Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kwa Owerenga

Kwa Owerenga

Kwa Owerenga

NDIFE osangalala kwambiri kukudziwitsani kuti kuyambira ndi Nsanja ya Olonda ino, magaziniyi yasintha zina ndi zina. Tisanafotokoze zimene zasintha, titchula kaye zimene sizinasinthe.

Dzina la magaziniyi lakuti Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova ndi lomweli silinasinthe. Choncho, Nsanja ya Olonda ipitiriza kulemekeza Yehova monga Mulungu woona ndiponso kulimbikitsa owerenga ndi uthenga wabwino wa Ufumu. Nkhani zoyambira pa tsamba 5 mpaka 9 za m’magazini ino zikulongosola kuti Ufumu umenewu n’chiyani ndiponso kuti udzabwera liti. Nsanja ya Olonda imalimbikitsanso anthu kukhulupirira Yesu Khristu. Imalongosolanso choonadi cha m’Baibulo ndi tanthauzo la zimene zikuchitika m’dzikoli masiku ano mogwirizana ndi maulosi a Baibulo, monga mmene yakhala ikuchitira kwa zaka zambiri.

Ndiyeno kodi chasintha n’chiyani? Tiyeni tione mbali zina zatsopano zosangalatsa kwambiri zimene zizikhala m’magazini ya pa 1 mwezi uliwonse. *

Mwezi uliwonse m’magaziniyi muzikhala nkhani zambiri zothandiza munthu kuganiza. Nkhani ya mutu wakuti “Kodi Mukudziwa?” izikhala ndi mfundo zochititsa chidwi zomwe zizifotokoza tanthauzo la nkhani zina za m’Baibulo. Nkhani yakuti “Yandikirani Mulungu” izitiuza mfundo zokhudza Yehova zimene tingaphunzire pa mavesi enaake a m’Baibulo. Ndiyeno nkhani yakuti “Zimene Owerenga Amafunsa” izifotokoza mayankho a mafunso a m’Baibulo amene anthu ambiri amafunsa. Mwachitsanzo, anthu ambiri amafunsa kuti “Kodi Ufumu wa Mulungu uli mu mtima?” Yankho la funso limeneli mulipeza patsamba 13.

Pali nkhani zinanso zimene zizituluka kawirikawiri zimene cholinga chake n’kuthandiza mabanja. Nkhani yakuti “Chinsinsi cha Banja Losangalala,” izituluka kanayi pachaka. Nkhani imeneyi izifotokoza mavuto enieni amene mabanja akukumana nawo ndipo izilongosola mmene mfundo za m’Baibulo zingathandizire kuthetsa mavutowo. Nkhani yakuti “Phunzitsani Ana Anu,” yomwe izituluka pakapita mwezi umodzi ndi yoti makolo aziwerenga pamodzi ndi ana awo. Nkhani imeneyi izituluka mosinthana ndi nkhani yakuti “Zoti Achinyamata Achite,” imene izikhala ndi zinthu zoti achinyamata achite zochokera m’Baibulo.

Nkhani zina zingapo zizituluka kanayi pachaka. Nkhani yakuti “Tsanzirani Chikhulupiriro Chawo” izitilimbikitsa kutsatira chitsanzo cha anthu otchulidwa m’Baibulo. Mwachitsanzo, m’magazini ino patsamba 18 mpaka 21, muwerenga nkhani yochititsa chidwi kwambiri ya mneneri Eliya ndipo muphunzira zimene muyenera kuchita potsanzira chikhulupiriro chake. Nkhani yakuti “Kalata Yochokera . . . ” izikhala ndi lipoti la amishonale ndiponso anthu ena a m’mayiko osiyanasiyana pa dziko lonse. Nkhani yakuti “Zimene Tikuphunzira kwa Yesu” izifotokoza mosavuta kumva zimene Baibulo limaphunzitsa.

Tikukhulupirira kuti anthu amene amalemekeza Baibulo ndiponso amene akufuna kudziwa zimene limaphunzitsa kwenikweni, apitiriza kusangalala ndi Nsanja ya Olonda. Tikukhulupiriranso kuti magaziniyi ikuthandizani kuthetsa ludzu lanu la choonadi cha m’Baibulo.

OFALITSA

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 4 Magazini a Nsanja ya Olonda tsopano azituluka awiri osiyana. Magazini ya pa 1 mwezi uliwonse ndi yogawira anthu onse ndipo ya pa 15 ndi imene Mboni za Yehova ziziphunzira pa misonkhano yawo ya mpingo imene aliyense ali wolandiridwa kufikapo.