Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Zimene Mukufuna Kuchita Zikugwirizana ndi Cholinga cha Mulungu?

Kodi Zimene Mukufuna Kuchita Zikugwirizana ndi Cholinga cha Mulungu?

Kodi Zimene Mukufuna Kuchita Zikugwirizana ndi Cholinga cha Mulungu?

M’NKHALANGO zakumadzulo kwa North America mumapezeka mtundu winawake wa mbalame zimene zimakonda kuimba. Pokonzekera nyengo yachisanu, mbalame iliyonse ya mtunduwu imasonkhanitsa njere pafupifupi 33,000 chaka chilichonse, n’kuzisunga pozikwirira m’malo osiyanasiyana okwana 2,500. Kunena zoona, mbalame zimenezi ‘n’zochenjeradi,’ tikaganizira mmene zimasungira chakudya cham’tsogolo.​—Miyambo 30:24, Malembo Oyera.

Komatu anthu ali ndi nzeru zoposa pamenepa. Pazinthu zonse zimene Yehova analenga padziko lapansi pano, anthu ali ndi luso lotha kuphunzira zinthu kuchokera pa zochitika zakale ndiponso kugwiritsa ntchito zinthuzo pokonzekera zoti adzachite m’tsogolo. Mfumu yanzeru Solomo inati: “Muli zolingalira zambiri m’mtima mwa munthu.”​—Miyambo 19:21.

Ngakhale zili choncho, nthawi zambiri anthu amakonzekera zimene akufuna kuchita malinga ndi zimene akuganiza kuti zidzachitika m’tsogolo. Mwachitsanzo, munthu amakonzekera zinthu zodzachita mawa poganizira kuti dzuwa lidzatuluka ndiponso kuti adzakhala ndi moyo. Zoti dzuwa lidzatuluka n’zotsimikizika; koma zoti adzakhala ndi moyo n’zosatsimikizika. N’chifukwa chake Yakobe amene analemba nawo Baibulo anati: “Simudziwa kuti moyo wanu udzakhala wotani mawa.”​—Yakobe 4:13, 14.

Yehova Mulungu ndi wosiyana ndi anthu chifukwa iye amadziwa zonse. Palibe chilichonse chimene chingalepheretse cholinga chake. Iye anati: “Uphungu wanga udzakhala, ndipo ndidzachita zofuna zanga zonse.” (Yesaya 46:10) Komano, kodi chimachitika n’chiyani ngati zimene munthu akufuna kuchita zasemphana ndi cholinga cha Mulungu?

Zofuna za Anthu Zikasemphana ndi Cholinga cha Mulungu

Zaka pafupifupi 4,000 zapitazo, anthu anakonza zomanga Nsanja ya Babele n’cholinga choti asafalikire ku madera ena a dziko lapansi. Iwo anati: “Tiyeni, timange mudzi ndi nsanja, pamutu pake pafikire kumwamba; ndipo tidzipangire ife tokha dzina kuti tisabalalike pa dziko lonse lapansi.”​—Genesis 11:4.

Komatu zimenezi zinali zosiyana kwambiri ndi cholinga cha Mulungu chokhudza dziko lapansili. Iye anali atalamula Nowa ndi ana ake kuti: “Mubalane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi.” (Genesis 9:1) Ndiye kodi Mulungu anatani ndi anthu opanduka a ku Babele? Iye anasokoneza chinenero chawo moti sanathenso kumvana. Ndiyeno zotsatira zake zinali zotani? Baibulo limati: “Yehova anabalalitsa iwo pa dziko lonse lapansi.” (Genesis 11:5-8) Zimene zinachitikazi zinapatsa anthu omwe ankamanga nsanjawo phunziro lofunika kwambiri, lakuti: Zolinga za anthu zikasemphana ndi za Mulungu, ‘uphungu wa Yehova ndiwo umaima.’ (Miyambo 19:21) Kodi inuyo mumalola kuti zochitika zakale ngati zimenezi zikuthandizeni pa zimene mukufuna kuchita pamoyo wanu?

Munthu Wachuma Koma Wopanda Nzeru

N’kutheka kuti simungafune kumanga nsanja, koma anthu ambiri masiku ano amafuna kusunga ndalama zambiri kubanki ndiponso kudziunjikira chuma n’cholinga choti asadzavutike atapuma pantchito. Mwachibadwa, munthu aliyense amafuna kudyerera thukuta lake. Ndipo Solomo analemba kuti: “Munthu yense adye namwe naone zabwino m’ntchito zake zonse; ndiwo mtulo [“mphatso,” Malembo Oyera] wa Mulungu.”​—Mlaliki 3:13.

Yehova amaona mmene tikugwiritsira ntchito mphatso imeneyi. Zaka pafupifupi 2,000 zapitazo, Yesu anafotokozera ophunzira ake fanizo limene linatsindika mfundo imeneyi. Iye anati: “Munda wa munthu wina wachuma unabereka bwino. Choncho anayamba kudzifunsa nati, ‘Ndichite chiyani tsopano, popeza ndilibe mosungira zokolola zangazi?’ Ndiyeno anati, ‘Ndidzachita izi: Ndidzapasula nkhokwe zanga ndi kumanga zikuluzikulu, ndipo tirigu wanga yense ndi zinthu zanga zonse zabwino ndidzazitutira mmenemo; ndipo ndidzauza moyo wanga kuti: “Moyo wangawe, uli ndi zinthu zambiri zabwino mwakuti zisungika kwa zaka zambiri; ungoti phee tsopano, udye, umwe, usangalale.”’” (Luka 12:16-19) Zimene munthu wachumayu ankafuna kuchita zikuoneka kuti zinali zabwino, sichoncho kodi? Mofanana ndi mbalame zimene tatchula koyambirira zija, zikuoneka kuti munthuyu ankakonzekera kuti asadzavutike m’tsogolo.

Komabe, maganizo a munthu wachumayu anali olakwika. Yesu anapitiriza motere: “Koma Mulungu anati kwa iye, ‘Wopanda nzeru iwe, usiku womwe uno moyo wako adzaufuna. Nanga chuma chimene wakundikachi chidzakhala cha ndani?’” (Luka 12:20) Ponena zimenezi, kodi Yesu anali kutsutsa mfundo ya Solomo yakuti munthu ayenera kugwira ntchito ndi kudyerera phindu lake limene ndi mphatso yochokera kwa Mulungu? Ayi sichoncho. Nangano Yesu ankatanthauza chiyani? Iye anati: “Umu ndi mmene zimakhalira kwa munthu amene wadziunjikira yekha chuma, koma amene sali wolemera kwa Mulungu.”​—Luka 12:21.

Yesu ankaphunzitsa anthu omwe anali kumumvetsera kuti Yehova amafuna kuti tiziganizira zolinga zake tikamafuna kuchita zinthu. Munthu wachumayu akanakhala wolemera kwa Mulungu mwa kuyesetsa kukhala wodzipereka kwambiri kwa Iye, kukhala wanzeru ndiponso kukhala ndi chikondi. Zimene munthuyu ananena zikusonyeza kuti analibe chidwi ndi zinthu zimenezi. Komanso zikusonyeza kuti sanafune kusiyako zokolola zake kuti osauka adzakunkhe kapena kupereka zokolola zake zina nsembe kwa Yehova. Munthu wachumayu sankaganizira n’komwe zochita zinthu mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu pamoyo wake. Maganizo ake onse anali pa kupeza ndi kudyerera zinthu zake basi.

Kodi mumaona kuti zofuna za anthu ambiri masiku ano n’zofanana ndi za munthu wachuma amene Yesu anafotokozayu? Kaya ndife olemera kapena osauka, n’zosavuta kukodwa mu msampha wokonda chuma, ndipo chifukwa chodera nkhawa kwambiri zinthu zofunika pamoyo, tingathe kufika posiya kuchita zinthu zauzimu. Kodi tingapewe motani msampha umenewu?

Kufuna Moyo Womwe Ambiri Amati ndi Wabwino

Mosiyana ndi munthu wachuma wotchulidwa m’fanizo la Yesu lija, mwina inuyo muli ndi mavuto a zachuma. Ngati ndinu wokwatira, mosakayikira mumafuna kupezera banja lanu zinthu zofunika pamoyo ndiponso kuti ana anu apite ku sukulu zapamwamba ngati n’zotheka. Ngati simuli pa banja, mwina mumafuna kupeza ntchito komanso kukhalitsa pa ntchitopo n’cholinga choti musamavutitse anthu ena. Kufuna kuchita zinthu ngati zimenezi sikulakwa.​—2 Atesalonika 3:10-12; 1 Timoteyo 5:8.

Ngakhale zili choncho, n’zotheka kuti kugwira ntchito, kudya ndi kumwa, zomwe ndi moyo umene anthu ambiri amati ndiye wabwino, zingachititse munthu zinthu zosemphana ndi zimene Mulungu amafuna. Kodi zingatheke bwanji zimenezo? Yesu anati: “Monga analili masiku a Nowa, ndi mmenenso kukhalapo kwa Mwana wa munthu kudzakhalire. Pakuti m’masiku amenewo chigumula chisanafike, anthu anali kudya ndi kumwa, amuna anali kukwatira ndipo akazi anali kukwatiwa, kufikira tsiku limene Nowa analowa mu chombo; ndipo sanazindikire kanthu mpaka chigumula chinafika ndi kuwaseseratu onsewo, zidzateronso ndi kukhalapo kwa Mwana wa munthu.”​—Mateyo 24:37-39.

Chigumula chisanachitike, anthu ambiri ankakhala moyo umene ankaona kuti ndi wosangalatsa. Koma vuto lawo linali lakuti “sanazindikire kanthu” ponena za cholinga cha Mulungu chowononga anthu onse oipa ndi Chigumula. Iwo ayenera kuti ankaganiza kuti Nowa akukhala moyo wosasangalala. Koma Chigumula chitabwera, Nowa ndi banja lake ndiwo anaoneka kuti anali anzeru kwambiri.

Zimene zikuchitika masiku ano zikusonyeza kuti tikukhala m’masiku otsiriza. (Mateyo 24:3-12; 2 Timoteyo 3:1-5) Posachedwapa, Ufumu wa Mulungu “udzaphwanya ndi kutha” dongosolo la zinthu limene lilipoli. (Danieli 2:44) Mu ulamuliro wa Ufumu umenewo, dziko lapansili lidzasintha n’kukhala paradaiso. Ufumu umenewu udzachotsa matenda ndi imfa. (Yesaya 33:24; Chivumbulutso 21:3-5) Sikudzakhalanso njala ndipo zamoyo zonse zimene Mulungu analenga padziko lapansi pano zidzakhala mwamtendere.​—Salmo 72:16; Yesaya 11:6-9.

Komabe Yehova wakonza zoti asanachite zimenezi, uthenga wabwino wa Ufumu wake ‘ulalikidwe padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti ukakhale umboni ku mitundu yonse.’ (Mateyo 24:14) Mogwirizana ndi cholinga cha Mulungu chimenechi, Mboni za Yehova pafupifupi 7 miliyoni zikulalikira uthenga wabwino m’mayiko 236, m’zinenero zoposa 400.

Anthu ena amaona kuti zimene Mboni za Yehova zikuchita pamoyo wawo n’zachilendo, ndipo mwinanso zoseketsa. (2 Petulo 3:3, 4) Mofanana ndi anthu amene analipo Chigumula chisanachitike, anthu ambiri masiku ano ndi otanganidwa ndi zochita zawo zatsiku ndi tsiku. Munthu wina aliyense amene sakutengera zochita zimene iwo amati ndiye moyo wabwino, angathe kumuona ngati ndi wosaganiza bwino. Koma kwa anthu amene amakhulupirira zimene Mulungu walonjeza, moyo wabwino ndiwo kutumikira Mulungu basi.

Motero, kaya ndinu wolemera kapena ayi, ndi bwino kuti nthawi ndi nthawi muziunika zimene mukufuna kudzachita m’tsogolo. Mukamachita zimenezi, dzifunseni kuti, ‘Kodi zimene ndikufuna kuchita zikugwirizana ndi cholinga cha Mulungu?’

[Chithunzi patsamba 11]

Zimene anthu akufuna kuchita zikasemphana ndi cholinga cha Mulungu, zofuna za Yehova sizilephereka

[Chithunzi patsamba 12]

Munthu wachuma wa m’fanizo la Yesu sanaganizire za cholinga cha Mulungu pamene ankaganiza zoti achite