Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mumachita Chidwi ndi Zinthu?

Kodi Mumachita Chidwi ndi Zinthu?

Kodi Mumachita Chidwi ndi Zinthu?

“Mwachibadwa anthu amakonda kufunsa mafunso. Tinayamba kufunsa mafunso titangobadwa . . . Tinganene kuti mbiri yonse ya anthu yangokhala ya mafunso ndi mayankho.”​—Anatero Octavio Paz, Mlakatuli wa ku Mexico.

N’CHIYANI chimapangitsa munthu kuphika chakudya m’njira yatsopano? N’chiyani chimachititsa munthu wofufuza malo kukafufuza malo akutali kwambiri? N’chiyani chimachititsa mwana kufunsa mafunso ambirimbiri? Nthawi zambiri chimachititsa ndi chidwi.

Bwanji inuyo? Kodi muli ndi chidwi chofuna kudziwa zinthu zatsopano kapena mayankho a mafunso ofunika? Mafunso monga akuti: Kodi moyo unayamba bwanji? N’chifukwa chiyani tili moyo? Kodi Mulungu alipo? Kuyambira tili aang’ono, ambirife timakhala ndi chidwi chofuna kudziwa mayankho amafunso ngati amenewa. Ngati tasangalala ndi chinthu chinachake, timayesetsa kuti tichidziwe bwinobwino. Choncho, chidwi chingatithandize m’njira zambiri koma chithanso kutiika m’mavuto.

M’pofunika Kusamala

Mwambi wina umati: Chidwi chinapha mkonzi. Indedi, ngati titapanda kusamala chidwi chitha kutiika m’mavuto. Mwachitsanzo, chifukwa cha chidwi mwana atha kugwira moto n’kupsa. Komabe, chidwi chomwecho chingatichitse kudziwa zambiri. Koma kodi ndi nzeru kumangochita chidwi ndi chinthu chilichonse?

Ndithudi, zinthu zina sizofunika kuchita nazo chidwi chifukwa n’zoipa. Kuchita chidwi ndi zinthu zolaula, zamatsenga, zikhulupiriro zoipa zachipembedzo kapena za zigawenga kungatiike m’mavuto. Pankhani zimenezi ndi zinanso zambiri, tingachite bwino kutsatira wamasalimo wachiheberi amene anapemphera kuti: “Muchititse mlubza maso anga ndisapenye zachabe.”​—Salmo 119:37.

Komanso pali zinthu zina zimene tingafune kuzidziwa zomwe si zoipa koma sizofunika kwenikweni. Mwachitsanzo, kodi kudziwa chilichonse chokhudza moyo wa munthu wotchuka m’mafilimu kapena m’dziko, mmene mpira uliwonse ukuyendera kapena mmene wosewera aliyense akuchitira, kapenanso kudziwa zonse zokhudza zipangizo zamakono ndi mitundu ya magalimoto yatsopano, kuli ndi phindu lanji? Anthu ambiri amadziwa kuti kukhala “katswiri” wodziwa zinthu zimenezi kulibe phindu lenileni.

Chitsanzo Chabwino

Koma chidwi chili ndi ubwino wake. Taganizirani za Alexander von Humboldt, katswiri wa ku Germany wa zinthu zachilengedwe komanso wofufuza malo wa m’zaka za m’ma 1800.

Nthawi ina Humboldt anati: “Kuyambira ndili wamng’ono ndinkafunitsitsa kupita malo a kutali kumene anthu ambiri a ku Ulaya sanafikeko.” Iye anati ankafuna kuchita zimenezi chifukwa chakuti anali ndi “chidwi kwambiri.” Ali ndi zaka 29, anapita ku Central America ndi ku South America kokaona malo ndipo anathako zaka zisanu. Zinthu zonse zimene anapeza, anazilemba m’mabuku okwana 30 onena za ulendo wakewu.

Humboldt, ankachita chidwi ndi chilichonse monga kutentha kwa madzi a m’nyanja, nsomba za m’madziwa, ndi zomera zimene anaziona paulendowu. Anakwera mapiri ndiponso anayenda m’mitsinje ndi m’nyanja zosiyanasiyana. Zimene Humboldt anafufuza zinathandiza kwambiri pa sayansi yamakono. Chimene chinayambitsa zonsezi ndi chidwi, kapena kuti mtima wake wofuna kudziwa zinthu. Wolemba mabuku wina dzina lake Ralph Waldo Emerson anati: “Humboldt anali mmodzi wa anthu odabwitsa . . . amene nthawi zambiri tikawerenga za iye, amatikumbutsa zimene munthu angakwanitse kuchita ndi mphamvu komanso nzeru zake.”

Zinthu Zofunika Kufufuza

Komabe, ambirife sitingakwanitse kukhala ofufuza malo kapena kupeza zinthu zimene zingathandize pa sayansi. Ngakhale zili choncho, pali zinthu zina zomwe tifunika kuikirapo mtima kuti tizidziwe ndipo tingapindule nazo kwambiri kuposa momwe kudziwa zinthu zina kungatipindulitsire. Yesu Khristu anatchula zimenezi popemphera kwa Atate wake akumwamba. Iye anati: “Pakuti moyo wosatha adzaupeza akamaphunzira ndi kudziwa za inu, Mulungu yekha woona, ndi za Yesu Khristu, amene inu munam’tuma.”​—Yohane 17:3.

Kudziwa Mulungu woona, amene dzina lake ndi Yehova, komanso kudziwa Mwana wake Yesu Khristu, kungatipindulitse kwambiri kuposa kudziwa zinthu zina. Takumbukirani mafunso amene tatchula kumayambiriro kwa nkhani ino aja. Mafunso enanso amene tifunika kudziwa mayankho ake ndi akuti: N’chifukwa chiyani padziko pali mavuto ambiri? Kodi dzikoli lidzawonongedwa ndi anthu? Nanga n’chiyani chimene Mulungu adzachite kuti zimenezi zisachitike? Kudziwa mayankho amafunso amenewa si nkhani yongochita chidwi chabe koma ndi kothandiza kwambiri. Monga Yesu ananenera, kudziwa zimenezi kudzatithandiza ‘kupeza moyo wosatha.’ Kodi tikudziwa bwanji zimenezi?

Baibulo ndi Mawu ouziridwa ndi Mulungu. Mtumwi wachikhristu Paulo analemba kuti: “Malemba onse anawauzira ndi Mulungu, ndipo ndi opindulitsa pa kuphunzitsa, kudzudzula, kuwongola zinthu, kulangiza m’chilungamo, kuti munthu wa Mulungu akhale woyenera mokwanira, wokonzeka bwino lomwe kuchita ntchito iliyonse yabwino.”​—2 Timoteyo 3:16, 17.

Onani kuti mtumwiyu anati, Baibulo limatithandiza kuchita ntchito iliyonse yabwino. Limatithandiza kuona zinthu mmene Mulungu amazionera. Ndipo tikudziwa kuti nzeru za Mulungu ndi zakuya kuposa za munthu wina aliyense. Mneneri Yesaya anauziridwa ndi Mulungu kulemba mfundo yofunika iyi: “Maganizo anga sali maganizo anu, ngakhale njira zanu sizili njira zanga, ati Yehova. Pakuti monga kumwamba kuli kutali ndi dziko lapansi, momwemo njira zanga zili zazitali kupambana njira zanu, ndi maganizo anga kupambana maganizo anu.”​—Yesaya 55:8, 9.

Kodi mukufuna kudziwa zambiri za njira za Mulungu ndi maganizo ake? Kodi muli ndi chidwi chofuna kudziwa zimene Mawu a Mulungu, Baibulo, amanena pa zinthu zimenezi? Kodi mukufunitsitsa kudziwa mmene Mulungu adzathetsere mavuto onse? Kodi mukufuna kudziwa zinthu zabwino zimene wasungira anthu omvera? Baibulo likukulimbikitsani kuti: “Talawani, ndipo onani kuti Yehova ndiye wabwino; wodala munthuyo wakukhulupirira Iye.”​—Salmo 34:8.

Monga mmene kuwala kumakhalira kwa munthu yemwe akuyamba kumene kuona, ndi mmenenso choonadi cha m’Mawu a Mulungu chimakhalira kwa anthu ofuna kuphunzira. Mtumwi Paulo anati: “Ha, kuchuluka kwa chuma cha Mulungu! Nzeru zake n’zozama, ndipo kudziwa kwake zinthu n’kozamanso zedi! Ziweruzo zake ndi zosasanthulika, ndipo ndani angatulukire njira zake?” (Aroma 11:33) Kunena zoona, sitingadziwe zonse zokhudza nzeru za Mulungu. Koma tili ndi chiyembekezo chakuti kutsogoloku tidzaphunzira zinthu zambiri ndipo sitidzatopa nazo.

Musaleke Kuchita Chidwi

N’zoona kuti ambirife sitingakhale anthu ofufuza malo kapena asayansi otchuka. Ndipo mwina sitingakwanitse kudziwa zinthu zonse zimene tingafune kudziwa. Ngakhale zili choncho, musaleke kuchita chidwi. Pitirizani kukhala ndi mtima wofuna kudziwa zinthu umene Mulungu anakupatsani.

Mphatso yochokera kwa Mulungu imeneyi ndi yofunika kwambiri ndipo khalani ndi mtima wofuna kudziwa Mawu a Mulungu molondola. Ngati mutatero, mungakhale ndi moyo wabwino komanso wosangalala pakali pano, ndipo mudzakhala ndi chiyembekezo chophunzira zimenezi kwa muyaya. Baibulo limati: “Chinthu chilichonse [Mulungu] anachikongoletsa pa mphindi yake; ndipo waika zamuyaya m’mitima yawo ndipo palibe munthu angalondetse ntchito Mulungu wazipanga chiyambire mpaka chitsiriziro.”​—Mlaliki 3:11.

[Bokosi/​Zithunzi patsamba 21]

Kodi Mukudziwa Kuti . . .

• Zaka mazana angapo Columbus ndi Magellan asanatulukire kuti dziko limaoneka bwanji, Baibulo linali litaneneratu kuti dziko si lophwatalala koma kuti ndi lozungulira?​Yesaya 40:22.

• Asayansi ya zakuthambo asanatulukire kuti dziko lili m’malere, Baibulo linali litaneneratu kuti lili pachabe?​Yobu 26:7.

• Patatsala zaka 2,500 kuti wa sayansi wa Chingelezi, William Harvey, atulukire mmene magazi amayendera m’thupi la munthu, Baibulo linali litatchula kale kuti mtima ndiwo magwero a moyo?​Miyambo 4:23.

• Zaka pafupifupi 3,000 zapitazo, Baibulo linali litanena kale mmene madzi amayendera kuti zinthu padziko lapansi zipitirize kukhala ndi moyo?​Mlaliki 1:7.

Kodi sizochititsa chidwi kuti Baibulo linaneneratu mfundo zasayansi zimenezi, anthu asanazimvetse kapena asanazitulukire n’komwe? Ndipotu m’Baibulo muli zinthu zambiri zofunikira pamoyo wathu zoti tizidziwe.

[Chithunzi patsamba 19]

Alexander von Humboldt