Kodi Chigumula cha Nowa Chinachitikadi Padziko Lonse?
Zimene Owerenga Amafunsa
Kodi Chigumula cha Nowa Chinachitikadi Padziko Lonse?
Chigumula cha Nowa chinachitika zaka zoposa 4,000 zapitazo. Choncho, palibe munthu amene anapulumuka chigumulachi yemwe ali ndi moyobe masiku ano amene angatiuze zimene anaona ndi maso ake. Komabe, tili ndi nkhani zolembedwa zimene zimanena kuti madzi a chigumulachi anamiza mapiri ataliatali amene analipo panthawiyo.
Nkhani ina imati: “Ndipo chigumula chinali pa dziko lapansi masiku makumi anayi . . . Ndipo madzi anapambana ndithu padziko lapansi; anamizidwa mapiri aatali onse amene anali pansi pa thambo lonse. Madzi anapambana ndithu nakwera mikono khumi ndi isanu [pafupifupi mamita 6 ndi theka]: namizidwa mapiri.”—Genesis 7:17-20.
Ena amaganiza kuti nkhani yakuti madzi anadzadza padziko lapansi ndi nthano kapena ndi kukokomeza nkhani. Koma zimenezi sizoona. Ngakhale masiku ano dziko ndi lodzadzabe ndi madzi, chifukwa mbali yaikulu ya dziko lathuli ndi madzi okhaokha. Choncho, tinganene kuti madzi a chigumula akadalipobe masiku ano. Ndipo ngati madzi oundana apadziko lapansili atasungunuka, nyanja zingasefukire mpaka kumiza mizinda yokhala ndi nyumba zazitali monga New York ndi Tokyo.
Akatswiri oona malo amaona kuti kumpoto chakumadzulo kwa United States kunasefukira madzi maulendo 100. Akuti nthawi ina madzi osefukirawo anafika mwamkokomo ndipo anakwera mpakana mamita 600, ndiponso ankathamanga pa liwiro la makilomita 105 pa ola limodzi. Zinthu ngati zimenezi zapangitsa asayansi ena kukhulupirira kuti n’zotheka kuti chigumula chichitike padziko lonse.
Komabe, anthu amene amakhulupirira kuti Baibulo ndi Mawu a Mulungu, samakayikira kuti chigumula chinachitika padziko lonse. Iwo amakhulupirira kuti chinachitikadi. Yesu anauza Mulungu kuti: “Mawu anu ndiwo choonadi.” (Yohane 17:17) Mtumwi Paulo analemba kuti Mulungu amafuna kuti “anthu, kaya akhale a mtundu wotani, apulumuke ndi kukhala odziwa choonadi molondola.” (1 Timoteyo 2:3, 4) Kodi Paulo akanaphunzitsa bwanji otsatira a Yesu mfundo za choonadi, Mawu a Mulungu akanakhala kuti ndi nthano chabe?
Yesu ankakhulupirira kuti chigumula chinachitikadi komanso kuti chinachitika padziko lonse. Mu ulosi wonena za kukhalapo kwake ndi mapeto a dongosolo la zinthu lino, Yesu anayerekezera nthawi imeneyi ndi masiku a Nowa. (Mateyo 24:37-39) Mtumwi Petulo analembanso za chigumula cha Nowa. Iye anati: “Mwa zimenezi, dziko la panthawiyo linawonongeka pamene linamizidwa ndi madzi.”—2 Petulo 3:6.
Nkhani ya Nowa ndi chigumula ikanakhala kuti ndi nthano chabe, zimene Petulo ndi Yesu anachenjeza anthu okhala m’masiku otsiriza, sizikanakhala ndi tanthauzo. Komanso, sizikanakhala zotichenjeza koma zotisokoneza mwauzimu. Ndipo zikanalepheretsa anthu kupulumuka pa chisautso choposa chigumula cha Nowa.—2 Petulo 3:1-7.
Pofotokoza za chifundo chake kwa anthu, Mulungu anati: “Monga ndinalumbira kuti madzi a Nowa sadzamizanso . . . dziko lapansi, momwemo ndinalumbira kuti sindidzakukwiyira iwe, pena kukudzudzula.” Monga momwe madzi anadzadzira padziko lapansi pa nthawi ya chigumula cha Nowa, ndi mmenenso chikondi ndi kukoma mtima kwa Mulungu zidzakhalire ndi anthu amene amamukhulupirira.—Yesaya 54:9.