Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mulungu Amavomereza Kulambira Kwina Kulikonse?

Kodi Mulungu Amavomereza Kulambira Kwina Kulikonse?

Kodi Mulungu Amavomereza Kulambira Kwina Kulikonse?

“ANTHU mwachibadwa amafuna kulambira.” Anatero pulofesa Alister Hardy m’buku limene analemba. Zotsatira za kafukufuku wina waposachedwapa zikugwirizana ndi mfundo imeneyi. Pakafukufukuyu anapeza kuti anthu 86 pa anthu 100 alionse padziko lapansili ndi opembedza.​—The Spiritual Nature of Man.

Pakafukufukuyu anapezanso kuti anthuwa ali m’zipembedzo zikuluzikulu 19. Ndipo m’chipembedzo cha Chikhristu chokha muli zipembedzo zing’onozing’ono 37,000. Kodi mukuganiza kuti zipembedzo zonsezi n’zovomerezeka kwa Mulungu? Kapena kodi pali kulambira kumene Mulungu amakuvomereza?

Pankhani yofunika ngati imeneyi sitingayendere maganizo athu koma m’pofunika kufufuza zimene Mulungu amafuna. Kuti tipeze zimenezi, m’pofunika kufufuza m’Mawu ake, Baibulo. Chifukwa chiyani? Chifukwa cha zimene Yesu Khristu ananena popemphera kwa Mulungu. Iye anati: “Mawu anu ndiwo choonadi.” (Yohane 17:17) Ndipo mtumwi wokhulupirika Paulo anati: “Malemba onse anawauzira ndi Mulungu, ndipo ndi opindulitsa pa kuphunzitsa, kudzudzula, kuwongola zinthu.”​—2 Timoteyo 3:16.

Baibulo limasonyeza kuti Mulungu savomereza kulambira kwina kulikonse. M’Baibulo muli zitsanzo zosonyeza kulambira kumene Mulungu amakuvomereza ndi kumene sakuvomereza. Kuwerenga mosamala zitsanzo zimenezi kungatithandize kudziwa zoyenera kuchita kuti kulambira kwathu kukhale kovomerezeka kwa Mulungu.

Chitsanzo cha M’nthawi Yakale

Kudzera kwa mneneri Mose, Yehova Mulungu anapatsa Aisiraeli malamulo a mmene angamulambirire. Malamulowo ankatchedwa kuti Chilamulo cha Mose ndipo anthuwo akamawatsatira, Mulungu ankawatenga kukhala anthu ake ndipo ankawadalitsa. (Eksodo 19:5, 6) Komabe, ngakhale kuti Mulungu ankawakonda Aisiraeli, iwo analeka kumulambira mmene iye amafunira. Nthawi zambiri ankasiya kulambira Yehova n’kuyamba kulambira milungu imene anthu m’dzikolo ankalambira.

M’masiku a mneneri Ezekieli ndi Yeremiya, cha m’ma 600 B.C.E., Aisiraeli ambiri sankatsatira Chilamulo cha Mulungu ndipo iwo anayamba kugwirizana ndi anthu a mitundu yoyandikana nawo. Chifukwa chotsatira miyambo ndi maphwando a anthu amenewa, Aisiraeli anayamba kuphatikiza zipembedzo. Aisiraeli ambiri ankanena kuti: “Tidzakhala ngati amitundu, ngati mabanja a m’mayiko, kutumikira mtengo ndi mwala.” (Ezekieli 20:32; Yeremiya 2:28) Iwo ankati amalambira Yehova Mulungu, koma ankalambiranso “mafano,” ndiponso ankapereka ana awo nsembe kwa milungu imeneyi.​—Ezekieli 23:37-39; Yeremiya 19:3-5.

Anthu ofufuza zinthu zakale amati kalambiridwe kosakaniza zipembedzo kameneka kanali kotchuka. Masiku anonso anthu ambiri amaganiza kuti tifunika kulolera zinthu zilizonse ndi pankhani yopembedza yomwe, chifukwa anthu ali ndi zikhulupiriro zosiyanasiyana. Choncho, amaona kuti palibe cholakwika kulambira Mulungu mulimonse mmene akufunira. Kodi zimenezi n’zoona? Kodi nkhani ya kulambira ndi nkhani yamakonda? Onani zinthu zina zimene Aisiraeli osakhulupirika ankachita polambira komanso zotsatira zake.

Kulambira Kosakaniza Zipembedzo kwa Aisiraeli

Aisiraeli akafuna kulambira milungu yambiri ankapita ku “misanje” kapena m’makachisi mmene munkakhala maguwa a nsembe, zofukizira, zipilala zopatulika za miyala, ndi zifanizo zopatulika. Zifanizo zimenezi mwina zinkaimira Asera, mulungu wamkazi wachikanani wamphamvu zobereketsa. Malo oterewa analipo ambiri m’Yuda. Lemba la 2 Mafumu 23:5, 8 limatchula za “misanje m’midzi ya Yuda, ndi pamalo pozinga Yerusalemu; . . . kuyambira Geba [malire a kumpoto] kufikira Beereseba [malire a kum’mwera].”

M’misanje imeneyi, ndi mmene Aisiraeli ‘ankafukizira zonunkhira Baala, ndi dzuwa, ndi mwezi, ndi nthanda, ndi khamu lonse la kuthambo.’ Aisiraeli analinso ndi nyumba za “anyamata adama . . . ku nyumba ya Yehova” ndipo ankapereka ana awo “pamoto kwa Moleki.”​—2 Mafumu 23:4-10.

Ofufuza zinthu zakale apeza mafano ambirimbiri ku Yerusalemu ndi ku Yuda, makamaka m’mabwinja a nyumba za anthu. Ambiri a mafano amenewa anali osonyeza akazi a mabere akuluakulu ali maliseche. Akatswiri ena akuti mafano amenewa anali a milungu yachikazi ya mphamvu zobereketsa yotchedwa Asitoreti ndi Asera. Anthu ankakhulupirira kuti mafanowa anali ngati “zithumwa zothandiza anthu kubereka.”

Kodi Aisiraeli ankawaona bwanji malo olambirira milungu yambirimbiriwa? Pulofesa Ephraim Stern wa ku yunivesite ya Hebrew anati malo ambiri otere ayenera kuti anali “opatulidwira kwa Yahweh [Yehova].” Mawu olembedwa pa miyala ina imene akatswiri a zinthu zakale anapeza amatsimikizira mfundo imeneyi. Mwachitsanzo, mwala wina uli ndi mawu akuti: “Ndikukudalitsa m’dzina la Yahweh wa ku Samariya ndi Asera wake,” ndipo wina uli ndi mawu akuti, “Ndikukudalitsa m’dzina la Yahweh wa ku Temani ndi Asera wake.”

Zimenezi zikusonyeza kuti Aisiraeli anasakaniza kulambira koona kwa Yehova Mulungu ndi miyambo yochititsa manyazi yachikunja. Chifukwa cha zimenezi, anayamba kuchita zinthu zoipa ndiponso anali mu m’dima wauzimu. Kodi kulambira kumeneku Mulungu anakuona bwanji?

Zimene Mulungu Anachita

Mulungu sanasangalale ndi kulambira konyansa kwa Aisiraeli ndipo kudzera mwa mneneri wake Ezekieli anati: “Pokhala inu ponse midzi idzapasuka, ndi misanje idzakhala yabwinja; kuti maguwa anu a nsembe akhale opasuka ndi mabwinja, ndi mafano anu asweke nalekeke, ndi zoimiritsa zanu zadzuwa zilikhidwe, ndi ntchito zanu zifafanizidwe.” (Ezekieli 6:6) N’zoonekeratu kuti Yehova sanavomereze kulambira kumeneku ndipo anakukana.

Yehova Mulungu ananeneratu za mmene adzawafafanizire. Iye anati: “Ndidzatuma . . . Nebukadinezara mfumu ya ku Babulo, mtumiki wanga, ndipo ndidzatengera iwo pa dziko lino, ndi pa okhalamo ake onse, ndi pa mitundu iyi yozungulira, ndipo ndidzathetsa iwo ndithu . . . Ndipo dziko lonseli lidzakhala labwinja.” (Yeremiya 25:9-11) Ndipo zimenezi zinachitikadi chifukwa mu 607 B.C.E., Ababulo anaukira Yerusalemu ndi kuwonongeratu mzindawo ndi kachisi wake.

Ponena za kuwonongedwa kwa Yerusalemu, Pulofesa Stern, amene tamutchula kale uja, ananena kuti zinthu zakale zimene zinapezedwa, “ndi umboni wogwirizana kwambiri ndi zimene Baibulo linanena (2 Mafumu 25:8; 2 Mbiri 36:18, 19) zokhudza kuwonongedwa, kuwotchedwa ndiponso kugwa kwa nyumba ndi malinga.” Iye ananenanso kuti: “Umboni umene akatswiri ofufuza zinthu zakale apeza wonena za kuwonongedwa kwa Yerusalemu . . . ndi wochititsa chidwi kwambiri kuposa maumboni ena onse otere amene anthu apeza okhudza malo otchulidwa m’Baibulo.

Kodi Tikuphunzirapo Chiyani?

Mfundo yaikulu imene tikuphunzirapo ndi yakuti Mulungu savomereza kulambira kophatikiza mfundo za m’Baibulo ndi miyambo ya zipembedzo zina. Mtumwi Paulo anadziwanso mfundo imeneyi. Iye anakulira m’chipembedzo cha Afalisi Achiyuda, komanso anaphunzira chilamulo cha anthu amenewa. Kodi iye anatani atadziwa kuti Yesu ndiye Mesiya wolonjezedwa? Iye anati: “Zinthu zimene zinali phindu kwa ine, zimenezo ndaziona kukhala zopanda phindu chifukwa cha Khristu.” Iye anasiya zimene amachita poyamba ndi kukhala wotsatira Khristu wodzipereka.​—Afilipi 3:5-7.

Paulo ankayendayenda pa ntchito yake ya umishonale ndipo chifukwa cha zimenezi ankadziwa bwino zikhulupiriro ndiponso miyambo ya anthu osiyanasiyana. N’chifukwa chake analembera Akhristu a ku Korinto kuti: “Pali kuyanjana kwanji pakati pa kuwala ndi mdima? Ndiponso, pali m’gwirizano wanji pakati pa Khristu ndi Beliyali? Kapena munthu wokhulupirira agawana chiyani ndi wosakhulupirira? Ndipo pali kumvana kwanji pakati pa kachisi wa Mulungu ndi mafano? . . . ‘Choncho tulukani pakati pawo, dzilekanitseni kwa iwo,’ atero Yehova, ‘ndipo musakhudze chonyansacho’; ‘ndipo ndidzakulandirani.’”​—2 Akorinto 6:14-17.

Popeza tadziwa kuti Mulungu savomereza kulambira kwina kulikonse, mungadzifunse mafunso awa: ‘Kodi Mulungu amavomereza kulambira kotani? Kodi ndingatani kuti ndikhale paubwenzi ndi Mulungu? Ndiponso kodi ndingatani kuti Mulungu azivomereza kulambira kwanga?’

Mboni za Yehova zingakuthandizeni kudziwa mayankho a mafunso amenewa ndi ena a m’Baibulo. Tikukulimbikitsani kuti mupezane ndi Mboni za Yehova ku Nyumba ya Ufumu ya kwanuko kapena mutilembere kalata yopempha munthu woti azidzaphunzira nanu Baibulo kwaulere panthawi ndi malo amene inuyo mungasankhe.

[Chithunzi patsamba 10]

Kachisi wakale wolambiriramo mafano, ku Tel Arad, m’dziko la Israel

[Mawu a Chithunzi]

Garo Nalbandian

[Chithunzi patsamba 10]

Mafano a Asitoreti a m’nyumba zakale za ku Yudeya

[Mawu a Chithunzi]

Photograph © Israel Museum, Jerusalem; courtesy of Israel Antiquities Authority