Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Petulo Akana Yesu

Petulo Akana Yesu

Zoti Achinyamata Achite

Petulo Akana Yesu

Malangizo: Powerenga Baibulo khalani pa malo abata. Pamene mukuwerenga malemba, yerekezerani kuti inuyo mulipo pamene zimene mukuwerengazo zikuchitika. Onani zochitikazo m’maganizo mwanu. Yerekezerani kuti mukumva zimene anthuwo akulankhula. Yerekezerani kuti mukumva monga mmene anthu a m’nkhaniyo akumvera.

FOTOKOZANI MWACHIDULE.​—WERENGANI MATEYO 26:31-35, 69-75.

Kodi mukuganiza kuti m’nkhaniyi munali anthu angati?

․․․․․

Kodi mukuganiza kuti anthu amene analankhula ndi Petulo anali aubwenzi? ofunitsitsa kudziwa? okwiya? zina?

․․․․․

Kodi mukuganiza kuti Petulo anamva bwanji ndi zimene anthuwo ankanena?

․․․․․

N’chifukwa chiyani Petulo anakana Yesu? Kodi n’chifukwa choti analibe chikondi, kapena pali chifukwa china?

․․․․․

SINKHASINKHANI KWAMBIRI.​—WERENGANI LUKA 22:31-34; MATEYO 26:55-58; YOHANE 21:9-17.

Kodi kudzidalira mopambanitsa kunachititsa bwanji kuti Petulo alakwe?

․․․․․

Kodi Yesu anasonyeza bwanji kuti ankakhulupirira Petulo, ngakhale kuti iye ankadziwa kuti Petuloyo amukana?

․․․․․

Ngakhale kuti Petulo anakana Yesu, kodi iye anasonyeza motani chikhulupiriro cholimba kuposa ophunzira ena?

․․․․․

Kodi Yesu anasonyeza bwanji kuti anakhululukira Petulo?

․․․․․

Kodi mukuganiza kuti n’chifukwa chiyani Yesu anafunsa Petulo katatu kuti: “Kodi umandikonda ine?”

․․․․․

Kodi mukuganiza kuti Petulo anamva bwanji atatha kukambirana zimenezi ndi Yesu, ndipo n’chifukwa chiyani mukuganiza choncho?

․․․․․

GWIRITSANI NTCHITO ZIMENE MWAPHUNZIRA. LEMBANI ZIMENE MWAPHUNZIRA ZOKHUDZA . . .

Kuopa anthu.

․․․․․

Mmene Yesu anasonyezera chifundo kwa ophunzira ake, ngakhale pamene ophunzirawo analakwa.

․․․․․

Kodi n’chiyani chimene chakusangalatsani kwambiri mu nkhaniyi, ndipo n’chifukwa chiyani?

․․․․․