Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Ndikawerenga Bukuli Pootha Moto Usiku Uno”

“Ndikawerenga Bukuli Pootha Moto Usiku Uno”

Kalata Yochokera ku Australia

“Ndikawerenga Bukuli Pootha Moto Usiku Uno”

MIDZI ya ku Australia imandikumbutsa za chipululu chouma ndi chotentha chomwe chili ndi malo ambiri opanda anthu. Komabe midzi ya kutali ndi nyanja imeneyi ili ndi anthu pafupifupi 180,000, omwe ndi 1 peresenti ya anthu onse a ku Australia.

Ndili mwana, makolo anga omwe ndi a Mboni za Yehova, ananditenga kukalalikira ku midzi imeneyi. Ndinachita chidwi kwambiri ndi dera limeneli chifukwa ndi lalikulu kwambiri komanso la mitundamitunda. Ndinasangalalanso kwambiri ndi anthu ake athanzi komanso ochezeka. Nditakhala ndi banja, ndinafunanso kuti ndipite kudera limeneli ndi mkazi wanga limodzi ndi ana anga awiri, wina wa zaka 10 ndipo wina wa zaka 12.

Kukonzekera Ulendo

Tisananyamuke ulendowu, tinawerengera kaye mtengo wake. Kodi tingakwanitse ulendo wautali bwanji? Kodi tikakhalako nthawi yaitali bwanji? Banja lina ndiponso atumiki awiri anthawi zonse a mu mpingo wathu anafunanso kuti apite nawo paulendowu. Tinagwirizana nthawi yopita kuderali kuti idzakhale chapakati pachaka chifukwa ana amakhala atatsekera sukulu. Tinalembera kalata ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ya m’dzikoli, kupempha gawo loti tikalalikireko. Anatiuza kuti tikhoza kukalalikira ku midzi yakufupi ndi ku Goondiwindi, yomwe ndi tauni yaing’ono imene ili pamtunda wa makilomita 400 cha kumadzulo kwa mzinda umene timakhala wa Brisbane.

Tinamva kuti ku Goondiwindi kunali mpingo waung’ono wa Mboni za Yehova. Izi zinatisangalatsa zedi chifukwa kukumana ndi abale athu achikhristu kunali chinthu chofunika kwambiri paulendowu. Tinalembera kalata mpingo umenewu kuwauza za ulendo wathu. Anatiyankha mosangalala ndipo tinadziwa kuti akutiyembekezera mwachidwi.

Tisananyamuke, tinakumana kaye kuti tikambirane mmene tikalalikirire uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu kumalo akumidziwa. Tinakambirana kuti tizikalemekeza anthu Achiborigine ndi chikhalidwe chawo. Anthu ena kumeneko amakhala ndi malo awoawo ndipo kupita kumalo amenewa osapempha amakutenga ngati ndi kupanda ulemu.

Tinanyamuka Ulendo Wathu

Tsiku la ulendo litafika, tinanyamuka pa magalimoto awiri titatenga katundu kulowera ku Goondiwindi. Tinadutsa m’minda ya mbewu komanso m’malo a udzu amene anali ndi mitengo ya bulugamu patalipatali. Ngakhale kuti inali nthawi yozizira, dzuwa limawala ndithu chifukwa kunalibe mitambo. Tinafika ku Goondiwindi patapita maola angapo ndipo tinakagona kumalo enaake a alendo.

Tsiku lotsatira linali Lamlungu, kunja kunacha bwino ndipo nyengo yake inali yabwino kulalikira. Kuno m’nyengo yotentha kumatentha kwambiri mpaka madigiri 40. Malo oyamba kulalikira anali pamtunda wa makilomita 30 ndipo anali a anthu a Chiborigine. Choyamba tinapita kwa mayi wina wokalamba yemwe anali mfumu ya derali, dzina lawo a Jenny. Titawalalikira, anamvetsera ndipo analandira mosangalala buku lakuti Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso. * Kenako anatilola kuti titha kulalikira kwa anthu a m’derali.

Ana akumeneko ankathamanga ndi kumauza anthu za kubwera kwathu. Munthu aliyense amene tinamulalikira, anamvetsera mosangalala uthenga wathu ndipo analandira magazini ndi mabuku athu. Mabuku ndi magazini athu sanachedwe kutha ndipo tinabwerera ku tauni kuja kuti tikapite ku misonkhano ya mpingo. Tisananyamuke, tinalonjeza kuti tidzabweranso kudzalalikira anthu amene sitinawafikire.

Tsiku limeneli masana ake, tinacheza kwambiri ndi anthu amene tinapezana nawo ku Nyumba ya Ufumu. Panthawi yochepa chabe tinapeza anzathu atsopano. Mboni za Yehova 25 za kumidzi imeneyi zakhala zikulalikira uthenga wa Ufumu mokhulupirika kwa anthu 11,000 amene amakhala motalikiranatalikirana m’dera lalikulu kwambiri limeneli, lokwana masikweya kilomita 30,000. Wa Mboni wina anatiuza moyamikira kuti: “Zikomo kwambiri chifukwa chobwera kudzatithandiza.” Misonkhano itatha, tonse tinapita kokadya chakudya. Tisanakagone tsiku limeneli, tinapatsira chakudya kanyama kenakake kooneka ngati Kangaroo kamene kamayendayenda pafupi ndi malo athu ogona.

“Pootha Moto Usiku Uno”

Masiku awiri otsatira, tinapita ku midzi yomwe inali motalikiranatalikirana cha kumalire kwa mzinda wa Queensland ndi New South Wales. Malo ambiri m’derali ali ndi mitengo yambiri ya bulugamu ndi udzu, komwe amadyetserako ng’ombe ndi nkhosa. Tili m’njira tinaona nyama za Kangaroo zambiri ndipo zimati zikationa zimanjenjemeretsa makutu awo. Tinaonanso mbalame ina yokhala ngati nthiwatiwa ikuyenda mwamatama mumsewu.

Lachiwiri masana tinakumana ndi gulu la ng’ombe zikuyenda pang’onopang’ono mumsewu. Abusa amabwera ndi ng’ombe m’derali makamaka panthawi ya chilala. Pasanapite nthawi yaitali, tinakumana ndi mbusa wina wokalamba atakwera hatchi. Ndinaimika galimoto ndipo ndinam’patsa moni. Atandiyankha moniyo, anaima ndi galu wake ndipo tinayamba kucheza.

Titakambirana kwa nthawi ndithu za chilala cha m’derali, ndinamuuza uthenga wa m’Baibulo. Mbusayo anati: “Sindinamvepo uthenga wa m’Baibulo.” Iye amaona kuti atsogoleri achipembedzo ndiwo akuchititsa kuti anthu akhale ndi makhalidwe oipa. Komabe, iye anali kulemekeza Baibulo. Titakambirana Malemba, ndinam’patsa buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? * Analandira ndi kuliika m’thumba, ndipo anati: “Ndikawerenga bukuli pootha moto usiku uno ngati likunena zimene Baibulo limaphunzitsa.”

Ulendo Wobwerera Kunyumba

Usiku womwewo tinafotokozera abale ndi alongo athu auzimu ku Nyumba ya Ufumu za momwe tinayendera. Anatilonjeza kuti adzapita kwa anthu onse amene anatiuza kuti tipitenso. Misonkhano itatha, zinali zovuta kutsanzikana, chifukwa panthawiyi tinali titapanga ubale. Tonse tinasangalala ndi kulimbikitsana mwauzimu.​—Aroma 1:12.

Tsiku lotsatira tinauyamba ulendo wobwerera kwathu. Tikamakumbukira ulendo wathuwu, timaona kuti Yehova anadalitsa kwambiri khama lathu. Tinatsitsimulidwa mwauzimu. Titafika kunyumba, ndinafunsa ana anga kuti: “Kodi tidzapite kuti tikadzakhala ndi tchuthi china? Kokaona mapiri kapena kuti?” Anayankha kuti: “Tidzakalalikirenso kumidzi yomwe ija.” Mkazi wanganso anavomereza kuti: “Tidzapite komwe kuja, chifukwa tinali ndi tchuthi chosangalatsa!”

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 11 Lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

^ ndime 17 Lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.