Mulungu Wandichitira Chifundo Kwambiri
Mulungu Wandichitira Chifundo Kwambiri
Yosimbidwa ndi Bolfenk Moc̆nik
“Tsopano limba mtima.” Mayi anga anandiuza mawu amenewa atandikumbatira. Kenako asilikali anabwera n’kutilekanitsa kuti ndikalowe m’khoti. Pambuyo pondizenga mlandu, anagamula kuti ndikakhale m’ndende zaka zisanu. N’kutheka kuti anthu ena akanakhumudwa kulandira chigamulo choterechi. Koma kunena zoona, ine sindinadandaule nazo m’pang’ono pomwe. Tandilolani ndikufotokozereni.
ZIMENEZI zinachitika mu 1952 m’dziko la Slovenia. * Koma zimene ndifotokoze m’nkhaniyi, kwenikweni zinayamba mu 1930. Panthawi imeneyi n’kuti Ophunzira Baibulo, dzina limene Mboni za Yehova zinkadziwika nalo, atakonza kuti kwa nthawi yoyamba m’dziko lathu, anthu ambiri abatizidwe pa tsiku limodzi. Mayi ndi bambo anga, omwe mayina awo anali a Berta ndi a Franz, anali m’gulu la anthu omwe anabatizidwa panthawiyo. Ine n’kuti ndili ndi zaka 6, ndipo mlongo wanga Majda ali ndi zaka zinayi. Tinkakhala mu mzinda wa Maribor ndipo zinthu zosiyanasiyana zauzimu mumzindawu zinkachitikira ku nyumba yathu.
Adolf Hitler anayamba kulamulira dziko la Germany mu 1933 ndipo anayamba kuzunza kwambiri Mboni. Anthu ambiri a Mboni a ku Germany anasamukira ku Yugoslavia kuti akathandize pantchito yolalikira. Makolo anga ankakonda kulandira ndi kuchereza anthu okhulupirika ngati amenewa kunyumba kwathu. Mmodzi mwa alendo amene ndimawakumbukira bwino kwambiri ndi Martin Poetzinger, yemwe anadzakhala zaka 9 m’ndende za a Nazi. Kenako iye anadzakhala m’Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova kuyambira mu 1977 mpaka pamene anamwalira mu 1988.
M’bale Martin akabwera kudzatichezera, ankagona pabedi langa ndipo ine ndi mchemwali wanga tinkagona limodzi ndi makolo athu. M’baleyu anali ndi kabuku kam’thumba kokongola kwambiri, komwe kankandisangalatsa kwambiri kukawerenga.
Nthawi ya Mayesero Oopsa
Mu 1936 pamene Hitler anayamba kukhala ndi mphamvu zambiri zolamulira, makolo anga anapita ku msonkhano wina wa Mboni za Yehova womwe unali wosaiwalika. Msonkhanowu unali wamayiko ndipo unachitikira ku Lucerne, m’dziko la Switzerland. Popeza kuti bambo anga anali ndi mawu abwino kwambiri, pamsonkhanowu anasankhidwa kuti awerenge ndi kujambula nkhani za Baibulo. Pambuyo pake nkhani zimenezi zinagwiritsidwa ntchito m’dziko lonse la Slovenia polalikira kuti anthu azimvetsera. Patangopita nthawi yochepa chichitikireni msonkhano umenewo, Mboni za Yehova ku Ulaya zinayamba kuzunzidwa kwambiri. Mboni zambiri zinazunzidwa m’ndende za a Nazi ndipo zina zinafa.
Mu September 1939, nkhondo yachiwiri ya padziko * Chifukwa cha zimenezi, Mboni zambiri zinatsekeredwa m’ndende ndipo zina zinaphedwa. Mmodzi mwa anthu amene anaphedwa anali mnyamata wina dzina lake Franc Drozg, yemwe ndinkamudziwa bwino. Tsiku lina, asilikali a Nazi anapha anthu pafupi kwambiri ndi nyumba yathu. Ndimakumbukirabe kuti patsikuli, mayi anga anatseka m’makutu kuti asamve kulira kwa mfuti. M’mawu omaliza a m’kalata yotsanzikana ndi mnzake, Franc anati: “Tidzaonana mu Ufumu wa Mulungu.”
lonse inayamba, ndipo pofika mu April 1941, asilikali a dziko la Germany anali atalanda madera ena a dziko la Yugoslavia. Sukulu za Chisiloveniya zinatsekedwa ndipo tinaletsedwa kulankhula chinenero chathuchi poyera. Popeza kuti Mboni za Yehova sizilowerera mikangano ya ndale, zinakana kumenya nawo nkhondo.Zinthu Zimene Ndimanong’oneza Nazo Bondo Kwambiri
Panthawi imene Franc ankaphedwa n’kuti ndili ndi zaka 19. Ndinali wamantha kwambiri ngakhale kuti ndinkasirira kulimba mtima komanso kukhulupirika kwa Franc. Ndinkaopa kuti nanenso ndikhoza kuphedwa. Chikhulupiriro changa chinali chofooka ndipo ubwenzi wanga ndi Yehova Mulungu sunali bwino. Kenako ndinaitanidwa kuti ndipite ku usilikali. Chifukwa choti ndinali ndi mantha kwambiri komanso chikhulupiriro changa chinali chofooka, ndinavomera.
Ndinatumizidwa kumalo amene gulu lathu linkamenyana ndi asilikali a dziko la Russia. Mosakhalitsa ndinaona mitembo ya asilikali ili mbwee, paliponse. Inalitu nkhondo yoopsa kwambiri. Ndinavutika ndi chikumbumtima kwambiri ndipo ndinapempha Yehova kuti andikhululukire komanso andipatse mphamvu zoti zindithandize kuyamba kuchitanso zinthu zoyenera. Kenako adani athu atachititsa chipwirikiti pagulu lathu, ndinapeza mpata wothawa.
Nditathawa, ndinkadziwa kuti ndiphedwa ngati atandigwira. Motero, kwa miyezi 7 yotsatira ndinakhala ndikubisala m’malo osiyanasiyana. Ngakhale zinali choncho, ndinakwanitsa kumutumizira Majda khadi lomwe ndinalembapo kuti: “Ntchito ija ndasiya ndipo ndapeza ina.” Ndinkatanthauza kuti tsopano ndikufuna kuyamba kutumikira Mulungu. Koma zinanditengera nthawi yaitali ndithu kuti ndichitedi zimenezi.
Mu August 1945, patangopita miyezi itatu dziko la Germany litagonja, ndinabwerera ku Maribor. Zinali zosangalatsa kwambiri kuti tonse m’banja mwathu tinapulumuka nkhondo yoopsa kwambiriyi. Komabe panthawi imeneyi, m’dziko lathu munali boma lachikomyunizimu ndipo linkazunza Mboni za Yehova. Bomali linali litaletsa ntchito yolalikira, koma Mboni zinapitirizabe kulalikira mobisa.
Mu February 1947, Mboni zitatu zokhulupirika zomwe mayina awo anali Rudolf Kalle, Dus̆an Mikić ndi Edmund Stropnik, zinaweruzidwa kuti ziphedwe. Koma kenako, chigamulochi chinasinthidwa kuti chikhale cha zaka 20 m’ndende. Mabungwe ofalitsa nkhani anafalitsa kwambiri nkhani imeneyi, ndipo zimenezi zinachititsa kuti anthu ambiri adziwe nkhanza zimene anthu ankachitira Mboni. Ndinamva chisoni kwambiri nditawerenga nkhanizi, komabe ndinadziwa zoyenera kuchita.
Ndinapeza Nyonga Mwauzimu
Ndinkadziwa ndithu kuti ndinafunika kutsatira choonadi cha m’Baibulo pamoyo wanga. Choncho ndinayamba kulimbikira kwambiri zinthu zauzimu n’cholinga choti ndizichita nawo ntchito yathu yolalikira mobisa. Chifukwa choti ndinkawerenga Baibulo mwakhama, ndinalimba mwauzimu ndipo ndinasiya makhalidwe oipa, monga kusuta fodya.
Mu 1951, ndinabatizidwa monga chizindikiro choti ndadzipereka kwa Mulungu, ndipo ndinakhalanso ndi moyo wokhulupirika ngati womwe ndinali nawo zaka 10 m’mbuyo mwake. Tsopano ndinayamba kuona Yehova ngati Atate weniweni ndipo ndinazindikira kuti ndi wokhulupirika ndiponso wachikondi chosatha. Ngakhale kuti ndili mnyamata ndinachita zinthu mopanda nzeru, ndinakhudzidwa kwambiri ndi mfundo ya m’Baibulo yakuti Mulungu amatikhululukira. Popeza Mulungu ndi Atate wachikondi, iye anapitiriza kundikoka “ndi zomangira zachikondi.”—M’nthawi yovuta imeneyi, tinkachita misonkhano yathu yachikhristu mobisa m’nyumba zosiyanasiyana za abale ndiponso tinkangolalikira mwamwayi basi. Kenako ndinamangidwa pasanathe n’komwe chaka chimodzi nditabatizidwa. Panthawi imene ndinkadikirira mlandu wanga kuti uyambe m’khoti, ndinaonana ndi mayi anga kwa nthawi yochepa. Monga mmene ndafotokozera kumayambiriro kwa nkhani ino, iwo anandikumbatira n’kundiuza kuti: “Tsopano limba mtima.” Nditapatsidwa chigamulo choti ndikakhale m’ndende zaka zisanu, sindinadandaule nazo m’pang’ono pomwe.
Ananditsekera m’kachipinda kakang’ono pamodzi ndi akaidi ena atatu, choncho ndinapeza mwayi wolalikira uthenga wa m’Baibulo kwa anthu amene mwina sizikanatheka kuwalalikira. Ngakhale kuti ndinalibe Baibulo kapena mabuku ofotokoza Baibulo, ndinadabwa kwambiri kuti ndinkatha kukumbukira ndi kulongosola bwinobwino malemba omwe ndinkawerenga ndisanalowe m’ndende. Nthawi ndi nthawi ndinkauza akaidi anzanga kuti ngati ndikhale m’ndendemo zaka zisanu, Yehova andithandiza kupirira. Ndinkawauzanso kuti, iye angandithandize kuti nditulukemo mwamsanga, ndipo ngati atafuna kuchita zimenezo, palibe amene angamuletse.
Tinayamba Kutumikira Mwaufulu
Mu November 1953, boma linalamula kuti Mboni za Yehova zonse zomwe zinali m’ndende zimasulidwe. Kenako ndinadziwa kuti lamulo loletsa ntchito yathu yolalikira linali litachotsedwa miyezi iwiri m’mbuyo mwake. Mwamsangamsanga, tinayambiranso kukhazikitsa mipingo ndiponso kukonza zoti ntchito yathu yolalikira izichitika mwadongosolo. Tinapeza malo a misonkhano ya mpingo m’chipinda chapansi m’nyumba ina yosanja, mkatikati mwa mzinda wa Maribor. Pakhoma la nyumbayi tinaika chikwangwani cholembedwa kuti: “Mpingo wa Mboni za Yehova wa Maribor.” Tinkayamikira kwambiri chifukwa tinali ndi chimwemwe chodzadza tsaya potumikira Yehova mwaufulu.
Chakumayambiriro kwa 1961, ndinayamba utumiki wa nthawi zonse wa upainiya. Patangopita miyezi pafupifupi 6, ndinaitanidwa kuti ndikatumikire ku ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ya m’dziko la Yugoslavia. Ofesiyi inali mu mzinda wa Zagreb, ku Croatia. Panthawi imeneyo, ofesiyo inali ya kachipinda kamodzi ndipo panali anthu atatu okha ogwira ntchito. Abale omwe ankakhala pafupi ndi ofesiyi ankabwera kudzathandiza ntchito zina ndi zina kuti magazini a Nsanja ya Olonda azituluka m’zinenero za ku Yugoslavia.
Nawonso alongo omwe ankakhala pafupi ankabwera kudzathandiza pa ofesiyi. Zina mwa ntchito zimene ankagwira zinali kusoka mapepala popanga magazini. Ine ndinkagwira ntchito zosiyanasiyana monga kumasulira magazini, kuonetsetsa kuti amasuliridwa molondola, kukasiya magaziniwa kumalo osiyanasiyana ndiponso kulemba ndi kuika zinthu m’mafaelo.
Utumiki Wanga Unasintha
Mu 1964, ndinapemphedwa kuti ndikhale woyang’anira woyendayenda. Muutumiki umenewu, ntchito yanga inali yoyendera ndi kulimbikitsa mwauzimu mipingo yosiyanasiyana ya Mboni. Ndinkasangalala kwambiri ndi ntchito imeneyi. Nthawi zambiri poyendera mipingoyi ndinkakwera basi kapena sitima. Pokachezera Mboni zomwe zinkakhala ku midzi, kawirikawiri ndinkakwera njinga kapena kuyenda pansi, ndipo nthawi zina tinkadutsa m’misewu yamatope kwambiri.
Muutumiki umenewu, nthawi zina pankachitika zinthu zoseketsa kwambiri. Mwachitsanzo, popita ku mpingo wina, ine ndi m’bale wina tinakwera ngolo yake yokokedwa ndi hatchi. Ulendowu uli mkati, tayala la ngoloyo linaguluka ndipo tonse tinagwera pansi. Tili pansi pomwepo, tinaona kuti hatchi ija ikungotiyang’anitsitsa ndipo inaoneka ngati kuti ikudabwa. Ngakhale patapita zaka zambiri, tinkasekabe tikakumbutsana zankhaniyi. Sindiiwala chikondi chenicheni cha abale ngati amenewa.
M’tawuni ya Novi Sad, ndinadziwana ndi Marika, yemwe ankachita utumiki waupainiya. Mlongoyu ankakonda kwambiri choonadi cha m’Baibulo ndiponso utumiki, zimene zinandikopa kwambiri ndipo
tinakwatirana. Kenaka, tinayamba kutumikira limodzi pantchito yoyendera mipingo.Nawonso makolo anga ndiponso mlongo wanga anapirira mavuto osiyanasiyana panthawi yomwe ntchito yathu inali yoletsedwa. Abambo anga ananamiziridwa kuti ankagwirizana ndi adani panthawi yankhondo ija ndipo anachotsedwa ntchito. Iwo anayesetsa kuti abwezeretsedwe pantchito yawo, koma zinakanika ndipo anakhumudwa kwambiri. Kwa kanthawi ndithu, chikhulupiriro chawo chinafooka, koma anadzakhalanso wolimba chakumapeto kwa moyo wawo. Pamene iwo ankamwalira mu 1984 n’kuti ali Mkhristu wolimba. Koma mayi anga omwe anali odzichepetsa komanso okhulupirika anamwalira mu 1965. Majda akutumikirabe mu mpingo wa ku Maribor.
Kutumikira ku Austria
M’chaka cha 1972, ine ndi Marika anatipempha kuti tipite ku dziko la Austria kuti tizikalalikira kwa anthu ambiri ochokera ku Yugoslavia omwe anali kugwira ntchito kumeneko. Pamene tinkafika mu mzinda wa Vienna, womwe ndi likulu la dzikoli, sitinadziwe kuti tikhazikika kumeneku pantchito yathuyo. Pang’ono ndi pang’ono, magulu ndiponso mipingo yatsopano yolankhula zinenero za ku Yugoslavia inakhazikitsidwa m’dziko lonse la Austria.
M’kupita kwa nthawi, ndinayamba kutumikira monga woyang’anira woyendayenda, ndipo ndinkachezera mipingo ndi magulu amenewa omwe anali kuchulukirachulukirabe m’dziko lonselo. Kenako tinapemphedwanso kuti tizikafika ku Germany ndi ku Switzerland, kumene kunalinso mipingo ya zinenero zoterezi. Ndinali ndi mwayi wothandiza kukonza misonkhano yambiri ikuluikulu ndiponso ing’onoing’ono m’mayiko amenewa.
Nthawi zina, pamisonkhano ikuluikulu yotereyi pankakhala abale a m’Bungwe Lolamulira, ndipo ndinali ndi mwayi wokumananso ndi M’bale Martin Poetzinger. Tinakumbutsana zimene zinkachitika zaka pafupifupi 40 m’mbuyo mwake, panthawi imene iye ankafika ku nyumba kwathu kawirikawiri. Ndinam’funsa kuti, “Kodi mukukumbukira kuti ndinkakonda kuwerenga kabuku kanu kam’thumba kaja?”
“Tadikira kaye,” anatero m’baleyo akutuluka m’chipinda chomwe tinali. Pobwera, anali atatenga kabukuko n’kundipatsa ndipo anati: “Ndakupatsa kabukuka ngati mphatso.” Mpaka pano, kabuku kameneka ndi kamodzi mwa mabuku amene ndimawakonda kwambiri.
Ndikutumikirabe Ngakhale Kuti Ndimadwaladwala
Mu 1983, madokotala anandipeza ndi matenda a khansa. Pasanathe nthawi yaitali, anandiuza kuti ndikhoza kufa ndi matendawa. Imeneyi inali nthawi yovuta zedi, makamaka kwa mkazi wanga Marika. Koma mpaka pano, ndikusangalalabe ndi moyo chifukwa choti iye amandisamalira bwino kwambiri komanso abale ambiri amatithandiza.
Ine ndi mkazi wanga Marika tikupirizabe utumiki wa nthawi zonse ku Vienna. Nthawi zambiri, ndimapita ku ofesi ya nthambi m’mawa kukathandiza pa ntchito yomasulira mabuku, ndipo Marika amakhala akulalikira mu mzindawu. Ndimasangalala kwambiri kuona kuti anthu omwe akhala Mboni atasamukira kuno kuchokera ku Yugoslavia, omwe poyamba anali kagulu kochepa achuluka mpaka kuposa 1,300. Ine ndi mkazi wanga takhala ndi mwayi wothandiza ambiri mwa anthu amenewa kuphunzira choonadi cha m’Baibulo.
Zaka zingapo zapitazo, ndinali ndi mwayi wokhala ndi mbali pamwambo wopereka kwa Mulungu maofesi atsopano anthambi mu ena mwa mayiko amene kale ankapanga dziko la Yugoslavia. Mu 1999, tinakachita mwambo wopereka ofesi ya ku Croatia ndipo mu 2006, ofesi ya ku Slovenia. Ndinali mmodzi mwa anthu omwe anapemphedwa kuti afotokoze mmene ntchito yolalikira inayambira m’mayikowa zaka pafupifupi 70 zapitazo.
Kunena zoona, Yehova ndi Atate wachikondi yemwe ndi wokonzeka kutikhululukira machimo athu. Ndimayamikira kwambiri kuti iye saganizira za zolakwa zathu. (Salmo 130:3) Zoonadi, iye wandichitira chifundo kwambiri.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 4 Mayiko 6, kuphatikizapo la Slovenia, anali atapanga dziko limodzi la Yugoslavia.
^ ndime 9 Kuti mudziwe zifukwa za m’Malemba zimene Mboni za Yehova sizimenyera nawo nkhondo, onani nkhani yakuti “Zimene Owerenga Amafunsa,” patsamba 22 m’magazini ino.
[Chithunzi patsamba 27]
Kuchokera kumanzere kupita kumanja: Makolo anga a Berta ndi a Franz, mlongo wanga Majda ndi ineyo, tili ku Maribor, ku Slovenia, m’ma 1940
[Chithunzi patsamba 29]
Ndili ndi mkazi wanga Marika