Kodi Nkhondo ya Aramagedo Idzamenyedwera Kuti?
Zimene Owerenga Amafunsa
Kodi Nkhondo ya Aramagedo Idzamenyedwera Kuti?
Nkhondo ya Aramagedo sidzamenyedwera ku malo enaake apadera. M’malo mwake, idzamenyedwera padziko lonse lapansili. N’chifukwa chiyani tikutero? N’chifukwa choti magulu awiri amene adzamenyane ndi aakulu kwambiri moti sangakwane pamalo amodzi.
Mawu akuti Aramagedo, kapena kuti Haramagedo, amadziwikanso kuti ndi “nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse.” Yehova Mulungu adzagwiritsa ntchito Mwana wake Khristu Yesu, posonkhanitsa gulu la angelo kuti amenyane ndi magulu oipa a olamulira onse a dziko lapansi.—Chivumbulutso 16:14; 19:11-16.
Satana ndi gulu lake akulimbikitsa mitundu ya anthu kuti agwirizane nawo pa nkhondoyi. Baibulo limanena za “mauthenga ouziridwa ndi ziwanda” kuti “akupita kwa mafumu [olamulira] a dziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti awasonkhanitsire pamodzi . . . kumalo amene m’Chiheberi amatchedwa Haramagedo.”—Chivumbulutso 16:14-16.
Mosiyana ndi mabuku ena a m’Baibulo, buku la Chivumbulutso limachititsa chidwi anthu ambiri. Anthu ena omwe amaona kuti nkhani za m’bukuli sizophiphiritsa, amatchula malo enieni amene akuganiza kuti kudzachitikira nkhondoyi ndipo amachita chidwi kwambiri ndi zinthu zochitika ku dera limenelo. Mfundo yoti Aramagedo idzamenyedwa ku malo enaake apadera imapezeka m’buku lina lakale kwambiri lofotokoza za buku la Chivumbulutso. Buku limeneli linalembedwa ndi Oecumenius m’zaka za m’ma 500 C.E.
Pogwirizana ndi maganizo a m’busa wina dzina lake John F. Walvoord, mkulu wa sukulu ya zachipembedzo yotchedwa Dallas Theological Seminary ananena kuti Aramagedo ndi “nkhondo yomaliza yoopsa kwambiri ya padziko lonse yomwe idzamenyedwere ku Middle East.” Mkulu ameneyu anachita kutchula malo enieni amene iye akuganiza kuti padzamenyedwera nkhondoyi. Iye akuti malowa ndi “‘phiri la Megido,’ lomwe ndi phiri laling’ono limene lili kumpoto kwa Palestine chakumapeto kwa chigwa chachikulu.”
Koma buku la Chivumbulutso silifotokoza za malo enieni kumene kudzachitikire nkhondo ya Aramagedo. Vesi loyambirira la bukuli limanena kuti nkhani zake zinalembedwa ngati “zizindikiro.” (Chivumbulutso 1:1) Kale kwambiri, Mboni za Yehova zinafotokoza m’buku lawo lina kuti: “Tisayembekezere kuti anthu adzasonkhanitsidwadi ku phiri lenileni la Megido.”—Studies in the Scriptures, Volume IV.
Nkhondo zomwe zakhala zikuchitika ku Megido zimasonyeza kuti adani a Mulungu sadzatha kuthawa. Choncho, pa Aramagedo, Mulungu adzaonetsetsa kuti zinthu zonse zoipa padziko lapansili zachotsedweratu, kulikonse komwe zingapezeke.—Chivumbulutso 21:8.
Anthu amene amakonda Yehova Mulungu ndiponso Mwana wake Yesu Khristu, sayenera kuopa Aramagedo. Nkhondo ya Mulungu imeneyi idzawononga anthu okhawo amene Mulungu adzawaweruze kuti ndi oipa moti sangasinthenso. Baibulo limati: “Yehova amadziwa kupulumutsa anthu odzipereka kwa iye.” (2 Petulo 2:9) Pa lemba la Salmo 37:34, pali mawu osangalatsa akuti: “Yembekeza Yehova, nusunge njira yake, ndipo Iye adzakukweza kuti ulandire dziko. Pakudulidwa oipa udzapenya.”