Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Sindinaonepo Chikondi Ngati Ichi”

“Sindinaonepo Chikondi Ngati Ichi”

Kalata Yochokera ku Dominican Republic

“Sindinaonepo Chikondi Ngati Ichi”

NIURKA wakamba nkhani yake yoyamba ya m’Baibulo mumpingo wathu mlungu uno. Iye anaikonzekera mwa kuilemba m’zilembo za anthu akhungu ndipo anailoweza pa mtima. Pokamba nkhaniyi papulatifomu ineyo ndinali ngati munthu yemwe ankafuna kuphunzira choonadi cha m’Baibulo. Ndipo tinkagwiritsa ntchito zida zokuzira mawu kuti zim’thandize Niurka kumva bwinobwino. Nkhaniyi itatha, anthu anayamikira powomba m’manja kwambiri moti Niurka anamva. Iye ankangomwetulira chifukwa cha chisangalalo chachikulu chimene anali nacho. Inenso ndinasangalala kwambiri. Ndipo n’zosangalatsa kwambiri kukhala mmishonale.

Ndimakumbukira tsiku loyamba limene ndinakumana ndi Niurka zaka ziwiri zapitazo. Unali ulendo wa pagalimoto wa mphindi 30 kuchokera kumene ndinkakhala kukafika kwawo. Patsikuli ndinam’peza atakhala pa khonde la nyumba ya zidina ndi matabwa yomwe denga lake ndi la malata adzimbiri. Fungo linali guu panyumbapo ndiponso panali phokoso lokhalokha chifukwa cha mbuzi, akalulu ndi agalu. Niurka anali atakhala pansi yekhayekha atazyolika kusonyeza kuti anali wovutika maganizo. Iye ankaoneka ngati wamkulu kwambiri kuposa zaka zake 34.

Nditam’gwira pa phewa anangotukula mutu ngakhale kuti anali atasiya kuona zaka 11 zapitazo. Kenako ndinamuuza dzina langa ndiponso la mnzanga yemwe ndinkalalikira naye mwa kulankhulira m’makutu ake mokweza. Patapita nthawi, tinauzidwa kuti Niurka amadwala matenda ena ake obadwa nawo osautsa kwambiri. Iye ankadwalanso matenda a shuga moti ankafunika chisamaliro chapadera kwambiri.

Nditam’patsa Baibulo, analizindikira ndipo ananena kuti ankakonda kwambiri kuliwerenga asanakhale wakhungu. Koma nkhawa yanga inali ya mmene ndikanam’phunzitsira Mawu a Mulungu munthuyu yemwe anali wadwaladwala, wosauka ndiponso wongokhala yekhayekha. Popeza ankadziwa alifabeti, ndinkaika zilembo zopangidwa ndi mapulasitiki m’manja mwake ndipo ankazizindikira. Kenako ankagwira manja anga ndikamalankhula ndi manja ndipo anayamba kudziwa chinenero cha manja cha ku America. M’kupita kwa nthawi anadziwa zambiri. Popeza inenso ndinali nditangoyamba kumene kuphunzira chinenerochi, ndinkathera nthawi yochuluka kukonzekera kuti ndikaphunzire naye. Komabe chifukwa choti ine ndi Niurka tinali ndi chidwi kwambiri, sitinachedwe kuchidziwa bwino chinenerochi.

Niurka anatha kupita patsogolo mwamsanga chifukwa bungwe lina linam’patsa zida zom’thandiza kuti azimva mosavuta. Ngakhale kuti zidazi sizinali zamakono, zinam’thandiza kwambiri. Niurka anakhala zaka zoposa 10 ali wakhungu komanso wosasangalala ndipo ankakonda kukhala kwa yekha. Koma tsopano mzimu wa Yehova unam’thandiza kudziwa zinthu za m’Baibulo, kukhala ndi chiyembekezo ndipo anayamba kukonda anthu ena. Posapita nthawi, anayamba kugwiritsa ntchito ndodo poyenda kuti apite kokalalikira choonadi cha m’Baibulo kwa anthu oyandikana nawo.

Niurka amaphunzitsa Baibulo azakhali ake ndi asuweni ake awiri. Iye amakonzekera bwino kwambiri ndipo amaloweza pa mtima phunziro lililonse. Anthu enawo amawerenga ndime, ndipo Niurka amawerenga funso m’buku lake la anthu akhungu. Mnzake amene amaphunzitsa naye anthuwa amamuuza zimene anthuwo ayankha mwa kulankhula m’makutu mwake mokweza kapena mwa kum’khudza pa mkono pake akamalankhula ndi manja.

Anthu onse a mumpingo wathu amam’thandiza ndi kum’limbikitsa. Abale ambiri a mumpingo amam’thandiza popita ku misonkhano ya mpingo ndiponso misonkhano ikuluikulu. Ndipo ena amapita naye kolalikira. Posachedwapa Niurka anandiuza kuti: “Sindinaonepo chikondi ngati ichi.” Iye akufunitsitsa kudzabatizidwa pa msonkhano wachigawo umene ukubwerawu.

Tikamadutsa kumene Niurka amakhala, timamuona atakhala pa khonde akuothera dzuwa. Timamuona akusangalala osati atazyolikanso ayi. Nditam’funsa chifukwa chake amakhala wosangalala, iye anati: “Ndimaganiza zam’tsogolo pamene dziko lonse lidzakhala paradaiso. Ndipo ndimadziona kuti ndili kale m’paradaiso ameneyu.”

[Chithunzi patsamba 25]

Niurka ali ndi anthu ena a mumpingo mwathu kutsogolo kwa Nyumba ya Ufumu

[Chithunzi patsamba 25]

Niurka akuphunzitsa anthu ena zimene waphunzira