa, Mabaibulo ena anamasulira molondola mawuwa mofanana ndi Baibulo la Dziko Latsopano. Mabaibulo ena amati Ufumu uli “pakati panu” kapena “uli mwa inu.” Kodi Yesu ankatanthauza chiyani panthawiyo pamene anati Ufumu wa Mulungu unali pakati pa anthuwo kuphatikizapo Afarisi? Iye ananena mawu amenewa chifukwa choti Yehova Mulungu anali atam’sankha kale kukhala Mfumu ya Ufumu Wake, ndipo panthawiyi Yesuyo anali pakati pa anthuwa. Ndipo Yesu anawaphunzitsa anthuwo za Ufumu wa Mulungu komanso anachita zinthu zambiri zozizwitsa posonyeza zimene Ufumuwo udzachite. Choncho kunena zoona, Ufumuwo unali pakati pa anthu amenewa.
Kunena mosapita m’mbali, mfundo yoti Ufumu wa Mulungu uli m’mitima ya anthu ndi yosagwirizana ndi Malemba. Komano Ufumuwu ndi boma lenileni limene lidzasinthe kwambiri zinthu padziko lapansi pano mogwirizana ndi zimene aneneri analosera.—Yesaya 9:6, 7; Danieli 2:44.