Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

N’chifukwa Chiyani Timakalamba ndi Kufa?

N’chifukwa Chiyani Timakalamba ndi Kufa?

N’chifukwa Chiyani Timakalamba ndi Kufa?

FUNSO limene asayansi aima nalo mitu kwa nthawi yaitali ndi loti: N’chifukwa chiyani anthu timakalamba ndi kufa? Asayansi ena amanena kuti mwachibadwa selo lili lonse lili ndi nthawi yake yokhalira ndi moyo. Ena amati ubongo umatulutsa timadzi tinatake timene timachititsa kuti munthu akalambe ndipo kenako n’kufa. Koma asayansi sali otsimikiza kuti mfundo yolondola ndi iti ndipo ambiri amavomereza kuti sakudziwa chimene chimachititsa kuti munthu akalambe.

Tikamaona zimene asayansi apeza, timaona kuti ambiri mwa iwo savomereza kuti kuli Mlengi. Iwo akuyesetsa kuti adziwe chimene chimachititsa anthu kuti azikalamba ndi kufa n’cholinga choti athandize anthu kuti azikhala ndi moyo wautali kapena kuti asamafe kumene. Asayansiwa amanyalanyaza mfundo ya Mlengi imene anauza Adamu ndi Hava kuti adzafa ngati sadzamvera. Ndiponso kuti anthu onse amene amakhulupirira Mwana wake adzalandira moyo wosatha.​—Genesis 2:16, 17; Yohane 3:16.

Chimene Chinayambitsa Imfa

Mulungu atalenga Adamu, anamuika m’munda wa Edeni momwe munali “mtengo wa moyo.” (Genesis 2:9) Zikuoneka kuti zipatso za mtengo umenewu zinalibe zinthu zina zake zapadera zopatsa moyo. Koma mtengowu unkaimira zimene Mulungu anafuna kuti aliyense yemwe angamulole kudya chipatsocho,akhale ndi moyo ku “nthawi zonse.” Koma Adamu atachimwa, sanaloledwenso kudya chipatso cha mtengo umenewu. (Genesis 2:16, 17) Yehova anati: “Ndipo tsopano kuti asatambasule dzanja lake ndi kutenga za mtengo wa moyo, ndi kudya, ndi kukhala ndi moyo nthawi zonse.” Kenako Yehova anachitadi monga mmene ananenera. Iye sanalole kuti anthu ochimwawo adye n’kupitirizabe kukhala ndi moyo m’munda umene munayenera anthu olungama okha basi.​—Genesis 3:22, 23.

Adamu ankasangalala ndi moyo wangwiro nthawi imene ankamvera Yehova. Koma tsopano anayamba kuvutika chifukwa cha uchimo ndipo kenako anafa. Komabe, iye anali ndi moyo wamphamvu ndithu. Ngakhale kuti tsopano anayamba kuvutika ndi uchimo ndiponso sanali pa ubwenzi ndi Mulungu, anakhalabe ndi moyo zaka 930. Ndipo iye anapatsira ana ake moyo wopanda ungwiro ndipo ena a iwo anakhala ndi moyo zaka 700 kapena 900.​—Genesis 5:3-32.

N’chiyani Chomwe Chili Chofunika Kuti Tikhale ndi Moyo?

Asayansi ambiri amanyalanyaza chimene chinachititsa kuti anthu azifa ndiponso mfundo ina yofunika zedi yothandiza kuti anthu apeze moyo wosatha. N’zoona kuti munthu amafunika mpweya wabwino, madzi akumwa ndi chakudya kuti apitirizebe kukhala ndi moyo. Koma pali chinthu china chofunika kwambiri kuposa zimenezi. Yehova anati: “Munthu sakhala wamoyo ndi mkate wokha, koma munthu akhala wamoyo ndi zonse zakutuluka m’kamwa mwa Yehova.”​—Deuteronomo 8:3.

Mulungu analenga munthu m’chifaniziro chake. (Genesis 1:26, 27) Zimenezi sizikutanthauza kuti munthu amaoneka ngati Mulungu chifukwa Mulungu ndi mzimu pomwe munthu ali ndi thupi lanyama. (Yohane 4:24) Izi zikutanthauza kuti munthu ndi amatha kuganiza, ali ndi makhalidwe a Mulungu monga chikondi, chilungamo, nzeru, ndi mphamvu, mosiyana ndi nyama zomwe ndi “zopanda nzeru.” (2 Petulo 2:12; yerekezerani ndi Akolose 3:10.) Munthu amadziwa chifukwa chake analengedwa ndiponso zimene Mlengi wake amafuna kwa iyeyo. N’chifukwa chake munthu ali ndi mtima wofuna kulambira. Choncho angathe kuyamikira ndi kulambira Mlengi. Munthu samangofunikira chakudya chenicheni chokha ayi, koma amafunikanso chakudya chauzimu. Munthu sangakhale ndi moyo wosatha popanda Yehova ndi zinthu zake za uzimu. Ponena za moyo wosatha, Yesu anati: “Moyo wosatha adzaupeza akamaphunzira ndi kudziwa za inu, Mulungu yekha woona, ndi za Yesu Khristu, amene inu munam’tuma.”​—Yohane 17:1-26.

Choonadi chimenechi chingatithandize kudziwa kuti Mulungu anapereka Yesu Khristu, yemwenso analolera “kudzapereka moyo wake dipo kuwombola anthu ambiri.” (Mateyo 20:28) Ndipo Khristu Yesu amatchedwa “Adamu womalizira . . . mzimu wopatsa moyo.” (1 Akorinto 15:45) Ulosi umanena kuti Khristu ndi “Atate Wosatha” ndiponso kuti iye “anathira moyo wake kuimfa.” Ndipo iye anapereka moyo wake “nsembe yopalamula.” Iye angathe kupereka moyo kwa anthu omwe ndi omvera komanso amene amakhulupirira nsembe yake ya dipo.​—Yesaya 9:6; 53:10-12.

Njira Yokhayo Yopezera Moyo Wosatha

Mtumwi Yohane anagwira mawu Yesu pamene ananena kuti: “Pakuti Mulungu anakonda kwambiri dziko mwakuti anapereka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense wokhulupirira mwa iye asawonongeke, koma akhale nawo moyo wosatha.” (Yohane 3:16) M’fanizo lake la nkhosa ndi mbuzi, Yesu ananena kuti anthu amene ali kudzanja lake lamanja, ndi nkhosa ndipo adzalandira “moyo wosatha.” (Mateyo 25:46) Adamu atalengedwa anali munthu wangwiro ndiponso “mwana wa Mulungu.” (Luka 3:38) Masomphenya a ulosi a pa lemba la Chivumbulutso 21:1-4 amanena za nthawi padzakhala “kumwamba kwatsopano” ndi “dziko lapansi latsopano.” Lembali limanenanso kuti: “Imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulira, kapena kubuula, ngakhale kupweteka.” Mulungu walonjeza anthu zinthu zimenezi osati angelo. Izi zikutitsimikizira kuti anthu m’dziko la pansi latsopano adzalamulidwa ndi “miyamba yatsopano” ndipo adzakhala ndi thanzi labwino ndiponso moyo wosatha monga “ana a Mulungu.”

Mulungu anauza Adamu kuti sadzafa ngati adzamvera malamulo ake. (Genesis 2:17) Imfa yomwe ndi mdani wamkulu wa anthu ikadzachotsedwa, anthu okhulupirika sadzafanso chifukwa adzakhala angwiro. (1 Akorinto 15:26) Imfayi idzachotsedwa ulamuliro wa Yesu wazaka 1,000 wotchulidwa m’buku la Chivumbulutso ukadzatha. Bukuli limanena kuti anthu adzalamulire ndi Khristu monga mafumu ndi ansembe “anakhalanso ndi moyo nalamulira monga mafumu limodzi ndi Khristu zaka 1,000.” Ndipo “akufa enawo” amene sadzakhala ndi moyo “kufikira zitatha zaka 1000” ayenera kuti ndi anthu amene adzakhale ndi moyo kumapeto kwa zaka 1000 koma Satana asanatulutsidwe ku phompho kuti adzayese anthu komaliza. Zaka 1000 zikadzatha, anthu padziko lapansi adzafika pokhala angwiro mofanana ndi m’mene Adamu ndi Hava analili asanachimwe. Anthu amene adzapambane mayesero omaliza, Satana akadzamasulidwa kuphompho kwa nthawi yochepa adzasangalala ndi moyo wosatha.​—Chivumbulutso 20:4-10.

Malinga ndi zimene Yesu ananena, n’zoonekeratu kuti zimene anthu akupanga poyesayesa kutalikitsa moyo, monga kudya zakudya zapadera kapena kuchita zinthu zina zapadera sizingatalikitse moyo. Komabe zimene akuchitazi zimangothandiza kwa nthawi yochepa. Njira yomwe ingatithandize kupeza moyo wosatha ndiyo kumvera uthenga wabwino, umene ndi “mawu a moyo.” (Afilipi 2:16) Kuti munthu apeze moyo wosatha ayenera kuika maganizo ake “pa zinthu za kumwamba, osati pa zinthu za padziko” (Akolose 3:1, 2) Yesu anauza omvera ake kuti: “Iye wakumva mawu anga ndi kukhulupirira iye amene anandituma ine ali nawo moyo wosatha, ndipo salowa m’chiweruzo koma wachoka ku imfa waolokera ku moyo.”​—Yohane 5:24; 6:40.