Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Phunzitsani Ana Anu

Timoteyo Anali Wokonzeka Komanso Wofunitsitsa Kutumikira

Timoteyo Anali Wokonzeka Komanso Wofunitsitsa Kutumikira

“KODI wakonzeka?” Kodi unayamba wafunsidwapo funso ngati limeneli?​— Munthu amene anakufunsayo ankafuna kudziwa ngati unali wokonzeka. Mwachitsanzo, mwina munthuyo ankatanthauza kuti: ‘Kodi watenga mabuku ako? Kodi wawerenga kale mabuku ako?’ Monga mmene tionere, Timoteyo anali wokonzeka.

Iye analinso wofunitsitsa. Kodi ukudziwa tanthauzo la zimenezi?​— Timoteyo atapemphedwa kuti ayambe kutumikira Mulungu, anasonyeza mtima wofanana ndi wa mtumiki wina wa Mulungu yemwe anati: “Ndine pano; munditumize ine.” (Yesaya 6:8) Timoteyo anasangalala kwambiri chifukwa anali wokonzeka ndiponso wofunitsitsa kutumikira. Kodi ukufuna kumva zambiri za iye?​—

Timoteyo anabadwira ku Lusitara komwe kunali kutali ndithu ndi mzinda wa Yerusalemu. Agogo ake a Loisi ndi amayi ake a Yunike, anali okonda kuphunzira Mawu a Mulungu. Iwo anayamba kum’phunzitsa Malemba Timoteyo ali wakhanda.​—2 Timoteyo 1:5; 3:15.

Mtumwi Paulo ndi Baranaba anakacheza ku Lusitara paulendo wawo woyamba wa umishonale. Ndipo panthawiyi, n’kuti Timoteyo ali wachinyamata. Zikuoneka kuti amayi ake komanso agogo ake anali atakhala kale Akhristu. Kodi ukufuna kuti umve za mavuto amene Paulo ndi Baranaba anadzakumana nawo?​— Panthawi imeneyi anthu amene ankadana ndi Akhristu anagenda Paulo ndi kum’gwetsera pansi kenako kum’khwekhwerezera kunja kwa mzinda. Ndipo anam’siya komweko anthuwo akuganiza kuti wafa.

Anthu amene anakhulupirira zimene Paulo ankaphunzitsa anafika pamene Paulo anali, ndipo iye anadzuka. Tsiku lotsatira, Paulo ndi Baranaba anachoka ku Lusitara, koma anadzabwererakonso patapita nthawi. Atabwerera ku Lusitara, Paulo anakamba nkhani ndipo anauza ophunzira kuti: “Tiyenera kukumana ndi masautso ambiri kuti tikalowe [mu Ufumu wa Mulungu].” (Machitidwe 14:8-22) Kodi ukudziwa zimene Paulo ankatanthauza?​— Iye ankatanthauza kuti anthu ena adzazunza anthu amene akutumikira Mulungu. Kenako, Paulo analembera Timoteyo kuti: “Onse ofuna kukhala ndi moyo wodzipereka kwa Mulungu . . . adzazunzidwa.”​—2 Timoteyo 3:12; Yohane 15:20.

Paulo ndi Baranaba atachoka ku Lusitara anabwerera kwawo. Patapita miyezi ingapo, Paulo anatengana ndi Sila n’kupitanso ku malo osiyanasiyana kumene Paulo anakacheza kuti akalimbikitse ophunzira atsopano. N’zosakayikitsa kuti Paulo atabwereranso ku Lusitara, Timoteyo anasangalala kwambiri kukumana naye. Komanso iye anasangalala zedi Paulo ndi Sila atamuuza kuti ayambe kuyenda nawo limodzi, ndipo iye anavomera. Zimenezi zikusonyeza kuti Timoteyo anali wokonzeka komanso wofunitsitsa kupita.​—Machitidwe 15:40–16:5.

Anthu atatuwo anayenda limodzi ulendo wautali kwambiri ndipo kenaka anakwera bwato. Atatsika bwatolo, anauyamba ulendo wopita ku dera la Tesalonika ku Girisi. Kudera limeneli, anthu ambiri anakhala Akhristu. Komabe, zimenezi zinakwiyitsa anthu ena ndipo anayamba zachiwawa. Ndiyeno Paulo, Sila ndiponso Timoteyo ataona kuti moyo wawo uli pangozi, anachoka n’kupita ku Bereya.​—Machitidwe 17:1-10.

Komabe Paulo ankadera nkhawa Akhristu atsopano a ku Tesalonika. Choncho anatumiza Timoteyo kuti apitenso kumeneko. Kodi ukudziwa chifukwa chake?​— Patapita nthawi, Paulo anauza Akhristu a ku Tesalonika kuti: ‘Kuti adzakulimbitseni ndi kukutonthozani kuti pasakhale wina wopatutsidwa ndi masautso.’ Kodi ukudziwa chifukwa chake Paulo anatumiza Timoteyo yemwe anali mnyamata kuti akagwire ntchito yoika moyo pangozi imeneyi?​— N’chifukwa choti Timoteyo anali wosadziwika kwambiri kudera limenelo, ndiponso chifukwa choti iye anali wofunitsitsa kupita. Panafunika kulimba mtima kwambiri kuti iye achite zimenezi. Kodi zinthu zinamuyendera bwanji Timoteyo? Atabwerako, anauza Paulo kuti anthu a ku Tesalonika anali okhulupirika kwambiri. Choncho Paulo anawalembera kuti: “Mwa kukhulupirika kumene mukuonetsa, mwatitonthoza mitima.”​—1 Atesalonika 3:2-7.

Kwa zaka 10 zotsatira, Timoteyo anatumikira limodzi ndi Paulo. Kenako Paulo anamangidwa ku Roma ndipo Timoteyo, amenenso anali atangotulutsidwa kumene m’ndende, anapita kuti azikam’tumikira. Ali m’ndendemo, Paulo analembera kalata Akhristu a ku Filipi, ndipo mwina anatuma Timoteyo kuti am’lembere kalatayo. Paulo anati: ‘Ndikuyembekeza kutumiza Timoteyo kwa inu, pakuti ndilibe wina wa mtima ngati iye amene angasamaledi za inu moona mtima.’​—Afilipi 2:19-22; Aheberi 13:23.

Timoteyo ayenera kuti anasangalala zedi ndi mawu amenewo. Ndipo Paulo ankam’konda kwambiri Timoteyo chifukwa iye anali wokonzeka komanso wofunitsitsa kutumikira. Tikukhulupirira kuti nawenso ukhala ngati Timoteyo.