Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mumawadziwa Atate Wanu wa Kumwamba?

Kodi Mumawadziwa Atate Wanu wa Kumwamba?

Kodi Mumawadziwa Atate Wanu wa Kumwamba?

KODI mumawadziwa bwino bambo wanu? Ngati munaleredwa ndi makolo achikondi mwina mungadabwe ndi funso limeneli. Ndipo mungayankhe mosakayika kuti, ‘Ee, ndimawadziwa bwinobwino.’ Inde, anthu ambiri amadziwa zimene bambo awo amakonda ndi zimene sakonda. Amadziwanso zimene angachite ngati patachitika zinthu zinazake, ndiponso amadziwa kuti amakonda kwambiri banja lawo.

Komabe n’kutheka kuti nthawi ina munadabwa kuona bambo anu atachita zinthu zinazake zimene simumayembekezera. Mwachitsanzo, mwana angaganize kuti bambo ake ndi munthu wofatsa waphee, koma angadabwe mmene bambowo angachitire patachitika zinazake mwadzidzidzi. Panthawiyi, angaone kuti bambo ake ndi olimba mtima kwambiri moti angalolere kuchita chilichonse kuti ateteze banja lawo.

Nanga bwanji Mlengi wathu? Baibulo limatiuza kuti: “Mwa iye tili ndi moyo, timayenda, ndi kukhalapo.” (Machitidwe 17:28) Moyo wathuwu anatipatsa ndi Mulungu, motero tingati iyeyo ndi Atate wa aliyense amene ali moyo. (Yesaya 64:8) Kodi Mulungu mumamuona m’njira imeneyi? Ngati mumatero ndiye kuti mukuchita bwino. Komatu pali zinthu zambiri zopindulitsa ndiponso zosalangalatsa zimene tiyenera kudziwa zokhudza iyeyu.

Bambo wanu mumawakonda ndi kuwalemekeza chifukwa choti mumawadziwa bwino. Umu ndi mmenenso zilili ndi Mulungu. Mukamudziwa bwino mumam’kondanso kwambiri. Mukam’dziwa bwino Mulungu n’kumachita chifuniro chake, angathe kukuthandizani pa mayesero ndi mavuto amene mumakumana nawo.

Ndiyeno kodi Mulungu ndi wotani kwenikweni? Kodi makhalidwe ake amayenera kukhudza bwanji mmene timam’kondera? Kodi kudziwa Mulungu kumakupatsani udindo uliwonse? Mayankho a mafunso amenewa muwapeza m’nkhani yotsatirayi.

[Mawu Otsindika patsamba 3]

Mumakonda munthu mogwirizana ndi mmene mumam’dziwira