Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mukudziwa?

Kodi Mukudziwa?

Kodi Mukudziwa?

Kodi timakobili tiwiri ta mkazi wamasiye tinali tokwana ndalama zingati?

M’nthawi ya atumwi, Ayuda ankafunika kupereka msonkho wapachaka wa pakachisi wa ndalama zokwana “madalakima awiri.” Zimenezi zinali zofanana ndi malipiro a masiku awiri. (Mateyo 17:24) Koma Yesu anati mpheta ziwiri zinkagulidwa ndi “kakobili kamodzi kochepa mphamvu.” Kakobili kameneka kanali kokwana ndalama yolipira munthu yemwe wagwira ntchito kwa mphindi 45. Ndipotu mpheta zisanu zinkagulidwa ndi ndalama yokwana kulipira munthu yemwe wagwira ntchito kwa mphindi pafupifupi 90.​—Mateyo 10:29; Luka 12:6.

Ndalama zimene mkazi wamasiye wosauka anapereka pa kachisi zinali zochepa kwambiri poyerekezera ndi ndalama zogulira mpheta zisanu. Timakobiliti tinali ndalama zochepetsetsa kwambiri zomwe Aisiraeli ankagwiritsa ntchito m’nthawi imeneyi. Timakobiliti tinali tofanana ndi malipiro a munthu yemwe wagwira ntchito mphindi pafupifupi 12 patsiku.

Yesu Khristu anayamikira kwambiri ndalama zimene mkazi wamasiyeyu anapereka kuti zinali zambiri kuposa za anthu ena omwe ‘anatapa pa zochuluka zimene anali nazo.’ N’chifukwa chiyani Yesu anayamikira kwambiri mkaziyu? Nkhaniyi imati mkaziyu anali ndi “timakobili tiwiri tating’ono,” ndipo akanatha kupereka khobili limodzi ndi kusunga linalo. Koma iye anapereka “zonse zimene akanatha kuchirikiza nazo moyo wake.”​—Maliko 12:41-44; Luka 21: 2-4.

Kodi Saulo anayamba liti kutchedwa Paulo?

Mtumwi Paulo anali Mheberi ndiponso nzika ya Roma. (Machitidwe 22:27, 28; Afilipi 3:5) Motero zikuoneka kuti kuyambira ali mwana anali ndi maina onse, lachiheberi loti Saulo ndi lachiroma loti Paulo. Ndipo achibale ena a Paulo nawonso anali ndi mayina awiri, lachiroma ndi lachigiriki. (Aroma 16:7, 21) Komanso sizinali zachilendo kwa Ayuda a m’nthawi imeneyo kukhala ndi mayina awiri makamaka amene sankakhala m’dziko la Isiraeli.​—Machitidwe 12:12; 13:1.

Patapita zaka 10 mtumwiyu atakhala Mkhristu, zikuoneka kuti ankadziwika kwambiri ndi dzina lake lachiheberi loti Saulo. (Machitidwe 13:1, 2) Koma zikuoneka kuti anayamba kugwiritsa ntchito kwambiri dzina lake lachiroma loti Paulo, paulendo wake woyamba waumishonale womwe anayenda m’zaka za pakati pa 47 C.E. ndi 48 C.E. Popeza ntchito yake inali yolalikira uthenga wabwino kwa anthu omwe sanali Ayuda, anaona kuti anthu angam’landire bwino chifukwa cha dzina lake lachiroma. (Machitidwe 9:15; 13:9; Agalatiya 2:7, 8) N’kutheka kuti ankagwiritsanso ntchito dzina lakuti Paulo chifukwa chakuti katchulidwe ka m’chigiriki ka dzina loti Saulo ndi kofanana kwambiri ndi mawu ena a m’chigiriki otukwana. Kaya panali zifukwa zotani zimene zinam’pangitsa kuti ayambe kugwiritsa ntchito dzina lina, Paulo anali wofunitsitsa ‘kukhala zinthu zonse kwa anthu osiyanasiyana, kuti mulimonse mmene zingakhalire apulumutsepo ena.’​—1 Akorinto 9:22.

[Chithunzi patsamba 12]

Mmene khobili linalili