Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Posachedwapa Dzikoli Likhala Paradaiso

Posachedwapa Dzikoli Likhala Paradaiso

Posachedwapa Dzikoli Likhala Paradaiso

“Atate wathu wa kumwamba, dzina lanu lilemekezedwe, ufumu wanu udze, chifuniro chanu chichitike pansi pano monga kumwamba.”​—Mateyo 6:9, 10, Chipangano Chatsopano mu Chichewa cha Lero.

PEMPHERO lotchuka limeneli, lomwe ambiri amalitcha kuti Pemphero la Ambuye, lili ndi uthenga wopatsa chiyembekezo. N’chifukwa chiyani tikutero?

Pemphero limeneli limasonyeza kuti Ufumu wa Mulungu udzakwaniritsa chifuniro cha Mulungu padziko lapansi, monga zilili kumwamba. Ndipotu chifuniro cha Mulungu n’chakuti dzikoli likhalenso paradaiso. (Chivumbulutso 21:1-5) Koma kodi Ufumu wa Mulungu n’chiyani kwenikweni, ndipo udzabwezeretsa bwanji paradaiso padziko lapansi?

Ndi Boma Lenileni

Ufumu wa Mulungu ndi boma lenileni. Boma lililonse limayenera kukhala ndi olamulira, malamulo ndiponso anthu ake. Kodi Ufumu wa Mulungu uli ndi zinthu zimenezi? Taonani mmene Baibulo limayankhira mafunso atatu otsatirawa:

Kodi olamulira mu Ufumu wa Mulungu ndani? (Yesaya 33:22) Yehova Mulungu anaika Mwana wake Yesu Khristu, kuti akhale wolamulira mu Ufumuwu. (Mateyo 28:18) Motsogoleredwa ndi Yehova, Yesu wasankha anthu ochepa “ochokera mu fuko lililonse, lilime, mtundu, ndi dziko lililonse” kuti adzalamulire naye “dziko lapansi monga mafumu.”​—Chivumbulutso 5:9, 10.

Kodi Ufumu wa Mulungu wakhazikitsa malamulo otani kuti anthu ake azitsatira? Ena mwa malamulo amenewa ndi okhudza zinthu zoti anthu ake azichita. Yesu anatchulapo lamulo limodzi lofunikira kwambiri pa malamulo amenewa. Iye anati: “‘Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi maganizo ako onse.’ Limeneli ndilo lamulo lalikulu koposa komanso loyamba. Lachiwiri, lofanana nalo ndi ili, ‘Uzikonda mnansi wako mmene umadzikondera wekha.’”​—Mateyo 22:37-39.

Malamulo ake ena ndi okhudza zinthu zoti anthu ake azipewa. Mwachitsanzo, Baibulo limanena mfundo yomveka bwino yakuti: “Musasochezedwe. Adama, opembedza mafano, achigololo, amuna osungidwira kugonedwa ndi amuna anzawo, kapena amuna ogonana ndi amuna anzawo, akuba, aumbombo, zidakwa, olalata, kapena olanda, onsewo sadzalowa mu ufumu wa Mulungu.”​—1 Akorinto 6:9, 10.

Kodi ndani adzakhale nzika za Ufumu wa Mulungu? Yesu anayerekezera nzika za Ufumu wa Mulungu ndi nkhosa. Ponena za nkhosazo iye anati: “Zidzamva mawu anga, ndipo zidzakhala gulu limodzi, m’busa mmodzi.” (Yoh. 10:16) Kuti munthu adzakhale mu Ufumu wa Mulungu ayenera kusonyeza mwa zochita, osati mwa mawu okha kuti amatsatiradi zimene Yesu, yemwe ndi Mbusa Wabwino, amalamula. Yesu anati: “Sikuti aliyense wonena kwa ine kuti, ‘Ambuye, Ambuye,’ adzalowa ufumu wa kumwamba ayi, koma yekhayo amene akuchita chifuniro cha Atate wanga wa kumwamba.”​—Mateyo 7:21.

Motero, anthu amene adzakhale mu Ufumu wa Mulungu amagwiritsira ntchito dzina la Mulungu, lakuti Yehova, ndipo amalilemekeza monga anachitira Yesu. (Yohane 17:26) Iwo amamvera lamulo la Yesu lakuti aphunzitse ena ‘uthenga wabwino wa ufumu.’ (Mateyo 24:14; 28:19, 20) Ndipo iwo amakondana kwambiri.​—Yohane 13:35.

Kuwononga “Owononga Dziko Lapansi”

Zinthu zimene zikuchitika padziko lonse masiku ano, zikusonyeza kuti Ufumu wa Mulungu watsala pang’ono kuchitapo kanthu kuti usinthiretu zinthu zonse padziko lapansi. Tikudziwa bwanji zimenezi? Zaka 2,000 zapitazo, Yesu anapereka chizindikiro chokhala ndi mbali zingapo chomwe anati chidzasonyeza kuti “ufumu wa Mulungu wayandikira.” (Luka 21:31) Monga tanenera m’nkhani yam’mbuyo ija, panopo tikuona zinthu zosiyanasiyana zomwe zili mbali ya chizindikiro chimenechi.

Ndiyeno kodi chichitike n’chiyani? Yesu anayankha kuti: “Kudzakhala chisautso chachikulu chimene sichinachitikepo kuchokera pachiyambi cha dziko kufikira lerolino, ndipo sichidzachitikanso.” (Mateyo 24:21) Sikuti zochita za anthu ndi zimene zidzabweretse chisautso chimenechi koma Mulungu ndi amene adzachite zimenezi pofuna “kuwononga iwo owononga dziko lapansi.” (Chivumbulutso 11:18) Anthu oipa, amene awononga kwambiri dzikoli chifukwa cha kudzikonda, “adzalikhidwa [kuwonongedwa] m’dziko.” Koma anthu owongoka mtima, amene amatumikira Mulungu molungama, ‘adzatsala.’​—Miyambo 2:21, 22.

Yehova Mulungu ali ndi zifukwa zomveka zochitira zimenezi. Kodi zifukwa zake n’zotani? Taganizirani chitsanzo ichi: Tiyerekezere kuti muli ndi nyumba yamdadada yochititsa lendi. Ena mwa anthu amene akukhala m’nyumbamo ndi akhalidwe labwino, amachita zinthu moganizira anzawo; amalipira lendi mokhulupirika, ndipo amasamalira nyumbayo. Koma alendi enawo amachita zinthu zosokoneza, saganizira anzawo; amakana kulipira lendi ndipo amawononga kwambiri nyumbayo. Mwawachenjezapo nthawi zambiri koma sakusintha. Kodi inuyo mungatani pamenepa? Monga mwini nyumbayo, simungachitire mwina koma kuthamangitsa alendi ovutawo.

Mofanana ndi chitsanzochi, Yehova Mulungu, yemwe ndi Mlengi wa dziko lapansi ndi zinthu zonse zimene zili m’dziko, ali ndi udindo wosankha anthu amene adzawalole kukhala padziko lapansi pano. (Chivumbulutso 4:11) Yehova ananena kuti adzachotsa anthu onse oipa amene satsatira chifuniro chake komanso amene amachita zinthu zopha ufulu wa anzawo.​—Salmo 37:9-11.

Dzikoli Lidzakhalanso Paradaiso

Posachedwapa, Ufumu wa Mulungu udzayamba kulamulira dziko lonse, motsogoleredwa ndi Yesu Khristu. Yesu ananena kuti nthawi imeneyi idzakhala “nthawi yakukonzanso zinthu zonse.” (Mateyo 19:28, Chipangano Chatsopano mu Chichewa cha Lero) Kodi akadzatero zinthu zidzakhala bwanji? Taonani malonjezo a m’Baibulo otsatirawa:

Salmo 46:9. “Aletsa nkhondo ku malekezero adziko lapansi.”

Yesaya 35:1. “Chipululu ndi malo ouma adzakondwa; ndipo dziko loti se lidzasangalala ndi kuphuka ngati duwa.”

Yesaya 65:21-23. “Osankhidwa anga adzasangalala nthawi zambiri ndi ntchito za manja awo. Iwo sadzagwira ntchito mwachabe, pena kubalira tsoka.”

Yohane 5:28, 29. “Idzafika nthawi pamene onse ali m’manda a chikumbutso adzamva mawu [a Yesu] ndipo adzatuluka.”

Chivumbulutso 21:4. “[Mulungu] adzapukuta msozi uliwonse m’maso mwawo, ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulira, kapena kubuula, ngakhale kupweteka.”

N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kukhulupirira Zimenezi?

Kodi inuyo mumakhulupirira malonjezo a m’Baibulo amenewa? Baibulo linaneneratu kuti ambiri sadzakhulupirira. Limanena kuti: “M’masiku otsiriza kudzakhala onyodola . . . otsatira zilakolako zawo, amene azidzati: ‘Kuli kuti kukhalapo kwake kolonjezedwa kuja? Taonani, kuchokera tsiku limene makolo athu anamwalira, zinthu zonse zikupitirirabe chimodzimodzi monga kuyambira pachiyambi cha chilengedwe.’” (2 Petulo 3:3, 4) Komatu anthu amene amanyodola chonchiwa akulakwitsa kwambiri. Taonani zifukwa zinayi izi zokuthandizani kukhulupirira zimene Baibulo limanena:

(1) M’mbuyomu Mulungu walangapo anthu oipa. Chitsanzo chabwino pankhani imeneyi ndi chigumula cha m’masiku a Nowa.​—2 Petulo 3:5-7.

(2) Mawu a Mulungu ananeneratu molondola zochitika za padziko lonse.

(3) Si zoona kuti “zinthu zonse zikupitirirabe chimodzimodzi monga kuyambira pachiyambi cha chilengedwe.” Mavuto okhudza moyo wa anthu, chikhalidwe ndiponso chilengedwe akuwonjezekabe.

(4) ‘Uthenga wabwino wa ufumu ukulalikidwa padziko lonse lapansi,’ ndipo izi zikusonyeza kuti posachedwapa “mapeto adzafika.”​—Mateyo 24:14.

Mboni za Yehova zikukulimbikitsani kuti muyambe kuphunzira Baibulo lomwe ndi Mawu a Mulungu kuti mudziwe bwino za chiyembekezo cha moyo wosatha mu Ufumu wa Mulungu. (Yohane 17:3) Ndithudi, zabwino zili m’tsogolo ndipo posachedwapa zinthu zisintha n’kuyamba kuyenda bwino. Kodi inuyo mudzakhalapo panthawi imeneyo?

[Mawu Otsindika patsamba 7]

Anthu amene amaganiza kuti zinthu zipitirirabe chimodzimodzi monga zakhalira kuyambira kale akulakwitsa kwambiri

[Chithunzi patsamba 8]

Kodi inuyo mudzakhalapo panthawi imeneyi?