Anali Watcheru Ndiponso Anadikira
Tsanzirani Chikhulupiriro Chawo
Anali Watcheru Ndiponso Anadikira
ELIYA ankafunitsitsa kukhala payekha n’cholinga choti apemphere kwa Atate wake wakumwamba. Koma gulu la anthu linamuzinga chifukwa linamuona mneneriyu akupempha moto kuchokera kumwamba. Mosakayikira anthuwo ankafunitsitsa kuchita zinthu zomukopa mneneriyu kuti aziwayanja. Komano Eliya asanakwere pamwamba penipeni pa phiri la Karimeli kuti akapemphere payekha kwa Yehova Mulungu, anapatsidwa ntchito yovuta kwabasi. Ntchitoyo inali yoti akalankhule ndi mfumu Ahabu.
Koma Ahabu ndi Eliya anali anthu osiyana kwambiri. Ahabu, yemwe anali atavala zovala zachifumu, anali wadyera ndiponso wogalukira Mulungu. Eliya, anali atavala chovala cha mneneri chomwe mwina chinali chachikopa, kapena chopangidwa ndi ubweya wa ngamila kapena wambuzi. Mneneriyu anali munthu wolimba mtima ndiponso wokhulupirika. Panthawiyi, dzuwa linali litatsala pang’ono kulowa ndipo zimene zinachitika pa tsiku limeneli zinaonetseratu makhalidwe a anthu awiriwa. *
Tsikuli silinamuyendere bwino Ahabu pamodzi ndi anthu ena olambira Baala. Anthu olambira monyenga a mu ufumu wa Isiraeli wa mafuko khumi, amene ankatsogoleredwa ndi Ahabu ndiponso mkazi wake Yezebeli, anali atachititsidwa manyazi kwambiri. Zomwe zinachitika patsikuli zinasonyezeratu kuti Baala anali mulungu wonyenga. Mulungu wonyengayu sanathe kuyatsa moto ngakhale kuti aneneri a ake ankamuchonderera, kuvina ndiponso kudzichekacheka popemphera. Baala analepheranso kuteteza aneneri ake 450 amenewa kuti asaphedwe. Ndipo mulungu wonyengayu analepheranso kuchita chinthu chinachake, chomwe chinali chitatsala pang’ono kuchitika. Baala anali atalephera kuthetsa chilala chomwe chinakhalapo kwa zaka zoposa zitatu ngakhale kuti aneneri ake ankamuchonderera kwambiri kuti achithetse. Koma Yehova anali atatsala pang’ono kuonetsa kuti iye ndiye Mulungu woona mwa kuthetsa chilalacho.—1 Mafumu 16:30–17:1; 18:1-40.
Kodi Yehova anali kudzachita zimenezi liti? Nanga Eliya anayenera kutani isanafike nthawi imeneyo? Ndipo ifeyo tingaphunzirepo chiyani pa zimene munthu wokhulupirikayu anachita? Tiyeni tione zimenezi pamene tikukambirana nkhani yopezeka pa 1 Mafumu 18:41-46.
Ankakonda Kupemphera
Eliya anapita kwa Ahabu n’kumuuza kuti: “Nyamukani, idyani, imwani; popeza kumveka mkokomo wa mvula yambiri.” (Vesi 41) Kodi mfumu yoipayi inali itaphunzirapo kanthu pa zimene zinachitika patsikuli? Nkhaniyi siinena mwachindunji, koma timaona umboni wakuti iye sanalape ndiponso sanapemphe mneneriyu kuti am’pempherere kwa Yehova n’cholinga choti am’khululukire. M’malomwake, “Ahabu anapita kukadya, ndi kumwa.” (Vesi 42) Nanga Eliya anatani?
Nkhaniyo imati: “Koma Eliya anakwera pamwamba pa Karimeli, nagwadira pansi, naika nkhope yake pakati pa maondo ake.” Panthawi imene Ahabu amapita kukadya, Eliya anapeza mpata wopemphera kwa Atate wake. Tangoonani mmene Eliya anadzichepetsera popemphera, iye anagwada pansi n’kuwerama mpaka nkhope yake inatsala pang’ono kugunda maondo ake. Kodi Eliya anali kupempha chiyani? Tiyeni tione zimene Baibulo limanena. Lemba la Yakobe 5:18, limatiuza kuti Eliya anapemphera kuti chilala chithe. Motero n’zosakayikitsa kuti iye anapemphera zimenezi ali pamwamba pa phiri la Karimeli.
1 Mafumu 18:1) Choncho Eliya anapemphera kuti zimene Atate wake analonjeza zikwaniritsidwe. Ndipo patapita zaka 1,000 chichitikireni zimenezi, Yesu nayenso anaphunzitsa otsatira ake kuti azipemphera kuti zimene Mulungu amafuna zikwaniritsidwe.—Mateyo 6:9, 10.
M’mbuyomu, Yehova anali atalonjeza kuti: “Ndidzatumiza mvula padziko.” (Chitsanzo cha Eliya chikutiphunzitsa zambiri pankhani ya pemphero. Chinthu chofunika kwambiri m’pemphero la Eliya chinali choti zimene Atate amafuna zikwaniritsidwe. Tikamapemphera, ndi bwino kukumbukira kuti: “Chilichonse chimene tingapemphe mogwirizana ndi chifuniro chake, [Mulungu] amatimvera.” (1 Yohane 5:14) N’zoonekeratu kuti tiyenera kudziwa zimene Mulungu amafuna kuti iye ayankhe mapemphero athu. Choncho tiyenera kuphunzira Baibulo tsiku ndi tsiku. Eliya ankafunitsitsanso kuti chilala chithe chifukwa ankaona kuti anthu a mtundu wake akuvutika kwambiri. Zikuonekanso kuti anathokoza kwambiri chifukwa cha chinthu chozizwitsa chimene Yehova anachita pa tsikulo. Nafenso tikamapemphera tiyenera kusonyeza kuti tikudera nkhawa anthu ena ndiponso tizithokoza Mulungu mochokera pansi pa mtima.—2 Akorinto 1:11; Afilipi 4:6.
Anali Wokhulupirika Ndiponso Watcheru
Ngakhale kuti Eliya sankadziwa nthawi imene Yehova anali kudzathetsa chilala, iye ankakhulupirira kuti Yehova adzachitadi zimenezi. Koma kodi mneneriyu ankachita chiyani podikira nthawi imeneyo? Taonani zimene vesi 43 limanena: “Ndipo anati kwa mnyamata wake, Kwera kapenyerere kunyanja. Iye nakwera, napenyetsetsa, nati, Kulibe kanthu. Nati, Bwerezanso kasanu ndi kawiri.” Tikuphunzirapo zinthu ziwiri pachitsanzo cha Eliya chimenechi. Choyamba, mneneriyu anali ndi chikhulupiriro. Chachiwiri, anali watcheru.
Eliya anali ndi chidwi chofuna kudziwa umboni wosonyeza kuti Yehova anali atatsala pang’ono kuthetsa chilala. Motero anatuma mnyamata wake kuti akwere pamwamba penipeni pa phirilo n’cholinga choti aone kutali ngati kunali zizindikiro zoti mvula ingagwe. Mnyamatayo atabwerako, anauza Eliya uthenga wosalimbikitsa woti: “Kulibe kanthu.” Kunja kunali kuli mbee, kopanda mitambo. Koma kodi mwaona chinachake chapadera pankhani imeneyi? Kumbukirani kuti Eliya anali atangouza kumene mfumu Ahabu kuti: ‘Kukumveka mkokomo wa mvula yambiri.’ Kodi n’chiyani chinachititsa mneneriyu kunena zimenezi pomwe kunja kunali kopanda mitambo?
Eliya ankadziwa bwino zimene Yehova anali atalonjeza. Popeza iye anali mneneri ndiponso woimira Mulungu, ankakhulupirira kuti Mulungu akwaniritsa zimene analonjeza. Eliya anali ndi chikhulupiriro cholimba kwambiri moti ankangokhala ngati akumva mkokomo wamvula. Zimenezi zikutikumbutsa nkhani ya m’Baibulo yokhudza Mose. Nkhaniyo imati: “Anapitirizabe kukhala wochirimika ngati kuti akuona Wosaonekayo.” Kodi inuyo mumaona kuti Mulungu ndi weniweni? Iye watipatsa zifukwa zomveka bwino zoti tim’khulupirire iye ndiponso malonjezo ake.—Aheberi 11:1, 27.
Komanso, taonani mmene Eliya analili watcheru. Iye anatuma mnyamata wake, osati kwanthawi imodzi kapena ziwiri, koma nthawi 7. Tikhoza kuona mmene mnyamatayo anatopera chifukwa Vesi 44) Kodi mungathe kuona m’maganizo mwanu mnyamatayo akuyerekezera dzanja lake ndi kuchepa kwa kamtambo kamene kanaonekera kufupi ndi Nyanja Yaikulu? * N’kutheka kuti mnyamata wantchitoyo anaderera kamtambo kameneka. Koma kwa Eliya kamtamboka kanali chizindikiro champhamvu. Kenako iye analangiza mnyamata wake mwachangu kuti: “Kauze Ahabu, kuti, Mangani galeta, tsikani, mvula ingakutsekerezeni.”
choyenda mobwerezabwereza, koma Eliya sanafooke chifukwa ankafunitsitsa kuona chizindikiro choti kugwa mvula. Potsiriza, mnyamatayo atabwerako pa ulendo wa 7, anati: “Taonani, kwatuluka kunyanja kamtambo konga dzanja la munthu.” (Pamenepanso, Eliya akutipatsa phunziro labwino kwambiri. Nafenso tikukhala m’nthawi imene Mulungu watsala pang’ono kuti akwaniritse zofuna zake. Mofanana ndi Eliya yemwe anadikira mpaka pamene chilala chinatha, masiku anonso atumiki a Mulungu akudikira kutha kwa dongosolo loipa la zinthu lino. (1 Yohane 2:17) Tiyenera kukhala anthu atcheru ngati mmene analili Eliya kufikira pamene Yehova Mulungu adzachitepo kanthu. Yesu, yemwe ndi Mwana wa Mulungu analangiza otsatira ake kuti: “Chotero khalanibe maso chifukwa simukudziwa tsiku limene Ambuye wanu adzabwera.” (Mateyo 24:42) Kodi pamenepa Yesu anali kutanthauza kuti otsatira ake sadzadziwa chilichonse ponena za nthawi imene mapeto adzafike? Ayi. Chifukwa iye analongosola kwambiri za zizindikiro za m’nthawi yamapeto. Aliyense wa ife angadziwe za zizindikiro zolongosoledwa bwino za “mapeto a dongosolo lino la zinthu.”—Mateyo 24:3-7. *
Chizindikiro chilichonse chikupereka umboni womveka bwino ndiponso wamphamvu. Kodi umboni umenewu ndi wokwanira kuti utilimbikitse kukhala anthu atcheru? Kamtambo kamene kanaonekera kutali kwambiri kaja kanali kokwanira kuti Eliya akhulupirire zoti Yehova anatsala pang’ono kuthetsa chilala. Kodi zimene mneneri wokhulupirikayu ankayembekezera zinachitikadi?
Yehova Amapulumutsa Ndiponso Amadalitsa
Nkhaniyo imapitiriza kuti: “Ndipo kunali, polinda kanthawi, thambo linada ndi mitambo ndi mphepo, nigwa mvula yaikulu. Ndipo Ahabu anayenda m’galeta, namuka ku Yezreeli.” (Vesi 45) Zinthu zinayamba kusintha mofulumira kwambiri. Pamene mnyamata wa Eliya anapita kukapereka uthenga kwa Ahabu, kamtambo kaja kanakula, n’kudzaza kumwamba konse ndipo kunachita mdima. Kenako kunawomba chimphepo. Pomalizira pake, ngakhale kuti chilalacho chinatha zaka zitatu ndi theka, mvula yamphamvu inagwa m’dziko lonse la Isiraeli. * Nthaka yomwe inali youma ija inadzaza ndi madzi okhaokha. Chifukwa choti mvulayo inali yochuluka, mtsinje wa Kisoni unasefukira, ndipo madziwo anayeretsa nthaka imene inali ndi magazi a aneneri a Baala omwe anaphedwa. Ndipo Aisiraeli ena omwe anali atasiya kulambira koona nawonso anapatsidwa mwayi woti abwerere kwa Yehova mwa kuwononga chilichonse chokhudzana ndi kulambira Baala.
Ndipo Eliya ankakhulupirira kuti Aisiraeliwo adzachitadi zimenezi. Koma kodi Ahabu analapa ndi kusiya kulambira Baala? Iye anali ndi zifukwa zomveka zoti asinthire poona zinthu zomwe zinachitika patsikuli. N’zoona kuti sitingadziwe zomwe Ahabu anali kuganiza panthawiyo. Nkhaniyo imangotiuza kuti “Ahabu anali akuyenda pa galeta mpaka anakafika ku Yezereeli.” Kodi anaphunzirapo chilichonse pa zimenezi? Kapena kodi iye anasintha njira zake? Zimene zinachitika pambuyo pake zimasonyeza kuti sanasinthe. Ndipo panalinso zinthu zina zoti Ahabu komanso Eliya achite.
Mneneri wa Yehovayo anayamba ulendo wodzera m’njira imene Ahabu anadutsa. Ulendo wake unali wautali, kunja kunali kuli mitambo yakuda ndipo njirayo inali madzi okhaokha. Kenako panachitika chinthu china chodabwitsa.
Nkhaniyo imapitiriza kuti: “Dzanja la Yehova linakhala pa Eliya; namanga iye za m’chuuno mwake, nathamanga m’tsogolo mwa Ahabu ku chipata cha Yezreeli.” (Vesi 46) N’zoonekeratu kuti “dzanja la Yehova” linali kum’thandiza Eliya modabwitsa. Chifukwa Eliya anali wachikulire ndipo kuchokera kumene iye anali kukafika ku Yezreeli panali mtunda wa makilomita 30. * Taganizirani mneneriyo akukwinya chovala chake, n’kuchimangira m’chiuno kuti athe kuthamanga bwino. Ndiyeno anathamanga kwambiri m’njira yomwe inali madzi okhaokha mpaka kupeza galeta limene Ahabu anakwera ndipo analipitirira.
Amenewatu anali madalitso aakulu kwa Eliya. Ndipo zinali zinthu zolimbikitsa kwambiri kwa Eliya chifukwa anapatsidwa mphamvu zapadera zomwe mwina zinaposa zimene anali nazo ali wachinyamata. Zimenezi zikutikumbutsa maulosi amene amatitsimikizira kuti anthu okhulupirika adzakhala ndi thanzi labwino kwambiri m’paradaiso padziko lapansi. ( Yesaya 35:6; Luka 23:43) Zoonadi, pamene Eliya anali kuthamanga m’njira yomwe inali madzi okhaokha, anali kudziwa kuti Atate wake yemwe ndi Mulungu woona yekha anali kum’thandiza.
Yehova ndi wofunitsitsa kuti atipatse madalitso amenewa. M’pake kuchita zonse zomwe tingathe kuti tiwalandire. Mofanana ndi Eliya tifunika kukhala tcheru, kuonetsetsa umboni uliwonse wosonyeza kuti Yehova watsala pang’ono kuwononga dongosolo la zinthu loipali. Ndiponso, tili ndi zifukwa zonse zokhulupirira malonjezo a Yehova yemwe ndi “Mulungu wa choonadi.”—Salmo 31:5.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 4 Kuti mumve zambiri, onani nkhani yakuti “Sanasunthike Pakulambira Koona,” mu Nsanja ya Olonda ya January 1, 2008.
^ ndime 16 Masiku ano, Nyanja Yaikulu imadziwika ndi dzina loti Mediterranean.
^ ndime 17 Kuti mumve zambiri zokhudza umboni wakuti mawu a Yesu akukwaniritsidwa masiku ano, onani buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? pa mutu 9, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.
^ ndime 20 Anthu ena amaganiza kuti Baibulo limadzitsutsa pankhani ya kutalika kwa nthawi yachilala. Koma onani bokosi lomwe lili patsamba 19.
^ ndime 23 Zitachitika zimenezi, Yehova anauza Eliya kuti aphunzitse Elisa, yemwe anadzakhala ‘wothira madzi m’manja a Eliya.’ (2 Mafumu 3:11) Elisa anakhala mtumiki wa Eliya ndipo anali kum’thandiza pa zinthu zina ndi zina popeza anali wachikulire.
[Bokosi/Chithunzi patsamba 19]
Kodi Panadutsa Nthawi Yotalika Motani Kuti Chilala cha M’masiku a Eliya Chithe?
Eliya, mneneri wa Yehova anauza Mfumu Ahabu kuti chilala chomwe chinatenga nthawi yaitali chinali chitatsala pang’ono kutha. Eliya ananena zimenezi mu “chaka chachitatu” kuchokera panthawi imene iye analengeza kuti kudzakhala chilala. (1 Mafumu 18:1) Ndipo Yehova anavumbitsadi mvula, Eliya atangolengeza kumene kuti chilalacho chitha. Choncho anthu ena angaganize kuti chilalacho chinatha m’kati mwa chaka cha chitatu ndipo zimenezi zingasonyeze kuti sichinathe zaka zitatu. Komabe, Yesu ndi Yakobe amati chilalacho chinatenga “zaka zitatu ndi miyezi isanu ndi umodzi.” (Luka 4:25; Yakobe 5:17) Kodi pamenepa Baibulo likudzitsutsa lokha?
Ayi, sichoncho. Monga mmene mwaonera, ku Isiraeli nyengo ya chilimwe inali yaitali ndithu mpaka miyezi 6. Mosakayikira Eliya anafika kwa Ahabu m’nyengo ya chilimwe kudzamuuza kuti kudzakhala chilala. Ndipo panthawiyi n’kuti chilala chitayamba kale chifukwa nthawi imene nyengo ya chilimwe imayenera kutha inali itapitirira. Ndipo zimenezi zikutanthauza kuti panali patapita pafupifupi miyezi 6 kuchokera pamene chilalacho chinayamba. Choncho, kuchokera pamene Eliya analengeza kuti kudzakhala chilala kufikira nthawi imene analengeza kuti chitha, panadutsa ‘zaka zitatu.’ Izi zikusonyeza kuti chilalacho chinatha zaka zitatu ndi theka. Motero, panthawi imene anthu anasonkhana ku phiri la Karimeli kudzaonerera zochitika za pakati pa aneneri a Baala ndi Eliya, panali patadutsa “zaka zitatu ndi miyezi isanu ndi umodzi.”
Taganiziraninso nthawi yoyamba imene Eliya anapita kukaonana ndi Ahabu. Anthu anali kukhulupirira kuti Baala ndiye “woyendetsa mitambo,” mulungu amene anali kubweretsa mvula kuti nyengo ya chilimwe ithe. Nyengo ya chilimwe ikatalika kwambiri, mwina anthu ankafunsa kuti: ‘Kodi Baala ali kuti? Kodi adzabweretsa liti mvula?’ Koma zimene Eliya analengeza zoti sikudzagwa mvula ngakhale mame mpaka nthawi imene adzalengezanso kuti mvula igwe, ziyenera kuti zinakhumudwitsa kwambiri anthu olambira Baala.—1 Mafumu 17:1.
[Mawu a Chithunzi]
Pictorial Archive (Near Eastern History) Est.
[Chithunzi patsamba 18]
Mapemphero a Eliya anasonyeza kuti anali wofunitsitsa kuona zofuna za Mulungu zikukwaniritsidwa