Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Zoona Zake za Mwambo wa Ukalisitiya

Zoona Zake za Mwambo wa Ukalisitiya

Zoona Zake za Mwambo wa Ukalisitiya

ANTHU ambiri padziko lonse amachita mwambo wa Ukalisitiya nthawi zonse, mwina kangapo pachaka, pamlungu, ngakhalenso patsiku. Komabe, mwambowu amati ndi chinsinsi cha chikhulupiriro chawo, ndipo anthu ambiri amene amachita mwambowu amavomereza kuti saumvetsa. Anthuwo amaona kuti mwambowu ndi wopatulika ndiponso wozizwitsa.

Mwambo umenewu ndi mbali ya Misa ya Chikatolika. Pamwambowu, wansembe amadalitsa buledi ndi vinyo ndipo anthu onse amauzidwa kuti alandire Khristu mwa kudya Ukalisitiya. * Ponena za Akatolika anzake, papa Benedikito wa chi 16 anati “chikhulupiriro chathu chagona pa mwambo umenewu.” Chaposachedwapa, tchalitchichi chinachita mwambo wa “Chaka cha Ukalisitiya” ndi cholinga “choyambitsanso komanso kulimbikitsa chikhulupiriro cha Ukalisitiya.”

Ngakhale akatolika ofooka m’chikhulupiriro chawo amaonabe kuti mwambo wa Ukalisitiyawu ndi wofunika kwambiri. Mwachitsanzo, m’nkhani ina imene inalembedwa m’magazini ina, mzimayi wina wachitsikana yemwenso ndi Mkatolika wolimbikira analemba kuti: “Pa zikhulupiriro zonse za Chikatolika, timalemekeza kwambiri mwambo wa Ukalisitiya chifukwa umatigwirizanitsa kwambiri.”​—Time.

Koma kodi Ukalisitiya n’chiyani? Kodi otsatira Khristu ayenera kumachita nawo mwambo umenewu? Choyamba, tiyeni tione kaye mmene mwambowu unayambira. Ndiyeno kenako tikambirana funso lofunika kwambiri lakuti: Kodi mwambo wa Ukalisitiya ndi wogwirizana ndi mwambo umene Yesu Khristu anayambitsa zaka 2,000 zapitazo?

Kodi Matchalitchi Achikhristu Amati Ukalisitiya N’chiyani?

N’zosavuta kuona chifukwa chimene anthu ena amati Ukalisitiya n’chinthu chozizwitsa. Mwambo umenewu umafika pachimake panthawi ya pemphero la Ukalisitiya. Panthawi imeneyi, malinga ndi Katekisimu wa Akatolika, “mphamvu ya mawu ndi zochita za Khristu, ndiponso mphamvu ya Mzimu Woyera,” imachititsa kuti thupi ndi magazi a Yesu “akhalepo mwa sakaramenti.” Ndiyeno wansembe akadya buledi ndi kumwa vinyo, amauza anthu onse okhulupirika kuti adye nsembeyo, ndipo kawirikawiri anthu amangodya buledi yekha, kapena kuti Thupi.

Tchalitchi cha Katolika chimaphunzitsa kuti buledi ndi vinyo zimasintha n’kukhala thupi ndi magazi enieni a Khristu. Chiphunzitso chimenechi chinayamba mwapang’onopang’ono, ndipo mawu amene amagwiritsidwa ntchito potchula chiphunzitsochi anawavomereza m’zaka za m’ma 1200. Koma panthawi imene anthu ena anayamba kugalukira Chikatolika, anthu ambiri anayamba kukayikira mfundo zina zokhudza mwambo wa Ukalisitiya. Ndipo Martin Luther anatsutsa mfundo yoti buledi ndi vinyo zimasintha n’kukhala thupi ndi magazi enieni a Khristu. Koma iye anati buledi ndi vinyo ndizo thupi ndi magazi enieni a Khristu. Komabe, mfundo zimenezi n’zosasiyana kwenikweni.

M’kupita kwa nthawi, matchalitchi a Chikhristu anasiyananso maganizo pa tanthauzo la Ukalisitiya ndiponso kuti azichita motani komanso kangati. Komabe, matchalitchi a Chikhristu amaona kuti mwambo umenewu udakali wofunika kwambiri. Koma kodi mwambo weniweni umene Yesu anayambitsa unali wotani?

Kuyambitsa Mwambo wa “Mgonero wa Ambuye”

Yesu ndi amene anayambitsa “Mgonero wa Ambuye” kapena kuti mwambo wokumbukira imfa yake. (1 Akorinto 11:20, 24) Komabe, kodi iye anayambitsa mwambo wosamvetsetseka bwino pamene otsatira ake anadyadi thupi ndiponso kumwa magazi ake enieni?

Yesu ndi ophunzira ake anali atangomaliza kuchita mwambo wa Ayuda wa Pasika ndipo anauza Yudasi Isikariyoti, yemwe anali atatsala pang’ono kum’pereka, kuti achoke. Mateyo, mmodzi mwa atumwi 11 omwe analipo panthawiyo analemba kuti: “Popitiriza kudya, Yesu anatenga mtanda wa mkate, ndipo atapempha dalitso, anaubenthulabenthula ndi kuupereka kwa ophunzira ake nati: ‘Eni, idyani. Mkate uwu ukuimira thupi langa.’ Kenako anatenga chikho ndipo, atayamika, [m’Chigiriki eu·kha·ri·ste΄sas] anachipereka kwa iwo ndi kunena kuti: ‘Imwani nonsenu; vinyoyu akuimira “magazi anga a chipangano,” amene adzakhetsedwa chifukwa cha anthu ambiri kuti machimo akhululukidwe.’”​—Mateyo 26:26-28.

Kupemphera asanadye chakudya inali nkhani yofunika kwambiri kwa Yesu, monganso mmene zilili kwa atumiki onse a Mulungu. (Deuteronomo 8:10; Mateyo 6:11; 14:19; 15:36; Maliko 6:41; 8:6; Yohane 6:11, 23; Machitidwe 27:35; Aroma 14:6) Ndiyeno kodi pali chifukwa chilichonse chokhulupirira kuti Yesu atapemphera, anasandutsa mozizwitsa mkate ndi vinyo n’kukhala thupi ndiponso magazi ake enieni kuti otsatira ake adye ndi kumwa?

Kodi Yesu Anati ‘Izi Zikuimira,’ Kapena ‘Izi Ndi’?

Mabaibulo ena amamasulira mawu a Yesu amenewa kuti: “Tengani, idyani; ichi ndi thupi langa,” ndiponso, “Imwani nonsenu. Uwu ndi mwazi wanga.” (Mateyo 26:26-28, Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu; Chipangano Chatsopano mu Chichewa cha Lero) Ndi zoona ndithu kuti mawu a Chigiriki akuti e·stin΄, angatanthauze “ndi.” Koma mawu omwewa angatanthauzenso “kuimira.” N’zochititsa chidwi kuti m’Mabaibulo ambiri mawu amenewa nthawi zambiri amawamasulira kuti “kutanthauza” kapena “kuimira.” * Ndipo chimene chimathandiza kusankha mawu oyenera pomasulira mawu a m’Chigiriki amenewa ndi mmene nkhaniyo ilili. Mwachitsanzo, m’Mabaibulo ambiri, mawu a Chigiriki opezeka pa Mateyo 12:7 akuti e·stin΄, anawamasulira kuti “tanthauzo.” Ndipo palembali, Baibulo la Chipangano Chatsopano mu Chichewa cha Lero limati: “Ngati mukanadziwa chomwe mawu atanthauza [m’Chigiriki e·stin], ‘Ine ndifuna chifundo osati nsembe.’ Inu simukanatsutsa osalakwa.”

Pankhani imeneyi, akatswiri a Baibulo ambiri otchuka amavomereza kuti mawu akuti “ndi” sathandiza anthu kumvetsa molondola mfundo imene Yesu anali kutanthauza pa vesili. Mwachitsanzo, katswiri wina wa Baibulo dzina lake Jacques Dupont anafufuza za chikhalidwe cha kumene Yesu anali kukhala. Ndiyeno anati “njira yabwino kwambiri” yomasulirira vesili ndi yoti: “Uwu ukutanthauza thupi langa” kapena kuti “Uwu ukuimira thupi langa.”

N’zodziwikiratu kuti Yesu sankatanthauza kuti otsatira ake anayenera kudya thupi lake lenileni ndi kumwa magazi ake enieni. N’chifukwa chiyani tikutero? Chigumula cha m’nthawi ya Nowa chitangodutsa, Mulungu analoleza anthu kuti azidya nyama. Koma sanawauze kuti azidya nyama ya munthu. Kuwonjezera apo, anawaletseratu kuti asamadye magazi. (Genesis 9:3, 4) Lamulo limeneli analibwerezanso m’Chilamulo cha Mose chimene Yesu anachitsatira mosamala. (Deuteronomo 12:23; 1 Petulo 2:22) Ndiponso Mulungu anauzira atumwi kuti alembere Akhristu onse lamulo loletsa kudya magazi. (Machitidwe 15:20, 29) Kodi Yesu akanayambitsa mwambo umene ukanachititsa otsatira ake kuti asamvere lamulo la Mulungu Wamphamvuyonse? Zimenezo n’zosatheka.

Motero, n’zoonekeratu kuti Yesu anagwiritsa ntchito mkate ndi vinyo ngati zizindikiro chabe. Mkate wopanda chofufumitsa unaimira, kapena kuti unatanthauza thupi lake lopanda uchimo limene linali kudzaperekedwa nsembe. Vinyo wofiira anaimira magazi ake amene anali kudzakhetsedwa “chifukwa cha anthu ambiri kuti machimo akhululukidwe.”​—Mateyo 26:28.

Cholinga cha Mgonero wa Ambuye

Yesu atamaliza kuchita mwambo woyamba wa Mgonero wa Ambuye, ananena kuti: “Muzichita zimenezi pondikumbukira ine.” (Luka 22:19) Kuchita mwambo umenewu kumatithandiza kuti tizikumbukira Yesu ndiponso madalitso amene timapeza chifukwa cha imfa yake. Mwambowu umatikumbutsanso kuti Yesu analemekeza kwambiri ulamuliro wa Atate wake, Yehova. Umatikumbutsanso kuti Yesu anali munthu wangwiro ndipo anapereka “moyo wake dipo kuwombola anthu ambiri.” Zimenezi zimathandiza munthu aliyense wokhulupirira nsembe yake kuti apulumutsidwe ku uchimo n’kudzalandira moyo wosatha.​—Mateyo 20:28.

Mgonero wa Ambuye ndi chakudya chodyera pamodzi, ndipo amene amakhudzidwa kwambiri ndi (1) Yehova Mulungu, yemwe anakonza zopereka dipolo, (2) Yesu Khristu, “Mwanawankhosa wa Mulungu” yemwe anapereka dipo limeneli, ndiponso (3) abale a Yesu auzimu. Akamadya mkate ndi kumwa vinyo, abale a Yesu amenewa amasonyeza kuti ndi ogwirizana kwambiri ndi Khristu. (Yohane 1:29; 1 Akorinto 10:16, 17) Amasonyezanso kuti ali mu “pangano latsopano” monga ophunzira a Yesu odzozedwa ndi mzimu. Amenewa adzalamulira ndi Khristu kumwamba monga mafumu ndi ansembe.​—Luka 22:20; Yohane 14:2, 3; Chivumbulutso 5:9, 10.

Kodi mwambo wokumbukira imfa ya Yesu uyenera kumachitika liti? Yankho la funso limeneli tingalidziwe tikakumbukira nthawi imene Yesu anasankha kuyambitsa mwambowu. Iye anayambitsa mwambowu pa tsiku la Pasika. Kwa zaka zoposa 1,500, anthu a Mulungu ankachita mwambo wa Pasika chaka chilichonse pa tsiku la Nisani 14 mogwirizana ndi kalendala yawo. Iwo ankachita zimenezi pokumbukira mmene Yehova anawapulumutsira. Motero n’zoonekeratu kuti Yesu anali kuuza otsatira ake kuti azikumbukira chinthu chinachake chapadera kwambiri patsiku limeneli. Chinthu chimenechi ndi zimene Mulungu anachita potumiza Khristu kudzatifera kuti tilandire chipulumutso. Motero otsatira a Yesu enieni amachita mwambo wa Mgonero wa Ambuye chaka chilichonse, patsiku lofanana ndi Nisani 14 pakalendala ya Chiheberi.

Ndipo otsatira enieni a Khristu amenewa sachita mwambowu chifukwa chongowukonda ayi. Koma anthu amene amachita mwambo wa Ukalisitiya amatero chifukwa chongokonda mwambowo basi. Ndipo munthu yemwe analemba nkhani ya m’magazini imene taitchula kale ija anati: “Ndimatsitsimulidwa kwambiri ndikamachita nawo mwambo wakale umenewu, womwenso anthu ambiri amauchita.” Monganso mmene zilili ndi Akatolika ambiri masiku ano, amene analemba nkhani imeneyi amasangalala kwambiri mwambowu ukamachitika m’Chilatini, monga mmene zinkachitikira kale. N’chifukwa chiyani amatero? Iye analemba kuti: “Ndimafuna kumva nyimbo za Misa m’chilankhulo chimene sindichidziwa chifukwa nthawi zambiri, sindimasangalala ndi zimene ndimamva m’nyimbo za Chingelezi.”

Mboni za Yehova, pamodzi ndi anthu ena mamiliyoni ambirimbiri amene amachita chidwi, amasangalala kuchita mwambo wa Mgonero wa Ambuye m’chinenero chawo, kulikonse kumene angakhale. Iwo amasangalala ndi mwambo umenewu chifukwa umawathandiza kumvetsa bwino kufunika kwa imfa ya Khristu. Mfundo za choonadi zimene amaphunzira kumeneko n’zopindulitsa ndipo n’zabwino kukambirana ndi anzawo chaka chonse. Anthu a Mboni amaona kuti kuchita mwambo wokumbukira imfa ya Yesu ndi njira yabwino kwambiri yowathandiza kukumbukira chikondi chachikulu chimene Yehova Mulungu ndiponso Mwana wake, Yesu Khristu anawasonyeza. Mwambowu umawathandizanso kuti ‘alengezebe imfa ya Ambuye, mpaka iye adzafike.’​—1 Akorinto 11:26.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 3 Mwambowu umatchedwanso Mgonero wa Ambuye, kunyema buledi, msonkhano wa Ukalisitiya, Nsembe, ndiponso Misa. Mawu akuti “Ukalisitiya” anachokera ku mawu a Chigiriki akuti eu·kha·ri·sti΄a, omwe amatanthauza kuyamika, kuthokoza, kapena kuyamikira.

^ ndime 15 Mwachitsanzo, onani Mateyo 13:38; 27:46; Luka 8:11; Agalatiya 4:24 m’Baibulo la Chingelezi la The New English Bible.

[Mawu Otsindika patsamba 27]

Kodi mwambo weniweni umene Yesu anayambitsa unali wotani?

[Chithunzi patsamba 28]

Yesu anayambitsa mwambo wokumbukira imfa yake

[Chithunzi patsamba 29]

Kuchita mwambo wokumbukira imfa ya Yesu Khristu