Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Ndani Ali Woyenerera Kulamulira Anthu Onse?

Kodi Ndani Ali Woyenerera Kulamulira Anthu Onse?

Nkhani ya Onse Yapadera

Kodi Ndani Ali Woyenerera Kulamulira Anthu Onse?

Kodi ndi wolamulira uti amene angachite izi:

• kuthetsa mavuto azachuma, njala ndiponso kupangitsa kuti anthu onse akhale ndi nyumba zabwino?

• kuthetsa masoka achilengedwe, kuti anthu asamavutike ndi matsunami, mphepo za mkuntho kapena zivomezi?

• kuthetsa matenda onse ngakhalenso kuchititsa anthu okalamba kukhalanso anyamata?

• kuthetsa nkhondo zonse kuti anthu onse azikhala mwabata ndi mtendere?

• kubwezeretsa chilengedwe chonse kuti chikhalenso mmene chinalili poyamba ndi kusintha dziko lonse kukhala paradaiso?

Pali Wolamulira mmodzi yekha amene angachite zimenezi. Kodi iye ndani? Funso limeneli lidzayankhidwa m’nkhani ya onse yapadera ya mutu wakuti: “Kodi Ndani Ali Woyenerera Kulamulira Anthu Onse?” Nkhani imeneyi idzakambidwa padziko lonse m’mayiko oposa 230. M’madera ambiri nkhaniyi idzakambidwa pa Nyumba ya Ufumu ya Mboni za Yehova, Lamlungu, April 6, 2008. Mboni za kwanuko n’zokonzeka ndipo zidzasangalala kukuuzani nthawi ndi malo kumene nkhaniyi idzakambidwire. Tikukuitanani ndi mtima wonse kuti mudzapezekepo.