Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Khalani Otsanzira Mulungu”

“Khalani Otsanzira Mulungu”

Yandikirani Mulungu

“Khalani Otsanzira Mulungu”

Aefeso 4:32–5:2

KUKOMA MTIMA, chifundo, kukhululuka ndiponso chikondi ndi makhalidwe amene anthu ambiri masiku ano sasonyeza. Nanga inuyo bwanji? Kodi mumtima mwanu munayamba mwamvapo kuti mukulephera kusonyeza makhalidwe amenewa ngakhale mukuyesetsa kutero? N’zotheka kumadziona kuti ndinu wokanika chifukwa cha makhalidwe oipa amene munazolowera, kapena zinthu zinazake zoipa zimene zinakuchitikirani muli mwana. Mungamaganize kuti zimenezi zimachititsa kuti musathe kusintha khalidwe lanu kuti mukhale munthu wabwino. Komatu Baibulo limatiphunzitsa mfundo yolimbikitsa kwambiri yakuti, Mlengi wathu amadziwa kuti anatilenga m’njira yoti tingathe kusintha khalidwe lathu n’kukhala ndi makhalidwe abwino.

Mawu a Mulungu amalimbikitsa Akhristu oona kuti: “Chifukwa chake, khalani otsanzira Mulungu, monga ana okondedwa.” (Aefeso 5:1) Mawu amenewa akusonyeza kuti Mulungu amakhulupirira kwambiri anthu amene amam’lambira. Kodi n’chifukwa chiyani amatero? Yehova Mulungu analenga munthu m’chifanizo Chake, monga mwa chikhalidwe Chake. (Genesis 1:26, 27) Motero Mulungu anapatsa anthu makhalidwe ofanana ndi makhalidwe ake. * Moti Baibulo likamalimbikitsa Akhristu kuti “khalani otsanzira Mulungu,” zili ngati kuti Yehova akuwauza kuti: ‘Sindimakukayikirani ngakhale pang’ono. Ngakhale kuti ndinu opanda ungwiro, ndikudziwa kuti mungathe ndithu kutsanzira makhalidwe anga.’

Kodi ena mwa makhalidwe a Mulungu amene tingatsanzire ndi ati? Mavesi oyandikana ndi vesi limene pachoka mawu amenewa amayankha funso limeneli. Onani kuti popereka malangizo akuti titsanzire Mulungu, Paulo anayamba ndi mawu akuti “chifukwa chake.” Mawu amenewa akugwirizanitsa mawu a m’vesili ndi mawu amene ali m’mavesi am’mbuyo mwake, omwe akunena za kukoma mtima, chifundo chachikulu ndi kukhululuka. (Aefeso 4:32; 5:1) Atapereka malangizo akuti tizitsanzira Mulunguwa, m’vesi lotsatira Paulo akuuza Akhristu kuti azisonyeza chikondi chenicheni pa moyo wawo. (Aefeso 5:2) Kunena zoona, Yehova Mulungu ndi chitsanzo chathu chabwino kwambiri pankhani yosonyeza kukoma mtima, chifundo chenicheni, kukhululuka ndi mtima wonse ndiponso chikondi.

N’chifukwa chiyani tiyenera kutsanzira Mulungu? Taonani mawu olimbikitsa amene ali m’malangizo a Paulo akuti: “Khalani otsanzira Mulungu, monga ana okondedwa.” Kodi mawu amenewa si olimbikitsa? Yehova amaona olambira ake ngati ana ake okondedwa kwambiri. Akhristu oona amayesetsa kutsanzira Atate wawo wakumwamba mofanana ndi mwana amene amayesetsa kutsanzira bambo ake.

Yehova sakakamiza anthu kuti azimutsanzira. Koma anatilemekeza potipatsa ufulu wosankha tokha zochita. Motero zili kwa inu kusankha kutsanzira Mulungu kapena ayi. (Deuteronomo 30:19, 20) Musaiwale kuti inuyo mungathe kutsanzira makhalidwe a Mulungu. Koma kuti muthe kutsanzira Mulungu muyenera kum’dziwa kaye kuti ndi wotani. Baibulo lingakuthandizeni kuphunzira za makhalidwe ake ndiponso njira zonse za Mulungu. Iye ali ndi makhalidwe apamwamba kwambiri moti anthu ambiri akopeka nawo n’kuyamba kumutsanzira.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 2 Lemba la Akolose 3:9, 10 limasonyeza kuti mawu akuti tinalengedwa m’chifanizo cha Mulungu amatanthauza kuti tili ndi makhalidwe ofanana ndi a Mulungu. Anthu amene akufuna kukondweretsa Mulungu amalimbikitsidwa kuti avale “umunthu watsopano,” umene “ukukhalitsidwa watsopano, kukhala wogwirizana ndi chifaniziro cha [Mulungu] amene anaulenga.”