Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Tikufunika Kupulumutsidwa

Tikufunika Kupulumutsidwa

MADZI ochuluka zedi anasefukira mu mgodi wina wa malasha womwe uli pafupi ndi mzinda wa Pittsburgh ku Pennsylvania, m’dziko la America. Panthawiyi n’kuti mumgodiwu muli anthu 9 ogwira ntchito ndipo anatsekerezedwa ku mbali ina ya mgodiwo komwe sikunafike madzi. Pamalo amenewa panali pokuya mamita 73 kuchokera pamwamba panthaka. Patapita masiku atatu, anthuwo anapezeka ali bwinobwino kunja kwa mgodiwo. Kodi anapulumutsidwa bwanji?

Anthu opulumutsa anzawo pangozi anagwiritsa ntchito mapu ndiponso makina ofufuzira malo apansi panthaka kuti adziwe pomwe panali anthuwo. Kuti atulutse anthuwo, anaboola dzenje lalikulu masentimita 65 koma lokuya kwambiri ndipo analowetsa chinthu chopangidwa ndi mawaya chooneka ngati chikwere. Anthuwo anatulutsidwa kunja mmodzimmodzi, kuwachotsa pa malo amene akanakhala manda awo. Ndiyeno anthu opulumutsidwawo anasangalala zedi ndipo anathokoza kwambiri anthu amene anawapulumutsawo.

Sikuti ambirife tingatsekerezedwe mu mgodi ngati mmene anachitira anthu 9 aja, ndipo mwina sitingafe pa ngozi. Komabe, m’pofunika kuti tipulumutsidwe ku mavuto osapeweka monga matenda, ukalamba ndi imfa. Ndipotu Yobu ananena kuti: “Munthu wobadwa ndi mkazi ngwa masiku owerengeka, nakhuta mavuto. Atuluka ngati duwa, nafota; athawa ngati mthunzi, osakhalitsa.” (Yobu 14:1, 2) Mawu amenewa adakali oona masiku ngakhale kuti tsopano papita zaka pafupifupi 3,500 kuchokera pamene ananenedwa. Izi zili choncho chifukwa palibe amene angazembe imfa. Motero, kaya tikukhala kuti kapena tikusamalira bwanji moyo wathu, tifunikira kupulumutsidwa ku mavuto monga ukalamba ndi imfa.

Asayansi komanso anthu ena amayesetsa mwakhama kuti atalikitse moyo. Ndipo bungwe lina linati cholinga chake ndi “kuthetsa imfa yosapeweka ndiponso kuthandiza anthu ake kuti azikhala ndi moyo wautali kapena asamafe kumene.” Koma mpaka pano, asayansi ndiponso anthu ena alephera kutalikitsa moyo kupyola zaka 70 kapena 80, zimene Mose ananena zaka 3,500 zapitazo.​—Salmo 90:10.

Kaya mukugwirizana ndi maganizo a Yobu pankhani ya moyo ndi imfa kapena ayi, simungapewe mfundo yakuti pamene zaka zikutha inunso ‘mudzathawa ngati mthunzi’ kapena kuti mudzafa. Mudzasiya anzanu, banja lanu, nyumba yanu ndiponso zinthu zanu zonse. Ndipotu Solomo, mfumu yanzeru ya Isiraeli wakale, inalemba kuti: “Pakuti amoyo adziwa kuti tidzafa; koma akufa sadziwa kanthu bi, sadzalandira mphotho; pakuti angoiwalika.”​—Mlaliki 9:5.

Chinthu chomvetsa chisoni chomwe Baibulo limafotokoza n’choti ‘imfa yakhala ikulamulira anthu monga mfumu’ yankhanza. Ndithudi, anthu akufunika kupulumutsidwa ku imfa yomwe ndi mdani womaliza. (Aroma 5:14; 1 Akorinto 15:26) Akatswiri opulumutsa anthu pangozi, ngakhale atakhala ndi zida zapamwamba, sangapulumutse anthu kumavuto awo onse. Komabe, Mlengi wathu Yehova Mulungu, wakonza njira yodalirika yotipulumutsira ku mavuto onse.