Kodi Dziko Lapansi Lidzawonongedwa?
Kodi Dziko Lapansi Lidzawonongedwa?
KODI mukuganiza kuti n’chiyani chidzachitikire dziko lapansili m’tsogolomu? Chifukwa choona zinthu zimene zikuchitika, anthu ambiri amakhulupirira kuti dziko lathu lokongolali lidzawonongedwa.
N’zoonadi, masiku ano anthu akuwononga kwambiri zinthu zachilengedwe monga madzi, nkhalango ndiponso mpweya. Asayansi ena akuchenjeza kuti dzikoli ndiponso zamoyo zonse zikhoza kudzawonongedwa ndi zinthu monga miyala yochokera m’mlengalenga, kuphulika kwa nyenyezi, kapena kutha kwa mphamvu ya dzuwa.
Asayansi amakhulupirira kuti dzikoli m’kupita kwanthawi, mwina patadutsa zaka mabiliyoni, silidzatha kuchirikiza moyo. Buku lina limafotokoza kuti limeneli lidzakhala “tsoka loopsa kwambiri ndiponso losapeweka.”—Encyclopædia Britannica.
Koma n’zosangalatsa kuti Baibulo limati, Yehova Mulungu sadzalola kuti dzikoli liwonongedwe kapena kuti lisadzakhalenso ndi chamoyo chilichonse. Popeza iye ndi Mlengi, angasamalire chilengedwe chonse kwamuyaya chifukwa iye ali ndi mphamvu zopanda malire. (Yesaya 40:26) Motero, timakhulupirira mawu akuti: “[Mulungu] anakhazika dziko lapansi pa maziko ake, silidzagwedezeka ku nthawi yonse.” Ndi akuti: “M’lemekezeni, dzuwa ndi mwezi; m’lemekezeni, nyenyezi zonse zounikira. . . . Popeza analamulira, ndipo zinalengedwa. Anazikhazikanso ku nthawi za nthawi.”—Salmo 104:5; 148:3-6.
Kodi Cholinga cha Mulungu cha Dziko Lapansili N’chiyani?
Sichinali cholinga cha Mulungu kuti anthu awononge dziko monga mmene aliwonongera masiku ano. Koma Mulungu analenga mwamuna ndi mkazi oyamba, Adamu ndi Hava, ndipo anawaika m’munda wokongola. Choncho anthuwa anafunika kusamalira Paradaisoyo kuti akhalabe wokongola. Mulungu anawauza kuti ‘aulime ndi kuuyang’anira’ munda wawowo. (Genesis 2:8, 9, 15) Imeneyi inali ntchito yabwino ndiponso yosangalatsa kwambiri yomwe Mulungu anapatsa makolo athu omwe anali angwiro.
Komabe cholinga cha Mulungu cha dziko lapansi sichinali chongoti anthu azilima ndi kusamalira dziko lapansi basi. Iye anafuna kuti dziko lonse likhale paradaiso. N’chifukwa chake Mulungu analamula Adamu ndi Hava kuti: “Mubalane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi, muligonjetse; mulamulire pa nsomba za m’nyanja, ndi pa mbalame za m’mlengalenga, ndi pa zamoyo zonse zakukwawa pa dziko lapansi.”—Koma n’zomvetsa chisoni kuti mngelo wina wonyada yemwe anatchedwa Satana anasokoneza cholinga cha Mulungu chimenechi. Iye ankafunitsitsa kuti Adamu ndi Hava azim’lambira. Motero, anagwiritsa ntchito njoka kuti imulankhulire powachititsa kuti agalukire ulamuliro wa Mulungu. (Genesis 3:1-6; Chivumbulutso 12:9) Mlengi wathu sanasangalale ndi kudzikonda ndiponso kusayamikira kwawo kumeneku. Komabe Yehova Mulungu sanasinthe cholinga chake cha dziko lapansili ngakhale kuti anthuwa anam’galukira. Ndipo iye anati: “Mawu anga amene atuluka m’kamwa mwanga, sadzabwerera kwa ine chabe, koma adzachita chimene ndifuna, ndipo adzakula mmene ndinawatumizira.”—Yesaya 55:11.
Pali chifukwa chomveka chimene chachititsa Yehova kulola anthu kum’tsutsa mpaka lerolino. Panthawi imeneyi, anthu ayesa kupanga maboma osiyanasiyana odzilamulira. Koma zotsatira zake zasonyeza kuti ulamuliro umene Satana amauchirikiza, woti anthu azidzilamulira okha popanda kudalira Mulungu, walephereratu. *—Yeremiya 10:23.
Komabe n’zosangalatsa kuti kwa zaka zambirimbiri, Mulungu wakhala akudalitsa anthu olungama. Ndiponso walemba m’Baibulo madalitso omwe anthu omvera adzalandire ndiponso chilango chimene anthu okana ulamuliro wake adzalandire. Iye watichitiranso zinthu zina zabwino kwambiri zotithandiza kuti tidzakhale ndi moyo wosangalatsa m’tsogolomu. Iye wasonyezanso kuti amatikonda chifukwa watipatsa Mpulumutsi yemwe ndi Mwana wake wokondedwa, Yesu Khristu. Ndipo Mwana wakeyu amatiphunzitsa zimene tingachite kuti tisangalatse Mulungu ndiponso anapereka moyo wake chifukwa cha ife. (Yohane 3:16) Popeza kuti Yesu anali wangwiro, Mulungu wagwiritsa ntchito imfa yake kuti anthu akhalenso ndi moyo umene Adamu ndi Hava anataya. Ndipo umenewu ndi moyo wosatha womwe tidzakhala nawo m’paradaiso padziko lapansi. * Kuti zimenezi zitheke, Yehova Mulungu wakhazikitsa boma kumwamba lomwe lidzalamulira anthu onse. Ndipo wasankha Mwana wake, Yesu Khristu, yemwe anaukitsidwa kuti akhale Mfumu ya Ufumu umenewu. Boma limeneli ndi lomwe lidzathandize kuti cholinga cha Mulungu cha dziko lapansi chikwaniritsidwe.—Mateyo 6:9, 10.
Motero, tingakhulupirire kwambiri malonjezo osangalatsa zedi a m’Baibulo otsatirawa: “Ochita zoipa adzadulidwa; koma iwo akuyembekeza Yehova, iwowa adzalandira dziko lapansi. Olungama adzalandira dziko lapansi, nadzakhala momwemo kosatha.” Ndiponso: “‘Taonani! chihema cha Mulungu chili pakati pa anthu. Iye adzakhala pamodzi nawo, ndipo iwo adzakhala anthu ake. Inde, Mulungu mwini adzakhala nawo. Iye adzapukuta msozi uliwonse m’maso mwawo, ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulira, kapena kubuula, ngakhale kupweteka. Zakalezo zapita.’ Ndipo Iye wokhala pampando wachifumu anati: ‘Taonani! Zinthu zonse zimene ndikupanga n’zatsopano.’”—Salmo 37:9, 29; Chivumbulutso 21:3-5.
Kodi Baibulo Limadzitsutsa?
Anthu ena amafunsa kuti, ‘Kodi pali kugwirizana kotani pakati pa mavesi ali pamwambawa ndi mavesi ena amene amamveka ngati akunena kuti dziko lidzawonongedwa?’ Tiyeni tikambirane ena mwa mavesi amenewa ndipo zimenezi zitithandiza kuona kuti Baibulo silidzitsutsa.
Asayansi asanayambe kunena zoti “tsoka Salmo 102:25-27.
loopsa kwambiri ndiponso losapeweka” lidzachitika pa dzikoli, wamasalmo anali atalemba kale m’Baibulo kuti: ‘Mulungu anakhazika dziko lapansi kalelo; ndipo zakumwamba ndizo ntchito ya manja ake. Zidzatha izi, koma Inu mukhala: Inde, zidzatha zonse ngati chovala; mudzazisintha ngati malaya, ndipo zidzasinthika: Koma Inu ndinu yemweyo, ndi zaka zanu sizifikira kutha.’—Polemba mawu amenewa, wamasalmo sanali kutsutsa cholinga cha Mulungu cha dziko lapansi. Koma amasonyeza kuti Mulungu ndi wamuyaya pamene zinthu zonse zimene analenga zikhoza kuwonongeka. Ndipo ngati Mulungu angasiye kuchirikiza zinthu zonse zimene analenga, monga dzuwa ndi mapulaneti ake zimene zimatithandiza, zinthuzi zikhoza kuwonongekeratu. Motero, ngati Mulungu angasiye kuchirikiza dzikoli, likhoza ‘kutha,’ kapena kuti kuwonongekeratu.
Palinso mavesi ena m’Baibulo amene amamveka ngati akutsutsana ndi cholinga cha Mulungu cha dziko lapansili. Mwachitsanzo, Baibulo limanena za kumwamba ndi dziko lapansi kuti ‘zikuchoka.’ (Chivumbulutso 21:1) Mawu amenewa sakutsutsana ndi lonjezo la Yesu lakuti: “Osangalala ali iwo amene ali ofatsa, popeza adzalandira dziko lapansi.” (Mateyo 5:5) Nangano Baibulo limatanthauza chiyani kwenikweni likamanena kuti kumwamba ndi dziko lapansi ‘zikuchoka’?
Nthawi zambiri Baibulo limagwiritsira ntchito mawu akuti “dziko lapansi” mophiphiritsira kutanthauza anthu. Mwachitsanzo, taonani vesi lotsatirali: “Dziko lapansi linali la chinenedwe chimodzi ndi chilankhulidwe chimodzi.” (Genesis 11:1) N’zoonekeratu kuti “dziko lapansi” palembali likutanthauza anthu okhala padzikolo. Chitsanzo china ndi cha lemba la Salmo 96:1, lomwe limati: “Muimbireni Yehova, inu, dziko lonse lapansi.” Choncho, n’zosakayikitsa kuti m’vesili komanso mavesi ena, mawu akuti “dziko lapansi” akuimira anthu.—Salmo 96:13.
Nthawi zina Baibulo limayerekezera olamulira adzikoli ndi kumwamba kapena zinthu zakumwamba. Mwachitsanzo, olamulira ankhanza a ku Babulo anayerekezeredwa ndi nyenyezi chifukwa anali odzikweza kwambiri kuposa mitundu yoyandikana nayo. (Yesaya 14:12-14) Mogwirizana ndi ulosi, “kumwamba,” komwe kunkaimira ulamuliro wa Babulo, monga gulu lolamulira, ndiponso “dziko lapansi,” lomwe ndi anthu amene ankalamulidwa ndi ufumu wa Babulowo, zinatha mu 539 B.C.E. (Yesaya 51:6) Zimenezi zinathandiza kuti Ayuda olapa abwerere ku Yerusalemu, kumene kunali ulamuliro watsopano womwe unkaimira “kumwamba kwatsopano.” Ndipo ulamuliro umenewu unkalamulira anthu olungama omwe anali “dziko lapansi latsopano.”—Yesaya 65:17.
Mawu a m’Baibulo onena za kumwamba ndi dziko lapansi zomwe ‘zikutha’ akutanthauza za kutha kwa maboma a anthu a masiku ano ndiponso anthu awo osaopa Mulungu. (2 Petulo 3:7) Zimenezi zidzachititsa kuti boma latsopano la Mulungu libweretse madalitso ambiri kwa anthu olungama. N’chifukwa chake Baibulo limati: “Pali miyamba yatsopano ndi dziko lapansi latsopano zimene ife tikuyembekeza malinga ndi lonjezo la [Mulungu], ndipo mmenemo mudzakhala chilungamo.”—2 Petulo 3:13.
Motero, tiyenera kukhulupirira lonjezo la Mulungu lakuti dziko lathu lapansili silidzawonongedwa. Ndiponso Baibulo limasonyeza zimene tiyenera kuchita kuti tidzakhale nawo nthawi imene dziko lonse lapansi lidzakhala paradaiso. Yesu anati: “Moyo wosatha adzaupeza akamaphunzira ndi kudziwa za inu, Mulungu yekha woona, ndi za Yesu Khristu, amene inu munam’tuma.” (Yohane 17:3) Motero, yesetsani kukhala ndi cholinga chophunzira zimene Baibulo limanena zokhudza dziko lapansi ndiponso anthu. Mboni za Yehova za kudera la kwanuko zidzasangalala kukuthandizani kuchita zimenezi.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 10 Kuti mudziwe zambiri pankhani yofotokoza chifukwa chimene Mulungu walolera anthu kuvutika, onani buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?, masamba 106 mpaka 114, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.
^ ndime 11 Kuti mumve zambiri za imfa yansembe ya Yesu, onani buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? masamba 47 mpaka 56.
[Mawu Otsindika patsamba 12]
Baibulo limalonjeza kuti dziko lathu lapansili Silidzawonongedwa
[Mawu a Chithunzi patsamba 10]
Background globe: NASA/The Visible Earth (http://visibleearth.nasa.gov/); polar bear: © Bryan and Cherry Alexander Photography