Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi N’kulakwa Kugwiritsa Ntchito Dzina la Mulungu?

Kodi N’kulakwa Kugwiritsa Ntchito Dzina la Mulungu?

Kodi N’kulakwa Kugwiritsa Ntchito Dzina la Mulungu?

M’MALEMBA oyambirira a Chiheberi, omwe nthawi zambiri amatchedwa “Chipangano Chakale,” dzina la Mulungu limapezekamo maulendo pafupifupi 7,000. Dzinali limalembedwa motere יהוה (limawerengedwa kuyambira kumanja kupita kumanzere). Zimenezi zikutanthauza kuti dzinali limaimiridwa ndi zilembo zinayi za Chiheberi zomwe ndi Yohdh, He, Waw ndi He. M’zinenero zambiri, zilembozi zikamasuliridwa motsatira katchulidwe kake zimalembedwa motere YHWH.

Kale kwambiri, Ayuda anayamba kuganiza kuti kugwiritsa ntchito dzina la Mulungu n’kulakwa. Chifukwa cha maganizo amenewa, iwo sankafuna kulitchula ndipo anayamba kulichotsa m’mabuku awo ndi kuikamo mayina ena. Komabe, anthu ambiri omasulira Mabaibulo alemba dzinali kuti “Yahweh” kapena “Yehova.” Limodzi mwa Mabaibulo amenewa ndi Baibulo la Akatolika la Jerusalem Bible. Malinga ndi Baibulo limeneli, Mose atafunsa Mulungu mmene akayankhire Aisiraeli ngati atakam’funsa za amene wam’tuma, Mulungu anayankha kuti: “Ukauze ana a Isiraeli kuti: ‘Yahweh, Mulungu wa makolo anu, Mulungu wa Abulahamu, Mulungu wa Isake, ndi Mulungu wa Yakobo wandituma kwa inu.’ Limeneli ndi dzina langa nthawi zonse; ichi ndi chikumbutso changa ku mibadwo yonse.”​—Eksodo 3:15.

Yesu akupemphera, anafotokoza mmene iye anagwiritsira dzina la Mulungu. Iye anati: “Dzina lanu ndalidziwikitsa kwa iwo ndipo ndipitiriza kulidziwikitsa.” Komanso m’pemphero limene anthu ambiri amati ndi la Atate Wathu, Yesu anati: “Atate wathu wakumwamba, dzina lanu likhale loyera.”​—Yohane 17:26; Mateyo 6:9, JB.

Ndiyetu n’zodabwitsa kuti m’buku lake laposachedwapa lofotokoza za moyo wa Yesu, Papa Benedikito wa nambala 16 ananena izi pankhani yogwiritsa ntchito dzina la Mulungu: “Aisiraeli . . . sanalakwitse chilichonse pokana kutchula dzina limene Mulungu anadzipatsali, lakuti YHWH, chifukwa kutero kukanachititsa kuti lingofanana ndi mayina a milungu ya akunja. Choncho Mabaibulo amene akumasuliridwa masiku ano akulakwitsa kugwiritsa ntchito dzinali mosasiyana ndi dzina lina lililonse lakale, pamene Aisiraeli ankaliona kuti n’losayenera n’komwe kulitchula.”​—Jesus of Nazareth.

Kodi inuyo mukuganiza bwanji? Kodi kugwiritsa ntchito dzina la Mulungu n’kulakwa? Ngati Yehova mwiniwakeyo anati: “Limeneli ndi dzina langa nthawi zonse; ichi ndi chikumbutso changa ku mibadwo yonse,” ndiye kodi m’poyenera kuti munthu atsutse zimenezi?

[Chithunzi patsamba 30]

Yesu anagwiritsa ntchito dzina la Mulungu popemphera