Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mukudziwa?

Kodi Mukudziwa?

Kodi Mukudziwa?

N’chifukwa chiyani Ayuda ankayamba madzulo kusunga Sabata?

Mmene Yehova ankapatsa anthu ake lamulo lonena za Tsiku la Chitetezo, anati: “Musamagwira ntchito iliyonse tsiku limenelo . . . Likhale ndi inu Sabata lakupumula . . . Kuyambira madzulo kufikira madzulo musunge Sabata lanu.” (Levitiko 23:28, 32) Lamulo limenelo limasonyeza kuti tsiku lililonse linkayamba madzulo, dzuwa litalowa, ndipo linkatha madzulo a tsiku lotsatira. Motero, umu ndi mmene Ayuda ankawerengera masiku.

Mulungu ndi amene anakhazikitsa njira yowerengera masiku imeneyi. Nkhani yonena za tsiku loyamba kulenga zinthu imati: “Panali madzulo ndipo panali mmawa, tsiku loyamba.” Masiku otsatirawo ankawerengedwanso chimodzimodzi, kuyambira “madzulo.”​—Genesis 1:5, 8, 13, 19, 23, 31.

Si Ayuda okha amene ankawerengera masiku m’njira imeneyi. Mwachitsanzo, anthu a ku Atene, ku Numidiya, ndiponso ku Foinike ankachitanso chimodzimodzi. Koma anthu a ku Babulo ankawerengera kuti tsiku limayamba m’mawa dzuwa likatuluka, ndipo Aiguputo ndi Aroma ankawerengera kuti tsiku limayambira pakati pa usiku n’kuthanso pakati pa usiku wa tsiku lotsatira. Zimenezi n’zimenenso tikutsatira masiku ano. Ayuda masiku ano amasungabe Sabata ndipo amayamba madzulo dzuwa likangolowa, n’kuthanso madzulo a tsiku lotsatira.

Kodi mawu akuti “ulendo wa tsiku la sabata” amatanthauza chiyani?

Ophunzira a Yesu anali pa phiri la Maolivi pamene anaona Yesu akukwera kumwamba. Kenako anabwerera ku Yerusalemu ndipo anayenda “ulendo wa tsiku la sabata.” (Machitidwe 1:12) Munthu ankatha kuyenda makilomita 30 kapena kuposerapo patsiku. Koma phiri la Maolivi silili kutali choncho ndi Yerusalemu. Ndiyeno kodi mawu akuti “ulendo wa tsiku la sabata” amatanthauza chiyani?

Tsiku la Sabata linali tsiku limene Aisiraeli ankapuma pa ntchito zawo zonse. Patsikulo iwo sankaloledwa ngakhale kukoleza moto kunyumba kwawo. ( Eksodo 20:10; 35:2, 3) Yehova analamula kuti: “Khalani yense m’malo mwake, munthu asatuluke m’malo mwake tsiku lachisanu ndi chiwiri.” (Eksodo 16:29) Lamulo limeneli linapatsa Aisiraeli mpata wopuma ku zintchito zawo zonse ndiponso woganizira mozama zinthu zauzimu.

Arabi okonda kuika malamulo ambirimbiri sanakhutire ndi mfundo zimene Yehova anawapatsa m’Chilamulo chake, choncho iwo ankakonda kuwonjezera malamulo ambirimbiri. Mwachitsanzo, iwo anachita kunena mtunda umene munthu anayenera kuyenda patsiku la sabata mwina popita kukalambira. Pamfundo imeneyi buku lina linati: “Chifukwa cha malamulo okhwima okhudza kusunga Sabata . . . , anakhazikitsa lamulo loti pasabata, Aisiraeli asamayende ulendo wopitirira mtunda wina wake umene unkatchedwa kuti ulendo wa tsiku la sabata.” Mtunda umenewu unali wotalika mamita 890 kapena kuti wosakwana kilomita imodzi.​—Cyclopedia of Biblical, Theological, and Ecclesiastical Literature.

[Chithunzi patsamba 11]

Mmene Mzinda wa Yerusalemu Umaonekera Mukaima pa Phiri la Maolivi