Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Anthu Ambiri Amakhulupirira za Helo

Anthu Ambiri Amakhulupirira za Helo

Anthu Ambiri Amakhulupirira za Helo

“Ndinkalota zoopsa. Nthawi zina ndinkalota ndikupsa m’moto wa helo. M’malotowo ndinkaponyedwa m’moto ndipo ndinkadzidzimuka kwinaku ndikukuwa. Komatu ngakhale ndinkalota zimenezi, ndinkayesetsa pamoyo wanga kuti ndisachimwe.”​—Arline.

KODI inu mumakhulupirira kuti helo ndi malo ozunzirako anthu ochimwa? Anthu ambiri amakhulupirira zimenezi. Mwachitsanzo, mu 2005, katswiri wina wa maphunziro a zaumulungu wa pa Yunivesite ya St. Andrews ku Scotland, anapeza kuti 33 peresenti ya atsogoleri a zipembedzo a ku Scotland amakhulupirira kuti anthu omwe saopa Mulungu “adzazunzika maganizo kosatha m’helo.” Ndipo okwana 20 peresenti amakhulupirira kuti anthu amene ali kuhelo amazunzika ndi ululu m’thupi mwawo.

M’mayiko ambiri, anthu ochuluka amakhulupirira za helo. Mwachitsanzo ku United States, bungwe la Gallup litachita kafukufuku womva maganizo a anthu mu 2007, linapeza kuti pafupifupi 70 peresenti ya anthu amene anafunsidwa amakhulupirira za helo. Ngakhale m’mayiko amene anthu ambiri sapembedza, anthu amakhulupirirabe za helo. Kafukufuku amene bungwe la Gallup linachita ku Canada mu 2004 anasonyeza kuti anthu okwana 42 peresenti amakhulupirira za helo. Ndipo ku Great Britain, anthu okwana 32 peresenti ananena motsimikiza kuti kuli helo.

Zimene Atsogoleri Azipembedzo Amaphunzitsa

Atsogoleri ambiri azipembedzo, asiya kuphunzitsa kuti helo ndi malo enieni amoto kumene anthu amakazunzidwa. M’malo mwake, iwo akulimbikitsa maganizo ofanana ndi amene ali mu buku la Catechism of the Catholic Church, limene linafalitsidwa mu 1994. Bukuli limati: “Chilango chachikulu cha helo ndicho kutalikirana ndi Mulungu kosatha.”

Ngakhale zili choncho, anthu ambiri akukhulupirirabe kuti helo ndi malo amene anthu amazunzika maganizo kapena kuzunzika ndi ululu m’thupi mwawo. Anthu amene amalimbikitsa chiphunzitso chimenechi amanena kuti ndi cha m’Baibulo. Mwachitsanzo, R. Albert Mohler, pulezidenti wa Southern Baptist Theological Seminary, ananena mwamphamvu kuti: “Imeneyitu ndi mfundo ya m’Malemba.”

N’chifukwa Chiyani Mufunika Kudziwa Zoona Zake?

Ngati helo alidi malo ozunzirako anthu, m’pake kuopa. Koma ngati chiphunzitso cha helo n’chabodza, ndiye kuti atsogoleri azipembedzo amene amaphunzitsa zimenezi amasokoneza anthu ndipo amachititsa kuti anthu amene amakhulupirira zimenezi azivutika maganizo ndi zinthu zimene kulibe. Komanso amatukwanitsa Mulungu.

Nanga kodi Baibulo, limene ndi Mawu a Mulungu, limanena chiyani pankhani imeneyi? M’nkhani zotsatira tigwiritsa ntchito Mabaibulo a Akatolika ndi Apolotesitanti poyankha mafunso atatu awa: (1) Kodi chimachitika n’chiyani munthu akamwalira? (2) Kodi Yesu anaphunzitsa chiyani za helo? (3) Kodi kudziwa zoona zake za helo kungakuthandizeni bwanji?