Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kuwonongedwa kwa Sodomu ndi Gomora

Kuwonongedwa kwa Sodomu ndi Gomora

Zoti Achinyamata Achite

Kuwonongedwa kwa Sodomu ndi Gomora

Malangizo: Chitani zotsatirazi muli pa malo opanda phokoso. Mukamawerenga mavesiwo, muziyerekezera kuti pamene zinthuzo zinkachitika inuyo munalipo. Yesani kuona nkhaniyi m’maganizo mwanu. Yerekezerani kuti mukumva mawu a m’nkhaniyi. Yesetsani kumva mu mtima mwanu ngati mmene ankamvera anthu a m’nkhaniyi.

ONANI BWINOBWINO NKHANIYI.​—WERENGANI GENESIS 19:1-14.

Ganizirani ndi kufotokoza maonekedwe a alendo a Loti.

․․․․․

Kodi ndi anthu otani amene anali pa gulu limene linafuna kupanga za chipongwe alendo a Loti?

․․․․․

FUFUZANI MOZAMA.​—WERENGANI GENESIS 13:7-13.

Kodi chinachitika n’chiyani kuti Loti azikhala ku Sodomu?

․․․․․

Kodi n’chifukwa chiyani Yehova anaona kuti n’koyenera kuwononga anthu okhala kumeneku?

․․․․․

WERENGANI GENESIS 19:15-26.

Kodi Yehova anasonyeza bwanji kum’komera mtima Loti?

․․․․․

Kodi n’chifukwa chiyani mkazi wa Loti anayang’ana m’mbuyo?

․․․․․

N’chifukwa chiyani anawonongedwa?

․․․․․

GWIRITSANI NTCHITO ZIMENE MWAPHUNZIRA. LEMBANI ZIMENE MWAPHUNZIRA PONENA ZA . . .

Mmene Yehova amaonera anthu ochita zoipa.

․․․․․

Chifundo cha Yehova.

․․․․․

Machenjezo amene Yehova amapereka asanalange anthu.

․․․․․

Kodi ndi mbali iti imene mwasangalala nayo kwambiri? Fotokozani chifukwa chake.

․․․․․