Kodi Mukudziwa?
Kodi Mukudziwa?
N’chifukwa chiyani Yesu anachiritsa munthu wosaona mwapang’onopang’ono?
Lemba la Maliko 8:22-26, limafotokoza kuti Yesu anachiritsa munthu wosaona ku Betsaida. Nkhaniyi imanena kuti choyamba, Yesu anaika malovu m’maso mwa munthuyo ndi kum’funsa ngati akutha kuona chilichonse. Zimene munthuyo anayankha zinasonyeza kuti sanali kuona bwinobwino. Iye anati: “Ndikuona anthu, chifukwa ndikuona zinthu zooneka ngati mitengo, koma zikuyendayenda.” Kenako Yesu anagwiranso m’maso mwa munthuyo. Ndipo atatero: “Munthuyo anayamba kuona bwinobwino, inde anam’chiritsa, moti anayamba kuona chilichonse bwino lomwe.” Zikuoneka kuti Yesu anachiritsa munthuyo mwa pang’onopang’ono. N’chifukwa chiyani anachita zimenezi?
Baibulo silimafotokoza mwachindunji koma tingafotokoze chifukwa chimene mwina chinachititsa Yesu kuchita zimenezi. Kunali kusintha kwakukulu pamoyo wa munthuyo kuti ayambe kuona atakhala zaka zambiri, mwinanso chibadwireni, ali wosaona. Mwachitsanzo, anthu ena ogwira ntchito mu mgodi anatenga mahatchi kuti aziwagwiritsa ntchito mu mgodimo. Mahatchiwo anazolowera kwambiri mdima wa mu mgodimo moti ankatha kuona bwinobwino. Koma atawaturutsamo anatha tsiku lathunthu kuti azolowere kuwala ndi kuyamba kuona bwinobwino. Choncho kwa munthu yemwe sanaonepo chibadwireni zinayenera kutenga nthawi yaitali. Masiku ano, ndi nthawi zochepa zokha pamene madokotala a maso athandiza anthu osaona kuti ayambenso kuona. Komabe, anthuwo akayamba kuona amasokonezeka kwambiri ndi zinthu zambirimbiri zimene amaona. Amachita chidwi kwambiri ndi mitundu ya zinthu ndiponso mmene zinthuzo zilili moti amalephera kuzindikira ngakhale zinthu zimene zili zodziwika bwino. Koma pakapita nthawi anthuwo amayamba kuzindikira bwinobwino zinthu zimene akuonazo.
Motero, Yesu anasonyeza chikondi kwa munthu wosaonayo mwa kum’chiritsa pang’onopang’ono. Pamapeto pake, munthuyo “anayamba kuona chilichonse bwino lomwe” moti ankatha kuzindikira chilichonse chimene anali kuona.
N’chifukwa chiyani kuwerenga mpukutu kunali kovuta m’nthawi ya Yesu?
Zikopa zambiri zimene ankagwiritsa ntchito popanga mipukutu m’nthawi imeneyi zinkakhala zotalika masentimita 23 mpaka 28 m’litali mwake ndipo m’lifupi masentimita 15 mpaka 23. Popanga mpukutu, ankatenga zikopa zingapo n’kuzilumikiza mwa kuzisoka ndi ulusi kapena kuzimata. Nthawi zina zikopa zimenezi zinkakhala zazitali ndithu. Mwachitsanzo, Mpukutu wa Yesaya womwe unapezeka ku Nyanja Yakufa ndi wautali pafupifupi mamita 7 ndipo unapangidwa ndi zikopa zokwana 17. N’kutheka kuti mpukutu womwe Yesu anawerenga m’sunagoge ku Nazarete unali wautali mofanana ndi umenewu.—Luka 4:16, 17.
Ponena za nkhani imeneyi, Alan Millard analemba m’buku lake lofotokoza za m’nthawi ya Yesu kuti: “Munthu wowerenga ankagwira mpukutu [buku] ndi kuutambasula ndi dzanja lake lamanzere kwinaku akuupinda ndi dzanja lake lamanja akamawerenga ndime za mu mpukutumo. Motero kuti Yesu apeze Yesaya chaputala 61 chomwe anawerenga, ayenera kuti anatambasula mbali yaikulu ya mpukutuwo kenako n’kuupindanso.”—Discoveries From the Time of Jesus.
Panthawi imeneyi, buku la Yesaya linali lisanagawidwe m’machaputala ndi mavesi monga mmene lilili masiku ano. Yesu atapatsidwa mpukutu wa Yesaya anafunika kufufuza gawo limene masiku ano lili Yesaya 61:1, 2. Iye sanavutike ‘kupeza pomwe panalembedwa’ zimene amafuna kuwerengazo. Zimenezi zikusonyeza kuti Yesu ankadziwa bwino Mawu a Mulungu.