Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

N’chifukwa Chiyani Mulungu Anayanja Nowa? Kodi Ifenso Angatiyanje?

N’chifukwa Chiyani Mulungu Anayanja Nowa? Kodi Ifenso Angatiyanje?

N’chifukwa Chiyani Mulungu Anayanja Nowa? Kodi Ifenso Angatiyanje?

AMBIRIFE timakumbukira nthawi inayake imene tinalandira uthenga wofunika kwambiri. Timakumbukira kumene tinali nthawi imeneyo, zimene timachita panthawiyo komanso zimene tinachita titamva uthengawo. Mosakayikira, Nowa sanaiwale tsiku limene analandira uthenga wochokera kwa Yehova Mulungu, Mfumu yachilengedwe chonse. Umenewutu unali uthenga wofunika kwambiri. Yehova ananena kuti awononga “anthu onse.” Nowa anapatsidwa ntchito yomanga chingalawa chachikulu, kuti iye ndi banja lake komanso nyama za mitundu yonse zipulumukiremo.​—Genesis 6:9-21.

Kodi Nowa anatani atauzidwa zimenezi? Kodi anasangalala kapena anakana? Kodi anakamuuza bwanji mkazi wake ndi banja lake? Baibulo silimanena chilichonse pankhani imeneyi, koma zimene limatiuza n’zakuti: “Anachita Nowa, monga mwa zonse anam’lamulira iye Mulungu, momwemo anachita.”​—Genesis 6:22.

Nowa anachita zimene Mulungu anam’pempha kuti achite. Mfundo imeneyi ndi yofunika kwambiri popeza ikufotokoza chifukwa chake Nowa anayanjidwa ndi Mulungu. (Genesis 6:8) Kodi n’chiyaninso chinapangitsa kuti Mulungu ayanje Nowa? Yankho la funso limeneli ndi lofunika kwambiri, chifukwa tiyenera kukhala ngati Nowa kuti tidzapulumuke Mulungu akamadzawononga oipa. Choyamba, tiyeni tione kaye mmene zinthu zinalili m’nthawi ya Nowa chigumula chisanachitike.

Ziwanda Zinabwera Padziko Lapansi

Nowa anabadwa patatha zaka 1,000 munthu woyamba atalengedwa. Komabe, si zoona kuti anthu panthawiyo ankakhala ku phanga, anali aubweyaubweya, opusa komanso oyenda mofooka ndi zibonga m’manja, monga mmene anthu ambiri amaganizira. Anthu ankapanga zitsulo ndipo Nowa ayenera kuti anagwiritsa ntchito zitsulo zimenezi pokhoma chingalawa. Analinso ndi zida zoimbira. Iwo ankakwatira, kukhala ndi ana, kulima ndiponso kuweta ziweto. Ankagula ndi kugulitsa malonda. Choncho tingati moyo wawo unali wofanana ndi wa masiku ano.​—Genesis 4:20-22; Luka 17:26-28.

Komabe, zinthu zina zinali zosiyana ndi za masiku ano. Panthawiyo anthu ankakhala ndi moyo nthawi yaitali. Sizinali zachilendo munthu kukhala zaka zoposa 800. Mwachitsanzo, Nowa anafa ali ndi zaka 950; Adamu ali ndi zaka 930; ndipo Metusela, agogo ake a Nowa anafa ali ndi zaka 969. *​—Genesis 5:5, 27; 9:29.

Kusiyana kwina kuli pa lemba la Genesis 6:1, 2, limene limati: “Ndipo panali pamene anthu anayamba kuchuluka padziko, ndi ana aakazi anawabadwira iwo, kuti ana aamuna a Mulungu anayang’ana ana aakazi a anthu, kuti iwo anali okongola; ndipo anadzitengera okha akazi onse amene anawasankha.” “Ana aamuna a Mulungu” amenewa, anali angelo amene anasintha n’kukhala anthu omwe anakubwera padziko lapansi. Si Mulungu amene anatumiza angelowa komanso sanabwere n’cholinga chodzathandiza anthu. Koma, “anasiya malo awo okhala” kumwamba kuti adzachite zachiwerewere ndi akazi okongola padziko lapansi. Chifukwa cha zimene anachitazi, angelowa anakhala ziwanda.​—Yuda 6.

Angelo opanduka amenewa anali ndi nzeru ndiponso mphamvu kuposa anthu ndipo ndi amene ankapangitsa kuti zinthu ziipe padziko. N’zoonekeratu kuti angelowa ankalamulira anthu kuchita zoipa. Sankachita zimenezi mobisa monga mmene amachitira munthu wachifwamba. Koma anapandukira Mulungu moonetsera.

Ana aamuna a Mulungu amenewa anagonana ndi akazi ndipo anabereka nawo ana amphamvu kwambiri. M’Chiheberi anawo ankatchedwa kuti “Anefili.” Baibulo limatiuza kuti: “Pa dziko lapansi panali anthu akulukulu [Anefili] masiku omwewo ndiponso pambuyo pake, ana aamuna a Mulungu atalowa kwa ana aakazi a anthu, ndipo anabalira iwo ana, amenewo ndiwo anthu amphamvu akalekale, anthu omveka.” (Genesis 6:4) Anefili amenewa ankaopedwa kwambiri. Mawu akuti “Anefili” amatanthauza anthu ogwetsa anzawo. N’kutheka kuti kuphana ndiponso zinthu zambiri zachiwawa zosimbidwa m’nthano zakale zinachokera pa nkhani ya Anefili.

Olungama Anavutika mu Mtima

Baibulo limafotokoza za anthu a m’nthawi imeneyi kuti anali a makhalidwe oipa kwambiri. Limati: “Kuipa kwa anthu kunali kwakukulu pa dziko lapansi, ndiponso kuti ndingaliro zonse za maganizo a mitima yawo zinali zoipabe zokhazokha. . . . Dziko lapansi ndipo linadzala ndi chiwawa. . . . Anthu onse anavunditsa njira yawo pa dziko lapansi.”​—Genesis 6:5, 11, 12.

Umu ndi mmene anthu analili m’nthawi ya Nowa. Koma “Nowa anali munthu wolungama” amene “anayendabe ndi Mulungu.” (Genesis 6:9) N’zovuta kwa munthu wolungama kukhala ndi anthu oipa. Nowa ayenera kuti anavutika kwambiri mumtima ndi zimene anthu ankanena ndiponso kuchita. N’kutheka kuti Nowa ankamva mmene Loti, amene anakhalako chigumula chitatha, ankamvera. Iye ankakhala ndi anthu oipa a ku Sodomu ndipo “anavutika mtima kwambiri ndi anthu ophwanya malamulo, mwa kulowerera kwawo khalidwe lotayirira,” ndipo ‘anazunzika m’moyo wake wolungama, pakuona ndi kumva zochita zawo za kusamvera malamulo.’ (2 Petulo 2:7, 8) Umu ndi mmenenso Nowa anamvera.

Kodi inunso mumavutika mumtima chifukwa cha nkhani zoopsa zimene mumamva kapena chifukwa cha makhalidwe oipa a anthu amene mumakhala nawo pafupi? Ngati ndi choncho, mungamvetse mmene Nowa anamvera. Ayenera kuti anavutika kwambiri kukhala ndi anthu oipa zaka 600, chifukwatu Nowa anali ndi zaka zimenezi pamene chigumula chimayamba. Iye ankafunitsitsa zinthu zoipa zitatha.​—Genesis 7:6.

Nowa Anali Wolimba Mtima

Nowa “anali munthu wolungama ndi wangwiro m’mibadwo yake.” (Genesis 6:9) Onani kuti Baibulo likuti, anali wolungama m’mibadwo yake, osati kuti anthu a m’mibadwo yake amamuona kuti anali wolungama. Tinganene kuti anali wolungama kwa Mulungu, osati pamaso pa anthu anzake. Iye samagwirizana ndi zimene anthu ambiri amachita, ndipo samachita nawo zinthu zoipa. Taganizirani mmene anthu anamuonera atayamba kukhoma chingalawa. Ayenera kuti ankamuseka ndi kumunyoza. Anthu ankangomuona ngati akuchita zamasewera.

Komanso Nowa anali munthu wopemphera ndipo amauza anthu ena zimene ankakhulupirira. Baibulo limati anali “mlaliki wa chilungamo.” (2 Petulo 2:5) Mosakayikira, Nowa ankadziwa kuti anthu amutsutsa. Enoke, yemwe anali agogo a bambo a Nowa, anali olungama ndipo ananeneratu kuti Mulungu adzawononga anthu oipa. Izi zinachititsa kuti Enoke azunzidwe ngakhale kuti Mulungu sanalole kuti aphedwe. (Genesis 5:18, 21-24; Aheberi 11:5; 12:1; Yuda 14, 15) Popeza kuti Satana, ziwanda, Anefili ndiponso anthu ambiri anamutsutsa komanso sanamvere uthenga wake, Nowa anafunika kulimba mtima komanso kukhulupirira kuti Yehova amuteteza.

Anthu otumikira Mulungu amatsutsidwa ndi anthu amene satumikira Mulungu. Ngakhale Yesu Khristu ndiponso amene ankamutsatira ankadedwa. (Mateyo 10:22; Yohane 15:18) Nowa analimba mtima kutumikira Mulungu, ngakhale kuti anthu ambiri sankatero. Iye anadziwa kuti kuyanjidwa ndi Mulungu n’kofunika kwambiri kuposa kuyanjidwa ndi anthu omutsutsawo. N’chifukwa chake Nowa anayanjidwa ndi Mulungu.

Nowa Anamvera Chenjezo

Monga taonera, Nowa ankalalikira molimba mtima. Kodi anthu anamvera uthenga wakewo? Baibulo limati chigumula chisanafike, anthu “anali kudya ndi kumwa, amuna anali kukwatira ndipo akazi anali kukwatiwa, kufikira tsiku limene Nowa analowa mu chombo; ndipo sanazindikire kanthu mpaka chigumula chinafika ndi kuwaseseratu onsewo.” Anthu amenewatu sanamvere chenjezo.​—Mateyo 24:38, 39.

Yesu ananenanso kuti zimenezi zidzachitika m’masiku athu ano. Kwa zaka zoposa 100, Mboni za Yehova zakhala zikuchenjeza anthu kuti Yehova adzasintha zinthu kuti akwaniritse lonjezo lake lokhazikitsa dziko lapansi lachilungamo. Ngakhale kuti anthu mamiliyoni angapo amvera chenjezoli, anthu mabiliyoni ambiri sakuzindikira kanthu. “Mwakufuna kwawo” amakana kuti chigumula sichinachitike komanso safuna kuphunzirapo kanthu.​—2 Petulo 3:5, 13.

Koma Nowa anamvera chenjezo. Anakhulupirira zimene Yehova Mulungu anamuuza. Kumvera kunamupulumutsa. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Mwa chikhulupiriro, Nowa atachenjezedwa ndi Mulungu za zinthu zimene zinali zisanaoneke, anasonyeza kuopa Mulungu ndipo anamanga chombo kuti banja lake lipulumukiremo.”​—Aheberi 11:7.

Chitsanzo Chofunika Kutengera

Chingalawa chimene Nowa anakhoma chinali chachikulu kwambiri. Chinali chachikulu kuposa bwalo la mpira ndipo chinali chachitali ngati nyumba zitatu zosanjikizana. Chingalawachi sichinali sitima komabe chimafunika kuti chiziyandama. Ngakhale zinali choncho, chinafunika kupangidwabe mwaluso zedi. Chinafunikanso kupakidwa phula mkati ndi kunja komwe. Nowa ayenera kuti anatha zaka zoposa 50 kuti amalize kukhoma chingalawacho.​—Genesis 6:14-16.

Nowa anafunikanso kusunga chakudya cha banja lake komanso cha nyama, chokwanira chaka chimodzi. Chigumula chisanafike, anafunikanso kusonkhanitsa nyama n’kudzilowetsa m’chingalawacho. Baibulo limati: “Anachita Nowa monga mwa zonse anam’lamulira iye Yehova.” Nowa ayenera kuti anasangalala kwambiri atamaliza ntchitoyo, Yehova n’kutseka chitseko cha chingalawacho.​—Genesis 6:19-21; 7:5, 16.

Kenako chigumula chinayamba. Kunagwa mvula masiku 40, masana ndi usiku womwe. Onse anafunika kuti akhale m’chingalawamo kwa chaka chimodzi mpaka madzi atauma. (Genesis 7:11, 12; 8:13-16) Anthu onse oipa anatheratu. Koma Nowa ndi banja lake lokha ndi amene anapulumuka.

Baibulo limanena kuti chigumula cha padziko lonse cha m’nthawi ya Nowa ndi “chitsanzo cha zinthu . . . [za] m’tsogolo.” Motani? Baibulo limati: “Miyamba imene ilipo tsopano limodzi ndi dziko lapansi, azisungira moto m’tsiku la chiweruzo ndi chiwonongeko cha anthu osaopa Mulungu.” Komabe, monga zinalili m’masiku a Nowa, anthu ena adzapulumuka. Musakayikire kuti “Yehova amadziwa kupulumutsa anthu odzipereka kwa iye m’mayesero.”​—2 Petulo 2:5, 6, 9; 3:7.

Nowa anali munthu woopa Mulungu ndi wolungama pakati pa anthu oipa. Iye anamvera chilichonse chimene Mulungu anamuuza. Iye analimba mtima kuchita zinthu zabwino ngakhale ankadziwa kuti zipangitsa kuti anthu osatumikira Mulungu azidana naye. Tikatengera chitsanzo cha Nowa, ifenso Mulungu adzatiyanja ndipo adzatipulumutsa kuti tidzakhale m’dziko latsopano limene latsala pang’ono kubwera.​—Salmo 37:9, 10.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 7 Onani nkhani yakuti “Kodi Anakhaladi Ndi Moyo Wautali Choncho?” mu Galamukani! ya July 2007, tsamba 30.

[Mawu Otsindika patsamba 5]

N’kutheka kuti zinthu zambiri zachiwawa zosimbidwa m’nthano zakale zinachokera pa nkhani ya Anefili

[Chithunzi patsamba 7]

Mulungu adzatiyanja tikatengera chikhulupiriro cha Nowa

[Mawu a Chithunzi patsamba 5]

Alinari/​Art Resource, NY