Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Tsoka Lalikulu ku Solomon Islands

Tsoka Lalikulu ku Solomon Islands

Tsoka Lalikulu ku Solomon Islands

Lolemba, pa April 2, 2007, chivomezi cha mphamvu kwambiri chinagwedeza madera ena a zilumba zotchedwa Solomon Islands zomwe zili m’dera lotentha kumpoto chakummawa kwa dziko la Australia. M’mphindi zochepa zokha, mafunde akuluakulu, omwe akuti ena anali otalika mamita 10, anasefukira m’dera la Western Province. Mafundewo anapha anthu 52 ndipo anthu ena okwana 6,000 anasowa malo okhala.

Tawuni ya Gizo yomwe ili m’mphepete mwa nyanja ndi imodzi mwa madera omwe anakhudzidwa kwambiri ndi tsokali. Tawuniyi ili ndi anthu pafupifupi 7,000, ndipo ili pa chilumba cha Ghizo, chomwe chili pa mtunda wa makilomita 45 kuchokera pamene panayambira chivomezicho. Anthu ochepa a Mboni za Yehova omwe ali m’tawuniyi anali atakonzeka kuti achite mwambo wokumbukira imfa ya Yesu madzulo a tsiku limeneli. (1 Akorinto 11:23-26) Patsikuli, kunja kunacha bwino monga mwa nthawi zonse, ndipo kunali dzuwa komanso panyanja panali bata. Kenako, nthawi itangokwana 7:39 m’mawa, kunachitika chivomezi.

Chivomezi

Panthawi imene chivomezicho chinkayamba, Ron Parkinson yemwe ndi mkulu mumpingo wa Mboni za Yehova wa kumeneko, pamodzi ndi mkazi wake Dorothy, anali akukonza chakudya chammawa. Ron anati: “Nyumba yathu inagwedezeka kwambiri ngati mtengo wa mgwalangwa koma siinagwe. Kunali chiphokoso chachikulu pamene makabati, mipando, ziwiya za kukhitchini, piyano ndiponso zinthu zina zambiri zinkagwera pansi. Kenako, tinayesetsa kutuluka m’nyumbayo movutikira. Dorothy, yemwe anali asanavale nsapato, anachekeka kuphazi ataponda magalasi osweka.”

Tony Shaw ndi mkazi wake Christine, omwe ndi amishonale, ndipo ankakhala pafupi ndi banjali nawonso anathawira panja. Christine anati: “Nthaka inanjenjemera kwambiri moti ndinagwera pansi ndipo ndinalephera kudzuka. Nyumba zinali kuyandama pa nyanja zitasesedwa ndi mafunde akuluakulu. Ndipo anthu anali yakaliyakali m’maboti awo panyanja pofunafuna anthu omwe anali adakali moyo. Ndiyeno kunachitika zivomezi zina ziwiri zamphamvu motsatizana. Nthaka inapitirizabe kugwedezeka kwa masiku asanu. Zinalitu zoopsa zedi.”

Kunachitikanso Tsunami

Panthawi imene chivomezicho chinkachitika, n’kuti Patson Baea, ali pa nyumba yake yomwe ili pa chilumba cha Sepo Hite, chomwe chili pa mtunda wa makilomita 6 kuchokera m’tawuni ya Gizo. Kodi bamboyu ndi banja lake anakhudzidwa bwanji ndi tsokali?

Pokumbukira zimene zinachitika, iye anati: “Ndinathamanga m’mbali mwa nyanja kupita kumene kunali mkazi wanga Naomi ndi ana anga anayi. Onse anali atagwa pansi chifukwa cha chivomezicho koma sanavulale. Anawo anali njenjenje ndi mantha ndipo ena ankalira. Komabe ine ndi mkazi wanga tinawatonthoza.

“Madzi a m’nyanjayo anali kuyenda modabwitsa kwambiri ndipo zinali zoonekeratu kuti kuchitika tsunami ndiponso kachilumba kathuko kamizidwa ndi madzi. Komanso moyo wa amayi anga a Evalyn, omwe ankakhala pa chilumba china kufupi ndi chilumba chathu, unali pangozi. Motero ndinauza banja langa kuti tikwere mofulumira boti lathu la injini n’cholinga choti tikawapulumutse.

“Titangoyenda pang’ono, funde lalikulu linadutsa pansi pa bwato lathu. Kenako nyanja yonse inayamba kuwinduka. Titafika, tinawapeza ali njenjenje ndi mantha moti ankachita kuwopa kulowa m’madzi kuti akwere boti. Ndiyeno mkazi wanga Naomi pamodzi ndi mwana wathu wamwamuna wazaka 15, dzina lake Jeremy, analumphira m’madzimo momwe munali mafunde akuluakulu, n’kuwathandiza mayiwo kukwera m’botilo. Kenako tinayenda mothamanga kwambiri kulowera m’katikati mwa nyanjayo.

“Panthawiyi, madzi anali atatsika ndithu moti matanthwe a m’mbali mwa zilumbazo ankaonekera. Mwadzidzidzi, mafunde akuluakulu anasefukira pa zilumba ziwiri zonsezo. Nyumba yathu yogona alendo yomwe inali m’mphepete mwa nyanjayi inaphwasukiratu ndipo madziwo anafika m’nyumba imene tinkakhala n’kuwononga katundu wambiri. Mafundewo atasiya, tinapita m’nyumba yathu ija n’kukachotsamo Mabaibulo ndi mabuku athu a nyimbo kenako n’kuyamba ulendo wopita ku Gizo.”

Anthu ambiri anafa komanso katundu wambiri anawonongeka. Dera lakumadzulo kwa chilumba cha Ghizo n’limene linakhudzidwa kwambiri ndi tsokali. Pafupifupi midzi yokwana 13 inamizidwa ndi funde lalikulu lomwe linali lalitali mamita asanu.

Madzulo a tsiku limenelo, anthu 22 anasonkhana pa Nyumba ya Ufumu ya Mboni za Yehova ku Gizo kuti achite mwambo wokumbukira imfa ya Yesu. Koma zinali zosangalatsa kuti panalibe ngakhale mmodzi mwa anthuwa amene anavulala modetsa nkhawa ndi tsunami uja. Ron, yemwe tam’tchula kale uja anati: “Panalibe magetsi, ndipo nyali zathu zinali zowonongeka. Choncho, M’bale Shaw anakamba nkhani ya mwambowu pogwiritsa ntchito tochi. Ngakhale tinali mu mdima, tinaimba mogwirizana bwino kwambiri nyimbo zotamanda Yehova.”

Kupereka Chithandizo

Nkhani ya tsokali itamveka mu mzinda wa Honiara womwe ndi likulu la dzikoli, ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova inakonza mofulumira zokapereka chithandizo kwa anthu okhudzidwa ndi tsokali. Ndipo anthu a ku ofesi ya nthambiyo anaimba foni mwachangu m’dera limene munachitika tsokali ndipo anapeza kuti Mboni zambiri zinali bwinobwino. Kenako ofesiyo inatumiza anthu odalirika kuti akafufuze mayi wina wa Mboni yemwe anali kukhala pa chilumba cha Choiseul. Anthuwo anapeza mayiyo ali bwinobwino. Ofesiyo inatumizanso ndalama ku Gizo zogulira zinthu zina zofunika kwambiri zothandizira patsokali.

Patsiku Lachinayi, anthu awiri ochokera ku ofesi ya nthambi anafika ku Gizo pandege yomwe inali yoyamba kufika m’tawuniyi chichitikireni tsokali. Craig Tucker, yemwe ali m’Komiti ya Nthambi anati: “Tinanyamula mabokosi angapo a zinthu zothandizira anthu okhudzidwa ndi tsokali. Anthu ena amene tinakwera nawo ndegeyo sanaloledwe kutenga katundu wawo wina chifukwa choti ndegeyo sikanatha kunyamula katundu yense. Komabe, tinasangalala kuona kuti katundu wathu yense wafika bwinobwino. Katunduyu anali m’gulu la zinthu zoyambirira kufika m’tawuniyi zothandizira anthu omwe anakhudzidwa ndi tsokali. Katundu wina anafika pa boti patatha masiku awiri.”

Panthawi imeneyi, Tony Shaw ndi Patson Baea pamodzi ndi Mboni zina zochokera ku Gizo, anayenda ulendo wa maola awiri paboti kuti akathandize Mboni za pachilumba cha Ranongga. Chivomezicho chinachititsa kuti madzi atsike ndi mamita awiri m’mphepete mwa chilumbachi, chomwe n’chachikulu makilomita 32 m’litali ndi makilomita 8 m’lifupi. Kutsika kwa madziku kunachititsa mafunde akuluakulu omwe anawononga kwambiri pazilumba zina zakufupi ndi chilumbachi.

Tony anati: “Anthu a mumpingo wa ku Ranongga anasangalala kwambiri atationa. Iwo anali bwinobwino ndipo anali atachoka m’nyumba zawo chifukwa choopa zivomezi zina. Boti lathu linali loyamba kufika ndi chithandizo pachilumbachi. Tisananyamuke kubwerera kwathu, tonse tinapemphera pamodzi kwa Yehova.”

Nayenso Patson anati: “Patapita masiku angapo, tinapitanso ku Ranongga kukapereka chithandizo china ndiponso kukafufuza banja la Matthew Itu, lomwe ndi la Mboni ndipo linkakhala m’dera lina lakutali pachilumbachi. Onse tinawapeza akukhala m’katikati mwa tchire ndipo atationa, onse anasangalala kwambiri poona kuti sitinawaiwale. Chivomezi chija chinawononga nyumba yawo komanso nyumba zina zambiri m’mudzi mwawo. Koma, nkhawa yaikulu ya banjali inali yoti apezenso Mabaibulo ena chifukwa choti amene anali nawo anawonongeka.”

Anthu Ena Anayamikira Mboni

Anthu ena anaona chikondi chachikhristu chimene Mboni zinasonyeza. Craig Tucker anati: “Mtolankhani wina yemwe sankagwirizana ndi mmene ntchito yonse yopereka chithandizo inali kuyendera, anadabwa ndiponso anachita chidwi kwambiri atamva kuti pasanapite masiku ambiri chivomezicho chitachitika, Mboni za Yehova zinathandiza Mboni zinzawo ndi chakudya, malona komanso zinthu zina zofunika.” Ndipo Patson anati: “Anthu a pachilumba cha Ranongga anatiyamikira kwambiri chifukwa chokapereka chithandizo mwamsanga, koma anadandaula chifukwa choti matchalitchi awo sanawathandize.” Ndipo mayi wina ananena kuti, “Gulu lanu linabweretsa chithandizo mofulumira kwambiri.”

Mbonizo zinathandizanso anthu a zipembedzo zina. Christine Shaw anafotokoza kuti: “Titapita ku chipatala chomwe chinakhazikitsidwa ku Gizo kuti chithandize anthu panthawi ya tsokali, tinapeza mwamuna ndi mkazi wake amene tinakumana nawo muutumiki kutangotsala masiku angapo kuti tsokali lichitike. Iwo anali atavulala ndiponso atasokonezeka maganizo kwambiri chifukwa cha chivomezicho. Mdzukulu wa mayiyo anafa atakokololedwa ndi mafunde akuluakulu. Choncho tinabwerera ku nyumba mwamsanga n’kukawatengera chakudya ndi zovala ndipo iwo anathokoza kwambiri chifukwa cha zimenezi.”

N’zoona kuti anthu amene akhudzidwa ndi masoka achilengedwe amafunikiranso zinthu zina kuwonjezera pa chithandizo cha zinthu zakuthupi. Kwenikweni, iwo amafunikira chilimbikitso chomwe sichingapezeke kwina kulikonse koma m’Baibulo, lomwe ndi Mawu a Mulungu. Ron anati: “Atsogoleri ena a zipembedzo ankanena kuti Mulungu ndi amene anachititsa tsokali polanga anthu chifukwa cha machimo awo. Koma tinawasonyeza m’Baibulo kuti Mulungu si amene amachititsa zinthu zoipa. Ndipo anthu ambiri anatiyamikira chifukwa chowalimbikitsa ndi mfundo ya m’Baibulo imeneyi.”​—2 Akorinto 1:3, 4; Yakobe 1:13. *

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 24 Onani nkhani yakuti “Kuyankha Funso Lovuta Kwambiri Loti ‘Chifukwa Chiyani?’” mu magazini ya Galamukani! ya November 2006, masamba 3 mpaka 9. Tsokali litachitika, magaziniwa anagawidwa ambiri ku Gizo.

[Chithunzi/​Mapu patsamba 13]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

Choiseul

Ghizo

Gizo

Ranongga

HONIARA

AUSTRALIA

[Chithunzi patsamba 15]

Banja la Baea m’boti lawo

[Chithunzi patsamba 15]

Mmene tsunami anawonongera ku Gizo

[Chithunzi patsamba 15]

Nyumba ya Ufumu iyi ndi nyumba yokhayo imene siinagwe m’dera la Lale pa chilumba cha Ranongga