Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Chionetsero Chokhala ndi Cholinga

Chionetsero Chokhala ndi Cholinga

Chionetsero Chokhala ndi Cholinga

“KODI amachitako chiyani kumeneku?” Ambiri mwa anthu amene amadutsa pafupi ndi likulu la Mboni za Yehova ku Mogale City (Krugersdorp), kufupi ndi Johannesburg, ku South Africa, amafunsa zimenezi. Choncho Mbonizo zinakonza chionetsero pamaofesi a nthambi yawoyi pa October 12 ndi 13, 2007. Chionetserochi chinali ndi zolinga ziwiri. Choyamba, kuthetsa nkhani zabodza zimene anthu amanena zokhudza malowa, ndipo chachiwiri chinali kudziwitsa anthu zimene nthambiyo imachita pothandiza ntchito imene Yesu Khristu analamula.​—Mateyo 28:19, 20.

Anthu ogwira ntchito pamaofesi a nthambiyi anaika zikwangwani zazikulu panjira yolowera, zoitanira anthu ku chionetserochi, ndipo anapereka makadi apadera kwa anthu apafupi. Anthu amene amagulitsa katundu wawo ku nthambiyi ndiponso mabanja awo anaitanidwa. Kodi zotsatira zake zinali zotani? Alendo oposa 500 amene si Mboni anabwera kudzaona malowa.

Iwo anachita chidwi kwambiri ndi makina osindikizira, otchedwa MAN Roland Lithoman, amene amasindikiza magazini okwana 90,000 pa ola limodzi. Chinanso chimene alendowa anachita nacho chidwi ndi malo aakulu opakirirako mabuku. Anthu ogwira ntchito kumeneku amapakira mabuku oposa matani 14 patsiku. Alendowa anachitanso chidwi ndi malo amene amaikirako mabuku zikuto. Mboni zogwira ntchito m’madipatimenti osiyanasiyana zinakonza zikwangwani zochititsa chidwi, kuphatikizapo chosonyeza mbiri ya ntchito yosindikiza mabuku, kuyambira pa makina a Gutenberg mpaka kufika pa makina osindikizira amakono. Chikwangwani china chinasonyeza mmene nthambiyi imasamalira chilengedwe. Mwachitsanzo, chinasonyeza makina apadera amene amachotsa mpweya ndi fungo loipa kuchokera m’zipangizo zoumitsira za makina osindikizira, komanso amasefa ndi kutulutsa fumbi la mapepala lomwe amakalitaya.

Nyuzipepala ina inalemba nkhani imene inafotokoza kuti anthu 700 ogwira ntchito amene amakhala panthambiyi, ndi “atumiki oikidwa amene anadzipereka kwa Yehova.” Inanenanso kuti “malowa ndi aukhondo kwambiri” ndipo kumalo osindikizira mabuku “zinthu zonse zimachitika panthawi yake.” Mwamuna wina yemwe ankatsutsa Mboni za Yehova anafikanso pa chionetserochi. Pambuyo pake, iye analemba kalata imene inati: “Mukuchita bwino. Ndi zosowa kuona zinthu zabwino kwambiri ngati zimenezi.”

Alendo ambiri anayamikira kwambiri chifukwa choitanidwa kudzaona malowa ndipo anadabwa kuona kuti nthambiyi ili ndi mabuku ofotokoza Baibulo m’zinenero 151, ndiponso imasindikiza mabuku amene amatumizidwa m’mayiko 18 kum’mwera ndi pakati pa Africa. Maofesi a nthambi a Mboni za Yehova padziko lonse amalola alendo kubwera kudzaona malo nthawi ya ntchito. Tikukulimbikitsani kufunsa nthambi ya dziko lanu za nthawi yoona malo.

[Chithunzi patsamba 14]

Alendo akufika panthambi

[Chithunzi patsamba 14]

Khadi loitanira alendo

[Zithunzi patsamba 15]

Nthambi ya South Africa ku Mogale City, South Africa

[Chithunzi patsamba 15]

Makina osindikizira a MAN Roland Lithoman

[Chithunzi patsamba 15]

Koikira mabuku zikuto

[Chithunzi patsamba 15]

Kopakirira mabuku