Phunzitsani Ana Anu
Abale Ake a Yosefe Anachita Nsanje Kodi Iwenso Umachita Nsanje?
CHOYAMBA tiye tione tanthauzo la nsanje. Kodi unaipidwapo ndi mnzako winawake chifukwa choti anthu ankanena kuti iyeyo ndi mwana wabwino, wooneka bwino, kapena wanzeru? *— Kuipidwa kumeneko n’kumene kumatchedwa kuti nsanje.
M’banja, ana angayambe kuchitirana nsanje ngati makolo amakondera mwana wina. M’Baibulo muli nkhani ya banja lina limene linakumana ndi vuto lalikulu kwambiri chifukwa cha nsanje. Tiye tione vuto limeneli ndi zimene tikuphunzirapo pa zomwe zinachitikazo.
Yosefe anali mwana wa nambala 11 wa Yakobo, ndipo abale ake ankamuchitira nsanje. Kodi ukudziwa chifukwa chake?— N’chifukwa choti bambo wawo, Yakobo, ankam’konda kwambiri. Mwachitsanzo, Yakobo anam’soketsera Yosefe malaya okongola kwambiri. Yakobo ankakonda kwambiri Yosefe “pakuti anali mwana wa ukalamba wake” ndiponso anali mwana woyamba wa Rakele, mkazi amene ankam’konda kwambiri.
Baibulo limati ‘abale ake ataona kuti atate wake anam’konda iye koposa abale ake onse anayamba kudana naye Yosefeyo.’ Kenaka tsiku lina Yosefe anauza banja lake kuti analota abale ake onsewo, kuphatikizapo bambo ake, akum’gwadira. Baibulo limatinso: “Ndipo abale ake anam’chitira iye nsanje.” Ngakhale bambo ake anam’kalipira chifukwa chowauza malotowo.—Genesis 37:1-11.
Patsogolo pake, Yosefe atafika zaka 17, abale ake anapita dera lakutali kwambiri kukadyetsa nkhosa ndi mbuzi za banja lawo. Ndiyeno Yakobo anatuma Yosefe kuti akawaone abale akewo. Kodi ukudziwa zimene ambiri mwa iwo anafuna kuchita atamuona akubwera poteropo?— Ankafuna kuti amuphe. Koma awiri mwa iwo, Rubeni ndi Yuda, sanafune zimenezi.
Ndiyeno amalonda ena opita ku Iguputo akudutsa, Yuda anati: “Tiyeni tim’gulitse.” Iwo anaterodi. Kenaka anapha mbuzi n’kuviika malaya a Yosefe aja m’magazi a mbuziyo. Atabwerera kwawo anawaonetsa bambo awo malaya amagaziwo. Bambowo ataona malayawo anafuula kuti: ‘Mwana wanga Yosefe, wajiwa ndi chilombo choopsa.’—Amalonda aja anapita naye ku Iguputo ndipo patapita nthawi, Farao, yemwe anali mfumu ya ku Igupto, anayamba kum’konda Yosefeyo. Mfumuyi inam’konda chifukwa choti Yosefe anamasulira maloto ake, mothandizidwa ndi Mulungu. M’maloto ake oyamba, mfumuyo inaona ng’ombe 7 zonenepa ndi ng’ombe 7 zowonda. M’maloto ake achiwiri, mfumuyo inaona ngala za tirigu 7 zonenepa ndi ngala 7 zowonda. Yosefe anati maloto awiri onsewa ankatanthauza kuti pa zaka 7 anthu adzakolola zakudya zambiri ndipo pa zaka 7 zotsatira kudzakhala njala. Farao analamula kuti pokonzekera zaka za njalazo, Yosefe aziyang’anira ntchito yosonkhanitsa ndi kusunga zakudya pa zaka zimene anthu adzakolole zambirizo.
Zaka za njalazo zitafika, banja la Yosefe, lomwe linkakhala kutali kwambiri, linasowa zakudya. Ndiyeno Yakobo anatumiza abale a Yosefe 10 aja kuti akagule chakudya ku Iguputo. Iwo anafika kwa Yosefe koma sanamuzindikire. Yosefe sanadziulule, m’malo mwake anawayesa abale akewo kuti aone ngati anasiya mtima wawo wa nsanje uja. Ndipo anaona kuti iwo anali achisoni kwambiri pokumbukira zinthu zoipa zimene anam’chitira Yosefeyo. Kenaka anawauza kuti iyeyo ndi Yosefe, m’bale wawo uja. Pamenepa anakumbatirana n’kusangalala kwambiri.—Genesis chaputala 40 mpaka 45.
Kodi nkhani ya m’Baibulo imeneyi ikukuphunzitsa chiyani pankhani yochitira ena nsanje?— Ikukuphunzitsa kuti nsanje imabweretsa mavuto aakulu, ndipo ingapatse munthu maganizo ofuna kuchita zinthu zoipa kwa m’bale wake. Tiye tiwerenge lemba la Machitidwe 5:17, 18 ndiponso la Machitidwe 7:54-59 kuti tione zimene anthu ena anachitira ophunzira a Yesu, chifukwa cha nsanje.— Kodi pankhani imene tawerengayi ukuona kuti m’pofunikadi kuti tizipewa kuchitira ena nsanje?—
Yosefe anakhala ndi moyo zaka 110. Anakhala ndi ana, zidzukulu ndiponso zidzukulutudzi. N’zosakayikitsa kuti nthawi zambiri Yosefe ankaphunzitsa ana onsewa kuti azikondana n’kumapewa nsanje.—Genesis 50:22, 23, 26.
^ ndime 3 Ngati mukuwerengera ana nkhaniyi, kamzereka n’kokuuzani kuti muime kuti anawo ayankhe funsolo.