Kodi Tinachokera Kuti?
Kodi Tinachokera Kuti?
N’CHIFUKWA CHIYANI TIYENERA KUDZIWA YANKHO LA FUNSOLI? Anthu ambiri amaphunzitsidwa kuti zamoyo padziko lino zinakhalako mwangozi. Iwo amauzidwa kuti anthufe tinachita kusanduka kuchokera ku zinthu zina ngakhale kuti timaganiza, tili ndi nzeru ndiponso timatha kudziwa cholinga cha moyo.
Koma taganizirani izi: Tikanakhaladi kuti anthufe tinachita kusanduka ndiponso ngati kulibe Mlengi, ndiye kuti tinakakhala amasiye. Tikanakhalanso opanda yemwe angatipatse nzeru zakuya, zotithandiza pa mavuto athu. Bwenzi tikungodalira nzeru zathu basi kuti tipewe kuwononga chilengedwe, mavuto azandale, ndiponso mavuto athu ena.
Kodi mfundo yongodalira nzeru za anthu basi ingakuthandizeni kukhala ndi mtendere wa mumtima? Ngati singakuthandizeni, taganizirani zodalira njira ina yapadera. Sikuti yangokhala yosangalatsa basi, koma ndi yoyenera.
Zimene Baibulo Limanena
Baibulo limanena kuti anthufe tinalengedwa ndi Mulungu mwachindunji. Sitinasanduke kuchokera ku zinthu zina koma ndife ana a Tate wachikondi ndi wanzeru. Taonani mawu omveka bwino a m’Baibulo awa:
Genesis 1:27. “Mulungu ndipo adalenga munthu m’chifanizo chake, m’chifanizo cha Mulungu adam’lenga iye; adalenga iwo mwamuna ndi mkazi.”
Salmo 139:14. “Ndikuyamikani chifukwa kuti chipangidwe changa n’choopsa ndi chodabwiza; ntchito zanu n’zodabwiza; moyo wanga uchidziwa ichi bwino ndithu.”
Mateyo 19:4-6. “Kodi simunawerenge kuti iye amene analenga iwo pachiyambi pomwe anapanga iwo mwamuna ndi mkazi ndi kunena kuti, ‘Pa chifukwa chimenechi mwamuna adzasiya atate wake ndi amayi wake ndipo adzaphatikana ndi mkazi wake, ndipo awiriwo adzakhala thupi limodzi’? Kotero kuti salinso awiri, koma thupi limodzi. Choncho, chimene Mulungu wachimanga pamodzi, munthu asachilekanitse.”
Machitidwe 17:24, 25. “Mulungu amene anapanga dzikoli ndi zinthu zonse zili mmenemu, Iyeyu ndiye Ambuye wa kumwamba ndi dziko lapansi. Iye sakhala mu akachisi opangidwa ndi manja. Satumikiridwanso ndi manja a anthu ngati kuti amasowa kanthu, chifukwa ndi iye amene amapatsa anthu onse moyo, mpweya, ndi zinthu zonse.”
Chivumbulutso 4:11. “Ndinu woyenera, inu Yehova Mulungu wathu, kulandira ulemerero, ndi ulemu, ndi mphamvu, chifukwa munalenga zinthu zonse, ndipo chifukwa cha chifuniro chanu, zinakhalapo, inde zinalengedwa.”
Baibulo Limatithandiza Kukhala ndi Mtendere wa Mumtima
Kudziwa kuti Mulungu ndi “amene [anapangitsa] banja lililonse, . . . padziko lapansi, kukhala ndi dzina” kumasintha mmene timaonera anthu ena. (Aefeso 3:15) Kudziwa zimenezi kumakhudzanso mmene timadzionera ndi mmene timaonera mavuto athu. Tikatero tidzayamba kuona zinthu m’njira zotsatirazi.
Tikafunika kusankha zochita pankhani zikuluzikulu, sitidzadalira kwambiri maganizo a anthu chifukwa amasinthasintha. M’malo mwake tidzadalira ndi mtima wonse malangizo a m’Baibulo. Chifukwa? Chifukwa chakuti “malemba onse anawauzira ndi Mulungu, ndipo ndi opindulitsa pa kuphunzitsa, kudzudzula, kuwongola zinthu, kulangiza m’chilungamo, kuti munthu wa Mulungu akhale woyenera mokwanira, wokonzeka bwino lomwe kuchita ntchito iliyonse yabwino.”—2 Timoteyo 3:16, 17.
Ndithudi, kuti tigwiritse ntchito malangizo a m’Baibulo tifunika khama ndi kudziletsa. Nthawi zina kuti titsatire malangizo a m’Baibulo tingafunike kuti tisatsatire zimene mtima wathu ukufuna. (Genesis 8:21) Komabe, ngati timavomereza kuti tinalengedwa ndi Atate wathu wa kumwamba wachikondi, m’pomveka kunena kuti amadziwa zimene ife tiyenera kuchita kuti tikhale ndi moyo wabwino. (Yesaya 55:9) N’chifukwa chake Mawu ake amatitsimikizira kuti: “Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, osachirikizika pa luntha lako; um’lemekeze m’njira zako zonse, ndipo Iye adzaongola mayendedwe ako.” (Miyambo 3:5, 6) Tikagwiritsa ntchito malangizo amenewa, nkhawa zambiri zimene timakhala nazo tikamavutika ndiponso tikamasankha zochita zimachepa.
Anthu ena akamatisala, sitidzavutika kwambiri ndi maganizo odziona ngati ndife osanunkha kanthu poyerekezera ndi anthu afuko lina, mtundu wina kapena chikhalidwe china. M’malo mwake tizidziona kuti ndife ofunika chifukwa chakuti Atate wathu, Yehova Mulungu, “alibe tsankho. Iye amalandira munthu wochokera mu mtundu ulionse, amene amamuopa ndi kuchita chilungamo.”—Machitidwe 10:34, 35.
Tikadziwa zimenezi tidzapewanso kusala anthu ena. Tidzadziwa kuti palibe chifukwa chomveka chodzionera kuti ndife ofunika kwambiri kuposa anthu amtundu wina, popeza Mulungu “anapanga mtundu wonse wa anthu, kuti akhale pa nkhope yonse ya dziko lapansi.”—Machitidwe 17:26.
Ndithudi, tikadziwa kuti tinachita kulengedwa ndiponso kuti Mlengi wathu amatiganizira, timakhala ndi mtendere weniweni wa mumtima. Komabe pali zinanso zofunika kuchita kuti tikhalebe ndi mtendere wa mumtima.
[Mawu Otsindika patsamba 4]
Kodi anthu anachita kusanduka?
[Chithunzi patsamba 5]
Kudziwa kuti Mlengi wathu amatiganizira kungatithandize kukhala ndi mtendere weniweni wa mumtima