Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Zimene Yehova Amalosera Zimakwaniritsidwa

Zimene Yehova Amalosera Zimakwaniritsidwa

Zimene Yehova Amalosera Zimakwaniritsidwa

“INE ndine Mulungu, ndipo palibenso wina; ndipo palibenso wina wofanana ndi Ine; ndilalikira za chimaliziro kuyambira pachiyambi, ndi kuyambira nthawi zakale ndinena zinthu zimene zisanachitidwe.” (Yesaya 46:​9, 10) Ananena zimenezi ndi Yehova, amene amatha kulosera za m’tsogolo mosaphonyetsa.

Anthu ambiri amadziwa kuti maulosi a anthu si odalirika. N’chifukwa chake anthu ofuna kudziwa choonadi amachita chidwi ndi mfundo yakuti Baibulo ndi buku la maulosi motero amayesetsa kufufuza zimene limanena zakuti linauziridwa ndi Mulungu. Tiyeni tione maulosi ena a m’Baibulo amene akwaniritsidwa kale.

Mitundu Yakale

Mulungu analosera kuti Edomu, Moabu, ndi Amoni adzawonongedwa kosatha. (Yeremiya 48:42; 49:​17, 18; 51:​24-26; Obadiya 8, 18; Zefaniya 2:​8, 9) Mitundu ya anthu imeneyi inatha yonse, ndipo zimenezi zikusonyeza kuti ulosi wa m’Mawu a Mulungu unakwaniritsidwa.

N’zoona kuti anthu ena angakayikirebe ulosiwu ndipo anganene kuti mtundu wina uliwonse, ngakhale utakhala wamphamvu bwanji, sungakhalepo mpaka kalekale. Komatu mfundo imeneyi si yomveka ayi, chifukwa ulosi wa m’Baibulo unatchula zinthu zambiri. Mwachitsanzo, unafotokoza mwatsatanetsatane za mmene mzinda wa Babulo udzawonongedwere. Baibulo linalosera kuti mzindawo udzagonjetsedwa ndi Amedi, kuti mtsogoleri wa adaniwo adzakhala Koresi, ndiponso kuti mitsinje yoteteza mzindawo idzaphwetsedwa.​—Yesaya 13:​17-19; 44:27–45:1.

Sikuti ulosi uliwonse wa m’Baibulo wonena za kuwonongedwa kwa mtundu wa anthu umati mtunduwo udzawonongedwa kosatha. Mwachitsanzo, polosera zakuti Ababulo adzawononga Yerusalemu, Mulungu anati mzindawo udzamangidwanso, ngakhale kuti Ababulo anali ndi mfundo zokhwima zosalola akaidi awo kumasulidwa. (Yeremiya 24:​4-7; 29:10; 30:​18, 19) Ulosiwu unakwaniritsidwa, ndipo tikunena pano mtundu wa Ayuda udakalipobe.

Yehova analoseranso kuti dziko la Aiguputo lidzagonjetsedwa moti silidzakhalanso ulamuliro wamphamvu kwambiri padziko lonse koma kuti “pambuyo pake adzakhalamo anthu, monga masiku akale.” Patapita nthawi, ulamulirowu unali kudzakhala “ufumu wopepuka.” (Yeremiya 46:​25, 26; Ezekieli 29:​14, 15) Zimenezinso zinakwaniritsidwa. Komanso Yehova analosera kuti ufumu wa Girisi udzagonjetsedwa moti sudzakhalanso ulamuliro waukulu kwambiri padziko lonse, koma sananenepo kuti ufumu umenewu sudzakhalaponso. Motero tingathe kuona kuti mitundu yonse imene Yehova analosera kuti idzatheratu inaterodi pamene imene sananene kuti idzatheratu, idakalipo. Kodi tikuphunzira chiyani pa mfundo imeneyi? Tikuphunzirapo kuti Mawu a Mulungu ali ndi maulosi odalirika.

Amanena Zinthu Mwatsatanetsatane

Monga taonera, Yehova ananena mwatsatanetsatane za mmene Babulo adzagonjetsedwere. Anachitanso chimodzimodzi polosera za kugonjetsedwa kwa Turo. Buku la Ezekieli limati miyala, mitengo, ndiponso fumbi zidzaikidwa “m’madzi.” (Ezekieli 26:​4, 5, 12) Ulosi umenewu unakwaniritsidwa mu 332 B.C.E. pamene Alesandro Wamkulu ndi gulu lake la asilikali anagwiritsira ntchito mabwinja a mzindawo pomanga msewu wopita ku mbali ina ya mzindawo, yomwe inali pa chilumba ndipo atatero anagonjetsanso chilumbacho.

Ulosi umene uli pa lemba la Danieli 8:​5-8, 21, 22 ndi 11:​3, 4 umanenanso mwatsatanetsatane za “mfumu ya Helene” yamphamvu zodabwitsa kwambiri. Ulosiwu unati wolamulira ameneyu adzafa atafika pachimake pa ulamuliro wake, ndipo ufumu wake udzagawidwa panayi koma sudzapita kwa anthu a mbumba yake. Patapita zaka zoposa 200 ulosiwu utalembedwa, Alesandro Wamkulu anadzakhala mfumu yamphamvu kwambiri. Mabuku a mbiri yakale amanena kuti iyeyu anafa mosayembekezereka ndipo anthu amene anagawana ufumu wake anali akazembe ake anayi, osati mbumba yake ayi.

Anthu ena otsutsa Baibulo amanena kuti ulosi umenewu uyenera kuti unalembedwa pambuyo poti zinthuzo zachitika kale. Onaninso nkhani ya m’buku la Danieli, imene tatchula pamwambayi. Nkhaniyi ndi yodabwitsa kwambiri mukaganizira kuti ndi yaulosi. Komano kodi kanakhala kuti inalembedwa pambuyo poti zinthuzo zachitika kale, sibwenzi itatchulanso zinthu zina zambirimbiri zomwe zinachitika panthawiyi? Ngati munthu winawake amene anakhalako Alesandro atamwalira ndi amene analemba nkhaniyi pofuna kugometsa anthu oiwerenga kuti aziona ngati ndi ulosi, n’chifukwa chiyani sanatchulemo mfundo yonena kuti Alesandro atangomwalira, ana ake awiri anayesa kulowa ufumu wa bambo awowo koma anaphedwa? N’chifukwa chiyani sananene kuti padzatenga zaka zambiri kuti akazembe anayiwo akhazikitse ulamuliro wawo m’madera osiyanasiyana a ufumu wa Alesandro? Ndiponso n’chifukwa chiyani sanatchule mayina a mfumu yamphamvuyo ndiponso akazembe ake anayiwo?

Anthu anayamba kale kunena kuti maulosi a m’Baibulo analembedwa pambuyo poti nkhanizo zachitika kale, koma mfundo imeneyi ndi yopanda umboni ndipo amaikonda ndi anthu amene amangothamangira kunena kuti n’zosatheka kuneneratu zam’tsogolo. Anthuwa savomereza kuti Baibulo ndi Mawu a Mulungu motero amafuna kuti chilichonse chizigwirizana ndi zimene anthu angathe kuchita basi. Komabe mwanzeru zake, Mulungu anachititsa kuti maulosi azikhala ndi mfundo zongokwanira kukhutiritsa anthu kuti iyeyo ndiye anauzira Baibulo. *

Maulosi a m’Baibulo angathe kulimbitsa chikhulupiriro chathu tikamapeza nthawi yosinkhasinkha za maulosi osiyanasiyana ndi mmene anakwaniritsidwira. Yesetsani kuphunzira maulosi a m’Baibulo. Bokosi limene lili pa tsamba 201 la m’buku la Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? lingakuthandizeni kutero. * Mukatsatira mfundo imeneyi, cholinga chanu chikhale kulimbitsa chikhulupiriro chanu. Cholinga chanu chisakhale kungowerenga kuti mumalize nkhaniyo. M’malo mwake sinkhasinkhani mfundo yakuti zimene Yehova walosera zimakwaniritsidwa.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 13 Kuti muwerenge mfundo zina zotsutsa bodza lakuti maulosi a m’Baibulo analembedwa zinthuzo zitachitika kale, onani masamba 106 mpaka 111 a buku lachingelezi lakuti Is There a Creator Who Cares About You? Lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

^ ndime 14 Lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova

[Bokosi/​Chithunzi patsamba 24]

MFUNDO ZOTHANDIZA PAMOYO

Taonani mfundo ina yofunika kuiganizira. Mulungu amene analosera za kukhalapo komanso kugwa kwa maulamuliro amphamvu padziko lonse ndi amenenso anapereka mfundo za m’Baibulo zotithandiza pamoyo. Zina mwa mfundozo ndi izi:

Chimene munthu wafesa, adzakololanso chomwecho.​Agalatiya 6:7.

Kupatsa kumabweretsa chisangalalo chochuluka kuposa kulandira.​Machitidwe 20:35.

Kuti munthu akhale wosangalala ayenera kuzindikira zosowa zake zauzimu.​Mateyo 5:3.

Musakayike zoti mudzakhala wosangalala ngati mutsatira mfundo zimenezi pamoyo wanu.

[Zithunzi pamasamba 22 23]

Mawu a Mulungu analosera zoti mitundu iyi idzatheratu . . .

EDOMU

BABULO

 . . koma sanalosere kuti mtundu uwu udzatheratu

GIRISI

IGUPUTO

[Mawu a Chithunzi]

Pictorial Archive (Near Eastern

WHO photo by Edouard Boubat

[Chithunzi patsamba 23]

Alesandro Wamkulu