Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Iye Amamvetsa Mavuto Athu

Iye Amamvetsa Mavuto Athu

Yandikirani Mulungu

Iye Amamvetsa Mavuto Athu

Yohane 11:33-35

MUNTHU wachifundo amamvetsa ululu umene munthu wina akumva. Yehova Mulungu ndi chitsanzo chabwino kwambiri cha munthu wachifundo. Anthu ake akamavutika nayenso amamva ululu. Kodi tikudziwa bwanji zimenezi? Yesu anasonyeza bwino kwambiri chifundo cha Yehova mwa zimene ananena komanso kuchita pamene anali padziko lapansi pano. (Yohane 5:19) Mwachitsanzo, taonani nkhani yopezeka pa Yohane 11:33-35.

Lazaro yemwe anali mnzake wa Yesu atamwalira, Yesu anapita kwawo kwa Lazaroyo. N’zomveka kuti Mariya ndiponso Marita, omwe anali alongo ake a Lazaro, anali ndi chisoni kwambiri. Ndipo Yesu ankalikonda kwambiri banja limeneli. (Yohane 11:5) Ndiyeno kodi Yesu akanachita chiyani? Nkhaniyo imati: “Yesu atamuona [Mariya] akulira, ndi Ayuda amene anabwera naye pamodzi akuliranso, anadzuma povutika mu mtima ndi kumva chisoni. Kenako anati: ‘Mwamuika kuti?’ Iwo anati kwa iye: ‘Ambuye tiyeni mukaone.’ Yesu anagwetsa misozi.” (Yohane 11:33-35) N’chifukwa chiyani Yesu analira? N’zoona kuti Lazaro, yemwe anali mnzake, anali atamwalira, komabe Yesu anali atatsala pang’ono kumuukitsa. (Yohane 11:41-44) Kodi pali chinthu chinanso chimene chinam’khudza mtima kwambiri Yesu?

Taonaninso mawu a m’Baibulo amene ali m’ndime yapitayi. Onani kuti Yesu ataona Mariya ndiponso anthu ena omwe anali naye akulira, iye “anadzuma” ndipo ‘anavutika mu mtima.’ Mawu a Chigiriki omwe anawagwiritsira ntchito palembali amasonyeza kukhudzidwa mtima kwambiri. * Zimene iye anaona zinamukhudza kwambiri. Umboni wa zimenezi ndi woti m’maso mwake munalengeza misozi. N’zoonekeratu kuti Yesu anakhudzidwa mtima ndi ululu umene anthu ena anali kumva. Kodi inuyo munayamba mwalirapo chifukwa choona munthu amene mumam’konda akulira?​—Aroma 12:15.

Chifundo chimene Yesu anasonyeza chimatithandiza kumvetsa bwino makhalidwe ndiponso mmene Atate wake Yehova amachitira zinthu. Kumbukirani kuti Yesu anasonyeza bwino kwambiri makhalidwe a Atate wake moti ananena kuti: “Amene waona ine waonanso Atate.” (Yohane 14:9) Motero tikamawerenga kuti “Yesu anagwetsa misozi” timadziwa kuti Yehova amamva ululu, olambira ake akamamva ululu. Ndipotu anthu ena amene analemba nawo Baibulo amatsimikizira zimenezi. (Yesaya 63:9; Zekariya 2:8) N’zoonadi, Yehova ndi Mulungu wachifundo zedi.

Timasangalala ndi anthu achifundo. Tikakhumudwa kapena kuthedwa nzeru, timafuna kukhala pafupi ndi munthu amene angamvetse vuto lathu, n’kutichitira chifundo. Koposa zonse, timafuna kukhala pafupi ndi Yehova, yemwe ndi Mulungu wachifundo, ndipo amamvetsa ululu umene tikumva ndiponso amamvetsa chifukwa chimene tikukhetsera misozi.​—Salmo 56:8.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 3 Mawu a Chigiriki omwe anamasuliridwa kuti “anagwetsa misozi” nthawi zambiri amatanthauza “kusisima.” Koma mawu amene anawagwiritsira ntchito pofotokoza kulira kwa Mariya ndi anthu ena aja angatanthauze “kulira mofuula kapena kubuma.”