Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Usakaleke Kulalikira ku Nyumba Ndi Nyumba”

“Usakaleke Kulalikira ku Nyumba Ndi Nyumba”

“Usakaleke Kulalikira ku Nyumba Ndi Nyumba”

Yosimbidwa ndi Jacob Neufeld

“Zivute zitani usakaleke kulalikira ku nyumba ndi nyumba.” Ndikuganizira mawu amenewa, ndinayamba ulendo wa makilomita 5 wopita ku mudzi wina. Koma nditafika ndinachita mantha kwambiri moti zinandivuta kuyamba kulalikira. Patapita kanthawi ndinapita ku nkhalango n’kupemphera kwambiri kuti Mulungu andilimbitse mtima. Nditatero, ndinapita khomo loyamba lija n’kuyamba kulalikira.

KODI chinachitika n’chiyani kuti ndipezeke m’mudzi wa m’chipululu ku Paraguay, n’kumalalikira ndekhandekha? Talekani ndifotokoze bwinobwino. Ndinabadwa mu November 1923, m’tawuni yotchedwa Kronstalʹ ku Ukraine. Anthu a m’tawuniyi anali Amenoni amene anasamukira ku Ukraine kuchokera ku Germany, kumapeto kwa zaka za m’ma 1700. Boma linawapatsa ufulu monga wa kulambira (popanda kutembenuza ena), ufulu wodzilamulira ndiponso wosakakamizidwa kulowa usilikali.

Chipani cha komyunizimu chitayamba kulamulira, anthuwo analandidwa ufulu wonsewu. Chakumapeto kwa m’ma 1920 boma linalandanso mafamu akuluakulu a Amenoni. Pofuna kuti anthu azilimvera, bomalo linkakananso kuwapatsa chakudya ndipo wotsutsa aliyense ankalangidwa koopsa. Cha m’ma 1930, amuna ambiri ankatengedwa ndi bungwe la chitetezo cha boma lotchedwa KGB, makamaka usiku. Patapita nthawi, m’midzi yambiri munatsala amuna ochepa kwambiri. N’chifukwa chake ndinasiyana ndi bambo anga ndili ndi zaka 14 mu 1938 ndipo mpaka pano sindinamvepo chilichonse chokhudza iwowo. Patatha zaka ziwiri mkulu wanga anatengedwanso.

Pofika mu 1941, asilikali a Hitler analanda dziko la Ukraine. Tinasangalala kuti boma la komyunizimu lasiya kutilamulira. Komabe tinangodabwa kuti mabanja 8 achiyuda amene ankakhala m’tawuni yathu asowa mwadzidzidzi. Zonsezi zinkandivuta kumvetsa ndipo ndinkadzifunsa kuti n’chifukwa chiyani zinthu zili chonchi?

Kuona Mtima Kunandipulumutsa

Mu 1943 asilikali a ku Germany anabwerera kwawo n’kutenga mabanja ambiri achijeremani, kuphatikizapo abale anga onse amene anatsala. Anthuwa anawatenga kuti akathandize pankhondo. Panthawiyi n’kuti ineyo nditatengedwa kale ndipo ndinali ku Romania m’gulu la asilikali a Hitler otchedwa SS. Ndiyeno panachitika nkhani yaing’ono imene inakhudza kwambiri moyo wanga.

Mkulu woyang’anira kagulu kathu ka asilikali ankafuna kundiyesa kuti aone ngati ndili woona mtima. Iye anandituma kuti ndikachapitse yunifolomu yake. Koma anasiya ndalama m’thumba lina la yunifolomuyo. Nditapeza ndalamazo ndinakam’bwezera koma anazikana n’kunena kuti sanasiye chilichonse mu yunifolomuyo. Ndinalimbikirabe kumuuza kuti ndalamazo ndazipeza m’thumba la yunifolomu yakeyo. Patapita nthawi yochepa anandisankha kukhala wachiwiri wake kuti ndizilemba zinthu zosiyanasiyana, kugawira ntchito asilikali olondera, komanso kuyang’anira ndalama za gulu lathu.

Tsiku lina usiku asilikali a dziko la Russia anagwira anthu a m’gulu lathu lonselo kupatulapo ineyo. Chinachitika n’chakuti, panthawiyo ndinatsalira kuti ndimalize ntchito imene mkulu wa gulu lathu uja anandipatsa. Zikuoneka kuti ine ndekha ndi amene sindinagwidwe. Ndinapulumuka chifukwa cha udindo umene ndinapatsidwa nditasonyeza kuona mtima. Pakanapanda zimenezi nanenso ndikanagwidwa.

Motero, mu 1944 anandiuza kuti ndikhale kaye pa tchuthi kwa kanthawi ndithu. Zitatero ndinapita kwathu kukaona mayi anga. Poyembekezera kuti andiitanenso kuntchito ya usilikali ija, ndinayamba kuphunzira ntchito yomanga nyumba imene inadzandithandiza kwambiri patsogolo pake. Mu April 1945 asilikali a ku America analanda tawuni imene tinkakhala, kufupi ndi mzinda wa Magdeburg. Patatha mwezi umodzi analengeza kuti nkhondoyo yatha. Tinapulumuka ndipo tinkaona kuti tili ndi tsogolo labwino.

Tsiku lina mu June tinamva munthu akulengeza mokuwa kuti: “Asilikali a ku America achoka dzulo usiku ndipo asilikali a Russia afika lero 11 koloko masana.” Tinakhumudwa kwambiri pozindikira kuti tikhalanso mu ulamuliro wa chikomyunizimu. Nthawi yomweyo ineyo ndi mwana wa bambo anga aang’ono tinayamba kukonza zothawa. Patatha miyezi ingapo tinafika m’chigawo cholamulidwa ndi dziko la America. Kenako mu November tinayenda movutikira ulendo woopsa wolowanso m’chigawo cholamulidwa ndi dziko la Russia n’kukatenga abale athu.

“Uzikayerekezera Zimene Uzikamva ndi Zimene Umamva Kuno”

Tinakakhala kumene kale ankati ku West Germany. Patapita nthawi ndinayamba kukonda kwambiri Baibulo. Lamlungu lililonse ndinkapita ku nkhalango kukawerenga Baibulo koma sindinkalimvetsa ndipo ndinkaona kuti nkhani zake n’zovuta kumva komanso n’zakalekale. Ndinkapitanso ku maphunziro a katekisimu pokonzekera ubatizo kuti ndikhale Mmenoni. Ndinadabwa kwambiri kuti mu katekisimu munali mawu akuti: “Atate ndi Mulungu, Mwana ndi Mulungu ndipo Mzimu Woyera ndi Mulungunso.” Pansi pa mawu amenewa panali funso lakuti: “Kodi pali Milungu itatu?” Ndiye pansi pa funsolo panali yankho lakuti: “Ayi atatu onsewa ndi mmodzi.” Ndinafunsa abusa kuti andifotokozere bwinobwino zimenezi. Iwo anandiyankha kuti: “Mwanawe usamaganizire kwambiri nkhani zimenezi; ena anapenga nazo.” Nthawi yomweyo ndinasintha maganizo ofuna kubatizidwa aja.

Patapita masiku angapo ndinamva munthu wina akulankhula ndi msuweni wanga. Pochita chidwi nanenso ndinayamba kuyankhira ndipo ndinamufunsa munthuyo mafunso angapo. Munthuyo anali Erich Nikolaizig ndipo anali atapulumuka ndende yozunzirako anthu yotchedwa Wewelsburg. Iye anandifunsa ngati ndikufuna kuphunzira Baibulo. Nditavomera anandiuza kuti umboni wa zonse zimene azindiphunzitsa uzichokera m’Baibulo langa.

Titakambirana maulendo ochepa chabe Erich anandiitana ku msonkhano waukulu wa Mboni za Yehova umene mwina unali m’gulu la misonkhano yoyamba kuchitika pambuyo pankhondo. Ndinagoma kwambiri ndi msonkhanowu ndipo ndinalemba vesi lililonse limene okamba nkhani anawerenga kapena kutchula. Posakhalitsa ndinazindikira kuti munthu akamaphunzira Baibulo amakhala ndi udindo winawake. Poopa zimenezi ndinaganiza zongosiya. Komanso mfundo yakuti pali chipembedzo chimodzi chokha choona inkandivuta kumvetsa. Erich ataona kuti ndikufuna kubwerera kutchalitchi changa, anandilangiza kuti: “Uzikayerekezera zimene uzikamva ndi zimene umamva kuno.”

Nditangopita kutchalitchiko kawiri kokha ndinazindikira kuti abusa athuwo sankadziwa chimene akunena ndiponso kuti analibe choonadi ngakhale pang’ono. Ndinayamba kulemba makalata kwa abusa angapo owafunsa mafunso okhudza Baibulo. Mmodzi anayankha kuti: “Iwe sunabadwe mwatsopano, ndiye ndani wakupatsa ufulu womafufuza Malemba?”

Ndinali pachibwenzi ndi mtsikana wina yemwe anali m’gulu lina la Amenoni lokhulupirira za kubadwanso mwatsopano. Chifukwa cha achibale ake, amene ankadana ndi Mboni za Yehova, mtsikanayu anandiuza kuti ndisankhepo pakati popitiriza chibwenzi ndi iyeyo kapena kusiya chipembedzo changa chatsopanochi. Panthawiyi n’kuti nditafika pozindikira kuti ndinali kuphunziradi choonadi moti sindikanabwereranso m’mbuyo ayi. Ndinamuuza mtsikanayo kuti chibwenzicho chatha.

Posakhalitsa Erich anabweranso kudzationa. Iye anandiuza kuti mlungu wotsatira kudzachitika msonkhano ndipo anandifunsa ngati ndingafune kudzabatizidwa. Pamenepa n’kuti nditatsimikiza kuti Mboni za Yehova zimaphunzitsa choonadi ndipo ndinkafunadi kutumikira Yehova Mulungu. Motero mu May, 1948, ndinavomera kubatizidwa ndipo ndinabatizidwira m’bafa losambira.

Nditangobatizidwa kumene, banja lathu linaganiza zosamukira ku Paraguay, ku South America, ndipo mayi anandichonderera kuti ndipite nawo. Sindinkafuna kupita chifukwa ndinkafuna kupitiriza kuphunzira Baibulo ndiponso kuti ndidziwe zinthu zambiri. Nthawi ina nditapita ku ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ku Wiesbaden, ndinakumana ndi August Peters. Iyeyu anandifotokozera kuti ndinali ndi udindo wosamalira banja langalo. Ndipo anandilimbikitsanso kuti: “Zivute zitani usakaleke kulalikira ku nyumba ndi nyumba. Ukakaleka, sukasiyana n’komwe ndi anthu a matchalitchi ena.” Mpaka pano, malangizo amenewo ndimawaona kuti ndi othandiza kwambiri moti ndimaona kuti ntchito yolalikira “ku nyumba ndi nyumba” ndi yofunika kwabasi.​—Machitidwe 20:20, 21.

Ku Paraguay Ankanditcha “Mneneri Wonyenga”

Pasanapite nthawi yaitali kuchokera pamene ndinalankhula ndi August Peters, ndinanyamuka pa sitima ya m’madzi, kupita ku South America limodzi ndi anthu a m’banja lathu. Tinakafikira m’chigawo chotchedwa Gran Chaco, ku Paraguay, ndipo ukunso kunkakhala Amenoni ambiri. Nditakhalako milungu iwiri, ndinayenda ulendo umene ndaufotokoza poyamba uja wopita kumudzi wina wapafupi kukalalikira ndekhandekha. Posakhalitsa, mbiri inamveka paliponse kuti alendo aja abwera ndi “mneneri wonyenga.”

Panthawiyi m’pamene ndinaona phindu la ntchito yomanga imene ndinaphunzira ija. Banja lililonse limene linafika kuno linafunikira nyumba ndipo nyumba zake zinali zaudzu, zomangidwa ndi zidina. Kwa miyezi 6 yotsatira, ndinali wotanganidwa kwambiri ndi ntchito yomanga nyumba za mabanja osiyanasiyana. Pamenepa ndinapezerapo mwayi wolalikira kwa anthuwa. Anthu ake anali aulemu, koma akangoona kuti nyumba yawo yatha sankafunanso kumvetsera uthenga wanga.

Nthawi yonseyi sitima zapamadzi zinali kubwera ndi Amenoni ambiri othawa nkhondo ku Germany. Mmodzi wa anthuwa anali Katerina Schellenberg, mtsikana amene m’mbuyomo anakumana ndi Amboni n’kudziwa nthawi yomweyo kuti iwo ankaphunzitsa choonadi. Ngakhale kuti anali asanabatizidwe, iye ankauza anthu musitima imene anakwera kuti ndi wa Mboni za Yehova. Chifukwa cha zimenezi anamukaniza kupitiriza ulendo wake ndi gulu limene linachokera ku Germany lija. Motero anatsala yekhayekha mumzinda wa Asunción, womwe ndi likulu la dziko la Paraguay. Iye anapeza ntchito yapakhomo n’kuphunzira Chisipanishi. Kenaka anafufuza Mboni za Yehova ndipo atazipeza anabatizidwa. Mu October 1950, mtsikana wolimba mtima ameneyu anakhala mkazi wanga. Iyeyu wandithandiza kwambiri pazovuta zonse zimene takumana nazo zaka zonse zimene takhala limodzi.

Posakhalitsa ndinapeza ndalama zokwanira kugula mahatchi awiri ndi ngolo imene ndinkayendera polalikira ndipo panthawi yonseyi sindinaiwale mawu a m’bale Peters aja. Kenaka mlongo wanga, yemwenso anali atakhala wa Mboni, anabwera kudzakhala nafe. Ndiyeno nthawi zambiri tonse tinkadzuka 4 koloko m’mawa n’kuyenda ulendo wa maola anayi, kenaka n’kulalikira kwa maola awiri kapena atatu basi n’kuuyambanso ulendo wobwerera ku nyumba.

Ndinawerenga m’mabuku athu kuti a Mboni za Yehova amakamba nkhani ya onse, motero ndinakonza zodzakamba nkhani yotere. Ndili ku Germany ndinali ndisanapitepo ku msonkhano wa mpingo, moti ndinangoyerekeza mmene nkhaniyo imakambidwira. Ndiye nkhani yangayo inali yonena za Ufumu wa Mulungu. Pankhaniyo panabwera anthu 8 odzamvetsera ndipo zimenezi sizinasangalatse abusa a tchalitchi cha Amenoni. Iwo anasonkhanitsa anthu kuti akalande mabuku onse ofotokoza Baibulo kwa anthu amene tinawapatsa, n’kuwauza kuti asadzalankhulenso nafe, ngakhale kutipatsa moni.

Zitatero, anandiitana ku likulu loyang’anira derali kuti akandifunse mafunso. Ndinakhalako maola angapo ndipo amene ankandifunsa mafunsowo anali mkulu wa kumeneko komanso abusa awiri ochokera ku Canada. Potsiriza, mmodzi wa anthuwa anati: “Udziwe kuti ife tilibe nazo ntchito zikhulupiriro zakozo, koma ulonjeze kuti sudzayerekezanso kulalikira aliyense kuno zikhulupiriro zakozo.” Ndinakana kulonjeza zimenezi. Motero anandiuza kuti ndisamuke chifukwa iwowo sangalole kumakhala ndi “mneneri wonyenga” pakati pawo. Koma nditakananso zosamukazo anandiuza kuti iwowo alolera kupereka ndalama yoti banja lathu lonse liyendere posamukapo. Ndinakanitsitsanso zimenezi.

Munyengo yachilimwe mu 1953, ndinapita ku msonkhano waukulu ku Asunción. Kumeneko ndinalankhula ndi m’bale Nathan Knorr, yemwe anachokera ku likulu lapadziko lonse la Mboni za Yehova ku Brooklyn, mumzinda wa New York. Iye anandiuza kuti ndisamukire ku likulu la dziko la Paraguay kuti ndizikalalikira pamodzi ndi kagulu ka amishonale kamene kanali kumeneko, makamaka chifukwa choti ntchito yathu yolalikira kwa Amenoni aja siinaphule kanthu kwenikweni.

Kuika Ufumu Patsogolo

Panthawiyi m’dziko lonse la Paraguay munali Mboni 35. Nditakambirana ndi mkazi wanga anavomera kusamukira ku likululo ngakhale kuti sankafuna kukakhala mumzinda waukulu. M’chaka cha 1954, ine ndi Katerina tinamanga nyumba yanjerwa, ndipo nyumbayi tinaimanga awiriwiri panthawi yathu yopuma. Sitinajombepo ku misonkhano ndipo nthawi zonse tinkalalikira Loweruka ndi Lamlungu.

Ndinali ndi mwayi winanso wotumikira poyenda limodzi ndi woyang’anira dera. Iyeyu anali mtumiki amene ankayendera mipingo ku Paraguay ndipo anandipempha kuti ndizim’thandiza pomasulira nkhani zake m’Chijeremani akamayendera magulu a anthu ochokera ku Germany. Ineyo sindinkadziwa kwambiri Chisipanishi, moti kumasulira nkhani yanga yoyamba kunali kovuta kwambiri kuposa utumiki uliwonse umene ndinachitapo.

Chifukwa choti mkazi wanga anayamba kudwaladwala tinasamukira ku Canada mu 1957. Kenaka, mu 1963, tinasamukira ku United States. Takhala tikuyesetsa kuika ntchito ya Ufumu patsogolo kulikonse kumene takhala tikusamukira. (Mateyo 6:33) Ndikuthokoza kwambiri Yehova Mulungu pondilola kuphunzira choonadi kuchokera m’Mawu ake, Baibulo, ndili wamng’ono. Kuphunzira Baibulo kwandithandiza kwambiri pamoyo wanga wonse.

Ndimaona kuti ndi mwayi waukulu kwambiri kuti ndathandiza anthu ena kuphunzira Baibulo n’kudziwa choonadi chosangalatsa chimene chandilimbikitsa pa moyo wanga wonse. Chimene chimandisangalatsa kwambiri n’chakuti ana ndi zidzukulu zanga zonse aphunzira Baibulo kuyambira ali aang’ono. Onse akutsatira malangizo a m’bale Peters amene anandiuza mawu akuti: “Zivute zitani usakaleke kulalikira ku nyumba ndi nyumba.”

[Mawu Otsindika patsamba 22]

Chimene chimandisangalatsa kwambiri n’chakuti ana ndi zidzukulu zanga zonse aphunzira Baibulo kuyambira ali aang’ono

[Zithunzi patsamba 20, 21]

Ine ndi Katerina titangotsala pang’ono kukwatirana mu 1950

[Chithunzi patsamba 21]

Tili ndi mwana wathu woyamba kunyumba kwathu ku Paraguay, mu 1952

[Chithunzi patsamba 23]

Banja lathu lonse panopo

[Mawu a Chithunzi]

Photo by Keith Trammel © 2000

[Mawu a Chithunzi patsamba 19]

Photo by Keith Trammel © 2000