Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

March 22, 2008 ndi Tsiku Lofunika Kulikumbukira

March 22, 2008 ndi Tsiku Lofunika Kulikumbukira

March 22, 2008 ndi Tsiku Lofunika Kulikumbukira

Madzulo a tsiku loti aphedwa mawa, Yesu anapatsa atumwi ake mkate wopanda chotupitsa ndi chikho cha vinyo n’kuwauza kuti adye ndi kumwa. Anawauzanso kuti: “Muzichita zimenezi pondikumbukira ine.”​—Luka 22:19.

Chaka chino mwambo wokumbukira imfa ya Yesu umenewu udzachitika Loweruka, March 22, dzuwa litalowa. Mboni za Yehova padziko lonse zidzasonkhana kuti zichite mwambowu monga mene Yesu analamulira. Tikukuitanani ndi mtima wonse kuti mudzabwere ndi kudzaonerera mwambowu. Funsani Mboni za Yehova za kwanuko kuti zikuuzeni nthawi yeniyeni ndiponso malo kumene kudzachitikire mwambowu.