Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Anthu Ozunzidwa Apatsidwa Ufulu

Anthu Ozunzidwa Apatsidwa Ufulu

Anthu Ozunzidwa Apatsidwa Ufulu

PA May 3, 2007, khoti lalikulu la ku Ulaya loona za ufulu wachibadwidwe wa anthu (European Court of Human Rights) mumzinda wa Strasbourg, ku France linapereka chigamulo chimene onse ozenga mlanduwo anagwirizana nacho. Chigamulocho chinali chokomera Mboni za Yehova m’dziko la Georgia. Khotilo linapeza kuti anthu a Mboni za Yehova anachitidwa nkhanza kwambiri ndiponso anawaphwanyira ufulu wawo wolambira. Khotilo linadzudzulanso boma lakale la dziko la Georgia chifukwa chosalanga anthu omwe ankachita nkhanza zimenezi. Kodi n’chiyani chinachititsa kuti khotili lipereke chigamulo chimenechi?

Pa October 17, 1999, anthu okwana 120 a mumpingo wa Mboni za Yehova wa Gldani mumzinda wa Tbilisi, anasonkhana mwamtendere n’cholinga choti alambire Yehova. Mwadzidzidzi gulu la anthu 200 linalowa mu chipinda chomwe munali Mbonizo. Gululi linatsogoleredwa ndi Vasili Mkalavishvili yemwe anachotsedwa pa udindo wa unsembe m’tchalitchi cha Orthodox. Kenako, gululi linamenya ndi kuvulaza ena mwa a Mboniwo ndi zibonga ndiponso zitsulo. Mayi wina anavulazidwa kwambiri diso moti silithanso kuona. Pafupifupi anthu 16 anawatengera ku chipatala. Anthu ena a Mboni anapita kukadandaula ku polisi. Koma mkulu wa apolisi anawauza kuti iyeyo akanakhala pa gululo, akanawakhaulitsa kwambiri a Mboniwo. Munthu wina yemwe anali pa gululo anajambula zachiwawazo pa vidiyo ndipo anakazionetsa pa wailesi ya kanema ya dzikolo. Choncho anthu onse amene anachita zachiwawazi anadziwika bwinobwino. *

Anthu a Mboni omwe anazunzidwawo analemba madandaulo awo n’kuwatumiza ku polisi. Koma apolisi sanamange anthu ochita zachiwawawo. Wapolisi amene anauzidwa kuti afufuze nkhani imeneyi anati anthu amene anachita zachiwawawo anali a tchalitchi chake cha Orthodox, choncho sakanatha kufufuza nkhaniyo mosakondera. Akuluakulu a boma sankachita chilichonse pankhaniyi ndipo zimenezi zinalimbikitsa anthu ena azipembedzo kumamenya Mboni za Yehova. Ndipo panali milandu yopitirira 100 yangati imeneyi.

Motero, pa June 29, 2001, Mboni za Yehova zinadula chisamani ku khoti lalikulu la ku Ulaya loona za ufulu wachibadwidwe wa anthu. * Khotili linapereka chigamulo chake chomaliza pa May 3, 2007. Popereka chigamulochi, khotili linafotokoza mwatsatanetsane za zimene zinachitika ndipo linadzudzula akuluakulu a boma chifukwa chosachitapo chilichonse pankhaniyi. Khotili linati: “A boma . . . anali ndi udindo woti afufuze mwamsanga nkhaniyi. Koma chifukwa choti iwo analekerera zimenezi, anthu ena angasiye kulemekeza boma ndiponso malamulo ake.”

Khotilo linamaliza mwa kugamula kuti: “Chiwawa chimene Mboni za Yehova zinachitiridwa pa 17 October 1999, chinali chachikulu kwambiri ndiponso iyi inali nthawi yoyamba kuti chiwawa choterechi chichitike. Choncho chifukwa chakuti boma silinachitepo chilichonse, zimenezi zinalimbikitsa anthu achiwawawo kuti apitirize kuzunza Mboni za Yehova m’dziko lonse la Georgia.”

Motero, anthu omwe anazunzidwawo anapatsidwanso ufulu wawo wachibadwidwe. Ndipo boma la Georgia analilamula kuti lilipire anthu a mumpingo wa Mboni za Yehova wa Gldani amene anazunzidwawo ndipo analilamulanso kuti likonzetse zinthu zonse zimene zinawonongeka. Sikuti Mboni za Yehova ku Georgia zikungosangalala chifukwa chakuti ziwawa zatha koma zikusangalalanso kuti chigamulo cha khoti chawapatsa ufulu wolambira. Chifukwa cha zimenezi, Mbonizi zikuyamikira kwambiri Atate wawo wa kumwamba Yehova Mulungu yemwe wakhala akuwatsogolera ndi kuwateteza nthawi yonseyi.​—Salmo 23:4.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 3 Kuti mumve zambiri, onani Galamukani! yachingelezi ya January 22, 2002, masamba 18 mpaka 24, yofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

^ ndime 5 Khoti limeneli (The European Court of Human Rights) ndi nthambi ya bungwe lina la ku Ulaya (Council of Europe) ndipo cholinga chake ndi kuonetsetsa kuti anthu sakuphwanya mfundo zimene anagwirizana pa msonkhano wina waukulu woona za ufulu wa anthu. Dziko la Georgia linasaina nawo panganoli pa May 20, 1999. Motero linavomereza kuti lizitsatira mfundo za kumsonkhanowu.