Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Phunzitsani Ana Anu

Ankafuna Kuthandiza Ena

Ankafuna Kuthandiza Ena

KODI unaonapo munthu akudwala kwambiri?​— Nanga unafuna utam’thandiza kuti apeze bwino?​— Bwanji akanakhala wochokera kunja kapena wachipembedzo china? Kodi ukanafunabe kumuthandiza kuti apeze bwino?​— Zaka 3,000 zapitazo, kamtsikana kena kamene kankakhala m’dziko la Isiraeli kanathandiza munthu wina kuti apeze bwino. Tiye tione zimene zinachitika.

Kalelo, anthu a kwawo kwa kamtsikanaka, ku Isiraeli, ankakonda kumenyana ndi anthu oyandikana nawo, a dziko la Aramu. (1 Mafumu 22:1) Tsiku lina anthu a ku Aramu anagwira kamtsikanaka ndi kupita nako kwawo. Kumeneko anakakhala wantchito wamkazi wa Namani. Namani anali mkulu wa gulu lankhondo la Aaramu ndipo amadwala matenda oopsa a khate. Matendawa amapangitsa kuti thupi lizidyekadyeka.

Kamtsikanaka kanauza mkazi wa Namani zimene angachite kuti mwamuna wakeyu achire. Iye anati: ‘Namani akadakhala ku Samariya, mneneri wa Yehova Elisa akanamuchiritsa khate lake.’ Chifukwa cha mmene kamtsikanaka kananenera mawuwa, Namani anakhulupirira kuti Elisa akhozadi kumuchiritsa. Choncho, mfumu ya Aaramu dzina lake Benihadadi inavomereza kuti Namani ndi anyamata ake anyamuke ulendo wopita kwa Elisa. Ulendowu unali wautali kwambiri pafupifupi makilomita 150.

Atafika, anapita kaye kwa mfumu ya Aisiraeli, Yehoramu. Kumeneko, anapereka kalata yochokera kwa Benihadadi yopempha kuti amuthandize Namani. Koma Yehoramu sankakhulupirira Yehova ngakhalenso mneneri wake Elisa. Yehoramu anaganiza kuti anthuwa abwerera zoyambana. Elisa atamva zimenezi, anauza Mfumu Yehoramu kuti: ‘Auzeni abwere kwa ine.’ Elisa anafuna kusonyeza kuti Mulungu anali ndi mphamvu yom’chiritsa Namani matenda ake oopsawo.​—2 Mafumu 5:1-8.

Namani atafika kunyumba ya Elisa ndi mahatchi komanso magareta ake, Elisa anatumiza mnyamata wake kudzamuuza kuti: ‘Ukasambe m’Yordano kasanu ndi kawiri, ndipo mnofu wako udzabwerera.’ Namani anakwiya zedi chifukwa amayembekezera kuona Elisa akubwera ndi kukhudza khate lake kuti achire. M’malo mwake anangokumana ndi mnyamata wake. Apa Namani anakwiya kwambiri ndipo anauyamba ulendo wobwerera kwawo.​—2 Mafumu 5:9-12.

Kodi ukanatani ukanakhala kuti ndiwe mmodzi wa anyamata a Namani?​— Anyamata ake anamufunsa kuti: ‘Elisa akadakuuzani chinthu chachikulu, kodi simunakachita? Ndiye bwanji osamvera n’kungosamba kuti mukhale bwino?’ Namani anamvera. Ndipo ‘anapita, namira m’Yordano kasanu ndi kawiri, . . . ; ndipo mnofu wake unakhala ngati wa mwana wamng’ono.’

Namani anapita kwa Elisa ndi kumuuza kuti: “Taonani, tsopano ndidziwa kuti palibe Mulungu pa dziko lonse lapansi, koma kwa Isiraeli.” Iye analonjeza Elisa kuti: “Sadzaperekanso nsembe yopsereza kapena yophera kwa milungu ina, koma kwa Yehova.”​—2 Mafumu 5:13-17.

Kodi ukufuna kuthandiza winawake kudziwa za Yehova ndiponso zimene ayenera kuchita, monga kanachitira kamtsikana kaja?​— Yesu ali padziko pano, munthu wakhate amene anali ndi chikhulupiriro mwa iye, anamuuza kuti: ‘Ngati mukufuna kundithandiza, mungandithandize.’ Kodi ukudziwa zimene Yesu anayankha?​— Iye anati: ‘Ndikufuna.’ Ndipo Yesu anamuchiritsa munthuyo, monga mmene Yehova anachiritsira Namani.​—Mateyo 8:2, 3.

Kodi umadziwa kuti Yehova adzakonza dziko lapansi latsopano limene lidzakhale ndi anthu athanzi omwe adzakhale ndi moyo kosatha?​— (2 Petulo 3:13; Chivumbulutso 21:3, 4) Ngati ndi choncho, uyenera kuuza ena zinthu zabwino zimenezi.