Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

‘Dzina Losafunika Kulitchula’?

‘Dzina Losafunika Kulitchula’?

‘Dzina Losafunika Kulitchula’?

CHIPILALA chooneka ngati uta, chotchedwa Gateway Arch, chomwe chili pafupi ndi mtsinje ku St. Louis, m’chigawo cha Missouri, ndi chachitali kwambiri ku United States konse chifukwa n’cha mamita 192. Pafupi ndi chipilalachi pali tchalitchi cha Akatolika chodziwika ndi dzina lakuti Old Cathedral.

Pofotokoza za polowera m’tchalitchichi, kabuku kena ka Akatolika kanati: “Pamwamba pa khomo lolowera m’tchalitchi pali mawu akuluakulu olembedwa m’Chiheberi a dzina la Mulungu losafunika kulitchula.” Pachithunzipa mungaone bwinobwino zilembo zinayi za m’Chiheberi יהוה (YHWH), zomwe zimaimira dzina la Mulungu.​—The Story of the Old Cathedral.

Pamene tchalitchichi chinkamangidwa mu 1834, anthu a m’dera la St. Louis ankaona kuti dzina la zilembo zinayi za m’chiheberi limeneli linali lofunika kwambiri. Koma kodi n’chifukwa chiyani anthu amati ‘dzina la Mulungu ndi losafunika kulitchula’?

Buku lina la Akatolika limafotokoza zimene zinachitika patapita nthawi ndithu Ayuda atachoka ku ukapolo ku Babulo cha m’ma 500 B.C.E. Bukuli limati: “Anthu anayamba kuona kuti dzina lakuti Yahweh [tikalemba zilembo zinayi zija moti ziziwerengeka] ndi lopatulika ndipo pamalo onse omwe pamapezeka dzinali anayamba kuikapo mawu akuti ADONAI [Ambuye] kapena ELOHIM [Mulungu]. . . . Patapita nthawi, zimenezi zinachititsa kuti anthu aiwale katchulidwe ka dzina lakuti Yahweh.” (New Catholic Encyclopedia) Choncho, anthu analeka kugwiritsa ntchito dzina la Mulungu. Mapeto ake, anthu anaiwala katchulidwe ka dzina la Mulungu ndipo samathanso kulitchula.

Ngakhale kuti sitingadziwe mmene dzina la Mulungu linkatchulidwira, mfundo yofunika kukumbukira ndi yakuti kutchula dzina la Mulungu kumatithandiza kuti tikhale naye paubwenzi. Kodi simungasangalale kuti anzanu pokuitanani azitchula dzina lanu m’malo momangoti “inu” kapena “iwe”? Ngakhale kuti anzanuwo salankhula chilankhulo chanu ndipo satha kutchula bwinobwino dzina lanulo, mungafunebe kuti azikuitanirani dzina lanu lomwelo. N’chimodzimodzinso ndi Mulungu. Iye amafuna kuti tizimutchula dzina lake lenileni lakuti Yehova.

M’Chichewa katchulidwe ka dzina lakuti “Yehova” n’kodziwika kwambiri. Kodi sizingakhale bwino kuti onse amene amakonda Mulungu azimutchula ndi dzina lake limeneli? Zimenezi zingachititse kuti tiyandikirane naye malinga ndi zimene Baibulo limanena kuti: “Yandikirani Mulungu, ndipo iyenso adzakuyandikirani.”​—Yakobe 4:8.