Yesu Anagometsa Anthu ndi Mawu Ake
Zoti Achinyamata Achite
Yesu Anagometsa Anthu ndi Mawu Ake
Malangizo: Chitani zotsatirazi muli pa malo opanda phokoso. Mukamawerenga mavesiwo, muziyerekezera kuti pamene zinthuzo zinkachitika inuyo munalipo. Yesani kuona nkhaniyi m’maganizo mwanu. Yerekezerani kuti mukumva mawu a m’nkhaniyi. Yesetsani kumva mu mtima mwanu ngati mmene ankamvera anthu a m’nkhaniyi.
ONANI BWINOBWINO NKHANIYI.—WERENGANI LUKA 2:41-47.
Kodi mukawerenga vesi 46 mukuganiza kuti Yesu ankakambirana zinthu zotani ndi aphunzitsi?
․․․․․
FUFUZANI MOZAMA.
Kodi mukuganiza kuti n’chifukwa chiyani Yesu anatha kukambirana ndi atsogoleri a chipembedzo adakali wamng’ono? Kodi n’chifukwa choti anali wangwiro basi, kapena panalinso zifukwa zina?
․․․․․
ONANI BWINOBWINO NKHANIYI.—WERENGANI LUKA 2:48-52.
Kodi mukuganiza kuti nkhope ya Yesu inkaoneka bwanji pamene ananena mawu akuti: “Mumandifunafuna chifukwa chiyani?”
․․․․․
N’chifukwa chiyani tinganene motsimikiza kuti polankhula ndi makolo ake, Yesu sanalankhule mwaukali kapena mopanda ulemu?
․․․․․
FUFUZANI MOZAMA.
N’chifukwa chiyani n’zosadabwitsa kuti Yosefe ndi Mariya anazunzika mumtima Yesu atasowa?
․․․․․
Ngakhale kuti Yesu anali wangwiro, n’chifukwa chiyani iye anafunikirabe kupitiriza kumvera makolo ake?
․․․․․
Kodi mukuganiza kuti Yesu anachita manyazi chifukwa choti anadzudzulidwa pamaso pa anthu amene anagoma naye?
․․․․․
GWIRITSANI NTCHITO ZIMENE MWAPHUNZIRA. LEMBANI ZIMENE MWAPHUNZIRA PONENA ZA . . .
Kugonjera.
․․․․․
Ubwino wa kuphunzira Baibulo munthu adakali wamng’ono.
․․․․․
M’NKHANIYI, KODI NDI MFUNDO ZITI ZIMENE ZAKUKHUDZANI KWAMBIRI NDIPO N’CHIFUKWA CHIYANI?
․․․․․