Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

‘Analingalira Mawuwo Mumtima Mwake’

‘Analingalira Mawuwo Mumtima Mwake’

Tsanzirani Chikhulupiriro Chawo

‘Analingalira Mawuwo Mumtima Mwake’

MARIYA ankatembenukira uku ndi uku ali pamsana pa bulu paulendo wa maola ambiri wopita ku Betelehemu. Mwamuna wake Yosefe anali kuyenda patsogolo pake potsogolera buluyo. Kenaka Mariya anamvanso mwana akusunthasuntha m’mimba mwake.

Panthawiyi n’kuti Mariya ali wotopa chifukwa Baibulo limachita kunena kuti anali “wolema ndi pathupi.” (Luka 2:5) Pamene ankadutsa m’minda yosiyanasiyana, nkutheka kuti panali alimi ena amene mwina anali kulima kapena kubzala omwe ankadabwa kuti mayi wotopa chonchi akupita kuti. Kodi n’chiyani chinachititsa kuti Mariya ayende ulendo wautali chonchi kuchoka kwawo ku Nazareti?

Miyezi ingapo m’mbuyomo, mayi wachiyudayu anapatsidwa ntchito yapadera kwambiri. Ntchito yake inali yoti abereke mwana woti adzakhale Mesiya, Mwana wa Mulungu. (Luka 1:35) Mwanayo atatsala pang’ono kubadwa, panafunika kuti ayende ulendowu. Paulendowu, Mariya anakumana ndi zinthu zambiri zoyesa chikhulupiriro chake. Tiyeni tione zimene zinam’thandiza kukhalabe wolimba mwauzimu.

Ulendo Wopita ku Betelehemu

Yosefe ndi Mariya sanali okha paulendowu. Kaisara Augusto anali atangopereka lamulo loti m’dzikomo muchitike kalembera, motero aliyense anayenera kubwerera kumzinda wa kwawo. Kodi Yosefe anatani? Nkhaniyi imati: “Yosefe nayenso anakwezeka mtunda kuchokera ku Galileya, mu mzinda wa Nazarete, ndi kupita ku Yudeya, ku mzinda wa Davide wotchedwa Betelehemu, chifukwa anali wa banja ndi fuko la Davide.”​—Luka 2:1-4.

N’zosadabwitsa kuti Kaisara anapereka lamuloli panthawi imeneyi, chifukwa ulosi wina umene unalembedwa zaka pafupifupi 700 m’mbuyomo, unalosera kuti Mesiya adzabadwira ku Betelehemu. Panali mzinda wina wotchedwa Betelehemu womwe unali pamtunda wa makilomita 11 kuchokera ku Nazareti. Koma ulosiwu unanena mwachindunji kuti Mesiya adzabadwira ku “Betelehemu Efrata.” (Mika 5:2) Tikatengera misewu ya masiku ano, Betelehemu Efrata ali kum’mwera, pamtunda wa makilomita 150 kuchokera ku mzinda wa Nazareti. Kumeneku n’kumene Yosefe anauzidwa kuti apite, chifukwa n’kumene kunali kumudzi kwa mbumba ya Mfumu Davide. Yosefe ndi mkazi wake Mariya anali a mbumba imeneyi.

Mwina sizinali zophweka kuti Mariya agwirizane ndi maganizo a Yosefe oti amvere lamuloli. Ulendowutu unali wowawa kwambiri kwa mayi wapakati ngati Mariya. Chinanso, iyi inali nyengo yoti mvula ya mawawa ikanatha kugwa nthawi ina iliyonse. Komanso mawu a m’Baibulo akuti “anakwezeka mtunda kuchoka ku Galileya,” ndi oyenerera kwambiri chifukwa choti mzinda wa Betelehemu unali m’dera lokwera kwambiri, pafupifupi mamita oposa 760. Moti zinali zovuta kuti munthu amene wayenda kale ulendo wa masiku angapo alimbanenso ndi chitunda chimenechi. Ndiye poti Mariya anali wotopa akanafunikira masiku ochulukirapo ndithu kuti ayende ulendo umenewu chifukwa chopuma pafupipafupi. Komanso panthawi ngati imeneyi mtsikana aliyense amafuna kukhala kunyumba, pafupi ndi achibale komanso anzake oti amuthandize panthawi yochira. Kunena zoona Mariya anafunika kulimba mtima kuti ayende ulendo umenewu.

Ngakhale zinali choncho, Luka analemba kuti Yosefe anapita “kukalembetsa limodzi ndi Mariya.” Iye anatinso Mariya “anamanga banja [ndi Yosefe] malinga ndi pangano.” (Luka 2:4, 5) Posankha zochita, Mariya anaganizira kwambiri zofuna za mwamuna wake Yosefe. Iye ankaona kuti mwamuna wakeyo ndiye mutu wake wauzimu, ndipo iye anakwaniritsa udindo umene Mulungu anam’patsa monga mkazi, woti azichirikiza zinthu zimene mwamuna wake wasankha kuchita. * Motero iye anagonjera ndipo sanalole kuti nkhani imeneyi iyese chikhulupiriro chake.

Kodi n’chinthu chinanso chiti chimene mwina chinachititsa kuti Mariya amvere mwamuna wake? Kodi n’zotheka kuti ankadziwa za ulosi wonena kuti Mesiya adzabadwira ku Betelehemu? Ngakhale kuti Baibulo silinena chilichonse pankhaniyi, n’zotheka kuti Mariya ankadziwa zimenezi. Tikutero chifukwa choti zikuoneka kuti atsogoleri achipembedzo ngakhalenso anthu wamba ambiri ankadziwa ulosi umenewu. (Mateyo 2:1-7; Yohane 7:40-42) Ndiponsotu Mariya sanali mbuli pankhani ya Malemba. (Luka 1:46-55) Mulimonsemo, kaya Mariya anachita zimenezi pomvera mwamuna wake, kaya pomvera lamulo la boma, kapena ulosi wa Yehova, kapena pa zifukwa zingapo mwa zifukwa zimenezi, mfundo ndi yakuti iye anatipatsa chitsanzo chabwino kwambiri. Yehova amasangalala kwambiri ndi amuna komanso akazi amene ali ndi mtima wodzichepetsa ndiponso womvera. Masiku ano anthu ambiri amanyoza kwambiri anthu okonda kugonjera. N’chifukwa chake, padziko lonse, anthu okhulupirika kwa Mulungu ayenera kutsatira chitsanzo chabwino kwambiri cha Mariya.

Kubadwa kwa Khristu

Mtima wa Mariya unakhala m’malo pamene mzinda wa Betelehemu unayamba kuonekera poteropo. Panthawiyi n’kuti iye ndi mwamuna wake akukwera zitunda kudutsa minda ya maolivi, yomwe inkakololedwa pa mapeto a nyengo yokolola. N’kutheka kuti atangoona mzindawo, iwo anayamba kuganizira za mbiri yake. Unali mzinda waung’ono kwambiri moti sunkaikidwa m’gulu la mizinda ya ku Yuda, monga mmene mneneri Mika ananenera. Komabe kumeneku n’kumene Boazi, Naomi, ndi Davide anabadwira zaka zoposa 1,000 m’mbuyomo.

Mariya ndi Yosefe atafika anapeza kuti mzindawo wadzaza ndi anthu. Anzawo ena odzalembetsa anali atafika kale, moti malo onse ogona anali atatha. * Ndiye chifukwa chozingwa anakagona m’khola. Kodi mukuganiza kuti Yosefe anamva bwanji kuona mkazi wake akuyamba kubuula ndi ululu wobereka kwa nthawi yoyamba? Ndipotu tangoganizirani kuti zonsezi zinkachitikira m’khola.

Mayi aliyense angathe kumvetsa zimene zinam’chitikira Mariya. Panthawiyi n’kuti patapita zaka 4,000 kuchokera pamene Yehova analosera kuti akazi onse azidzamva ululu pobereka, chifukwa cha uchimo umene anthu anatengera kwa Adamu ndi Hava. (Genesis 3:16) Palibe umboni uliwonse woti Mariya yekha sanamve ululu. Luka sananene chilichonse pankhani imeneyi, m’malomwake anangoti: “Anabereka mwana wake woyamba wamwamuna.” (Luka 2:7) Uyu anali “mwana woyamba” wa Mariya, mwa ana osachepera 7 amene iye anabereka. (Maliko 6:3) Komabe mwana woyambayo anali wosiyana kwambiri ndi anzake onsewo. Iyeyu kwenikweni anali mwana wa Yehova “woyamba kubadwa wa chilengedwe chonse,” kapena kuti Mwana wobadwa yekha wa Mulungu.​—Akolose 1:15.

Apa Luka anatchulapo mfundo yodziwika kwambiri yakuti: “Anamukulunga ndi nsalu n’kumugoneka modyeramo ziweto.” (Luka 2:7) Padziko lonse, m’zithunzi ndiponso m’masewero ambiri a kubadwa kwa Ambuye Yesu, amaonetsa zimenezi m’njira yokometsera kwambiri. Koma kodi zenizeni zimene zinachitika zinali zotani? Malo odyera ziweto sakhala malo aukhondo ayi. Motero banjali linagona m’khola monunkha komanso mwauve, monga mmene makola ambiri amakhalira. Palibe makolo amene angasankhe kuti mwana wawo akabadwire m’malo amenewa ngati patakhala malo ena abwinopo. Makolo ambiri amayesetsa kusamalira kwambiri ana awo. Ndiye kodi mukuganiza kuti Mariya ndi Yosefe akanasankha dala kuti Mwana wa Mulungu abadwire malo osasamalika chonchi?

Ngakhale kuti sakanatha kupeza malo abwino, iwo sanakhumudwe koma anayesetsa kuchita zimene akanatha mogwirizana ndi kupeza kwawo. Mwachitsanzo taonani kuti Mariya anam’samalira yekha mwanayo, anamukulunga bwinobwino ndi nsalu. Kenaka anamugoneka modyera ziweto kuti azimva kutenthera n’kugona tulo tabwino. Mariya sanalole kuti kuganizira mavuto awo kumulepheretse kuchita zimene akanatha posamalira mwana wake. Iyeyu pamodzi ndi Yosefe ankadziwa kuti chinthu chofunika kwambiri ndicho kum’samalira mwanayo mwauzimu. (Deuteronomo 6:6-8) Masiku ano, makolo anzeru amaonanso kuti kusamalira ana awo mwauzimu m’dziko losakonda Mulunguli n’kofunika kwambiri kuposa zinthu zonse.

Alendo Anawalimbikitsa

Kenaka panamveka phokoso mwadzidzidzi. Abusa anangotulukira m’kholalo pofuna kudzaona banjalo, koma makamaka mwanayo. Abusa amenewa anali ndi chimwemwe chodzaza tsaya. Iwo anali atayenda mothamanga kuchokera kumapiri kumene ankadyetsa ziweto zawo. * Ndiye anasimbira makolowo zinthu zodabwitsa zimene anaona. Anawauza kuti ali ku phiriko, mngelo anaonekera mwadzidzidzi pakati pausiku. Ulemerero wa Yehova unaonekera ponsepo ndipo mngeloyo anawauza kuti Khristu, kapena kuti Mesiya, wabadwa ku Betelehemu. Anawauzanso kuti mwanayo akam’peza modyera ziweto atakulungidwa m’nsalu. Kenaka panachitika chinthu china chodabwitsa kwambiri. Anaona chigulu cha angelo chikuimba za ulemerero wa Yehova.

N’zosadabwitsa kuti abusawa, omwe anali anthu wamba, anafika ku Betelehemu akuthamanga. Ayenera kuti anasangalala mosaneneka kuona mwanayo ali gonee modyera ziweto, monga mmene mngelo uja anawauzira. Ataona zimenezi sanangochoka osauzako anthu ena nkhani yabwinoyi, koma ‘anafotokoza zimene anauzidwa ndipo onse amene anamva anadabwa ndi zimene abusawo anali kuwauza.’ (Luka 2:17, 18) N’zoonekeratu kuti atsogoleri achipembedzo ankaona abusa ngati anthu achabechabe. Koma Yehova anasonyezeratu kuti abusawo ankawawerengera kwambiri, chifukwa cha kudzichepetsa, komanso kukhulupirika kwawo. Komano kodi alendowa analimbikitsa bwanji Mariya?

Panthawiyi Mariya anali wofooka chifukwa chobereka, komabe anamvetsera mwachidwi mawu onse amene abusawo ankanena. Komanso “Mariya anasunga mawu onsewa, ndi kuwalingalira mu mtima mwake.” (Luka 2:19) Mariya anali munthu woganiza kwambiri. Iye anadziwa kuti uthenga wa mngeloyo unali wofunika kwambiri. Anadziwa kuti Mulungu wake, Yehova, ankafuna kuti azindikire kuti mwana amene anaberekayo sanali munthu wamba. Motero Mariya sanangomvetsera chabe ayi. Iye anasunga mumtima mwake mawu onse amene anauzidwawo kuti aziwaganizira pafupipafupi kwa miyezi ndiponso zaka zambirimbiri m’tsogolo. Mfundo imeneyi ikusonyeza chinsinsi chimene chinam’thandiza Mariya kukhala ndi chikhulupiriro cholimba chimene anaonetsa pa moyo wake wonse.

Kodi inuyo mutsatira chitsanzo cha Mariya? Yehova watipatsa Mawu ake a choonadi m’Baibulo. Koma sitingapindule ndi choonadi chimenechi ngati sitikuchita nacho chidwi. Tingasonyeze chidwi chimenechi pophunzira Baibulo nthawi zonse. Tisamawerenge Baibulo ngati buku wamba ayi, koma tizidziwa kuti Baibulo ndi Mawu ouziridwa ndi Mulungu. (2 Timoteyo 3:16) Kenaka, monga Mariya, tiyenera kusunga mumtima mwathu zimene tikuwerengazo, n’kumazilingalira. Tikamasinkhasinkha zinthu zimene timawerenga m’Baibulo, n’kumaona njira zosiyanasiyana zimene tingagwiritsire ntchito malangizo a Yehova pa moyo wathu, chikhulupiriro chathu chidzalimba.

Mawu Enanso Amene Mariya Anasunga

Mwana uja atakwanitsa masiku 8, Mariya ndi Yosefe anapita naye kokadulidwa potsatira Chilamulo cha Mose, ndipo anam’patsa dzina loti Yesu, monga mmene Mulungu anawauzira. (Luka 1:31) Kenaka atakwanitsa masiku 40, anachoka naye ku Betelehemu n’kupita kukachisi wa ku Yerusalemu, yemwe sanali kutali kwenikweni. Atafika kumeneku anakapereka nsembe yowayeretsa. Nsembe imene iwo anapereka inali njiwa ziwiri kapena maunda awiri a nkhunda, mogwirizana ndi nsembe imene Chilamulo chinkalola kuti anthu osauka azipereka. Iwo sanalole kuti manyazi awalepheretse kupereka nsembeyi chifukwa choti sakanatha kukwanitsa nsembe ya nkhosa yamphongo ndi njiwa, monga mmene makolo ena ankachitira. Ndipotu atafika kukachisiku analimbikitsidwa kwambiri.​—Luka 2:21-24.

Ali kumeneko, munthu wina wokalamba dzina lake Simiyoni anawapeza n’kumuuza Mariya mawu enanso amene iye anawasunga mumtima mwake. Simiyoni analonjezedwa kuti sadzafa asanaone Mesiya, ndipo mzimu woyera wa Yehova unamuthandiza kuzindikira kuti mwana wa khanda wotchedwa Yesu uja ndiye anali Mpulumutsi amene analonjezedwayo. Iye anamuuzanso Mariya kuti tsiku lina adzawawidwa mtima kwambiri chifukwa cha zimene zidzachitike. Iye anati adzamva ngati kuti lupanga lalitali lapyoza moyo wake. (Luka 2:25-35) Zimenezi zinachitika patatha zaka zoposa 30, ndipo n’kutheka kuti mawu a Simiyoni ochititsa manthawa ndiwo anam’thandiza Mariya kupirira panthawi yovutayi. Simiyoni atachoka, panabwera mneneri wina wamkazi, dzina lake Anna. Iye ataona Yesu, anayamba kunena za mwanayu kwa aliyense amene anali kuyembekezera chipulumutso cha Yerusalemu.​—Luka 2:36-38.

Popita ndi mwana wawo ku kachisi wa Yehova ku Yerusalemu, Mariya ndi Yosefe anaganiza bwino kwambiri. Kwa mwanayo chimenechi chinali chiyambi chabwino cha kukhala munthu wopita ku kachisi wa Yehova mokhulupirika. Ali kukachisiko anachita zonse zimene akanatha potumikira Mulungu ndipo anamvakonso mawu owalimbikitsa kwambiri. N’zosakayikitsa kuti Mariya anachoka kumeneko chikhulupiriro chake chitalimbitsidwa ndiponso atamva mawu ambiri oti awalingalire mumtima mwake ndi kuuza anthu ena.

Masiku anonso n’zosangalatsa kwambiri kuona makolo akutsatira chitsanzo chimenechi. Makolo a Mboni za Yehova amatenga ana awo popita ku misonkhano yachikhristu nthawi zonse. Makolowa amayesetsa kuchita zimene angathe ponena mawu olimbikitsa kwa okhulupirira anzawo. Ndipo akamachoka kumisonkhanoyo amakhala atalimbikitsidwa, ali osangalala, ndiponso ali ndi zinthu zambiri zabwino zoti akauze ena. Mukuitanidwa kuti mukasonkhane nawo anthu amenewa. Mukadzatero, chikhulupiriro chanu chidzalimbitsidwa kwambiri, monga mmene zinalili ndi Mariya.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 10 Taonani kusiyana kwa mawu a m’lembali ndi mawu ofotokoza ulendo wa Mariya wa m’mbuyomo. Ponena za ulendo wa m’mbuyomo, Malemba amati: “Mariya ananyamuka . . . ndi kupita” kwa Elizabeti. (Luka 1:39) Panthawiyi Mariya sanam’funse kaye Yosefe, chifukwa anali atangotomerana, motero anangonyamuka. Komano atakwatiwa, Yosefe ndi amene akutchulidwa ngati mwini wa ulendowo, osati Mariya.

^ ndime 14 Masiku amenewo mzinda uliwonse unkakhala ndi malo ogona anthu apaulendo, kaya ndi oyenda pansi kapena paziweto.

^ ndime 19 Mfundo yakuti panthawiyi abusawa anali kuphiri posamalira ziweto zawo ikutsimikizira zimene Baibulo limasonyeza zakuti: Khristu sanabadwe m’mwezi wa December chifukwa panthawiyi ziweto sankapita nazo kutali. Choncho ayenera kuti anabadwa cha kumayambiriro kwa October.

[Chithunzi patsamba 25]

Simiyoni anadalitsidwa poona Mpulumutsi wolonjezedwa