“Anditsogolera M’mabande a Chilungamo”
“Anditsogolera M’mabande a Chilungamo”
Yosimbidwa ndi Olga Campbell
“Munthu wa chitsanzo chabwino ali ngati munthu yemwe akuimba belu kuti ena azitsatira. Iweyo unaimba belu ndipo ine ndinatsatira.” Anatero mng’ono wanga Emily m’kalata yomwe anandilembera yondiyamikira chifukwa chotha zaka 60 ndikugwira ntchito yolalikira nthawi zonse. Tandilolani ndikufotokozereni za mmene moyo wanga unalili ndili mwana ndiponso mmene ndinayambira ntchito yolalikira nthawi zonse.
NDINABADWA pa January 19, 1927, ndipo makolo anga anali a ku Ukraine omwe ankakhala pa famu ina pafupi ndi tauni ya Wakaw ku Saskatchewan, m’chigawo chakumadzulo kwa Canada. Ine ndi mchimwene wanga, Bill, tinabadwa mapasa m’banja la ana 8. Anafe tinkathandiza bambo athu amene anali olimbikira kwambiri pantchito ya kumunda. Tinali kukhala m’nyumba yaing’ono ndipo amayi athu anali kutisamalira bwino kwambiri ngakhale kuti anali kudwala nyamakazi. Ndipo m’kupita kwa nthawi anamwalira ndi matendawa ali ndi zaka 37, ndipo ine ndinali ndi zaka zinayi zokha.
Patangopita miyezi 6 mayi atamwalira, bambo anakwatiranso. Ndipo banja lathu linawonjezeka ndi ana ena opeza asanu ndipo panali kusagwirizana kwambiri. Ndinali kuyesetsa kulemekeza amayi anga ondipeza koma mchimwene wanga wamkulu John sanali kugwirizana nawo.
Chakumapeto kwa m’ma 1930, ine ndi Bill tinayamba sukulu ya pulayimale ndipo tikakhala ku sukulu tinali kuiwalako mavuto apanyumba. Pamene nkhondo yachiwiri yapadziko lonse inali pafupi kuyamba, anthu ambiri anali kuchita zinthu zosonyeza kukonda kwambiri dziko lawo. Ndipo mphunzitsi wathu watsopano anayambitsa lamulo lolambira mbendera koma mtsikana wina anakana kuchita zimenezi. Ana ena pasukulupo anam’nyoza kwambiri. Komabe, ineyo ndinachita chidwi kwambiri ndi kulimba mtima kwake ndipo ndinam’funsa chifukwa chake anakana kulambira mbendera. Iye ananena kuti anali Wophunzira Baibulo, dzina lomwe Mboni za Yehova zinali kudziwika nalo nthawi imeneyo. Ndipo iye anati ayenera kukhala wokhulupirika kwa Mulungu yekha basi.—Eksodo 20:2, 3; Machitidwe 5:29.
Ndinachoka Panyumba
Mu 1943, ndinayamba ntchito m’mzinda wa Prince Albert yopakira m’galimoto zakumwa zoziziritsa kukhosi ndi kumakasiya ku malo osiyanasiyana. Kenako ndinagula Baibulo chifukwa ndinkafuna kuti Mulungu azinditsogolera. Koma ndinali kuvutika kwambiri kulimvetsa moti ndinali kulira chifukwa chokhumudwa. Pa zinthu zonse za m’Baibulo, ndinali kudziwa pemphero la Atate Wathu lokha basi.—Mateyo 6:9-13.
Lamlungu lina, mayi wina yemwe anali mwininyumba imene ndinkakhala komanso ankakonda kupita ku tchalitchi, anandiuza monyada kuti anakankha “mzimayi wa Baibulo” pakhomo pake. Ndinadabwa kuti anachita zimenezo chifukwa chiyani. Patapita milungu ingapo ndinadwala, motero sindinapite ku tchalitchi ndipo tsiku limenelo “mzimayi wa Baibulo” uja anabweranso.
Mzimayiyu anandifunsa kuti: “Kodi umapemphera?”
Ineyo ndinamuyankha kuti: “Ndimadziwa pemphero la Atate Wathu.”
Ndinamvetsera mwachidwi pamene iye ankafotokoza tanthauzo la mawu a Yesu opezeka m’pempheroli. Ndipo anandilonjeza kuti adzabweranso Lachitatu.
Mwininyumba uja atabwera, ndinamuuza mosangalala za “mzimayi wa Baibulo” yemwe anali wa Mboni za Yehova. Koma ndinakhumudwa mayiyu atandiuza kuti: “Amene uja akabweranso Lachitatulo ndidzakukankhirani panja nonse.”
Kenako ndinafufuza m’dera lonselo mzimayi wa mboni uja ndipo ndinauzidwa kuti dzina lake ndi mayi Rampel. Nditam’peza ndinam’fotokozera zomwe zinachitika ndipo ndinamupempha kuti andifotokozere zonse zokhudza Baibulo. Tinakambirana zambiri moti ndinkaona ngati tamaliza Baibulo lonse. Iye anayerekezera nthawi ino ndi masiku a Nowa, nthawi imene Mulungu anawononga dziko losalungama ndipo anapulumutsa Nowa ndi banja lake kuti akhale pa dziko lopanda anthu oipa.—Mateyo 24:37-39; 2 Petulo 2:5; 3:5-7, 12.
Titakambirana kwa nthawi yaitali, mayi Rampel ananena kuti: “Tsopano ndikuona kuti ukukonda choonadi cha m’Baibulo. Ndipo milungu iwiri ikubwerayi Mboni za Yehova zikhala ndi msonkhano waukulu ndipo iweyo ufunika kuti udzabatizidwe.” Tsiku limenelo sindinagone chifukwa ndinkangoganizira zimene ndinaphunzira zija. Ndinkaona kuti ubatizo unali chinthu chofunikira kuchiganizira kwambiri. Komabe ndinkafuna kutumikira Mulungu. Ngakhale kuti ndinali kudziwa zinthu zochepa za m’Baibulo, ndinabatizidwa pa October 15, 1943 ndili ndi zaka 16.
Ndinasamukira Kum’mawa kwa Canada
Mu November, mchimwene wanga Fred anandipempha kuti ndikayambe kugwira ntchito yosamalira m’nyumba yake yosanja yomwe inali m’mzinda wa Toronto kum’mawa kwa Canada. Ndinavomera chifukwa ndinkaona kuti ndikakhala ndi mwayi wolambira Yehova popanda zovuta zilizonse. Koma ndisanachoke ndinapita kukaona mkulu wanga yemwe ankakhala ku Saskatchewan. Iye anali ndi nkhani yabwino yoti andiuze. Nkhani yake inali yoti iye ndi Doris anali atayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova ndipo anandilimbikitsa kuti inenso ndiyambe. Kenako ndinamuuza kuti ndinali kale Mboni ya Yehova yobatizidwa.
Ineyo ndi mng’ono wanga Emily tinayenda ulendo wautali wa pasitima wopita ku Toronto. Titafika kumeneko tinapeza Bill akutidikirira pa siteshoni ndipo anatitengera ku nyumba kumene ankakhala pamodzi ndi Fred ndiponso John. Ndinafunsa Fred kuti ndaninso wina yemwe ankakhala m’nyumbayo. Iye anati: “Sukhulupirira zomwe nditi ndikuuze. Kodi ukumukumbukira Alex Reed yemwe tinkakhala naye kumudzi kuja? Iye ndi amene akukhala pamwambapa ndipo akuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova.” Ndinasangalala zedi.
Ndinayenda mwakachetechete kupita ku chipinda chosanja kumene Alex anali kukhala ndipo ndinagwirizana naye kuti tipite ku msonkhano usiku womwewo. Ndinkafunitsitsa kuti ndiyambe nthawi yomweyo kumapita ku misonkhano n’cholinga choti azichimwene anga asakhale ndi mpata wondifooketsa. Patapita nthawi yochepa, ndinapita kokalalikira kwa nthawi yoyamba ngakhale kuti ndinali ndisanaphunzitsidwe Baibulo mokhazikika. Ndinali kusangalala kwambiri kulankhula ndi anthu ambiri a ku Ukraine m’chinenero chimene ndinaphunzira ndili mwana.
Bill ankakonda kwambiri kuwerenga Nsanja ya Olonda, yomwe nthawi zambiri ndinkamuikira m’chipinda chake. Atasamukira ku chigawo cha British Columbia, chomwe chili kumadzulo kwa Canada, ndinam’lembetsera kuti azilandira magazini a Nsanja ya Olonda nthawi zonse. Ngakhale kuti Bill anali wosalankhulalankhula, anandilembera kalata yaitali ya masamba 10 yondithokoza. M’kupita kwa nthawi anabatizidwa n’kukhala mkulu wolimbikira kwambiri mumpingo. Ndinasangalala kwambiri pamene abale anga asanu omwe ndi Bill, Ann, Fred, Doris, ndi Emily anabatizidwa n’kukhala Mboni za Yehova.
Pa May 22, 1945, boma la Canada linachotsa lamulo loletsa ntchito ya Mboni za Yehova. * Ndipotu ineyo sindinkadziwa kuti Mboni za Yehova zinali zoletsedwa kufikira pamene ndinkamva chilengezochi. Ineyo ndi mnzanga Judy Lukus tinaganiza zoti tiyambe ntchito yolalikira nthawi zonse monga apainiya. Ndipo tinasankha kukatumikira ku dera lakutali kum’mawa kwa Quebec komwe anthu amalankhula Chifalansa. Azichemwali anga, Doris ndi Emily atamva zimenezi nawonso anaganiza zochita upainiya mu mzinda wa Vancouver, ku British Columbia, womwenso unali kutali.
Mboni za Yehova Zinkazunzidwa ku Quebec
Nditasamukira ku Quebec, zinthu zingapo zinasintha pa moyo wanga. Mboni za Yehova kumeneku zinkazunzidwa kwambiri chifukwa cha ntchito yawo yolalikira. * Ndinasangalala kwambiri kugawira nawo kapepala kenakake kapadera. (Quebec’s Burning Hate for God and Christ and Freedom Is the Shame of All Canada) Kapepalaka kanafotokoza nkhanza zimene anthu ankachitira Mboni za Yehova.
Tsiku lililonse kwa masiku 16, tinkadzuka 2 koloko ya m’mamawa n’kupita mwakachetechete kukasiya timapepalati pa makomo a anthu. Titafika pa nyumba ina, tinazindikira kuti apolisi ankatitsatira kuti adzatigwire motero tinabisala m’kanjira kakang’ono. Tsiku lotsatira, tinabwereranso m’misewu n’kumagawira magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! M’kati mwa miyezi ingapo tinamangidwa kambirimbiri. Nthawi zonse ndinkayenda ndi nswachi ndiponso tizinthu tina tofunika kwambiri n’cholinga choti ndidzatigwiritse ntchito ngati n’tamangidwa.
Mu November 1946, Nathan Knorr, yemwe ankatsogolera ntchito yonse ya Mboni za Yehova anatichezera kuchokera ku Brooklyn, New York. Apainiya tonse a ku Quebec okwana 64, anatiitana kuti tikalowe nawo m’kalasi ya chi 9 ya Sukulu ya Gileadi Yophunzitsa Baibulo, ku South Lansing, New York. Kusukuluyi tinaphunzitsidwa Baibulo mozama kwa miyezi isanu. Titamaliza maphunzirowa mu August 1947, anatitumiza ku matauni osiyanasiyana a mu Quebec kuti tikayambitse mipingo yatsopano.
Utumiki Wosangalatsa
Anayi mwa atsikana omwe tinamaliza maphunzirowa tinatumizidwa ku mzinda wa Sherbrooke. Tinkayesetsa mwa khama kuphunzira Chifalansa ndipo tikamapita kapena kubwera kolalikira tinkatchula mawu achifalansa mobwerezabwereza kuti tisaiwale. Nthawi zina panthawi yopuma masana sitinkakhala ndi ndalama zogulira chakudya, motero tinkangopita ku nyumba n’kumakawerenga. Mnzanga Kay Lindhorst, ankadziwa kwambiri Chifalansa. Motero iye choyamba anandiphunzitsa Chingelezi n’cholinga choti ndisavutike kuphunzira Chifalansa.
Nthawi yosangalatsa kwambiri paupainiya wathu ndi imene tinali ku Victoriaville, tauni yomwe panthawiyo inali ndi anthu okwana 15,000. M’tauni imeneyi munali anthu ochepa otha kulankhula Chingelezi, motero anali malo abwino oti tiphunzire bwino Chifalansa. Mlungu woyamba womwe tinakhala kumeneku unali wosangalatsa kwambiri. Kulikonse kumene tinkapita, anthu ankalandira mabuku athu. Koma titabwererako, tinaona kuti zitseko ndi mawindo zinali zotseka. Kodi chinachititsa zimenezi n’chiyani?
Wansembe wina wachikatolika anali atachenjeza anthuwo kuti asamvetsere uthenga wathu. Motero pamene tinkayenda khomo ndi khomo, ana ankatitsatira n’kumatigenda ndi miyala ndiponso zibulumwa za chipale chofewa. Komabe, anthu ambiri ankafuna kumvetsera uthenga wathu wa m’Baibulo. Poyamba, ankangotilola kuti tizifika pakhomo pawo mdima ukagwa. Koma atayamba kudziwa zinthu
zambiri za m’Baibulo, anayamba kuvomera kuti tiziphunzira nawo poyera ngakhale kuti anthu omwe anayandikana nawo sanali kusangalala nazo.M’ma 1950, ine ndi azichemwali anga tinapita ku Wakaw kukacheza. Ndipo pamsonkhano wina wa mpingo tinafotokoza zina mwa zinthu zomwe tinasangalala nazo m’ntchito yathu yolalikira. Msonkhano utatha, mkulu wina wa mumpingowo anatiuza kuti: “Amayi anu adzasangalala kwambiri akadzaukitsidwa n’kudzamva kuti ana awo anakhala Mboni za Yehova.” Mkuluyu anapitiriza kunena kuti amayi athu ankaphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova asanamwalire. Misozi inalengeza m’maso mwathu titadziwa kuti amayi athu anali kuphunzira choonadi cha m’Baibulo chomwe sitikukayika kuti akanakhala moyo akanatiphunzitsanso.
Kutumikira Limodzi ndi Mwamuna Wanga
Mu 1956, ndinakumana ndi Merton Campbell, m’bale yemwe anakhala m’ndende kwa miyezi 27 chifukwa chosalowerera m’nkhani zandale panthawi ya nkhondo yachiwiri yapadziko lonse. Iye anali atatumikira ku likulu la Mboni za Yehova ku Brooklyn pafupifupi zaka 10. Merton anali ndi makhalidwe abwino chifukwa chophunzira Baibulo ndipo ndinaona kuti angakhale mwamuna wabwino. Tinalemberana makalata kwa miyezi ingapo, ndipo chikondi chathu chinakula kwambiri.
Pa September 24, 1960, ineyo ndi Merton tinakwatirana. Ndadalitsidwa kwambiri kutumikira limodzi ndi mwamuna wanga kwa zaka 47, yemwe ndi wokonda kwambiri zinthu zauzimu. Iye wakhala akutumikira pa Beteli mu Dipatimenti ya Utumiki kwa zaka 58. Ndipo dipatimentiyi imayang’anira ndi kupereka malangizo ku mipingo yonse ya Mboni za Yehova m’dziko la America. Ndipo ineyo ndakhala ndikugwira ntchito yokongoletsa zipinda zogona alendo pa Beteli ya ku Brooklyn kwa zaka zoposa 30. Ndipo kenaka ndinayamba kugwira ntchito yokongoletsa Nyumba za Misonkhano zikuluzikulu za ku New York City. Ndiyeno, mu 1995, ineyo ndi mwamuna wanga anatisamutsira ku Watchtower Educational Center ku Patterson, mtunda wa makilomita pafupifupi 110 kumpoto kwa New York City.
Nthawi imene ndinkachoka panyumba ndili ndi zaka 12, sindinkadziwa kuti tsiku lina ndingadzakhale m’banja lalikulu lauzimu kuphatikizapo abale anga enieni. Ndikuyembekezera mwachidwi dziko la Mulungu latsopano pamene ineyo ndi azibale anga tidzawaunjirira amayi athu, n’kuwauza zomwe zinkachitika iwo atamwalira, makamaka mmene Yehova Mulungu anatithandizira kuti tidziwe choonadi. Ndife osangalala kwambiri chifukwa Yehova watithandiza kuti tiyende “m’mabande a chilungamo.”—Salmo 23:3.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 21 Chifukwa choti Mboni za Yehova sizilowerera nawo zandale, boma linaika lamulo loletsa ntchito ya Mbonizi pa July 4, 1940.
^ ndime 23 Kuti mumve zambiri zokhudza nkhanza zimene anthu ankachitira Mboni za Yehova ku Quebec, onani Galamukani! ya chingelezi ya April 22, 2000, masamba 20 mpaka 23.
[Zithunzi patsamba 27]
Awa ndi makolo anga ndipo iyi ndi nyumba imene tinkakhala ndi azibale anga 7
[Chithunzi patsamba 29]
Ndili ndi anzanga muutumiki ku Ottawa, 1952
[Chithunzi patsamba 29]
Ndili ndi azibale anga (kuchokera kumanzere mpaka ku manja) Ann, Mary, Fred, Doris, John, ineyo, Bill ndi Emily
[Chithunzi patsamba 29]
Ndili ndi Mwamuna wanga, Merton, masiku ano