Mulungu Amakhululuka
Yandikirani Mulungu
Mulungu Amakhululuka
“INU, Ambuye, ndinu wabwino, ndi wokhululukira.” (Salmo 86:5) Ndi mawu olimbikitsa amenewa, Baibulo likutitsimikizira kuti Yehova Mulungu amakhululuka kwambiri. Zimene zinachitikira mtumwi Petulo, zikusonyezeratu kuti Yehova amakhululuka “koposa.”—Yesaya 55:7.
Petulo anali mnzake wa pamtima wa Yesu. Komabe, usiku womaliza wa moyo wa Yesu padziko lapansi, Petulo anachita tchimo lalikulu chifukwa cha mantha. Petulo anakana Yesu osati kamodzi kokha koma katatu, m’bwalo limene Yesu anam’zengera mlandu. Atamukana Yesu kachitatu, Yesu “anacheuka ndi kuyang’ana Petulo.” (Luka 22:55-61) Kodi mukuganiza kuti Petulo anamva bwanji Yesu atamuyang’ana? Petulo atazindikira kulakwa kwake “anasweka mtima nayamba kulira.” (Maliko 14:72) Mtumwi wolapayu ayenera kuti anakayikira zoti Mulungu angamukhululukire tchimo lakeli.
Yesu ataukitsidwa, zimene iye anakambirana ndi Petulo zinasonyeza kuti tchimo lake linakhululukidwa. Yesu sanakalipire kapena kudzudzula Petulo, koma anam’funsa kuti: “Kodi ine umandikonda?” Petulo anayankha kuti: “Inde Ambuye, mukudziwa inunso kuti ndimakukondani kwambiri.” Yesu anati: “Dyetsa ana ankhosa anga.” Yesu anam’funsanso funso lomweli, ndipo Petulo anayankha chimodzimodzi, mwina mwamphamvuko. Yesu anati: “Weta tiana tankhosa tanga.” Ndipo Yesu anam’funsanso funso lomweli kachitatu: “Kodi ine umandikonda kwambiri?” Apa, “Petulo anamva chisoni” ndipo anati: “Ambuye, inu mumadziwa zonse; mukudziwanso bwino lomwe kuti ndimakukondani kwambiri.” Yesu anati: “Dyetsa tiana tankhosa tanga.”—Yohane 21:15-17.
Kodi n’chifukwa chiyani Yesu anafunsa zimene anali kuzidziwa kale? Yesu amadziwa zimene zili m’mitima ya anthu, ndipo ankadziwa kuti Petulo amam’konda. (Maliko 2:8) Koma pofunsa mafunso amenewa, Yesu anam’patsa Petulo mwayi katatu wotsimikizira kuti amamukonda. Zimene Yesu anamuuza kuti: “Dyetsa ana ankhosa anga. . . . Weta tiana tankhosa tanga. . . . Dyetsa tiana tankhosa tanga,” zinamutsimikizira mtumwi wolapayu kuti anali kumudalirabe. N’chifukwa chake Yesu anam’patsa Petulo ntchito yosamalira otsatira ake onga nkhosa amene amawakonda kwambiri. (Yohane 10:14, 15) Petulo ayenera kuti mtima wake unakhala pansi poona kuti Yesu anali kum’dalirabe.
Apa n’zoonekeratu kuti Yesu anamukhululukira mtumwi wolapayu. Popeza kuti Yesu amasonyeza kwambiri makhalidwe ndi zochita za Atate wake, tinganenenso kuti Yehova anam’khululukira Petulo. (Yohane 5:19) Yehova ndi wokonzeka kukhululuka, ndipo iye ndi Mulungu wachifundo, “wokhululukira” ochimwa amene alapa. Kodi zimenezi si zolimbikitsa?