Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Aramagedo Nkhondo ya Mulungu Yothetsa Nkhondo Zonse

Aramagedo Nkhondo ya Mulungu Yothetsa Nkhondo Zonse

Aramagedo Nkhondo ya Mulungu Yothetsa Nkhondo Zonse

“Iwo amaona kuti kupha munthu ndi chinthu choipa kwambiri, motero amaona kuti nkhondo ndi chinthu choipa zedi ndipo chilibe dzina lochitchulira n’komwe m’chilankhulo chawo.” ANATERO FRIDTJOF NANSEN, M’CHAKA CHA 1888, PONENA ZA ANTHU A KU GREENLAND.

ALIYENSE amalakalaka atakhala m’dziko lopanda nkhondo. Ndipotu palibe yemwe safuna kukhala m’dziko lomwe anthu ake amaona kuti nkhondo ndi chinthu choipa zedi. Zingamveke ngati zosatheka kuti tikhale m’dziko lopanda nkhondo, makamaka ngati tingadalire anthu kuti ndi amene adzatibweretsere mtendere.

Komabe kudzera mu ulosi wa Yesaya, Mulungu analonjeza kuti adzabweretsa dziko lamtendere. Iye anati: “Iwo adzasula malupanga awo akhale zolimira, ndi nthungo zawo zikhale anangwape; mtundu sudzanyamula lupanga kumenyana ndi mtundu wina, ndipo sadzaphunziranso nkhondo.”​—Yesaya 2:4.

Motero, kuti lonjezo limeneli likwaniritsidwe, anthu ayenera kusintha maganizo awo chifukwa choti pali asilikali okwana 20 miliyoni padziko lonse omwe ali kunkhondo. Ndiponso padziko lonse pakuchitika nkhondo pafupifupi 20. N’zosadabwitsa kuti Yehova, Mulungu wamphamvu yonse, adzalowerera pa zochitika za anthu. Zimenezi zidzafika pachimake pankhondo imene Baibulo limaitcha Aramagedo.​—Chivumbulutso 16:14, 16.

M’zaka zaposachedwapa mawu akuti “Aramagedo” akhala akugwiritsidwa ntchito ponena za nkhondo yapadziko lonse ya zida za nyukiliya. Koma buku lina lotanthauzira mawu limafotokoza tanthauzo lenileni la mawuwa kuti ndi “malo omwe kudzachitikire nkhondo yaikulu yomaliza ya pakati pa anthu abwino ndi oipa.” Koma kodi zidzathekadi kuti anthu abwino agonjetse oipa, kapena amenewa angokhala maloto basi?

Tingalimbikitsidwe kudziwa kuti Baibulo limanena mobwerezabwereza kuti oipa onse adzawonongedwa. Ndipo wamasalmo analosera kuti: “Ochimwa athedwe ku dziko lapansi, ndi oipa asakhalenso.” (Salmo 104:35) Komanso buku la Miyambo limati: “Oongoka mtima adzakhala m’dziko, angwiro nadzatsalamo. Koma oipa adzalikhidwa m’dziko, achiwembu adzazulidwamo.”​—Miyambo 2:21, 22.

Komanso Baibulo limanena momveka bwino kuti anthu oipa sadzavomereza mwamtendere kuti agonja. N’chifukwa chake Mulungu adzafunika kumenya nkhondo yomaliza imene idzathetsa zoipa zonse kuphatikizapo nkhondo. (Salmo 2:2) Ndipo dzina la m’Baibulo la nkhondo yapadera imeneyi loti Aramagedo ndi lofunika kwambiri.

Nkhondo Zakale ku Megido

Mawu akuti “Aramagedo” amatanthauza “phiri la Megido.” Mzinda wakale wa Megido ndiponso chigwa chake cha Yezreeli, ndi malo otchuka zedi chifukwa cha nkhondo zoopsa zimene zinkachitika kumeneko. Katswiri wina wolemba mbiri yakale dzina lake Eric H. Cline analemba m’buku lake kuti: “M’mbiri yonse ya anthu, ku Megido ndiponso ku chigwa cha Yezreeli, kunali kuchitikira nkhondo zoopsa zedi zomwe zakhudza kwambiri anthu.”​—The Battles of Armageddon.

Monga momwe katswiriyu anafotokozera, nkhondo zimene zinkachitikira ku Megido zinkakhala zoopsa zedi. Mwachitsanzo, asilikali a ku Mongolia omwe anali atalanda dera lalikulu la Asia m’zaka za m’ma 1200, anagonja kwa nthawi yoyamba pankhondo yomwe inachitikira m’chigwachi. Ndiponso asilikali a ku Britain motsogozedwa ndi Edmund Allenby anagonjetsa asilikali a ku Turkey pafupi ndi dera la Megido pankhondo yoyamba yapadziko lonse. Ponena za kupambana kwa Britain, wolemba mbiri yakale wina anati: “Nkhondo imeneyi anaimenya mofulumira kwambiri ndiponso anagonjetsa adani awo onse mwachangu kwambiri kuposa nkhondo zina zonse.”

Nkhondo zina zoopsa kwambiri zotchulidwa m’Baibulo zinachitikiranso ku Megido. Mwachitsanzo, Woweruza Baraki anagonjetsa asilikali a ku Kanani otsogoleredwa ndi Sisera. (Oweruza 4:14-16; 5:19-21) Komanso Gideoni ndi asilikali ake ochepa 300 anagonjetsa gulu lankhondo la a Midiyani ku dera lomweli. (Oweruza 7:19-22) Nayenso Mfumu Sauli ndi mwana wake Jonatani anaphedwa ndi Afilisti pafupi ndi phiri la Giliboa, pamene Aisiraeli anagonjetsedwa.​—1 Samueli 31:1-7.

Kwa zaka zoposa 4,000, ku dera la Megido ndiponso chigwa chake, kwakhala kukuchitikira nkhondo zankhaninkhani chifukwa cha mmene malowa alili. Wolemba mbiri yakale wina anati kumalowa kunachitikira nkhondo pafupifupi 34.

Mbiri ya dera la Megido ndiponso mmene malowa alili zimagwirizana kwambiri ndi tanthauzo lophiphiritsa la mawu akuti “Aramagedo.” Ngakhale kuti mawu oti Aramagedo amapezeka kamodzi kokha m’Baibulo, mmene buku la Chivumbulutso limawagwiritsira ntchito zimasonyeza kuti nkhondoyi idzakhudza munthu aliyense padziko lapansi.

Kodi Baibulo Limati Aramagedo N’chiyani?

Nkhondo zakale zimene zinamenyedwa ku Megido zinali zoopsa zedi, koma palibe ndi imodzi yomwe imene inathetsa zoipa. Ndiponso palibe gulu lenileni la anthu abwino ndi anthu oipa amene anamenyanadi m’dera limeneli. Motero n’zomveka kunena kuti nkhondo imeneyi idzakhala ya Mulungu. Monga mmene Yesu ananenera, “palibe wabwino, koma Mulungu yekha.” (Luka 18:19) Ndiponso Baibulo limanena momveka bwino kuti Aramagedo ndi nkhondo ya Mulungu.

Buku la Chivumbulutso limati: “Mafumu a dziko lonse lapansi kumene kuli anthu,” adzasonkhanitsidwa pamodzi “ku nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse.” (Chivumbulutso 16:14) Ndipo ulosiwu umanenanso kuti: “Ndipo anawasonkhanitsa pamodzi, kumalo amene m’Chiheberi amatchedwa Haramagedo,” kapena kuti Aramagedo. * (Chivumbulutso 16:16) Kenako buku la Chivumbulutso limafotokoza kuti: “Mafumu a dziko lapansi, ndi magulu awo ankhondo [adzasonkhanitsidwa] pamodzi kuti amenyane ndi wokwera pa kavalo uja ndi gulu lake la nkhondo.” (Chivumbulutso 19:19) Munthu wokwera pa kavaloyu si winanso ayi koma Yesu Khristu.​—1 Timoteyo 6:14, 15; Chivumbulutso 19:11, 12, 16.

Kodi tikuphunzirapo chiyani pa mavesi amenewa? Tikuphunzira kuti Aramagedo ndi nkhondo ya pakati pa Mulungu ndi anthu osamvera. Komano kodi n’chifukwa chiyani Yehova ndi Yesu Khristu akufunika kumenya nkhondo imeneyi? Chifukwa chimodzi n’choti nkhondo ya Aramagedo ‘idzawononga anthu owononga dziko lapansi.’ (Chivumbulutso 11:18) Komanso idzabweretsa mtendere padziko lapansi, limeneli ndi ‘dziko lapansi latsopano limene ife tikuyembekeza malinga ndi lonjezo la Mulungu, ndipo mmenemo mudzakhala chilungamo.’​—2 Petulo 3:13.

N’chifukwa Chiyani Aramagedo ndi Yofunika?

Kodi mukuona kuti n’zovuta kumvetsa kuti Yehova yemwe ndi “Mulungu wachikondi,” asankhe Mwana wake, yemwe ndi “Kalonga wa Mtendere” kuti amenye nkhondoyi? (2 Akorinto 13:11; Yesaya 9:6) Kudziwa zolinga zawo kungatithandize kumvetsa bwino nkhani imeneyi. Buku la Masalmo limafotokoza kuti Yesu ndi wankhondo wokwera kavalo. N’chifukwa chiyani Khristu adzamenya nkhondoyi? Wamasalmo akulongosola kuti, “kaamba ka choonadi ndi chifatso ndi chilungamo.” Iye adzamenya nkhondoyi chifukwa choti amakonda chilungamo ndipo amadana ndi zoipa.​—Salmo 45:4, 7.

Baibulo limalongosolanso kuti Yehova amadana ndi zinthu zopanda chilungamo zimene zikuchitika padzikoli. Ndipo mneneri Yesaya analemba kuti: ‘Yehova adzaona ichi, ndipo chidzamuipira kuti palibe chiweruzo. Ndipo adzavala chilungamo monga chida cha pachifuwa, ndi chisoti chachipulumutso pamutu pake; adzavala zovala zakubwezera chilango, adzavekedwa ndi changu monga chofunda.’​—Yesaya 59:15, 17.

Anthu olungama sangakhale pamtendere chifukwa choti amene akulamulira dzikoli ndi anthu oipa. (Miyambo 29:2; Mlaliki 8:9) Ndipotu n’zosatheka kusiyanitsa zoipa ndi anthu ochita zoipazo. Motero mtendere weniweni ndi chilungamo zingabwere pokhapokha anthu oipawo atawonongedwa. Ndipo Solomo analemba kuti: “Wochimwa ndiye chiombolo cha wolungama.”​—Miyambo 21:18.

Popeza Mulungu ndiye Woweruza, tikukhulupirira kuti adzaweruza mwachilungamo mlandu uliwonse wokhudza anthu ochimwa. N’chifukwa chake Abulahamu anafunsa kuti: “Kodi sadzachita zoyenera Woweruza wa dziko lonse lapansi?” Ndipo iye anapeza yankho lakuti Yehova amachita zolungama nthawi zonse. (Genesis 18:25) Komanso Baibulo limatitsimikizira kuti Yehova sasangalala kuwononga anthu oipa, koma amawawononga ngati sakusintha.​—Ezekieli 18:32; 2 Petulo 3:9.

Aramagedo ndi Nkhondo Yeniyeni

Kodi inuyo mudzakhala ku mbali iti pankhondo imeneyi? Ambirife timati tidzakhala ku mbali ya Mulungu. Koma tingasonyeze bwanji zimenezi? Mneneri Zefaniya akutilimbikitsa kuti: “Funani chilungamo, funani chifatso.” (Zefaniya 2:3) Nayenso mtumwi Paulo ananena kuti Mulungu amafuna kuti “anthu, kaya akhale a mtundu wotani, apulumuke ndi kukhala odziwa choonadi molondola.”​—1 Timoteyo 2:4.

Kuphunzira za Yehova ndi mmene adzabweretsere mtendere, ndi chinthu choyamba ndiponso chofunika kwambiri kuchita kuti tidzapulumuke. Chinthu chachiwiri ndicho kuchita chilungamo, ndipo zimenezi ndi zofunika kuti Mulungu azitiyanja ndiponso azititeteza.

Tikamachita zinthu zofunika kwambiri zimenezi ndiye kuti tikukonzekera bwino Aramagedo, yomwe ndi nkhondo imene idzathetseratu nkhondo zonse. Nkhondo ya Aramagedo ikadzatha, anthu kwina kulikonse kumene angakhale padziko lapansili, adzaona kuti nkhondo ndi chinthu choipa zedi. Ndipo Baibulo limati anthu “sadzaphunziranso nkhondo.”​—Yesaya 2:4.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 17 Kuti mumve zambiri ngati Aramagedo ndi malo enieni kapena ayi, onani nkhani yakuti “Zimene Owerenga Amafunsa,” patsamba 31.

[Mawu Otsindika patsamba 5]

Aramagedo ndi nthawi imene Mulungu adzalowerera pa zochitika za anthu

[Chithunzi patsamba 6]

Megido

[Chithunzi patsamba 6]

Gideoni ndi asilikali ake anapambana nkhondo yoopsa kwambiri ku Megido

[Chithunzi pamasamba 6, 7]

Nkhondo ya Aramagedo ikadzatha, anthu kwina kulikonse padziko lapansili, adzaona kuti nkhondo ndi chinthu choipa zedi

[Chithunzi patsamba 8]

Kuphunzira za Yehova ndi mmene adzabweretsere mtendere, ndi chinthu choyamba ndiponso chofunika kwambiri kuchita kuti tidzapulumuke